Munthu Wofatsa Amasonyeza Kuti Ndi Wanzeru
Mlongo wina dzina lake Toñi amagwira ntchito yosamalira okalamba. Tsiku lina atafika kunyumba ina anaimba belu ndipo mayi wina anatuluka. Mayiyo anayamba kumukalipira komanso kumunyoza n’kumanena kuti wachedwa kubwera kudzasamalira amayi ake okalamba. Sikuti Toñi anachedwadi. Komabe anapepesa mayiyo.
TSIKU lina mayi uja anamukalipiranso. Kodi Toñi anatani? Iye anati: “Kunena zoona zinali zovuta kwambiri. Ankandikalipira popanda chifukwa.” Koma Toñi anapepesanso n’kuuza mayiyo kuti akumvetsa mavuto ake.
Kodi inuyo mukanakhala Toñi mukanatani? Kodi mukanayesetsa kukhala wofatsa kapena zikanakuvutani kuugwira mtima? Kunena zoona, zimakhaladi zovuta kuugwira mtima pakachitika zinthu ngati zimenezi. Komanso kukhala wofatsa kumavuta kwambiri tikakhala ndi mavuto enaake kapena tikaputidwa.
Koma Baibulo limalimbikitsa Akhristu kukhala ofatsa ndipo limanena kuti kufatsako kumasonyeza nzeru. Paja Yakobo analemba kuti: “Kodi pakati panu pali aliyense wanzeru ndi womvetsa zinthu? Ameneyo ayenera kukhala ndi khalidwe labwino limene limasonyeza kuti amachita chilichonse mofatsa ndipo kufatsa kwake kumachokera mu nzeru.” (Yak. 3:13) Koma kodi kufatsa kumasonyeza bwanji nzeru? Nanga tingatani kuti tikhale ofatsa?
KODI KUKHALA WOFATSA KUMATHANDIZA BWANJI?
Kuyankha mofatsa kumathetsa mkangano. “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”—Miy. 15:1.
Miy. 26:21) Pamene kuyankha mofatsa kumathandiza kuti nkhani ithe bwino. Ngakhale munthu amene wakwiya kwambiri akayankhidwa mofatsa, mkwiyo wake umachepa.
Kuyankha mokwiya kuli ngati kuthira mafuta pamoto chifukwa kumangopangitsa kuti zinthu ziipireipire. (Mlongo Toñi anaona kuti zimenezi ndi zoona. Mayi ankamukalipira aja ataona mmene ankayankhira anayamba kulira. Iwo anafotokoza kuti anakhumudwa chifukwa cha mavuto a m’banja lawo ndi mavuto ena. Toñi anayamba kuwalalikira ndipo kenako anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Zonsezi zinatheka chifukwa iye anachita zinthu modekha komanso mwamtendere.
Munthu wofatsa amakhala wosangalala. “Odala [kapena kuti osangalala] ndi anthu amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi.”—Mat. 5:5.
N’chifukwa chiyani anthu ofatsa amakhala osangalala? Anthu ambiri amene poyamba anali amwano komanso okonda kupsa mtima panopa ndi osangalala chifukwa anasintha n’kukhala ofatsa. Moyo wawo unasinthiratu komanso akuyembekezera kudzapeza madalitso ambiri. (Akol. 3:12) Woyang’anira dera wina wa ku Spain dzina lake Adolfo anafotokoza mmene moyo wake unalili asanaphunzire choonadi.
Adolfo anati: “Moyo wanga unali wachabechabe. Ndinali munthu wolusa komanso wachiwawa moti ngakhale anzanga ankandiopa kwambiri. Koma zimene zinachitika tsiku lina zinachititsa kuti ndisinthe. Ndinabayidwa ndi mpeni ka 6 ndipo ndinataya magazi ambiri moti ndinangotsala pang’ono kufa.”
Koma panopa Adolfo amaphunzitsa ena mmene angakhalire ofatsa poona chitsanzo chake komanso zolankhula zake. Anthu ambiri amamukonda chifukwa cha khalidwe lake labwino. Adolfo ananena kuti amasangalala chifukwa choti anasintha ndipo amayamikira Yehova pomuthandiza kuti akhale wofatsa.
Munthu wofatsa amasangalatsa Yehova. “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”—Miy. 27:11.
Yehova wakhala akutonzedwa ndi Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wake wamkulu. Iye akanatha kukwiya kwambiri ndi zimenezi. Koma Baibulo limati Yehova ndi “wosakwiya msanga.” (Eks. 34:6) Tikamayesetsa kumutsanzira pa nkhani yosakwiya msanga komanso kufatsa, timakhala anthu anzeru ndipo timasangalatsa kwambiri mtima wake.—Aef. 5:1.
Masiku ano dzikoli lafika poipa. Nthawi zambiri timakumana ndi anthu “odzimva, odzikweza, onyoza, . . . onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa.” (2 Tim. 3:2, 3) Komabe zimenezi zisamatilepheretse kukhala ofatsa. Paja Baibulo limati, ‘nzeru yochokera kumwamba ndi yamtendere ndi yololera.’ (Yak. 3:17) Choncho tikakhala amtendere komanso ololera, timasonyeza kuti tili ndi nzeru yochokera kwa Mulungu. Nzeru imeneyi imatithandiza kuti tikaputidwa tizikhalabe oleza mtima. Imatithandizanso kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi Chimake cha nzeru.