NKHANI YOPHUNZIRA 33
Muziphunzira pa Chitsanzo cha Danieli
“Ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.”—DAN. 9:23.
NYIMBO NA. 73 Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima
ZIMENE TIPHUNZIRE a
1. N’chifukwa chiyani Ababulo anachita chidwi ndi mneneri Danieli?
MNENERI Danieli anali wachinyamata pamene Ababulo anamugwira monga kapolo n’kupita naye kudziko lakutali ndi kwawo. Anthuwo ayenera kuti anachita naye chidwi. Iwo anaona “zooneka ndi maso,” monga zakuti Danieli “analibe chilema chilichonse” ndiponso ankachokera m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulo anamuphunzitsa kuti azikatumikira kunyumba yachifumu.—Dan. 1:3, 4, 6.
2. Kodi Yehova ankamuona bwanji Danieli? (Ezekieli 14:14)
2 Yehova ankakonda Danieli, osati chifukwa cha mmene ankaonekera kapena mmene banja lawo linalili, koma chifukwa cha zimene mnyamatayu anasankha kuti azichita pa moyo wake. Ndipotu n’kutheka kuti iye anali ndi zaka pafupifupi 20 zokha, pamene Yehova anamutchula pamodzi ndi Nowa ndi Yobu, amuna amene anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; werengani Ezekieli 14:14.) Danieli anakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali ndipo Yehova anapitiriza kumukonda kwa moyo wake wonse munthu wokhulupirikayo.—Dan. 10:11, 19.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
3 Munkhaniyi, tikambirana makhalidwe awiri a Danieli omwe anamuchititsa kuti akhale wofunika kwambiri kwa Yehova. Choyamba, tizikambirana khalidwe lililonse komanso nthawi imene analisonyeza. Kenako tiziona chimene chinathandiza Danieli kukhala ndi makhalidwewa. Ndipo pomaliza tikambirana zimene tingachite kuti timutsanzire. Ngakhale kuti nkhaniyi alembera achinyamata, tonsefe tingaphunzirepo kanthu pa chitsanzo cha Danieli.
MUZIKHALA OLIMBA MTIMA NGATI DANIELI
4. Kodi Danieli anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima? Perekani chitsanzo.
4 Anthu olimba mtima angathe kuchita mantha koma samalola kuti manthawo awalepheretse kuchita zoyenera. Danieli anali mnyamata wolimba mtima kwambiri. Taganizirani nthawi ziwiri pamene iye anasonyezera kulimba mtima. Nthawi yoyamba, ndi zimene zinachitika patatha zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu. Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inasokonezeka maganizo ndi zimene inalota zokhudza chifaniziro chachikulu kwambiri. Mfumuyi inaopseza kuti ipha amuna onse anzeru kuphatikizapo Danieli ngati sakanaiuza zomwe inalota komanso kumasulira kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli ankafunika kuchitapo kanthu mwamsanga chifukwa ngati sakanatero anthu ambiri akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.” (Dan. 2:16) Apatu anasonyeza kulimba mtima komanso chikhulupiriro. Palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti Danieli anali atamasulirapo maloto. Iye anapempha anzake omwe mayina awo a Chibabulo anali Sadirake, Mesake ndi Abedinego kuti “apemphe Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kuwaululira chinsinsi chimenechi.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphero amenewo. Mothandizidwa ndi Mulungu, Danieli anamasulira maloto a Nebukadinezara ndipo iye ndi anzake sanaphedwe.
5. Kodi ndi pa nthawi inanso iti pamene Danieli ankafunika kukhala wolimba mtima?
5 Patapita nthawi kuchokera pamene Danieli anamasulira maloto a chifaniziro chachikulu aja, panachitikanso zinthu zina zomwe zinkafunika kuti akhale wolimba mtima. Nebukadinezara analota maloto enanso omwe anamuvutitsa maganizo. Malotowa anali okhudza mtengo waukulu. Molimba mtima Danieli anafotokozera mfumuyo tanthauzo lake, kuphatikizapo zoti mfumuyo idzachita misala komanso idzasiya kulamulira kwa kanthawi. (Dan. 4:25) Zimenezi zikanachititsa kuti mfumuyo izimuona kuti ndi woukira ndipo ikanamupha. Koma Danieli analimbabe mtima ndipo anafotokoza tanthauzo la malotowo.
6. Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza Danieli kuti akhale wolimba mtima?
6 Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza Danieli kuti akhale wolimba mtima kwa moyo wake wonse? Ayenera kuti ali mwana, anaphunzira pa chitsanzo cha mayi ake ndi bambo ake. N’zosakayikitsa kuti iwo ankamvera malangizo amene Yehova anapatsa makolo a Chiisiraeli ndipo anaphunzitsa mwana wawoyu Chilamulo cha Mulungu. (Deut. 6:6-9) Sikuti Danieli ankangodziwa malamulo akuluakulu a m’Chilamulo monga Malamulo Khumi. Koma ankadziwanso zambiri zokhudza zimene Aisiraeli ankayenera kudya ndi zimene sankayenera kudya. b (Lev. 11:4-8; Dan. 1:8, 11-13) Danieli anaphunziranso mbiri ya anthu a Mulungu ndipo ankadziwa zomwe zinawachitikira chifukwa cholephera kutsatira mfundo za Yehova. (Dan. 9:10, 11) Zimene zinamuchitikira pa moyo wake zinamutsimikizira kuti Yehova komanso angelo ake amphamvu ankamuthandiza.—Dan. 2:19-24; 10:12, 18, 19.
7. Kodi n’chiyaninso chinathandiza Danieli kuti akhale wolimba mtima? (Onaninso chithunzi.)
7 Danieli ankaphunzira zolemba za aneneri a Mulungu kuphatikizapo maulosi a mneneri Yeremiya. Chifukwa cha zimenezi, iye anadzazindikira kuti ukapolo wa Ayuda ku Babulo unali utatsala pang’ono kutha. (Dan. 9:2) Mosakayikira, kuona maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa kunathandiza Danieli kuti azikhulupirira Yehova, ndipo anthu amene amakhulupirira kwambiri Yehova angathe kukhala olimba mtima kwambiri. (Yerekezerani ndi Aroma 8:31, 32, 37-39.) Chofunika kwambiri n’chakuti Danieli ankapemphera kwa Atate wake wakumwamba pafupipafupi. (Danieli 6:10) Iye anavomereza kuti anali atachimwira Yehova ndipo ankamufotokozera mmene ankamvera. Danieli anapemphanso Yehova kuti amuthandize. (Danieli 9:4, 5, 19) Iye anali munthu ngati ife tomwe, choncho sanabadwe ndi khalidwe la kulimba mtima. M’malomwake anakhala ndi khalidweli chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu, kupemphera komanso kudalira Yehova.
8. Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima?
8 Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale olimba mtima? Makolo athu angatilimbikitse kuti tikhale olimba mtima koma limeneli si khalidwe lomwe timatengera pobadwa. Kuphunzira kulimba mtima kuli ngati kuphunzira luso linalake. Njira imodzi imene imatithandiza kuphunzira luso linalake ndi kuonetsetsa zimene mphunzitsi wathu akuchita, n’kumamutsanzira. Mofanana ndi zimenezi, timaphunzira kukhala olimba mtima poonetsetsa mmene ena akusonyezera khalidweli n’kumawatsanzira. Ndiye kodi tikuphunzira chiyani kwa Danieli? Mofanana ndi Danieli, tiyenera kuwadziwa bwino Mawu a Mulungu. Tiziyesetsa kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova popemphera kwa iye momasuka komanso nthawi zonse. Tiyeneranso kumakhulupirira kwambiri Yehova ndipo tisamakayikire kuti ali kumbali yathu. Kenako pamene chikhulupiriro chathu chayesedwa, tidzakhala olimba mtima.
9. Kodi kukhala olimba mtima kumatithandiza bwanji?
9 Kukhala olimba mtima kumatithandiza m’njira zingapo. Taganizirani zimene zinachitikira Ben. Iye ankaphunzira pasukulu ina ku Germany, kumene aliyense ankakhulupirira kuti zinthu zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina komanso kuti nkhani ya m’Baibulo yakuti zinthu zinachita kulengedwa ndi nthano chabe. Tsiku lina Ben anapatsidwa mwayi woti afotokoze pamaso pa kalasi yonse chifukwa chake ankakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Molimba mtima, iye anafotokoza zimene amakhulupirira. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Ben anati: “Aphunzitsi anga anamvetsera mwatcheru ndipo anapulinta mfundo zomwe ndinkafotokoza n’kugawira aliyense m’kalasimo.” Ndiye kodi ana a sukulu anzakewo anatani? Ben anati: “Ambiri anamvetsera ndipo anandiuza kuti ankafunitsitsa atakhala olimba mtima ngati ineyo.” Chitsanzo cha Ben chikusonyeza kuti, kulimba mtima kumachititsa kuti anthu ena azikulemekeza. Kungathandizenso anthu a maganizo abwino kuti aphunzire za Yehova. Kunena zoona, tili ndi zifukwa zomveka zokhalira olimba mtima.
MUZIKHALA OKHULUPIRIKA NGATI DANIELI
10. Kodi kukhulupirika n’kutani?
10 M’Baibulo, mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “kukhulupirika” kapena chikondi “chokhulupirika,” nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito pofotokoza za chikondi chimene Mulungu ali nacho kwa atumiki ake. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito pofuna kufotokoza chikondi chimene chimakhalapo pakati pa atumiki a Mulungu. (2 Sam. 9:6, 7) Kukhulupirika kwathu kumawonjezereka nthawi ikamadutsa. Mfundo imeneyi ndi yoona tikaganizira zimene zinachitika pa moyo wa Danieli.
11. Kodi kukhulupirika kwa Danieli kunayesedwa bwanji atakalamba? (Onani chithunzi chapachikuto.)
11 Kwa moyo wake wonse Danieli ankayesedwa pa nkhani yokhala wokhulupirika kwa Yehova. Koma ena mwa mayesero aakulu, anakumana nawo ali ndi zaka za m’ma 90. Mzinda wa Babulo unali utagonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi ndipo unkalamuliridwa ndi Mfumu Dariyo. Anthu omwe ankatumikira m’nyumba yachifumu sankasangalala ndi Danieli ndipo sankalemekeza Mulungu amene iye ankamulambira. Choncho anakonza chiwembu choti Danieli aphedwe. Iwo anakhazikitsa lamulo lomwe likanachititsa kuti Danieli asankhe kukhalabe wokhulupirika kwa Mulungu kapena kumvera mfumu. Kuti asonyeze kuti anali wokhulupirika kwa mfumu komanso kuti akhale ngati anthu ena onse, Danieli ankangofunika kusiya kupemphera kwa Yehova kwa masiku 30. Koma iye anasankha kuti akhalebe wokhulupirika kwa Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti aponyedwe m’dzenje la mikango. Koma Yehova anadalitsa Danieli chifukwa chokhalabe wokhulupirika, pomupulumutsa. (Dan. 6:12-15, 20-22) Kodi tingatani kuti nthawi zonse tizikhala okhulupirika kwa Yehova ngati mmene Danieli anachitira?
12. Kodi Danieli anatani kuti asasiye kukhala wokhulupirika kwa Yehova?
12 Monga tafotokozera kale, munthu amakhala wokhulupirika kwa Mulungu chifukwa chomukonda kwambiri. Nthawi zonse Danieli ankakhala wokhulupirika kwa Yehova chifukwa chakuti ankakonda kwambiri Atate wake wakumwambayu. Mosakayikira, Danieli anayamba kukonda Yehova chifukwa choganizira makhalidwe ake komanso mmene ankawasonyezera. (Dan. 9:4) Ankaganiziranso zinthu zabwino zonse zimene Yehova anali atamuchitira komanso zimene anachitira anthu a mtundu wake ndipo ankayamikira.—Dan. 2:20-23; 9:15, 16.
13. (a) Kodi achinyamata athu amakumana ndi mayesero ati pa nkhani yokhala okhulupirika? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.) (b) Mogwirizana ndi vidiyo, kodi mungayankhe bwanji munthu wina atakufunsani zimene a Mboni za Yehova amachita ndi anthu amene amasankha kugonana ndi amuna kapena akazi anzawo?
13 Mofanana ndi Danieli, achinyamata athu azunguliridwa ndi anthu amene salemekeza Yehova ndi mfundo zake. Anthu amenewa sasangalala ndi aliyense amene amanena kuti amakonda Mulungu. Ena mpaka amafika powakakamiza achinyamatawa kuti achite zinthu zimene zingachititse kuti akhale osakhulupirika. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitikira wachinyamata wina dzina lake Graeme, yemwe amakhala ku Australia. Iye anakumana ndi mayesero aakulu atapita kusekondale. Aphunzitsi anafunsa ophunzirawo zimene angachite ngati mnzawo atawafotokozera kuti amagonana ndi amuna kapena akazi anzake. Aphunzitsiwo ananena kuti aliyense amene akuona kuti palibe vuto aime mbali ina ya kalasiyo, ndipo onse amene sangasangalale nazo aimenso mbali ina. Graeme anati: “Ophunzira onse anapita mbali yosonyeza kuti saona vuto, kupatulapo ine ndi wophunzira wina yemwenso anali wa Mboni.” Koma zinthu zinafika povuta kwambiri chifukwa chakuti iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova, ndipo anati: “Kwa ola lonse lomwe tinali pa phunzirolo, ana asukulu anzathu ngakhalenso aphunzitsiwo ankatinyoza komanso kutilankhula zachipongwe. Ndinayesetsa kuti ndiwafotokozere modekha komanso m’njira yabwino kwambiri zimene ndimakhulupirira koma sanandimvetsere ngakhale pang’ono.” Ndiye kodi Graeme anamva bwanji atakumana ndi mayeserowa? Iye anati: “Sindinkasangalala kuti ndizinyozedwa komabe ndinasangalala kuti ndinafotokoza molimba mtima zimene ndimakhulupirira.” c
14. Kodi ndi chinthu chimodzi chiti chomwe tingachite kuti tizikhala okhulupirika kwa Yehova nthawi zonse?
14 Mofanana ndi Danieli, tingapitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova ngati timamukonda kwambiri. Tingakulitse chikondi chimenechi tikamaphunzira makhalidwe a Yehova. Mwachitsanzo, tikhoza kuphunzira zinthu zimene analenga. (Aroma 1:20) Ngati mukufuna kuti muzikonda komanso kulemekeza kwambiri Yehova, mukhoza kuwerenga nkhani zachidule zakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” kapena kuonera mavidiyo ake. Mukhozanso kuwerenga mfundo za m’timabuku takuti, Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa? ndi Mmene Moyo Unayambira—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri. Taonani zimene mlongo wina wa ku Denmark dzina lake Esther ananena zokhudza timabukuti. Iye anati: “Mfundo zake zinafotokozedwa bwino. Timabukuti sitimakuuza zoti uzikhulupirira, m’malomwake timafotokoza mfundo zoona n’kukupatsa mwayi woti usankhe wekha zoti ukhulupirire.” Ben yemwe tamutchula kale uja anati: “Timabukuti timakuthandiza kulimbitsa chikhulupiriro chako. Tinandithandiza kutsimikizira kuti Mulungu analenga zamoyo.” Ngati inunso mutaphunzira timabukuti, mudzafika povomereza zimene Baibulo linanena, kuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chiv. 4:11. d
15. Kodi tingachitenso chiyani kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?
15 Chinthu china chimene chingatithandize kuti tizikonda kwambiri Yehova ndi kuphunzira mosamala zokhudza Mwana wake, Yesu. Mlongo wina wachitsikana dzina lake Samira, yemwe amakhala ku Germany, anachita zimenezi. Iye anati: “Ndinamudziwa bwino Yehova chifukwa chophunzira za Yesu.” Ali mwana, Samira ankavutika kumvetsa mfundo yakuti Yehova amasangalala kapenanso kukhumudwa. Koma ankatha kumvetsa mmene Yesu ankamvera. Iye anawonjezera kuti, “Ndinkamukonda Yesu chifukwa anali wochezeka komanso ankakonda anthu.” Pamene ankaphunzira zambiri zokhudza Yesu, m’pamenenso anayamba kukhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Iye anati: “Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kumvetsa kuti Yesu amatsanzira kwambiri Atate wake. Iwo amafanana pa zinthu zambiri. Ndinazindikira kuti chimenechi ndi chimodzi mwa zifukwa zomwe zinachititsa Yehova kutumiza Yesu padzikoli, kuti zikhale zotheka kuti anthu amudziwe bwino Yehovayo.” (Yoh. 14:9) Ngati mukufuna kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, mungachite bwino kukonza zoti muphunzire zokhudza Yesu mmene mungathere. Mukachita zimenezi mudzayamba kukonda kwambiri Yehova komanso kukhala wokhulupirika kwa iye.
16. Kodi kukhala okhulupirika kumatithandiza bwanji? (Salimo 18:25; Mika 6:8)
16 Nthawi zambiri anthu okhulupirika amakhala ndi anzawo abwino, omwenso amakhala okhulupirika. (Rute 1:14-17) Kuwonjezera pamenepo, anthu okhulupirika kwa Yehova ali ndi chifukwa chabwino chowachititsa kukhala ndi mtendere wamumtima. Tikutero chifukwa Yehova amalonjeza kuti adzakhala wokhulupirika kwa anthu omwe ndi okhulupirika kwa iye. (Werengani Salimo 18:25; Mika 6:8.) Tangoganizani, Mlengi wamphamvuyonse ndi wofunitsitsa kuti akhale nafe pa ubwenzi wolimba. Tikakhala pa ubwenzi woterewu, anthu otsutsa, mayesero ngakhalenso imfa, sizingathe kutilekanitsa ndi iye. (Dan. 12:13; Luka 20:37, 38; Aroma 8:38, 39) Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizitsanzira Danieli n’kumapitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova.
PITIRIZANI KUPHUNZIRA PA CHITSANZO CHA DANIELI
17-18. Kodi tingaphunzirenso chiyani kwa Danieli?
17 Munkhaniyi, tangoona makhalidwe awiri a Danieli. Koma palinso zambiri zomwe tingaphunzire kwa iye. Mwachitsanzo, Yehova anamuonetsa masomphenya angapo komanso kumulotetsa maloto ndipo anamupatsa luso lotha kumasulira maulosi. Ambiri mwa maulosiwa anakwaniritsidwa kale. Koma ena amafotokoza zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo, zomwe zidzakhudze aliyense padzikoli.
18 Munkhani yotsatira, tidzakambirana maulosi awiri amene analembedwa ndi Danieli. Kumvetsa maulosiwa kungatithandize tonsefe, kaya ndife achinyamata kapena achikulire, kuti tizisankha zochita mwanzeru. Maulosiwa angatithandize kuti tikhale okhulupirika komanso olimba mtima kwambiri n’cholinga choti tikhale okonzeka kudzapirira mayesero omwe tidzakumane nawo m’tsogolo.
NYIMBO NA. 119 Tiyenera Kukhala Ndi Chikhulupiriro
a Achinyamata amene akutumikira Yehova masiku ano amakumana ndi mavuto omwe amawayesa pa nkhani ya kulimba mtima komanso kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. Anzawo a m’kalasi angamawanyoze chifukwa chokhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Kapenanso anzawo ena angawachititse kuti azidzimva kuti ndi opusa chifukwa chotumikira Mulungu komanso kutsatira mfundo zake. Koma munkhaniyi tiona kuti, anthu amene amatsanzira mneneri Danieli ndiponso kutumikira Yehova molimba mtima komanso mokhulupirika, ndi anzeru.
b N’kutheka kuti panali zifukwa zitatu zomwe zinachititsa Danieli kuganiza kuti zakudya za ku Babulo zinali zodetsedwa: (1) Mwina nyama yomwe anapatsidwa inali m’gulu la nyama zoletsedwa m’Chilamulo. (Deut. 14:7, 8) (2) Kapenanso nyama yake inali yosazinga. (Lev. 17:10-12) (3) Kudya chakudyacho kukanaoneka ngati mbali yakulambira mulungu wonyenga.—Yerekezerani ndi Levitiko 7:15 ndi 1 Akorinto 10:18, 21, 22.
d Kuti muzikonda kwambiri Yehova, mukhozanso kuphunzira buku lakuti Yandikirani kwa Yehova, lomwe limafotokoza mozamirapo zokhudza iye ndi makhalidwe ake.