Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 32

Achinyamata, Pitirizani Kupita Patsogolo Mwauzimu Pambuyo Pobatizidwa

Achinyamata, Pitirizani Kupita Patsogolo Mwauzimu Pambuyo Pobatizidwa

“Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi.”​—AEF. 4:15.

NYIMBO NA. 56 Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene achinyamata ambiri akwanitsa kale kuchita?

 CHAKA chilichonse, Akhristu ambiri achinyamata amabatizidwa. Kodi inunso munabatizidwa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti abale ndi alongo komanso Yehova amasangalala chifukwa cha zimenezo. (Miy. 27:11) Taganizirani zimene mwakwanitsa kale kuchita pofika pano. Mwakhala mukuphunzira Baibulo mwakhama mwina kwa zaka zingapo. Kuphunzirako kwakuthandizani kutsimikizira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Kuposa pamenepo, munadziwa komanso kuyamba kukonda kwambiri mwiniwake wa buku lopatulikali. Chifukwa chokonda kwambiri Yehova, munafika podzipereka kwa iye n’kubatizidwa. Zimenezitu ndi zosangalatsa kwambiri.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

 2 N’zosakayikitsa kuti chikhulupiriro chanu chinkayesedwa pamene munkayesetsa kuti mubatizidwe. Komabe pamene mukukula, muzikumana ndi mayesero ena. Satana ayesetsa kukuchititsani kuti musiye kukonda Yehova komanso kumutumikira. (Aef. 4:14) Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova n’kumakwaniritsa lonjezo lomwe munapanga podzipereka kwa iye? Muyenera kupitirizabe kupita patsogolo n’kumachita ‘khama’ kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu. (Aheb. 6:1) Koma kodi mungachite bwanji zimenezi?

KODI MUNGATANI KUTI MUPITIRIZE KUPITA PATSOGOLO?

3. Kodi Akhristu onse amafunika kuchita chiyani pambuyo pobatizidwa?

3 Tonsefe tikabatizidwa timafunika kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Efeso. Iye anawalimbikitsa kuti akhale ‘achikulire’ mwauzimu. (Aef. 4:13) Zinali ngati akuwauza kuti, ‘Pitirizani kupita patsogolo.’ Tingamvetse zimene Paulo anatanthauza pomwe anayerekezera kukula mwauzimu ndi zimene zimachitika mwana akamakula. Makolo amanyadira komanso kusangalala kwambiri mwana wawo akangobadwa. Koma sikuti mwanayo amangokhalabe wakhanda mpaka kalekale. N’kupita kwa nthawi amayenera kukula kapena kuti ‘kusiya zachibwana.’ (1 Akor. 13:11) Ndi mmenenso zimakhalira ndi Akhristufe. Tikabatizidwa, timafunika kupitirizabe kukula mwauzimu. Tsopano tiyeni tione mfundo zina zimene zingatithandize.

4. Kodi ndi khalidwe liti limene lingakuthandizeni kuti mupitirizebe kupita patsogolo mwauzimu? Fotokozani. (Afilipi 1:9)

4 Muzikonda kwambiri Yehova. Panopa mumakonda kale kwambiri Yehova. Koma mukhoza kuwonjezera chikondi chanucho. Motani? Mtumwi Paulo anatchula njira imodzi yochitira zimenezi pa Afilipi 1:9. (Werengani.) Paulo anapemphera kuti chikondi cha Akhristu a ku Filipi “chipitirire kukula.” Choncho tikhoza kukulitsa chikondi chathu pa Yehova. Tingachite zimenezi popitirizabe “kudziwa zinthu molondola, komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.” Tikamamudziwa bwino Yehova, m’pamenenso timayamba kumukonda kwambiri komanso kuyamikira makhalidwe ake ndiponso mmene amachitira zinthu. Timakhala ofunitsitsa kumusangalatsa n’kumapewa chilichonse chomwe chingamukhumudwitse. Timayesetsa kuzindikira chifuniro chake komanso mmene tingachitire zinthu mogwirizana ndi chifuniro chakecho.

5-6. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizikonda kwambiri Yehova? Fotokozani.

5 Tingayambe kukonda kwambiri Yehova ngati titadziwa bwino Mwana wake, yemwe ankasonyeza bwino kwambiri makhalidwe a Atate wake. (Aheb. 1:3) Njira yabwino imene tingadziwire Yesu, ndi kuphunzira mabuku 4 a Uthenga Wabwino. Ngati mulibe chizolowezi chowerenga Baibulo tsiku lililonse, bwanji osayamba panopa? Mukamawerenga nkhani zokhudza Yesu, muziganizira kwambiri makhalidwe ake. Iye anali wofikirika moti nthawi ina ananyamula ana m’manja mwake. (Maliko 10:13-16) Ankachititsa ophunzira ake kukhala omasuka moti akamacheza nawo, iwo sankaopa kufotokoza mmene ankamvera. (Mat. 16:22) Pochita zimenezi, Yesu ankatsanzira Atate wake wakumwamba. Yehova nayenso ndi wofikirika. Tikhoza kupemphera kwa iye ndipo tikamapemphera tingamuuze zonse zamumtima mwathu. Ndife otsimikiza kuti sangatiweruze chifukwa cha zimenezo. Iye amatikonda komanso amatidera nkhawa.​—1 Pet. 5:7.

6 Yesu ankachitira chifundo anthu. Mtumwi Mateyu analemba kuti: “Poona chikhamu cha anthu, iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Ndiye kodi nayenso Yehova amamva bwanji? Yesu anati: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.” (Mat. 18:14) Zimenezitu n’zolimbikitsa kwambiri. Choncho tikamudziwa bwino Yesu, timayambanso kukonda kwambiri Yehova.

7. Kodi kucheza ndi Akhristu olimba mwauzimu kungakuthandizeni bwanji?

7 Mungaphunzirenso mmene mungakulitsire chikondi komanso mungapite patsogolo mukamacheza ndi abale ndi alongo olimba mwauzimu mumpingo mwanu. Muziona mmene akusangalalira. Iwo samanong’oneza bondo chifukwa chosankha kutumikira Yehova. Muziwapempha kuti akufotokozereni zimene zakhala zikuwachitikira pa utumiki wawo. Mukafuna kusankha zochita pa nkhani inayake yofunika, muziwapempha malangizo. Muzikumbukira kuti “pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.”​—Miy. 11:14.

Kodi mungakonzekere bwanji zokanena kusukulu akamakaphunzitsa zoti zamoyo zinachita kusintha? (Onani ndime 8-9)

8. Kodi mungatani ngati nthawi zina mumakayikira zimene Baibulo limanena?

8 Musamakayikire zimene mumakhulupirira. Monga mmene taonera  mundime 2, Satana amayesetsa kuti akulepheretseni kupita patsogolo mwauzimu. Njira ina imene angachitire zimenezo ndi kukuchititsani kuti muzikayikira zinthu zina zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, mwina mukhoza kumva mfundo yosalemekeza Mulungu yakuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. N’kutheka kuti muli wamng’ono munali musanaganizirepo kwambiri nkhani imeneyi. Koma pamene mukukula, mwayamba kuphunzira zimenezi kusukulu. Zimene aphunzitsi anu amanena polimbikitsa mfundoyi, zingaoneke ngati zomveka. Komabe n’kutheka kuti iwo sanafufuze kuti apeze umboni wotsimikizira kuti kuli Mlengi. Kumbukirani mfundo ya pa Miyambo 18:17, yomwe imati: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.” M’malo momangokhulupirira zilizonse zimene mwamva kusukulu, muzifufuza mosamala mfundo za choonadi za m’Mawu a Mulungu. Muzifufuza m’mabuku athu. Muzicheza ndi abale ndi alongo omwe poyamba ankakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha. Muziwafunsa kuti akufotokozereni chimene chinawachititsa kuyamba kukhulupirira zoti kuli Mlengi yemwe amatikonda. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muziganizira umboni woti kuli Mlengi.

9. Kodi mukuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Melissa?

9 Mlongo wina dzina lake Melissa, anapindula kwambiri chifukwa chofufuza nkhani yokhudza kulengedwa kwa zinthu. * Iye anati: “Kusukulu, nkhani yoti zinthu zinachita kusintha imafotokozedwa m’njira yoti izioneka ngati ndi yoona. Poyamba sindinkafuna kufufuza nkhaniyi, chifukwa ndinkaopa kuti mwina ndingapeze kuti nkhani yoti zinthu zinachita kusintha ndi yoona. Koma ndinayamba kuganizira mfundo yoti Yehova safuna kuti tizingokhulupirira zinthu zimene zilibe umboni. Choncho ndinayamba kufufuza za nkhaniyi. Ndinawerenga buku lakuti, Is There a Creator Who Cares About You? komanso kabuku kakuti, Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? ndi kakuti, Mmene Moyo Unayambira​—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri. Mabuku amenewa ndi omwe ndinkafunikiradi. Ndipo ndinkalakalaka ndikanawawerenga kalekale.”

10-11. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupitirize kukhala ndi makhalidwe abwino? (1 Atesalonika 4:3, 4)

10 Muzipewa makhalidwe oipa. Pamene achinyamata akukula, chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu ndipo mwina ena angamawakakamize kuti achite chiwerewere. Satana amafuna kuti muzingochita zimene mumalakalaka. Ndiye kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mupewe kuchita makhalidwe oipa? (Werengani 1 Atesalonika 4:3, 4.) Mukamapemphera muzimufotokozera Yehova mmene mukumvera. Ndipo muzimupempha kuti akupatseni mphamvu. (Mat. 6:13) Kumbukirani kuti Yehova amafuna kukuthandizani, osati kukuweruzani. (Sal. 103:13, 14) Komanso Mawu a Mulungu angakuthandizeni. Melissa yemwe tamutchula uja ankavutika ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. Iye anati: “Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kunandithandiza kuti ndisagonje. Kunkandithandiza kukumbukira kuti ndine wa Yehova ndipo ndikufuna kumutumikira.”​—Sal. 119:9.

11 Musamayese kulimbana ndi mavuto anu panokha. Muzifotokozera makolo anu zimene mukulimbana nazo. N’zoona kuti kukambirana nkhani ngati zimenezi si kophweka koma n’kofunika kwambiri. Melissa anati: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize kukhala wolimba mtima ndipo ndinafotokozera bambo anga za vuto langa. Nditachita zimenezi ndinayamba kumva bwino mumtimamu chifukwa ndinadziwa kuti Yehova akusangalala nane.”

12. Kodi mungatani kuti muzisankha zochita mwanzeru?

12 Muzitsogoleredwa ndi mfundo za m’Baibulo. Mukamakula, pang’ono ndi pang’ono makolo anu adzayamba kukupatsani ufulu wosankha nokha zochita. Komabe dziwani kuti simunafike podziwa zambiri. Ndiye kodi mungatani kuti musachite zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wanu ndi Yehova? (Miy. 22:3) Mlongo wina dzina lake Kari, anafotokoza zimene zinamuthandiza kuti azisankha zochita mwanzeru. Iye anazindikira kuti Mkhristu wolimba mwauzimu safunikira malamulo pa nkhani ina iliyonse. Iye anati, “Ndinkafunika kumvetsa mfundo za m’Baibulo m’malo mongodziwa malamulo.” Mukamawerenga Baibulo, muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikuwerengazi zikundiuza chiyani zokhudza maganizo a Yehova? Kodi ndikupezamo mfundo zimene zingandithandize kuchita zoyenera? Nanga kodi ndingapindule bwanji ngati nditagwiritsa ntchito mfundozo?’ (Sal. 19:7; Yes. 48:17, 18) Mukamawerenga Baibulo komanso kuganizira mozama mfundo zake, zidzakhala zosavuta kuti muzisankha zochita zimene zingasangalatse Yehova. Pamene mukupitiriza kupita patsogolo, mudzaona kuti simukufunikira malamulo pa nkhani iliyonse chifukwa mudzamvetsa mmene Yehova amaganizira pa nkhani zosiyanasiyana.

Kodi mlongo wina wachitsikana anasankha anzake otani? (Onani ndime 13)

13. Kodi anzanu abwino angakuthandizeni bwanji? (Miyambo 13:20)

13 Muzisankha anzanu omwe amakonda Yehova. Monga tafotokozera kale, kusankha anzanu abwino kungakuthandizeni kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu. (Werengani Miyambo 13:20.) Pa nthawi ina mlongo wina dzina lake Sara sankasangalala. Koma panachitika zinthu zina zimene zinachititsa kuti ayambirenso kusangalala. Sara anati: “Ndinapeza anzanga abwino pa nthawi yoyenera. Ine ndi mlongo wina wachitsikana tinkakumana mlungu uliwonse kuti tiphunzire Nsanja ya Olonda. Mnzanga winanso anandithandiza kuti ndiyambe kumayankha pamisonkhano. Chifukwa chothandizidwa ndi anzangawa, ndinayamba kuona kuti kuphunzira pandekha komanso kupemphera n’zofunika kwambiri. Zimenezi zinandithandiza kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndipo ndinayambiranso kusangalala.”

14. Kodi Julien anatani kuti apeze anzake abwino?

14 Kodi mungapeze bwanji anzanu omwe angakuthandizeni? Julien yemwe panopa ndi mkulu anati: “Ndili wamng’ono, ndinkapeza anzanga abwino ndikamagwira ntchito yolalikira. Anzangawa anali akhama, ndipo anandithandiza kuona kuti munthu angamasangalale ndi utumiki. Choncho ndinayamba kukhala ndi cholinga chofuna kudzachita utumiki wa nthawi zonse. Ndinazindikiranso kuti ndinkataya mwayi wokhala ndi anzanga abwino chifukwa chongofuna kukhala ndi anzanga a msinkhu wanga okha. Patapita nthawi ndinakhalanso ndi anzanga abwino ku Beteli. Chitsanzo chawo chinandithandiza kuti ndizisankha bwino zosangalatsa zomwe zinachititsa kuti ndikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.”

15. Kodi Paulo anachenjeza chiyani Timoteyo pa nkhani ya anthu ocheza nawo? (2 Timoteyo 2:20-22)

15 Bwanji ngati mwazindikira kuti winawake mumpingo sangakhale munthu wabwino kucheza naye? Paulo ankadziwa kuti ena mumpingo wa Chikhristu woyambirira sankakonda zinthu zauzimu. Choncho anachenjeza Timoteyo kuti aziwapewa. (Werengani 2 Timoteyo 2:20-22.) Timaona kuti ubwenzi wathu ndi Atate wathu Yehova ndi wamtengo wapatali. Choncho sitiyenera kulola kuti aliyense asokoneze ubwenziwu, umene takhala tikuyesetsa mwakhama kuti tikhale nawo.​—Sal. 26:4.

KODI KUKHALA NDI ZOLINGA KUNGAKUTHANDIZENI BWANJI KUTI MUPITE PATSOGOLO?

16. Kodi mungakhale ndi zolinga ziti?

16 Muzikhala ndi zolinga zothandiza. Muzisankha zolinga zimene zingalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kukuthandizani kuti mukhale Mkhristu wolimba. (Aef. 3:16) Mwachitsanzo, mungasankhe kuti muziphunzira panokha komanso kuwerenga Baibulo nthawi zonse. (Sal. 1:2, 3) Kapenanso mungakonze zoti muzipemphera pafupipafupi komanso mochokera pansi pa mtima. Mwinanso mungaone kuti mukufunika kumadziletsa pa nkhani yosankha zosangalatsa komanso mmene mumagwiritsira ntchito nthawi yanu. (Aef. 5:15, 16) Yehova adzasangalala akaona kuti mukuyesetsa kupita patsogolo.

Nanga mlongoyu anadziikira cholinga chiti? (Onani ndime 17)

17. Kodi kuthandiza ena kungakuthandizeni bwanji?

17 Mungakhale Mkhristu wolimba mukamathandiza anthu ena. Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Mac. 20:35) Mudzapindula kwambiri mukamagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zanu pothandiza ena. Mwachitsanzo, mungakhale ndi cholinga choti muzithandiza achikulire komanso odwala mumpingo mwanu. Mwina mungamakawagulire zinthu kapenanso kuwathandiza mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zawo zamakono. Ngati ndinu m’bale, mungakhale ndi cholinga choti mukhale mtumiki wothandiza, kuti muzitumikira abale ndi alongo anu. (Afil. 2:4) Mungasonyezenso kuti mumakonda anthu omwe si a Mboni powalalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 9:36, 37) Ngati n’zotheka, mungadziikire cholinga choti muchiteko utumiki winawake wa nthawi zonse.

18. Kodi kuchita utumiki wa nthawi zonse kungakuthandizeni bwanji kuti mukule mwauzimu?

18 Kuchita utumiki wa nthawi zonse kungakuthandizeni kuti mupite patsogolo mwauzimu. Upainiya ungakutsegulireni mwayi wolowa nawo Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Mungathenso kukatumikira pa Beteli kapena kugwira nawo ntchito zomangamanga. Mpainiya wina wachitsikana dzina lake Kaitlyn ananena kuti, “Nditangobatizidwa, kulowa mu utumiki ndi abale ndi alongo odziwa zambiri ndi kumene kunandithandiza kwambiri kuti ndikule mwauzimu. Chitsanzo chawo chinandithandiza kuti ndidziwe mfundo zambiri za m’Baibulo komanso ndiwonjezere luso langa lophunzitsa.”

19. Kodi mudzapeza madalitso otani mukapitiriza kupita patsogolo mwauzimu?

19 Pamene mukupitiriza kupita patsogolo mwauzimu, mudzapeza madalitso ochuluka. Mudzapewa kugwiritsa ntchito mphamvu zanu pochita zinthu zosathandiza. (1 Yoh. 2:17) Mudzapewanso zotsatirapo zowawa zimene zimabwera chifukwa chosankha zinthu molakwika. M’malomwake zinthu zidzakuyenderani bwino ndipo mudzapeza chimwemwe chenicheni. (Miy. 16:3) Chitsanzo chanu chabwino chidzalimbikitsa Akhristu anzanu, achinyamata ndi achikulire omwe. (1 Tim. 4:12) Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti mudzakhala ndi mtendere ndiponso moyo wokhutira, zomwe zimabwera chifukwa choti Yehova akusangalala nanu komanso muli naye pa ubwenzi wolimba.​—Miy. 23:15, 16.

NYIMBO NA. 88 Ndidziwitseni Njira Zanu

^ Atumiki onse a Yehova amasangalala achinyamata akabatizidwa. Komabe pambuyo pobatizidwa, ophunzira atsopano ayenera kupitirizabe kupita patsogolo mwauzimu. Pofuna kuthandiza onse mumpingo, nkhaniyi ifotokoza zimene achinyamata omwe angobatizidwa kumene angachite kuti apitirizebe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

^ Mayina ena asinthidwa.