Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 33

Yehova Amayang’anira Anthu Ake

Yehova Amayang’anira Anthu Ake

“Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa.”—SAL. 33:18.

NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. N’chifukwa chiyani Yesu anapempha Yehova kuti aziyang’anira otsatira ake?

 PA USIKU wake womaliza, Yesu anapereka pemphero lapadera kwa Atate wake wakumwamba, lopempha kuti aziyang’anira otsatira ake. (Yoh. 17:15, 20) N’zoona kuti Yehova wakhala akuyang’anira, kusamalira komanso kuteteza anthu ake. Komabe Yesu ankadziwa kuti otsatira ake azidzatsutsidwa kwambiri ndi Satana. Yesu ankadziwanso kuti ophunzirawo adzafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti athe kupirira Mdyerekezi akamawaukira.

2. Mogwirizana ndi Salimo 33:18-20, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa tikamakumana ndi mavuto?

2 Dziko lolamulidwa ndi Satanali limachititsa kuti Akhristu oona azikumana ndi mavuto ambiri. Timakumana ndi mavuto omwe angatifooketse komanso angayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova. Koma monga mmene tionere munkhaniyi, sitiyenera kuopa. Yehova amatiyang’anira, amaona mavuto amene timakumana nawo ndipo nthawi zonse ndi wokonzeka kutithandiza. Tiyeni tsopano tione zitsanzo ziwiri za m’Baibulo zomwe zimasonyeza kuti “diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa.”​—Werengani Salimo 33:18-20.

TIKAMADZIMVA KUTI TILI TOKHATOKHA

3. Kodi ndi pa nthawi ziti pamene tingamadzimve kuti tili tokhatokha?

3 Ngakhale kuti tili ndi abale ndi alongo ambiri, nthawi zina tingamadzimve kuti tili tokhatokha. Mwachitsanzo, achinyamata angamaone kuti ali okhaokha akamafotokoza zomwe amakhulupirira kwa anzawo a m’kalasi kapena akasamukira mumpingo watsopano. Ambirife tingavutike kapena kufooka poganiza kuti timafunika kulimbana ndi maganizo ofooketsawa patokha. N’kutheka kuti tingamaope kuuza ena mmene tikumvera poganiza kuti mwina satimvetsa. Ndipo mwina nthawi zina tingamaganize kuti palibe amene amatiganizira. Kaya timamva kuti tili tokhatokha pa zifukwa ziti, zimenezi zingachititse kuti tiziona kuti tilibe pogwira komanso tikhale ndi nkhawa. Komatu Yehova safuna kuti tizimva choncho. N’chifukwa chiyani tikutero?

4. N’chifukwa chiyani mneneri Eliya ananena kuti: “Ndatsala ndekhandekha”?

4 Taganizirani chitsanzo cha Eliya yemwe anali munthu wokhulupirika. Iye anakhala akuthawathawa kwa masiku oposa 40 chifukwa chakuti Yezebeli analumbira kuti amupha. (1 Maf. 19:1-9) Pamapeto pake ali yekhayekha kuphanga, iye anauza Yehova kuti: “Ine ndatsala ndekhandekha [mneneri].” (1 Maf. 19:10) Komatu panalinso aneneri ena m’dzikolo. Obadiya anakwanitsa kupulumutsa aneneri ena 100 kuti Yezebeli asawaphe. (1 Maf. 18:7, 13) Ndiyeno n’chifukwa chiyani Eliya ankadzimva kuti anali yekhayekha? Kodi ankaganiza kuti aneneri onse omwe Obadiya anawateteza aja anali atafa? Kodi mwina anamva choncho chifukwa anthu ena sanamutsatire polambira Yehova, pambuyo poti Yehovayo anasonyeza kuti ndi Mulungu woona pa phiri la Karimeli? Kapena mwina iye ankaona kuti palibe amene akudziwa zoti moyo wake uli pangozi kapenanso mwina ankaganiza kuti palibe amene ankamudera nkhawa? Nkhaniyi sifotokoza zonse zokhudza mmene Eliya ankamvera. Koma chomwe tikudziwa n’chakuti Yehova ankamvetsa chifukwa chake Eliya ankadzimva kuti ali yekhayekha ndipo ankadziwa mmene angamuthandizire.

Tikamadzimva kuti tili tokhatokha, kodi ndi mfundo yolimbikitsa iti yomwe tingaphunzire pa zimene Yehova anachita pothandiza Eliya? (Onani ndime 5-6)

5. Kodi Yehova anatsimikizira bwanji Eliya kuti sanali yekhayekha?

5 Yehova anathandiza Eliya m’njira zingapo. Iye analimbikitsa Eliya kuti afotokoze mmene ankamvera. Kawiri konse anamufunsa Eliya kuti: “Ukufuna chiyani kuno?” (1 Maf. 19:9, 13) Pa ulendo uliwonse Yehova ankamvetsera pamene Eliya ankafotokoza za mumtima mwake. Kenako Yehova anamusonyeza kuti anali naye komanso ndi wamphamvu kwambiri. Anatsimikizira Eliya kuti panalinso anthu ambiri omwe ankamulambira. (1 Maf. 19:11, 12, 18) N’zosakayikitsa kuti Eliya anamva bwino atafotokozera Yehova za mumtima mwake komanso kuona mmene anamuyankhira. Yehova anapatsa Eliya ntchito zofunika zingapo kuti agwire. Anamuuza kuti akadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya Siriya, Yehu akhale mfumu ya Isiraeli komanso Elisa akhale mneneri. (1 Maf. 19:15, 16) Pom’patsa zochita zimenezi, Yehova anathandiza Eliya kuti aziganizira kwambiri zinthu zolimbikitsa. Mulungu anamupatsanso Elisa kuti akhale mnzake woti azimuthandiza. Kodi inuyo mungatani kuti Yehova azikuthandizani ngati mukudzimva kuti muli nokhanokha?

6. Kodi mungapempherere zinthu ziti mukamadzimva kuti muli nokhanokha? (Salimo 62:8)

6 Yehova amakuuzani kuti muzipemphera kwa iye. Iye amaona mavuto amene mukukumana nawo ndipo amakutsimikizirani kuti adzamvetsera mapemphero anu nthawi iliyonse.(1 Ates. 5:17) Amasangalala kumvetsera atumiki ake akamapemphera kwa iye. (Miy. 15:8) Kodi mungapempherere zinthu ziti mukamadzimva kuti muli nokhanokha? Muziuza Yehova zonse za mumtima mwanu ngati mmene anachitira Eliya. (Werengani Salimo 62:8.) Muzimufotokozera zimene zikukudetsani nkhawa komanso mmene zimenezo zikukukhudzirani. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita. Mwachitsanzo, mukamadziona kuti muli nokhanokha komanso kuchita mantha kuti mufotokozere anzanu a kusukulu zimene mumakhulupirira, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima. Mungamupemphenso kuti akupatseni nzeru kuti muthe kufotokoza mwaluso zimene mumakhulupirirazo. (Luka 21:14, 15) Ngati mukuvutika ndi maganizo ena ake ofooketsa, mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kulankhula ndi Mkhristu wolimba mwauzimu. Mungamupemphenso kuti athandize munthu amene mukumufotokozerayo kuti amvetse mmene mukumvera. Muziuza Yehova za mumtima mwanu, kuona mmene akuyankhira mapemphero anu komanso kulola ena kuti akuthandizeni. Mukamachita zimenezi mudzayamba kuona kuti simuli nokhanokha.

Kodi mumapeza njira zochitira zambiri pa ntchito yolalikira limodzi ndi ena? (Onani ndime 7)

7. Kodi mukuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Mauricio?

7 Yehova watipatsa tonsefe ntchito yofunika yoti tizigwira. Musamakayikire kuti iye amaona komanso kuyamikira zonse zomwe mumachita mumpingo komanso pa ntchito yolalikira. (Sal. 110:3) Kodi kutanganidwa ndi ntchito zimenezi kungakuthandizeni bwanji mukamadzimva kuti muli nokhanokha? Taganizirani chitsanzo cha m’bale wina wachinyamata dzina lake Mauricio. * Patapita nthawi yochepa kuchokera pamene anabatizidwa, mnzake wapamtima anasiya choonadi. Mauricio anati, “Kuona mnzanga akusiya kutumikira Yehova, kunachititsa kuti ndizidzikayikira. Ndinkakayikira ngati ndingakhalebe wodzipereka kwa Yehova n’kupitiriza kukhala m’banja lake. Ndinkadzimva kuti ndili ndekhandekha ndipo ndinkaganiza kuti palibe amene ankamvetsa mmene ndikumvera.” Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza? Iye anati, “Ndinakonza zoti ndizigwira kwambiri ntchito yolalikira. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisamangoganizira kwambiri za ineyo komanso zinthu zofooketsa. Ndikamalalikira ndi ena ndinkasangalala komanso sindinkadziona kuti ndili ndekhandekha.” Ngakhale kuti sitingapite kolalikira ndi Akhristu anzathu, timalimbikitsidwa tikamalalikira nawo patelefoni komanso polemba makalata. Kodi n’chiyaninso chinathandiza Mauricio? Iye anawonjezera kuti, “Ndinkatanganidwanso ndi ntchito zampingo. Ndinkayesetsa kukonzekera komanso kukamba nkhani za ophunzira pamisonkhano. Ndikamachita zimenezi ndinkaona kuti Yehova komanso abale ndi alongo amandiyamikira.”

TIKAPANIKIZIKA NDI MAYESERO AAKULU

8. Kodi tingamve bwanji ngati titakumana ndi mayesero aakulu?

8 Masiku otsiriza ano timayembekezera kukumana ndi mayesero. (2 Tim. 3:1) Komabe mayesero ena omwe sitimawaganizira angatipeze pa nthawi imene sitimayembekezera. Mwadzidzidzi tingakumane ndi mavuto azachuma, matenda aakulu komanso munthu amene timamukonda angamwalire. Pa nthawi ngati zimenezi tingakhumudwe kapena kufooka makamaka ngati mayeserowo abwera motsatizana kapena pa nthawi imodzi. Komabe tizikumbukira kuti Yehova amatiyang’anira ndipo angatithandize kupirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo.

9. Fotokozani ena mwa mayesero amene Yobu anakumana nawo.

9 Taganizirani mmene Yehova anathandizira Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika. Iye anakumana ndi mayesero ambiri m’kanthawi kochepa. M’tsiku limodzi lokha, iye anamva zinthu zoopsa zokhudza kubedwa ndi kuphedwa kwa ziweto zake, kuphedwa kwa antchito ake ndipo chopweteka kwambiri chinali choti ana akenso okondedwa anaphedwa. (Yobu 1:13-19) Patangopita nthawi yochepa adakali ndi chisoni chachikulu chonchi, Yobu anadwala matenda opweteka kwambiri. (Yobu 2:7) Zinthu zinafika poipa kwambiri pa moyo wake moti iye anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.”​—Yobu 7:16.

Pofuna kutsimikizira Yobu kuti amamukonda, Yehova anamufotokozera mmene amasamalirira zolengedwa zake m’njira zosiyanasiyana (Onani ndime 10)

10. Kodi Yehova anamuthandiza bwanji Yobu kuti apirire mayesero? (Onani chithunzi chapachikuto.)

10 Yehova ankayang’anira Yobu. Chifukwa choti ankamukonda, iye anamupatsa zomwe ankafunikira kuti athe kupirira mayesero komanso kukhalabe wokhulupirika. Yehova anakumbutsa Yobu za nzeru zake zopanda malire komanso kuti amasamalira mwachikondi zinthu zimene analenga. Anafotokoza za nyama zambiri zomwe ndi zochititsa chidwi. (Yobu 38:1, 2; 39:9, 13, 19, 27; 40:15; 41:1, 2) Iye anagwiritsanso ntchito wachinyamata wina wokhulupirika dzina lake Elihu kuti amulimbikitse komanso kumutonthoza. Elihu anamutsimikizira kuti Yehova nthawi zonse amapereka mphoto kwa atumiki ake omwe amapirira. Koma Yehova anathandizanso Elihu kuti amupatse Yobu malangizo mwachikondi. Elihu anathandiza Yobu kuti asamangoganizira kwambiri za iyeyo pomukumbutsa kuti anthufe ndi aang’ono kwambiri poyerekeza ndi Yehova, yemwe ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. (Yobu 37:14) Yehova anapatsanso Yobu ntchito yoti agwire. Iye ankafunika kupempherera anzake atatu omwe anachimwa. (Yobu 42:8-10) Kodi masiku ano Yehova amatithandiza bwanji tikakumana ndi mayesero aakulu?

11. Kodi Baibulo limatilimbikitsa bwanji tikakumana ndi mayesero?

11 Yehova salankhula nafe mwachindunji ngati mmene anachitira ndi Yobu, koma amalankhula nafe kudzera m’Mawu ake Baibulo. (Aroma 15:4) Iye amatilimbikitsa potipatsa chiyembekezo cham’tsogolo. Taonani zina zomwe Baibulo limanena zomwe zingatilimbikitse tikamakumana ndi mayesero. M’Malemba, Yehova amatitsimikizira kuti china chilichonse kuphatikizapo mayesero aakulu sichidzatha “kutilekanitsa ndi chikondi [chake].” (Aroma 8:38, 39) Amatitsimikiziranso kuti iye “ali pafupi ndi onse oitanira pa iye” m’pemphero. (Sal. 145:18) Yehova amatiuza kuti tikamamudalira tingathe kupirira mayesero aliwonse ndipo tikhoza kumasangalalabe ngakhale kuti tikuvutika. (1 Akor. 10:13; Yak. 1:2, 12) Mawu a Mulungu amatikumbutsanso kuti mayesero athu ndi a kanthawi poyerekeza ndi madalitso osatha omwe Mulungu amatipatsa. (2 Akor. 4:16-18) Yehova amatipatsa chiyembekezo chotsimikizika chakuti adzachotsa Satana Mdyerekezi, yemwe amayambitsa mavuto komanso onse amene amatsatira njira zake zoipa. (Sal. 37:10) Kodi mwaloweza mavesi ena a m’Baibulo omwe angadzakuthandizeni kupirira mayesero m’tsogolo?

12. Kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani ngati tikufuna kuti Mawu ake azitithandiza kwambiri?

12 Yehova amayembekezera kuti tiziwerenga Baibulo nthawi zonse komanso kuganizira mozama zomwe tawerengazo. Tikamagwiritsa ntchito zomwe tikuphunzira, chikhulupiriro chathu chimalimba ndipo timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba. Zotsatira zake n’zakuti timakhala olimba ndipo tingathe kupirira mayesero. Yehova amaperekanso mzimu wake woyera kwa omwe amadalira Mawu ake. Ndipo mzimuwo umatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tithe kupirira mayesero aliwonse.​—2 Akor. 4:7-10.

13. Kodi chakudya chauzimu chomwe “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa chimatithandiza bwanji kupirira mayesero?

13 Mothandizidwa ndi Yehova “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amakonza nkhani, mavidiyo komanso nyimbo zomwe zingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi iye. (Mat. 24:45) Tiyenera kumagwiritsa ntchito bwino zinthu zimene Yehova amatipatsa pa nthawi yakezi. Posachedwapa mlongo wina wa ku United States, anasonyeza kuti amayamikira chakudya chauzimu chonsechi. Iye anati: “Pa zaka 40 zomwe ndakhala ndikutumikira Yehova, chikhulupiriro changa chakhala chikuyesedwa mobwerezabwereza.” Mlongoyu wakhala akukumana ndi mayesero aakulu kwambiri. Mwachitsanzo, agogo ake anaphedwa ndi dalaivala yemwe ankayendetsa galimoto ataledzera, makolo ake anadwala matenda oopsa ndipo anamwalira komanso iye anadwalapo khansa kawiri konse. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira? Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zonse Yehova wakhala akundisamalira. Chakudya chauzimu chimene wakhala akundipatsa kudzera mwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, chandithandiza kuti ndipirire. Chifukwa cha chakudya chauzimuchi, ndimamva ngati mmene Yobu anamvera, yemwe anati: ‘Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.’”​—Yobu 27:5.

Kodi tingathandize bwanji ena mumpingo? (Onani ndime 14)

14. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji abale ndi alongo athu potithandiza tikakumana ndi mayesero? (1 Atesalonika 4:9)

14 Yehova waphunzitsa anthu ake kuti azikondana komanso kulimbikitsana pa nthawi yovuta. (2 Akor. 1:3, 4; werengani 1 Atesalonika 4:9.) Potsanzira Elihu, abale ndi alongo athu amafunitsitsa kutithandiza kuti tikhalebe okhulupirika tikamakumana ndi mavuto. (Mac. 14:22) Mwachitsanzo, taganizirani mmene abale ndi alongo a mumpingo umene Diane ankasonkhana anamulimbikitsira komanso kumuthandiza kuti akhalebe wolimba mwauzimu, mwamuna wake atadwala matenda aakulu. Iye ananena kuti: “Zinali zovuta kwambiri. Koma tinaona Yehova akutithandiza mwachikondi pa miyezi yovuta imeneyo. Mpingo wathu unatithandiza kwambiri. Abale ndi alongo ankatiyendera, kutiimbira foni komanso kutikumbatira ndipo zimenezi zinatithandiza kuti tipirire. Popeza kuti sindiyendetsa galimoto, abale ndi alongowa ankaonetsetsa kuti ndikupezeka pamisonkhano komanso kulowa mu utumiki ngati ndingakwanitse kutero.” Ndi mwayitu waukulu kukhala m’banja la abale ndi alongo amene amatikonda.

TIMAYAMIKIRA KUTI YEHOVA AMATISAMALIRA MWACHIKONDI

15. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti tingathe kupirira mayesero?

15 Tonsefe tidzakumana ndi mayesero ena ake. Komabe monga mmene taphunzirira, sikuti timakhala tokhatokha polimbana ndi mayeserowo. Monga Atate wachikondi, Yehova nthawi zonse amatiyang’anira. Iye amakhala nafe pafupi ndipo ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero athu opempha kuti atithandize ndipo amakhala wofunitsitsa kutithandiza. (Yes. 43:2) Sitikayikira kuti tingathe kulimbana ndi mavuto chifukwa iye watipatsa chilichonse chomwe timafunikira kuti tipirire. Yehova watipatsa mwayi wa pemphero, Baibulo, chakudya chauzimu chochuluka komanso abale ndi alongo achikondi omwe amatithandiza pa nthawi ya mavuto.

16. Kodi tingatani kuti Yehova apitirize kutikonda?

16 Timayamikira kwambiri kuti Atate wathu wakumwamba amatiyang’anira. “Mitima yathu imakondwera mwa iye.” (Sal. 33:21) Tingasonyeze kuti timayamikira chikondi cha Yehova pogwiritsa ntchito bwino zinthu zonse zimene amatipatsa kuti atithandize. Timafunikanso kuchita mbali yathu kuti Mulungu apitirize kutikonda. M’mawu ena, tikamayesetsa kumvera Yehova komanso kuchita zinthu zimene amaziona kuti n’zoyenera, iye adzatiyang’anira mpaka kalekale.​—1 Pet. 3:12.

NYIMBO NA. 30 Atate Wanga, Mulungu Wanga Ndiponso Bwenzi Langa

^ Timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tikwanitse kulimbana ndi mavuto amene timakumana nawo masiku ano. Nkhaniyi ititsimikizira kuti Yehova amayang’anira anthu ake. Iye amaona mavuto amene aliyense akukumana nawo ndipo amatipatsa zomwe timafunikira kuti tithe kupirira.

^ Mayina ena asinthidwa.