Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 31

NYIMBO NA. 12 Yehova Mulungu Wamkulu

Zimene Yehova Wachita Kuti Atipulumutse ku Uchimo ndi Imfa

Zimene Yehova Wachita Kuti Atipulumutse ku Uchimo ndi Imfa

“Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.”​—YOH. 3:16.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona zimene Yehova wakhala akuchita potithandiza kuti tizimumvera komanso kumutumikira ngakhale kuti ndife ochimwa. Tionanso zimene wachita kuti tidzapeze moyo wosatha, pa nthawi yomwe sitidzavutikanso ndi uchimo.

1-2. (a) Kodi uchimo n’chiyani, nanga tingatani kuti tizimvera komanso kutumikira Yehova ngakhale kuti ndife ochimwa? (Onaninso “Tanthauzo la Mawu Ena.”) (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi komanso nkhani zina zopezeka m’magaziniyi? (Onaninso “Mawu kwa Owerenga” m’magaziniyi.)

 KODI mungakonde kudziwa mmene Yehova Mulungu amakukonderani? Njira imodzi yomwe tingapezere yankho la funsoli ndi kuphunzira zomwe iye wachita kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa. Uchimo a ndi mdani woopsa yemwe sitingamugonjetse patokha. Timachimwa tsiku lililonse ndipo timafa chifukwa cha uchimowo. (Aroma 5:12) Komabe nkhani yosangalatsa ndi yakuti Yehova angatithandize kugonjetsa uchimo. Ndipotu n’zosakayikitsa kuti tingapambane pankhondoyi.

2 Yehova wakhala akuthandiza anthu kulimbana ndi uchimo kwa zaka pafupifupi 6,000. Chifukwa chiyani? Chifukwa amatikonda. Iye wakhala akukonda anthu kungoyambira pachiyambi ndipo amachita zambiri kuti awathandize kulimbana ndi uchimo. Mulungu amadziwa kuti uchimo umabweretsa imfa ndipo samafuna kuti anthufe tizifa. Amafuna kuti tizikhala ndi moyo mpaka kalekale. (Aroma 6:23) Izi ndi zimene iye amafuna. Munkhaniyi tikambirana mafunso atatu: (1) Kodi Yehova anapereka chiyembekezo chotani kwa anthu ochimwa? (2) Kodi anthu otchulidwa m’Baibulo omwe anali ochimwa ankachita chiyani kuti azisangalatsa Yehova? (3) Kodi Yesu anachita chiyani kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa?

KODI YEHOVA ANAPEREKA CHIYEMBEKEZO CHOTANI KWA ANTHU OCHIMWA?

3. Kodi chinachitika n’chiyani kuti makolo athu oyamba achimwe?

3 Yehova atalenga mwamuna ndi mkazi oyamba ankafuna kuti iwo azisangalala. Anawapatsa malo okongola okhala, mphatso ya banja komanso ntchito yosangalatsa yoti azigwira. Iwo ankafunika kubereka ana n’kudzadza dziko lonse lapansi komanso kulikonza kuti likhale lokongola ngati munda wa Edeni. Koma anangowapatsa lamulo limodzi. Ndipo anawachenjeza kuti ngati mwadala sangamvere lamulolo adzafa. Timadziwa zimene zinachitika pambuyo pake. Mngelo yemwe sankawakonda komanso yemwe sankakonda Mulungu, anawanyengerera kuti achimwe. Adamu ndi Hava anachita zomwe mngelo woipayo ankafuna. Chifukwa choti analephera kukhulupirira Atate wawo wachikondi, iwo anachimwa. Ndipotu mmene tikudziwira, zimene Yehova ananena zinachitika. Kuchokera tsiku limenelo iwo anayamba kukumana ndi zotsatirapo zake zomwe ndi kukalamba ndipo pamapeto pake anafa.​—Gen. 1:28, 29; 2:8, 9, 16-18; 3:1-6, 17-19, 24; 5:5.

4. N’chifukwa chiyani Yehova amadana ndi uchimo n’kumatithandiza kuti tizilimbana nawo? (Aroma 8:20, 21)

4 Yehova anachititsa kuti nkhaniyi ilembedwe n’cholinga choti izitithandidza. Imatithandiza kumvetsa chifukwa chake iye amadana kwambiri ndi uchimo. Uchimo umachititsa kuti titalikirane ndi Atate wathu komanso umabweretsa imfa. (Yes. 59:2) N’chifukwa chake Satana yemwe anayambitsa mavutowa, amakonda uchimo komanso kulimbikitsa anthu kuti azichimwa. Iye ayenera kuti ankaganiza kuti kuchimwitsa Adamu ndi Hava kwasokoneza cholinga cha Mulungu chokhudza anthu. Koma sankadziwa kukula kwa chikondi cha Yehova. Mulungu sanasinthe cholinga chomwe anali nacho chokhudza ana a Adamu ndi Hava. Iye amakonda kwambiri anthu choncho mwamsanga anawapatsa chiyembekezo. (Werengani Aroma 8:20, 21.) Yehova ankadziwa kuti ena mwa ana a Adamuwo adzasankha kumukonda komanso kumumvera. Choncho pokhala Atate komanso Mlengi wawo, iye adzawamasula ku uchimo ndiponso kuwathandiza kuti akhale naye pa ubwenzi. Kodi Yehova anachita bwanji zimenezi?

5. Kodi ndi pa nthawi iti pamene Yehova anapereka koyamba chiyembekezo kwa anthu? Fotokozani. (Genesis 3:15)

5 Werengani Genesis 3:15. Nthawi yoyamba imene Yehova anapereka chiyembekezo kwa anthu, ndi pamene ankamuuza Satana za chiweruzo chimene adzalandire. Mulungu ananeneratu kuti padzakhala “mbadwa” imene idzapulumutse anthu. Mbadwa imeneyi idzawononga Satana n’kukonza zonse zimene anawononga m’munda wa Edeni. (1 Yoh. 3:8) Komabe pochita zimenezi, mbadwayo idzakumana ndi mavuto. Satana adzaukira mbadwayo mpaka kuipha. Zimenezi zikanachititsa kuti Yehova amve ululu waukulu. Komabe iye analolera kumva ululu wonsewo chifukwa amakonda anthu ndipo ankafuna kuwapulumutsa ku uchimo ndi imfa.

KODI ANTHU OCHIMWA AKALE ANATANI KUTI YEHOVA AZISANGALALA NAWO?

6. Kodi amuna okhulupirika monga Abele ndi Nowa anachita chiyani kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova?

6 Kwa zaka zambiri, Yehova wakhala akufotokoza momveka bwino zimene zingathandize anthu ochimwa kuti akhalenso naye pa ubwenzi. Abele yemwe anali mwana wachiwiri wa Adamu ndi Hava anali munthu woyamba kukhulupirira Yehova pambuyo poti makolo ake achimwa. Chifukwa chakuti Abele ankakonda Yehova komanso ankafuna kumusangalatsa ndi kukhala naye pa ubwenzi, anapereka nsembe. Abele anali m’busa choncho anatenga ena mwa ana ankhosa zake n’kuwapereka nsembe. Yehova “anasangalala ndi Abele komanso nsembe yake.” (Gen. 4:4) Yehova anasonyeza kuti ankasangalala ndi nsembe zimene anthu enanso omwe ankamukonda ndi kumukhulupirira monga Nowa ankapereka. (Gen. 8:20, 21) Povomereza nsembe zimenezi, Yehova anasonyeza kuti anthu ochimwa angathe kukhalanso naye pa ubwenzi komanso kuti iye angathe kumasangalala nawo. b

7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Abulahamu ankafunitsitsa kuchita, Yehova atamupempha kuti apereke mwana wake nsembe?

7 Abulahamu ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Yehova anamupempha kuti achite chinthu china chovuta kwambiri chomwe ndi kupereka mwana wake Isaki monga nsembe. Zimenezitu ziyenera kuti zinali zovuta kwambiri kwa Abulahamu. Koma ngakhale zinali choncho, iye anali wokonzeka kumvera. Koma atangotsala pang’ono kupha mwana wakeyo, Mulungu anamuletsa. Chitsanzo chimenechi chimaphunzitsa anthu onse okhulupirira Mulungu mfundo ya choonadi yofunika kwambiri. Mfundo yake ndi yakuti Yehova anali wofunitsitsa kupereka Mwana wake wokondedwa monga nsembe. Izi zikusonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu.​—Gen. 22:1-18.

8. Kodi nsembe zimene zinkaperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo zinkaimira chiyani? (Levitiko 4:27-29; 17:11)

8 Patapita zaka zambiri, Mulungu anapereka Chilamulo kwa Aisiraeli chomwe chinkasonyeza kuti anthu a Mulungu ankafunika kupereka nsembe mobwerezabwereza kuti machimo awo azikhululukidwa. (Werengani Levitiko 4:27-29; 17:11.) Nsembe zimenezi zinkaimira nsembe yaikulu imene ikanadzapulumutsiratu anthu ku uchimo. Aneneri a Mulungu anauziridwa kuti alembe zokhudza mbadwa yolonjezedwa, yomwe ndi Mwana wapadera wa Mulungu. Iwo anafotokoza kuti Mwanayo adzazunzidwa komanso kuphedwa. Iye anali kudzaphedwa ngati nkhosa yoperekedwa nsembe. (Yes. 53:1-12) Ndiye tangoganizani: Yehova anakonza zoti Mwana wake wokondedwa aperekedwe monga nsembe, n’cholinga chofuna kupulumutsa anthu kuphatikizapo inuyo ku uchimo ndi imfa.

KODI YESU ANACHITA CHIYANI KUTI APULUMUTSE ANTHU?

9. Kodi Yohane M’batizi ananena chiyani zokhudza Yesu? (Aheberi 9:22; 10:1-4, 12)

9 Mu 29 C.E., Yohane M’batizi yemwe anali mtumiki wa Mulungu, ataona Yesu wa ku Nazareti ananena kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yoh. 1:29) Mawu amenewa anasonyeza kuti Yesu anali mbadwa imene Mulungu analonjeza. Iye ndi amene akanapereka nsembe imene Mulungu analonjeza. Apa tsopano kuposa ndi kale lonse anthu anali ndi chiyembekezo chodzapulumutsidwa ku uchimo.​—Werengani Aheberi 9:22; 10:1-4, 12.

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ‘anabwera kudzaitana ochimwa’?

10 Yesu ankachita chidwi kwambiri ndi anthu amene ankadzimvera chisoni chifukwa choti anali ochimwa ndipo anawapempha kuti akhale otsatira ake. Iye ankadziwa kuti uchimo ndi umene umachititsa mavuto onse amene anthu amakumana nawo. Choncho iye ankathandiza amuna ndi akazi omwe ankadziwika kuti ndi ochimwa. Pogwiritsa ntchito fanizo, iye ananena kuti: “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” Anawonjezeranso kuti: “Sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Mat. 9:12, 13) Zimenezi ndi zomwedi Yesu ankachita. Iye analankhula mokoma mtima komanso anakhululukira mayi wina yemwe anatsuka mapazi ake ndi misozi. (Luka 7:37-50) Yesu anaphunzitsanso mfundo za choonadi kwa mayi wina wa Chisamariya pachitsime ngakhale kuti ankadziwa kuti mayiyo anali wachiwerewere. (Yoh. 4:7, 17-19, 25, 26) Mulungu anapatsanso Yesu mphamvu yothetsa imfa yomwe ndi zotsatirapo za uchimo. Tikudziwa bwanji zimenezi? Yesu anaukitsa anthu, amuna ndi akazi, ana ndi achikulire omwe.​—Mat. 11:5.

11. N’chifukwa chiyani anthu ochimwa ankamukonda Yesu?

11 N’zosadabwitsa kuti ngakhale anthu omwe ankachita zoipa kwambiri ankamukonda Yesu. Iye ankamvetsa mmene iwo ankamvera ndipo ankawasonyeza chifundo. Iwo sankaopa kulankhula naye. (Luka 15:1, 2) Ndipo Yesu ankawayamikira chifukwa chomukhulupirira. (Luka 19:1-10) Zimenezi zinkasonyeza bwino kuti Atate wake ndi wachifundo. (Yoh. 14:9) Zimene Yesu ankalankhula komanso kuchita zinasonyeza kuti Yehova, yemwe ndi wokoma mtima, amakonda anthu ndipo amafuna kuwathandiza kuti azimumvera komanso kumutumikira ngakhale kuti ndi ochimwa. Yesu amafuna kuti anthu ochimwa alape n’kuyamba kumutsatira.​—Luka 5:27, 28.

12. Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani zokhudza imfa yake?

12 Yesu ankadziwa kuti adzapereka moyo wake monga nsembe. Mobwerezabwereza iye anauza otsatira ake kuti adzaperekedwa m’manja mwa adani komanso kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo. (Mat. 17:22; 20:18, 19) Mogwirizana ndi zimene Yohane komanso aneneri ena ananeneratu, iye ankadziwa kuti nsembe yake idzachotsa machimo a dziko. Yesu anaphunzitsanso kuti akadzapereka moyo wake, ‘adzakokera anthu osiyanasiyana’ kwa iye. (Yoh. 12:32) Anthu ochimwa angasangalatse Yehova ngati amavomereza Yesu kukhala Mbuye wawo komanso kutengera chitsanzo chake. Iwo akamachita zimenezi pamapeto pake ‘adzamasulidwa ku uchimo.’ (Aroma 6:14, 18, 22; Yoh. 8:32) Choncho mofunitsitsa komanso molimba mtima, Yesu analolera kufa imfa yowawa kuti atipulumutse.​—Yoh. 10:17, 18.

13. Kodi Yesu anachitiridwa zinthu ziti pa imfa yake, nanga imfayi ikutiphunzitsa chiyani za Yehova Mulungu? (Onaninso chithunzi.)

13 Yesu anaperekedwa ndi mmodzi wa anzake apamtima, anamangidwa, ananyozedwa, ananeneredwa zabodza, anaweruzidwa kuti aphedwe komanso anazunzidwa. Pamapeto pake asilikali anamutengera kumalo amene anakamuphera pomupachika pamtengo. Yesu anapirira mokhulupirika ululu komanso mavuto onse omwe anakumana nawo. Koma Yehova Mulungu ndi amene anamva ululu kwambiri poona Mwana wake akuvutika. Ngakhale kuti iye ali ndi mphamvu zopanda malire, sanalowererepo n’kuthetsa mavuto omwe Mwana wake anakumana nawo. Popeza kuti Yehova amakonda kwambiri Mwana wake, n’chifukwa chiyani analolera kuti avutike komanso aphedwe? Mwachidule tingati ndi chikondi. Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.”​—Yoh. 3:16.

Polola kuti Mwana wake aphedwe, Yehova anamva ululu wosaneneka n’cholinga choti atipulumutse ku uchimo ndi imfa (Onani ndime 13)


14. Kodi nsembe ya Yesu imatiphunzitsa chiyani?

14 Nsembe ya Yesu ndi umboni waukulu wakuti Yehova amakonda ana a Adamu ndi Hava. Nsembeyi imasonyeza kuti Yehova amakukondani kwambiri inuyo. Iye anachita zazikulu polola kuti amve ululu woopsa n’cholinga choti akupulumutseni ku uchimo ndi imfa. (1 Yoh. 4:9, 10) Choncho iye amafuna kuthandiza wina aliyense wa ife kuti apambane pankhondo yolimba ndi uchimo.

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti mphatso ya Mulungu ya nsembe ya Yesu izitithandiza?

15 Mulungu anatipatsa nsembe ya Mwana wake wobadwa yekha monga mphatso ndipo imatheketsa kuti machimo athu akhululukidwe. Koma kuti Mulungu azitikhululukira pali zomwe tiyenera kuchita. Yohane M’batizi ndiponso Yesu Khristu anafotokoza zomwe tiyenera kuchita, pomwe anati: “Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mat. 3:1, 2; 4:17) Choncho kulapa ndi kofunika kwambiri kuti tithe kulimbana ndi uchimo komanso tikhale pa ubwenzi ndi Atate wathu. Koma kodi kulapa kumatanthauza chiyani, nanga kungatithandize bwanji kuti tizisangalatsabe Yehova ngakhale kuti ndife ochimwa? Nkhani yophunzira yotsatira idzayankha funso limeneli.

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

a TANTHAUZO LA MAWU ENA: M’Baibulo, mawu akuti “uchimo” angaimire zoipa zimene munthu angachite kapena kulephera kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Koma mawuwa angaimirenso kukhala kwathu “ochimwa” chifukwa chakuti ndife ana a Adamu. Tonsefe timafa chifukwa cha uchimo umene tinatengerawu.

b Yehova ankalandira nsembe zanyama zimene anthu okhulupirika omwe anakhalapo Chikhristu chisanayambe ankapereka, chifukwa ankadziwa kuti m’tsogolo Yesu Khristu adzapereka moyo wake kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa mpaka kalekale.​—Aroma 3:25.