Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 34

Muziphunzira Maulosi a M’Baibulo

Muziphunzira Maulosi a M’Baibulo

“Anthu ozindikira adzawamvetsetsa.”​—DAN. 12:10.

NYIMBO NA. 98 Malemba Anauziridwa ndi Mulungu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala pophunzira maulosi a m’Baibulo?

 M’BALE wina wachinyamata dzina lake Ben ananena kuti: “Ndimakonda kuphunzira maulosi a m’Baibulo.” Kodi ndi zimene inunso mumakonda? Kapena mumaona kuti maulosi a m’Baibulo ndi ovuta kumvetsa? N’kuthekanso kuti mumaona kuti kuphunzira maulosi n’kosasangalatsa. Komabe ngati mutaphunzira chifukwa chake Yehova analola kuti maulosi alembedwe m’Mawu ake, mukhoza kusintha mmene mumawaonera.

2. Kodi tiphunzira chiyani munkhaniyi?

2 Sikuti nkhaniyi ingofotokoza chifukwa chake tiyenera kuphunzira maulosi a m’Baibulo koma ifotokozanso mmene tingawaphunzirire. Kenako tikambirana maulosi awiri a m’buku la Danieli komanso mmene kuwamvetsa kungatithandizire panopa.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUPHUNZIRA MAULOSI A M’BAIBULO?

3. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikufuna kumvetsa ulosi wa m’Baibulo?

3 Tiyenera kupempha Mulungu kuti atithandize kumvetsa ulosi wa m’Baibulo. Taganizirani chitsanzo ichi: Tayerekezerani kuti mukuyenda m’dera lachilendo koma mnzanu amene mwayenda naye akudziwa bwino deralo. Akudziwa bwino pamene muli komanso kumene msewu uliwonse ukulowera. Mosakayikira mungasangalale kuti mnzanuyo anavomera kuti muyende naye. Mofanana ndi zimenezi, Yehova akudziwa bwino nthawi yomwe tikukhalamoyi komanso zimene zichitike kutsogoloku. Choncho kuti tizimvetsa maulosi a m’Baibulo, modzichepetsa tiyenera kupempha Yehova kuti atithandize.​—Dan. 2:28; 2 Pet. 1:19, 20.

Kuphunzira maulosi a m’Baibulo kungatithandize kukonzekera zimene zichitike posachedwapa (Onani ndime 4)

4. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti maulosi alembedwe m’Mawu ake? (Yeremiya 29:11) (Onaninso chithunzi.)

4 Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, Yehova amafuna kuti ana ake akhale ndi tsogolo labwino. (Werengani Yeremiya 29:11.) Koma mosiyana ndi makolo athu, Yehova akhoza kuneneratu zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo molondola kwambiri. Iye analola kuti maulosi alembedwe m’Mawu ake ndi cholinga choti tizidziwa zinthu zofunika zisanachitike. (Yes. 46:10) Maulosi a m’Baibulo ndi mphatso imene Atate wathu wakumwamba anatipatsa chifukwa choti amatikonda. Koma kodi n’chiyani chimene chingakuthandizeni kukhala otsimikiza kuti zimene Baibulo linaneneratu zidzachitikadi?

5. Kodi Mkhristu wachinyamata angaphunzire chiyani pa zimene zinachitikira Max?

5 Nthawi zambiri kusukulu, achinyamata athu amakhala ndi anthu amene salemekeza Baibulo. Zoyankhula komanso zochita zawo zingachititse wachinyamata wa Mboni kuti azikayikira zimene amakhulupirira. Taganizirani zimene zinachitikira m’bale wina dzina lake Max. Iye anati: “Ndisanakwanitse zaka 20 ndinayamba kukayikira ngati zimene makolo anga ankandiphunzitsa zinali zochokera m’chipembedzo choona komanso kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu.” Ndiye kodi makolo ake anachita chiyani? Iye anati: “Iwo ankachita zinthu modekha ngakhale kuti ankada nkhawa.” Makolo ake a Max anayankha mafunso ake pogwiritsa ntchito Baibulo. Max anachitanso zinthu zina. Ananena kuti: “Ndinaphunzira maulosi a m’Baibulo pandekha ndipo ndinakambirana zimene ndinaphunzirazo ndi achinyamata ena.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Max ananena kuti: “Pambuyo pake ndinatsimikizira kuti Baibulo linauziridwadi ndi Mulungu.”

6. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati muli ndi maganizo okayikira, nanga n’chifukwa chiyani?

6 Ngati inunso mwayamba kukayikira kuti Baibulo limanena zoona, musamadziimbe mlandu. Komabe muyenera kuchitapo kanthu. Maganizo okayikira ali ngati dzimbiri. Mofanana ndi dzimbiri, pang’ono ndi pang’ono maganizowa angawononge chinthu chinachake cha mtengo wapatali ngati mutawanyalanyaza. Kuti muchotse “dzimbiri” lililonse limene lingawononge chikhulupiriro chanu muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimakhulupirira zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo?’ Ngati mukukayikira, ndiye kuti muyenera kuphunzira maulosi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa kale. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

MMENE MUNGAPHUNZIRIRE MAULOSI A M’BAIBULO

Kuti tizidalira Yehova ngati mmene Danieli ankachitira, tiyenera kuphunzira maulosi a m’Baibulo modzichepetsa, mosamala komanso tili ndi zolinga zoyenera (Onani ndime 7)

7. Kodi Danieli anapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya mmene tingaphunzirire maulosi? (Danieli 12:10) (Onaninso chithunzi.)

7 Danieli anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene tingaphunzirire maulosi. Ankaphunzira maulosi ali ndi cholinga chabwino kuti adziwe choonadi. Iye analinso wodzichepetsa ndipo anazindikira kuti Yehova amathandiza anthu amene amamudziwa komanso kutsatira mfundo zake za makhalidwe abwino kuti amvetse bwino zinthu. (Dan. 2:27, 28; werengani Danieli 12:10.) Iye anasonyeza kuti ndi wodzichepetsa podalira Yehova kuti amuthandize. (Dan. 2:18) Danieli ankaphunziranso maulosi mosamala. Ankafufuzanso m’Malemba ouziridwa omwe analipo pa nthawiyo. (Yer. 25:11, 12; Dan. 9:2) Kodi mungatsanzire bwanji Danieli?

8. N’chifukwa chiyani anthu ena safuna kukhulupirira kuti maulosi a m’Baibulo amakwaniritsidwa, koma kodi tiyenera kuchita chiyani?

8 Muzifufuza zolinga zanu. Kodi mumaphunzira maulosi a m’Baibulo chifukwa chofunitsitsa kudziwa choonadi? Ngati ndi choncho, Yehova adzakuthandizani. (Yoh. 4:23, 24; 14:16, 17) Kodi munthu angaphunzire maulosi pa chifukwa chinanso chiti? Ena angachite zimenezi pofuna kupeza umboni wakuti Baibulo silinauziridwe ndi Mulungu. Pochita zimenezi, angamaone kuti si vuto kudziikira mfundo zokhudza chabwino ndi choipa n’kumazitsatira. Komabe, tiyenera kuphunzira maulosi tili ndi cholinga chabwino. Kuwonjezera pamenepo, timafunikanso kukhala ndi khalidwe lina kuti timvetse maulosi a m’Baibulo.

9. Kodi timafunika khalidwe liti kuti tizimvetsa maulosi a m’Baibulo? Fotokozani.

9 Muzikhala odzichepetsa. Yehova amalonjeza kuti azithandiza anthu odzichepetsa. (Yak. 4:6) Choncho tiyenera kumupempha kuti azitithandiza kumvetsa maulosi a m’Baibulo. Tiyeneranso kuvomereza kuti timafunika kuthandizidwa ndi kapolo wokhulupirika amene Yehova akumugwiritsa ntchito potipatsa chakudya pa nthawi yake. (Luka 12:42) Yehova ndi Mulungu wadongosolo, choncho n’zomveka kuti amagwiritsa ntchito njira imodzi pofuna kutithandiza kumvetsa choonadi chopezeka m’Mawu ake.​—1 Akor. 14:33; Aef. 4:4-6.

10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Esther?

10 Muziphunzira mosamala. Muziyamba ndi kuphunzira ulosi umene umakusangalatsani ndipo muzifufuza zambiri zokhudza ulosiwo. Zimenezi ndi zomwe mlongo wina dzina lake Esther anachita. Iye ankachita chidwi ndi maulosi ofotokoza za kubwera kwa Mesiya. Esther anati: “Ndili ndi zaka za m’ma 15, ndinayamba kufufuza umboni wotsimikizira kuti maulosiwa analembedwa Yesu asanabwere padzikoli.” Zimene anaphunzira atawerenga zokhudza mipukutu ya ku Nyanja Yakufa yomwe inapezeka, zinamuthandiza. Iye anati: “Yambiri mwa mipukutuyi, inalembedwa Yesu asanabwere, choncho maulosiwa ayenera kuti anauziridwadi ndi Mulungu.” Esther anavomerezanso kuti, “Ndinkafunika kuwerenga zinthu kwa maulendo angapo kuti ndizimvetse.” Komabe iye amasangalala chifukwa cha khama limene anachitali. Ataphunzira mosamala maulosi angapo a m’Baibulo, iye anati: “Ndinkatha kuona ndekha kuti Baibulo limanena zoona.”

11. Kodi kupeza umboni woti Baibulo limanena zoona kumatithandiza bwanji?

11 Tikamaona mmene maulosi ena opezeka m’Mawu a Mulungu akhala akukwaniritsidwira, timayamba kukhulupirira kwambiri Yehova komanso njira imene amagwiritsa ntchito potitsogolera. Kuwonjezera pamenepo, maulosi a m’Baibulo amatithandiza kuti tipitirizebe kukhala ndi chiyembekezo cham’tsogolo, kaya tikukumana ndi mayesero otani panopa. Tiyeni tikambirane mwachidule maulosi awiri amene Danieli analemba, omwe akukwaniritsidwa panopa. Kumvetsa maulosiwa kungatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru.

CHIFUKWA CHAKE MUYENERA KUDZIWA ZOKHUDZA MAPAZI ACHITSULO NDI DONGO

12. Kodi mapazi ‘achitsulo chosakanizika ndi dongo lonyowa’ amaimira chiyani? (Danieli 2:41-43)

12 Werengani Danieli 2:41-43. M’maloto a Mfumu Nebukadinezara omwe Danieli anamasulira, mapazi a chifaniziro omwe mfumuyo inaona anali opangidwa ndi “chitsulo chosakanizika ndi dongo lonyowa.” Tikayerekezera ulosiwu ndi maulosi ena opezeka m’buku la Danieli ndi Chivumbulutso, tinganene kuti mapazi akuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse masiku ano, wa Britain ndi America. Ponena za ulamulirowu, Danieli ananena kuti “ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.” N’chifukwa chiyani pa zinthu zina udzakhale wosalimba? Chifukwa chakuti anthu amene ayerekezeredwa ndi dongo amachititsa kuti ufumuwo uzilephera kuchita zinthu mwamphamvu ngati chitsulo.” b

13. Kodi timapeza mfundo zofunika ziti za choonadi chifukwa chomvetsa ulosiwu?

13 Timaphunzira mfundo zofunika zingapo za choonadi pa zimene Danieli anafotokoza zokhudza maloto a chifaniziro, makamaka mapazi ake. Choyamba, ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America wakhala ukusonyeza kuti ndi wamphamvu pa zinthu zina. Mwachitsanzo, mayikowa ndi awiri mwa mayiko amene anapambana pa nkhondo yoyamba komanso yachiwiri yapadziko lonse. Komabe ulamulirowu wakhala uli wofooka pa zinthu zina ndipo ukupitirizabe kukhala wofooka chifukwa choti nzika zake zimakangana zokhazokha komanso ndi boma. Chachiwiri, ulamulirowu udzakhala womaliza, Ufumu wa Mulungu usanathetse maboma onse a anthu. Ngakhale kuti nthawi zina mayiko ena angamalimbane ndi ulamuliro wa Britain ndi America, sadzaulowa m’malo. Tikudziwa zimenezi chifukwa “mwala” womwe ukuimira Ufumu wa Mulungu udzawononga mapazi a chifanizirochi, omwe akuimira ulamuliro wa Britain ndi America.​—Dan. 2:34, 35, 44, 45.

14. Kodi kumvetsa ulosi wokhudza mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo kumatithandiza bwanji kuti tizisankha zochita mwanzeru?

14 Kodi mumakhulupirira kuti ulosi wa Danieli wokhudza mapazi achitsulo chosakanizika ndi dongo ndi woona? Ngati ndi choncho, zimenezi zingakhudze mmene mumachitira zinthu pa moyo wanu. Simungamafunefune chuma m’dziko limene liwonongedwe posachedwapa. (Luka 12:16-21; 1 Yoh. 2:15-17) Kumvetsa ulosiwu kungakuthandizeninso kuti muziona kufunika kwa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Mat. 6:33; 28:18-20) Pambuyo pophunzira ulosiwu, mungachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimasankha zimasonyeza kuti ndimakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu uthetsa maboma onse posachedwapa?’

KODI ZOCHITA ZA “MFUMU YA KUMPOTO” NDI “MFUMU YA KUM’MWERA” ZIMAKUKHUDZANI BWANJI?

15. Kodi masiku ano ndi ndani amene ali “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kum’mwera”? (Danieli 11:40)

15 Werengani Danieli 11:40. Chaputala 11 cha buku la Danieli chimafotokoza za mafumu awiri, kapena kuti maulamuliro, omwe amalimbana kuti azilamulira dziko lonse. Tikayerekezera ulosi umenewu ndi maulosi ena otchulidwa m’Baibulo, timazindikira kuti “mfumu ya kumpoto” ndi dziko la Russia ndi mayiko omwe amagwirizana nalo komanso “mfumu ya kum’mwera” ndi ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. c

Tingalimbitse chikhulupiriro chathu komanso kupewa kuda nkhawa kwambiri ngati timazindikira kuti kutsutsidwa ndi “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kum’mwera” kukukwaniritsa maulosi a m’Baibulo (Onani ndime 16-18)

16. Kodi ndi mavuto otani amene anthu omwe ali m’madera olamuliridwa ndi “mfumu ya kumpoto” amakumana nawo?

16 Anthu a Mulungu omwe amakhala m’madera olamuliridwa ndi “mfumu ya kumpoto” akuzunzidwa ndi mfumuyi. A Mboni ena akhala akumenyedwa komanso kuikidwa m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. M’malo moti zochita za “mfumu ya kumpoto” zizifooketsa abale athu, zimangolimbitsa chikhulupiriro chawo. Tikutero chifukwa chakuti abale athu amadziwa kuti kuzunzidwa kwa anthu a Mulungu kukukwaniritsa ulosi wa Danieli. d (Dan. 11:41) Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo ndiponso tipitirizebe kukhala okhulupirika.

17. Kodi anthu a Mulungu omwe ali m’madera olamuliridwa ndi “mfumu ya kum’mwera” akhala akukumana ndi mavuto otani?

17 M’mbuyomu, nayonso “mfumu ya kum’mwera” yakhala ikuzunza anthu a Yehova. Mwachitsanzo, zisanafike zaka za m’ma 1950, abale athu ambiri anamangidwa chifukwa chokana kutenga nawo mbali n’zochitika za m’dzikoli ndipo ana ena a Mboni ankachotsedwa sukulu pachifukwa chomwechi. Komabe m’zaka zaposachedwapa, atumiki a Yehova omwe akukhala m’madera olamuliridwa ndi mfumuyi akhala akuyesedwanso m’njira zina zosaonekera. Mwachitsanzo, pa nthawi ya zisankho Mkhristu angayesedwe kuti akhale kumbali inayake ya chipani chandale kapena munthu winawake yemwe akupikisana nawo. N’kutheka kuti sangafike pokavota, komabe mumtima ndi m’maganizo mwake angakhale kuti ali mbali inayake. Apatu n’zofunika kwambiri kuti tisamalowerere ndale, osati n’zochita zathu zokha koma ngakhalenso m’maganizo ndi mumtima mwathu.​—Yoh. 15:18, 19; 18:36.

18. Kodi ifeyo timamva bwanji pamene “mfumu ya kumpoto” ikukangana ndi “mfumu ya kum’mwera”? (Onaninso chithunzi.)

18 Anthu amene sakhulupirira maulosi a m’Baibulo angamade nkhawa kwambiri akamaona “mfumu ya kum’mwera” ‘ikukankhana’ ndi “mfumu ya kumpoto.” (Dan. 11:40) Mayiko onsewa ali ndi zida za nyukiliya zamphamvu zoti zikhoza kuwononga zamoyo zonse padzikoli. Koma tikudziwa kuti Yehova sangalole kuti zimenezi zichitike. (Yes. 45:18) Choncho m’malo moti tizida nkhawa ndi mkangano umene uli pakati pa mafumu awiriwa, chikhulupiriro chathu chimalimba. Zimatitsimikizira kuti mapeto adzikoli ali pafupi.

PITIRIZANI KUCHITA CHIDWI NDI MAULOSI

19. Kodi tizikumbukira chiyani pa nkhani ya maulosi a m’Baibulo?

19 Sitikudziwa mmene maulosi ena a m’Baibulo adzakwaniritsidwire. Ngakhalenso mneneri Danieli sanamvetse tanthauzo la zinthu zonse zimene analemba. (Dan. 12:8, 9) Koma ngati sitikumvetsa bwino mmene ulosi winawake udzakwaniritsidwire sizitanthauza kuti sudzakwaniritsidwa. Tizikhulupirira kuti Yehova adzatiululira mmene udzakwaniritsidwire pa nthawi yoyenera monga wakhala akuchitira m’mbuyomu.​—Amosi 3:7.

20. Kodi ndi maulosi osangalatsa ati omwe tione akukwaniritsidwa posachedwapa, nanga tiyenera kupitiriza kuchita chiyani?

20 Anthu adzalengeza za “bata ndi mtendere.” (1 Ates. 5:3) Kenako maboma a dzikoli adzaukira zipembedzo zonyenga n’kuziwonongeratu. (Chiv. 17:16, 17) Pambuyo pake adzaukira anthu a Mulungu. (Ezek. 38:18, 19) Zimenezi zidzachititsa kuti nkhondo ya Aramagedo iyambike. (Chiv. 16:14, 16) Sitimakayikira kuti zimenezi zichitika posachedwapa. Choncho panopa tiyeni tipitirize kuyamikira Atate wathu wakumwamba pochita chidwi ndi maulosi a m’Baibulo komanso kuthandiza ena kuti azichita zomwezo.

NYIMBO NA. 95 Kuwala Kukuwonjezerekabe

a Kaya zinthu ziipe bwanji padzikoli, ndife otsimikiza kuti zikhala bwino posachedwapa. Timakhulupirira kwambiri zimenezi tikamaphunzira maulosi a m’Baibulo. Munkhaniyi, tikambirana zifukwa zimene ziyenera kutichititsa kukhulupirira maulosi. Tikambirananso mwachidule awiri mwa maulosi amene Danieli analemba komanso mmene kuwamvetsa kumatithandizira.

b Onani nkhani yakuti “Yehova Waulula ‘Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa,’” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2012 ndime 7-9.

c Onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mfumu ya Kumpoto’ Ndi Ndani Panopa?” mu Nsanja ya Olonda ya May 2020, ndime 3-4.

d Onani nkhani yakuti “Kodi ‘Mfumu ya Kumpoto’ Ndi Ndani Panopa?” mu Nsanja ya Olonda ya May 2020, ndime 7-9.