Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwawerenga mosamala magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

N’chifukwa chiyani makolo amene asamukira dziko lina ayenera kuganizira kwambiri za chilankhulo chimene azigwiritsa ntchito pothandiza ana awo kuti azikonda Yehova?

Ana angaphunzire chilankhulo cha dziko limene asamukira kusukulu kapena kudera limene akukhala. Kudziwa zilankhulo zingapo kungathandize kwambiri ana. Makolo ayenera kuganizira bwino mpingo wachilankhulo chimene ana awo angaphunzire mokwanira zokhudza Yehova. Choncho ayenera kuona ngati akufunika kumasonkhana mumpingo wachilankhulo chawo kapena wachilankhulo cha dzikolo. Makolo achikhristu ayenera kuona kuti kuthandiza ana awo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndi kofunika kwambiri kuposa chilichonse.​—w17.05, tsa. 9-11.

Kodi Yesu ankatanthauza zinthu ziti pamene anafunsa Petulo kuti: “Kodi umandikonda ine kuposa izi?” (Yoh. 21:15)

Zikuoneka kuti Yesu ankanena za nsomba zimene zinali pafupi ndi Petuloyo kapena ntchito ya usodzi. Yesu atamwalira, Petulo anayambiranso ntchito yake ya usodzi. Akhristu ayenera kuona ngati amakonda kwambiri Khristu kuposa ntchito.​—w17.05, tsa. 22-23.

N’chifukwa chiyani Abulahamu anauza mkazi wake kuti anene kuti ndi mlongo wake? (Gen. 12:10-13)

Sara analidi mlongo wake koma wobadwa kwa mayi ena. Sara akananena kuti ndi mkazi wa Abulahamu, mwamuna wakeyo akanaphedwa ndipo cholinga cha Yehova, choti ana a Abulahamu adzakhale mtundu waukulu chikanasokonezeka.​—wp17.3, tsa. 14-15.

Kodi Elias Hutter anagwiritsa ntchito luso lotani pofuna kuthandiza anthu omwe ankafuna kuphunzira Chiheberi?

Iye ankafuna kuti anthu azitha kusiyanitsa masinde a mawu achiheberi a m’Baibulo ndi mawu okhala koyambirira (m’phatikiram’mbuyo) kapena kumapeto (m’phatikiram’tsogolo). Choncho posindikiza Baibulo ankadetsa kwambiri masinde a mawu kuti aoneke mosavuta. Anthu amene anamasulira Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lachingelezi lokhala ndi malifalensi, anagwiritsanso ntchito njira imeneyi pomasulira mawu am’munsi.​wp17.4, tsa. 11-12.

Kodi Mkhristu ayenera kuganizira mfundo ziti pa nkhani yosunga mfuti kuti azidziteteza kwa anthu?

Ayenera kuganizira mfundo izi: Mulungu amaona kuti moyo ndi wopatulika. Yesu sanauze ophunzira ake kuti atenge lupanga n’cholinga choti adziteteze. (Luka 22:36, 38) Tiyenera kusula malupanga athu kuti akhale makasu a pulawo. Moyo ndi wofunika kuposa katundu. Timalemekeza chikumbumtima cha anzathu ndipo tiyenera kupereka chitsanzo chabwino. (2 Akor. 4:2)​—w17.07, tsa. 31-32.

N’chifukwa chiyani nkhani zokhudza moyo wa Yesu ali mwana zimene Mateyu ndi Luka analemba zimasiyana?

Mateyu anafotokoza kwambiri za Yosefe. Mwachitsanzo, anafotokoza zimene Yosefe anachita atadziwa kuti Mariya ali ndi mimba, atauzidwa m’maloto kuti athawire ku Iguputo komanso zimene anachita atauzidwa kuti abwerere ku Isiraeli. Koma Luka anafotokoza kwambiri za Mariya. Mwachitsanzo, anafotokoza za ulendo wa Mariya wokaona Elizabeti komanso zimene anachita pamene Yesu anatsala kukachisi ali mwana.​—w17.08, tsa. 32.

Kodi Baibulo likupezekabe ngakhale kuti linakumana ndi mavuto ati?

Pamene nthawi inkadutsa, matanthauzo a mawu ena a m’Baibulo ankasintha. Ulamuliro ukasintha chilankhulo chachikulu chinkasinthanso. Anthu ena ankaletsa kuti Baibulo limasuliridwe m’zilankhulo zimene anthu ambiri ankadziwa.​—w17.09, tsa. 19-21.

Kodi aliyense ali ndi mngelo amene amamuyang’anira?

Ayi. Yesu ananena kuti angelo a ophunzira ake amaona nkhope ya Mulungu. (Mat. 18:10) Koma sikuti ankatanthauza kuti aliyense ali ndi mngelo amene amamuteteza. M’malomwake ankatanthauza kuti angelo amachita chidwi ndi ophunzira ake ndipo amafuna kuti zinthu ziziwayendera bwino.​—wp17.5, tsa. 5.

Kodi chikondi chapamwamba kwambiri ndi chiti?

Chikondi cha a·gaʹpe chimakhala chapamwamba munthu akachisonyeza chifukwa chotsatira mfundo zabwino kwambiri. Munthu amene ali ndi chikondi chimenechi amachitira ena zabwino popanda kufuna phindu lililonse, ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa anthu amene si anzake.​—w17.10, tsa. 7.