NKHANI YOPHUNZIRA 34
NYIMBO NA. 107 Tizitsanzira Chikondi cha Mulungu
Mmene Tingasonyezere Chikondi ndi Chifundo Wina Akachita Tchimo
“Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu . . . nʼcholinga choti ulape.”—AROMA 2:4.
ZIMENE TIPHUNZIRE
Munkhaniyi tikambirana mmene akulu angathandizire munthu amene wachita tchimo lalikulu.
1. Kodi n’chiyani chingachitike kwa anthu ena omwe achita tchimo lalikulu?
MUNKHANI yapita ija tinaona zimene mtumwi Paulo anachita, munthu wina atachita tchimo lalikulu mumpingo wa ku Korinto. Munthu wochimwayo sanalape ndipo anafunika kuchotsedwa mumpingo. Koma mogwirizana ndi lemba lotsogolera nkhaniyi, ena omwe achita tchimo lalikulu akhoza kuthandizidwa kuti alape. (Aroma 2:4) Kodi akulu angawathandize bwanji kuti alape?
2-3. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikadziwa kuti Mkhristu mnzathu wachita tchimo lalikulu, nanga n’chifukwa chiyani?
2 Kuti akulu athandize munthu amafunika kudziwa zimene munthuyo wachita. Ndiye kodi tiyenera kutani tikadziwa kuti Mkhristu mnzathu wachita tchimo lalikulu lomwe lingachititse kuti achotsedwe mumpingo? Tiyenera kumulimbikitsa kuti akauze akulu n’cholinga choti amuthandize.—Yes. 1:18; Mac. 20:28; 1 Pet. 5:2.
3 Koma bwanji ngati munthu amene wachita tchimoyo akukana kupita kwa akulu? Ifeyo tiyenera kukawauza akulu n’cholinga choti munthuyo athandizidwe. Tikachita zimenezi timasonyeza chikondi chifukwa sitimafuna kuti m’bale kapena mlongo wathu awonongeke. Munthu wochimwa akamachitabe zoipa, amapitiriza kuwononga ubwenzi wake ndi Yehova. Akhoza kuwononganso mbiri ya mpingo. Choncho molimba mtima timachitapo kathu chifukwa timakonda Yehova komanso munthuyo.—Sal. 27:14.
MMENE AKULU AMATHANDIZIRA ANTHU OMWE ACHITA MACHIMO AAKULU
4. Kodi cholinga cha akulu chimakhala chiyani akamakumana ndi munthu yemwe wachita tchimo?
4 Munthu wina mumpingo akachita tchimo lalikulu, bungwe la akulu limasankha akulu atatu oyenerera kuti akhale m’komiti ya akulu yokumana ndi munthuyo. a Akulu amenewa amafunika kukhala odzichepetsa. Akamathandiza munthu wochimwa kuti alape amazindikira kuti sangamukakamize kuti asinthe. (Deut. 30:19) Akulu amazindikira kuti si anthu onse omwe achita tchimo amene angatsatire malangizo ngati mmene anachitira Mfumu Davide. (2 Sam. 12:13) Anthu ena omwe achita tchimo amakana malangizo a Yehova. (Gen. 4:6-8) Ngakhale zili choncho, cholinga cha akulu chimakhala kuthandiza munthu yemwe wachimwa kuti alape ngati n’zotheka. Kodi ndi mfundo ziti zimene amatsatira akamakumana ndi munthu yemwe wachita tchimo?
5. Kodi akulu amatsatira malangizo ati akamakumana ndi munthu yemwe wachita tchimo? (2 Timoteyo 2:24-26) (Onaninso chithunzi.)
5 Akulu amaona kuti munthu yemwe wachita tchimo ndi nkhosa yamtengo wapatali yomwe yasochera. (Luka 15:4, 6) Choncho akamakumana ndi munthuyo salankhula kapena kuchita naye zinthu mwankhaza. Iwo samakumana ndi munthu mwamwambo chabe n’cholinga choti azingomufunsa mafunso. M’malomwake, amasonyeza makhalidwe opezeka pa 2 Timoteyo 2:24-26. (Werengani.) Akulu amakhala odekha, ofatsa komanso okoma mtima akamayesetsa kuti amufike pamtima munthu yemwe wachita tchimoyo.
6. Kodi akulu angakonzekeretse bwanji mtima wawo asanakumane ndi munthu yemwe wachita tchimo? (Aroma 2:4)
6 Akulu amakonzekeretsa mtima wawo. Iwo amayesetsa kutsanzira Yehova akamachita zinthu ndi munthu wochimwayo ndipo amakumbukira malangizo a Paulo akuti: “Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu . . . nʼcholinga choti ulape.” (Werengani Aroma 2:4.) Akulu ayenera kukumbukira kuti iwo ndi abusa omwe amatsatira malangizo a Khristu. (Yes. 11:3, 4; Mat. 18:18-20) Akulu omwe ali mu komiti asanakumane ndi munthu amapemphera komanso kuganizira cholinga chawo chomwe ndi kuthandiza wochimwayo kuti alape. Iwo amafufuza m’Malemba komanso m’mabuku athu ndipo amapemphera kuti Mulungu awathandize kukhala ozindikira. Amaganiziranso ngati pali zina zimene ayenera kudziwa zokhudza munthuyo zomwe zimachititsa kuti aziganiza kapena kuchita zinthu m’njira inayake.—Miy. 20:5.
7-8. Kodi akulu angatsanzire bwanji kuleza mtima kwa Yehova akamathandiza munthu yemwe wachita tchimo?
7 Akulu amatsanzira kuleza mtima kwa Yehova. Iwo amakumbukira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi anthu ochimwa m’mbuyomo. Mwachitsanzo, Yehova analankhula ndi Kaini moleza mtima kumuchenjeza za zotsatirapo za tchimo komanso kumuuza zimene angachite kuti akhale nayenso pa ubwenzi. (Gen. 4:6, 7) Yehova anagwiritsa ntchito mneneri Natani popereka malangizo kwa Davide. Natani anagwiritsa ntchito chitsanzo chomwe chinafika pamtima mfumuyi. (2 Sam. 12:1-7) Ndipo Yehova ‘anapitiriza kutumiza’ aneneri ake “mobwerezabwereza” kwa Aisiraeli omwe ankachita machimo. (Yer. 7:24, 25) Iye sanadikire kuti iwo alape kaye, kenako n’kumawathandiza. M’malomwake anayamba ndi iye kuchitapo kathu powathandiza kuti alape.
8 Akulu amatsanzira chitsanzo cha Yehova pothandiza munthu yemwe wachita tchimo lalikulu. Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 4:2, iwo amakambirana “moleza mtima kwambiri” ndi munthu amene akuvutika mumtima. Akulu omwe amatsatira mfundo ya palembali, nthawi zonse amayesetsa kudziletsa komanso kuthandiza moleza mtima wochimwayo kuti akhale ndi mtima wofuna kuchita zoyenera. Ngati mkuluyo atasonyeza kukhumudwa kapena kukwiya, zingakhale zovuta kuti wochimwayo alape.
9-10. Kodi akulu angathandize bwanji munthu yemwe wachita tchimo kuti aganizire zimene wakhala akuchita?
9 Akulu amafufuza kuti adziwe zimene zinachititsa kuti munthu achite tchimo. Mwachitsanzo, kodi Mkhristuyo anafooka chifukwa choti anasiya kuphunzira Baibulo payekha kapena kulowa mu utumiki? Kodi sapemphera kawirikawiri kapena amangopemphera mwamwambo? Kodi wakhala akungotengeka ndi zimene amalakalaka? Kodi wakhala akusankha molakwika anthu ocheza nawo kapena zosangalatsa? Kodi zimene amasankhazo zakhudza bwanji mtima wake? Kodi akudziwa mmene zochita zake zakhala zikukhudzira Atate wake Yehova?
10 Akulu akamafunsa mafunso mwanzeru, amathandiza munthu yemwe wachita tchimoyo kuti amasuke ndiponso aganizire zomwe wakhala akuchita. (Miy. 20:5) Iwo akhoza kugwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuthandiza wochimwayo kuti aganizire zimene analakwitsa ngati mmene Natani anachitira ndi Davide. Mwina pa ulendo woyamba womwewo munthuyo akhoza kuyamba kumva chisoni ndi zimene wakhala akuchita ndipo akhoza kulapa.
11. Kodi Yesu ankachita bwanji zinthu ndi anthu ochimwa?
11 Akulu amayesetsa kutsanzira Yesu. Yesu ataukitsidwa analankhula ndi Saulo wa ku Tariso ndipo anamufunsa funso lakuti: “Saulo, Saulo, nʼchifukwa chiyani ukundizunza?” Apa Yesu anamuthandiza kuganizira zinthu zolakwika zimene ankachita. (Mac. 9:3-6) Ndipo ponena za “mayi uja Yezebeli,” Yesu anati: “Ndamupatsa nthawi kuti alape.”—Chiv. 2:20, 21.
12-13. Kodi akulu amapereka bwanji nthawi kwa munthu wochimwa kuti alape? (Onaninso chithunzi.)
12 Potsanzira Yesu, akulu safulumira kuganiza kuti munthu yemwe wachita tchimo sangalape. Anthu ena akhoza kusonyeza mtima wolapa pa nthawi yoyamba yomwe akumana ndi komiti pomwe ena angatenge nthawi. Choncho akulu amakonza kuti akumane ndi munthu wochimwayo maulendo angapo. N’kutheka kuti pambuyo pokumana naye pa ulendo woyamba, Mkhristu yemwe wachita tchimoyo akhoza kuganizira zomwe wauzidwa. Akhoza kupemphera kwa Yehova modzichepetsa. (Sal. 32:5; 38:18) Ndipo pa ulendo wotsatira, akhoza kukhala ndi maganizo osiyana ndi omwe anali nawo poyamba.
13 Akulu amasonyeza chifundo ndi kukoma mtima kuti athandize munthu wochimwa kuti alape. Iwo amapemphera kwa Yehova ndipo amakhala ndi chiyembekezo kuti iye adalitsa khama lawo pothandiza Mkhristuyo kuti azindikire zomwe walakwitsa ndi kulapa.—2 Tim. 2:25, 26.
14. Kodi ndi ndani amene ayenera kulemekezedwa munthu wochimwa akalapa? Perekani chifukwa.
14 Zimakhala zosangalatsa kwambiri munthu wochimwa akalapa. (Luka 15:7, 10) Kodi zikatero ndi ndani amene amayenera kulemekezedwa? Kodi ndi akulu? Kumbukirani zimene Paulo analemba zokhudza anthu ochimwa. Iye anati: “Mwina Mulungu angawalole kulapa.” (2 Tim. 2:25) Munthu wochimwa akasintha maganizo komanso mtima wake, woyenera kulemekezedwa si munthu aliyense koma Yehova chifukwa ndi amene amathandiza munthuyo kuti asinthe. Paulo anafotokozanso zinthu zina zabwino zimene zimachitika munthuyo akalapa. Anafotokoza kuti wochimwayo amadziwa choonadi molondola, nzeru zimamubwerera komanso amapulumuka ku misampha ya Satana.—2 Tim. 2:26.
15. Kodi akulu angatani kuti apitirize kuthandiza munthu wochimwa yemwe walapa?
15 Munthu wochimwa akalapa, akulu omwe anali m’komiti imene inakumana naye amakonza maulendo a ubusa n’cholinga choti apitirize kumuthandiza kupewa misampha ya Satana ndiponso kuwongola njira zake. (Aheb. 12:12, 13) Akulu samauza ena zoipa zimene munthu wochimwayo anachita. Koma kodi ndi zinthu ziti zomwe mpingo uyenera kudziwa?
“UZIWADZUDZULA PAMASO PA ONSE”
16. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 5:20, kodi Paulo ankanena za ndani pamene ananena kuti “onse”?
16 Werengani 1 Timoteyo 5:20. Amenewa ndi mawu amene Paulo analembera Timoteyo yemwe anali mkulu mnzake omuuza zoyenera kuchita ndi “anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo.” Kodi pamenepa ankatanthauza chiyani? Iye sankatanthauza kuti anthu “onse” mumpingo akuyenera kudziwa zokhudza nkhaniyo. Koma ankanena za anthu ochepa omwe ankadziwa kale za nkhaniyo. Akhoza kukhala anthu omwe anaona tchimolo likuchitika kapena amene munthu wochimwayo anawafotokozera. Akulu angawafotokozere anthuwo mwanzeru kuti nkhaniyo yasamalidwa ndipo wochimwayo wathandizidwa.
17. Ngati tchimo ladziwika kumpingo kapena likhoza kudziwika kodi payenera kuperekedwa chilengezo chotani, nanga n’chifukwa chiyani?
17 Koma nthawi zina zimakhala kuti tchimolo ladziwika mumpingo wonse kapenanso kuti lidzadziwika. Zikatero mawu akuti “onse” angatanthauze mpingo wonse. Choncho mkulu angalengeze kumpingo kuti m’bale kapena mlongo wadzudzulidwa. N’chifukwa chiyani zimenezi ziyenera kuchitika? Paulo anafotokoza kuti: “Kuti ena onsewo akhale ndi mantha” n’cholinga choti asamachite tchimo.
18. Kodi akulu angathandize bwanji ana obatizidwa akachita tchimo lalikulu? (Onaninso chithunzi.)
18 Kodi akulu angathandize bwanji ana obatizidwa osaposa zaka 18 omwe achita tchimo lalikulu? Bungwe la akulu lidzakonza zoti akulu awiri akumane ndi mwanayo ndi makolo ake kapena amene amamuyang’anira ngati ali Akhristu. Akuluwo adzafufuza zimene makolowo achita pothandiza mwanayo kuti alape. Ngati mwanayo ali ndi maganizo abwino ndipo makolowo akumuthandiza, akuluwo akhoza kusankha kuti nkhaniyo ithere pomwepo. Ndipotu Mulungu anapereka kwa makolo udindo wolangiza ana awo mwachikondi. (Deut. 6:6, 7; Miy. 6:20; 22:6; Aef. 6:2-4) Nthawi zina akuluwo angamafunse makolowo kuti adziwe ngati mwanayo akuthandizidwa moyenera. Koma bwanji ngati mwanayo sakulapa ndipo akupitiriza kuchita zoipa? Zikatero komiti ya akulu idzakumana ndi mwanayo limodzi ndi makolo ake kapena amene amamuyang’anira.
“YEHOVA NDI WACHIKONDI CHACHIKULU KOMANSO WACHIFUNDO”
19. Kodi akulu amatsanzira bwanji Yehova akamathandiza munthu amene wachita tchimo?
19 Akulu omwe ali m’komiti amakhala ndi udindo pamaso pa Yehova wothandiza kuti mpingo ukhale woyera. (1 Akor. 5:7) Amafunanso kuthandiza anthu ochimwa kuti alape ngati n’kotheka. Kuti zimenezi zitheke iwo ayenera kukhala ndi maganizo abwino, n’kumayembekezera kuti munthuyo akhoza kusintha. Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo amafuna kutsanzira Yehova yemwe ndi “wachikondi chachikulu komanso wachifundo.” (Yak. 5:11) Mtumwi Yohane nayenso ankakonda abale ndi alongo ake. Iye analemba kuti: “Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo. Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.”—1 Yoh. 2:1.
20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
20 N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zina Mkhristu sangafune kulapa. Zikatero amayenera kuchotsedwa mumpingo. Kodi akulu amasamalira bwanji nkhani ngati zimenezi? Tikambirana izi mumbali yomaliza ya nkhani zimenezi.
NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso
a M’mbuyomu akulu amenewa ankatchedwa komiti yoweruza. Koma popeza kuweruza ndi mbali imodzi yokha ya ntchito imene amagwira, sitizigwiritsanso ntchito mawu amenewa. M’malomwake tizingonena kuti komiti ya akulu.