NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) August 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa September 30 mpaka October 27, 2019.

“Sitikubwerera M’mbuyo”

Kodi zimene tikuyembekezera m’tsogolo zingatithandize bwanji kuti tisabwerere m’mbuyo?

Chikondi Chanu Chipitirire Kukula

Kalata yopita kumpingo wa Afilipi imatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti chikondi chathu chipitirire kukula ngakhale titakumana ndi mavuto.

“Anthu Okumvera” Adzapulumuka

Kodi tingathandize bwanji achibale athu kuti aphunzire za Yehova?

Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Utumiki Wathu Ukasintha

Akhristu ambiri amavutika kusiya utumiki umene ankakonda kwambiri. N’chiyani chingawathandize kuzolowera utumiki watsopano?

Chikhulupiriro Chimatipatsa Mphamvu

Chikhulupiriro n’champhamvu kwambiri. Chingatithandize kulimbana ndi mavuto okhala ngati phiri.

Yohane M’batizi—Chitsanzo Chabwino pa Nkhani Yokhalabe Wosangalala

Kodi tingatani kuti tizitumikirabe Mulungu mosangalala ngakhale patachitika zinthu zokhumudwitsa?