Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndili ndi Chiyembekezo mwa Mulungu”

“Ndili ndi Chiyembekezo mwa Mulungu”

“Adamu womalizira anakhala mzimu wopatsa moyo.”​—1 AKOR. 15:45.

NYIMBO: 151, 147

1-3. (a) Kodi ndi mfundo iti imene tiyenera kuiona kuti ili m’gulu la mfundo zikuluzikulu zimene timakhulupirira? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti nkhani ya kuuka kwa akufa ndi yofunika kwambiri? (Onani chithunzi choyambirira.)

KODI munthu atakuuzani kuti mutchule mfundo zikuluzikulu zimene mumakhulupirira, inuyo mungatchule ziti? N’zosakayikitsa kuti munganene kuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse komanso kutipatsa moyo. Munganenenso kuti Yesu Khristu anafa kuti apereke dipo lotiwombola. Simungalepherenso kunena kuti m’tsogolomu dzikoli lidzakhala paradaiso ndipo anthu a Mulungu adzakhalamo kwamuyaya. Koma kodi mfundo yoti akufa adzauka mungaiikenso m’gululi?

2 Ngakhale kuti tikuyembekezera kupulumuka chisautso chachikulu n’kulowa m’dziko latsopano, tili ndi zifukwa zomveka zonenera kuti kuuka kwa akufa ndi mfundo yofunika kwambiri. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti mfundo imeneyi ndi yofunika pa chikhulupiriro chathu. Iye anati: “Ngati akufa sadzauka, ndiye kuti Khristu nayenso sanauke.” Kunena zoona zikanakhala kuti Khristu sanauke ndiye kuti sakanakhala Mfumu yathu ndipo zonse zimene timaphunzitsa pa nkhani ya ulamuliro wa Khristu zikanakhala zopanda ntchito. (Werengani 1 Akorinto 15:12-19.) Koma timadziwa kuti Yesu anaukitsidwa. Ndipo kukhulupirira zimenezi kumatisiyanitsa ndi Asaduki amene ankakana zoti akufa angauke. Ngakhale pamene anthu akutinyoza sitisiya kukhulupirira ndi mtima wonse zoti akufa adzauka.​—Maliko 12:18; Mac. 4:2, 3; 17:32; 23:6-8.

3 Pamene Paulo ankafotokoza mfundo zimene zili m’gulu la “chiphunzitso choyambirira cha Khristu” anatchulanso za “kuuka kwa akufa.” (Aheb. 6:1, 2) Iye ananenanso motsindika kuti ankakhulupirira zoti akufa adzauka. (Mac. 24:10, 15, 24, 25) Ngakhale kuti mfundo imeneyi ili m’gulu la chiphunzitso choyambirira kapena kuti “mfundo zoyambirira za m’mawu opatulika a Mulungu,” tikhoza kunenabe kuti ndi mfundo yozama. (Aheb. 5:12) N’chifukwa chiyani tikutero?

4. Kodi munthu angafunse mafunso ati okhudza kuuka kwa akufa?

4 Anthu ambiri akayamba kuphunzira Baibulo, amawerenga za anthu amene anaukitsidwa monga Lazaro. Amaphunziranso kuti Abulahamu, Yobu ndiponso Danieli sankakayikira zoti m’tsogolomu akufa adzauka. Koma kodi inuyo mungayankhe bwanji ngati munthu atakufunsani umboni wakuti lonjezo la kuuka kwa akufa likhoza kukwaniritsidwa ngakhale patapita zaka zambirimbiri? Nanga kodi Baibulo lingatithandize kudziwa nthawi imene akufa adzauke? Mfundo zimenezi ndi zofunika kwambiri pa chikhulupiriro chathu. Choncho tingachite bwino kuona zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.

LONJEZO LINAKWANIRITSIDWA PATAPITA ZAKA ZAMBIRI

5. Kodi tiyamba ndi kukambirana chiyani munkhaniyi?

5 Mwina sitingavutike kukhulupirira nkhani ya kuuka kwa munthu yemwe anali atangomwalira kumene. (Yoh. 11:11; Mac. 20:9, 10) Koma nanga bwanji lonjezo loti munthu adzauka patapita zaka zambirimbiri? Kodi inuyo mungakhulupirire lonjezo lotereli, kaya litaperekedwa munthu atangomwalira kumene kapena atamwalira kalekale? Kunena zoona pali lonjezo lina lokhudza kuuka kwa munthu limene linakwaniritsidwa patapita zaka zambiri ndipo nkhani yake ndi yoti inuyo mumaikhulupirira. Kodi nkhani yake ndi iti? Nanga nkhaniyi ingakuthandizeni bwanji kukhulupirira kuti akufa adzauka m’tsogolomu?

6. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji mawu a pa Salimo 118?

6 Kuti timvetse nkhaniyi, tiyeni tikambirane lemba la Salimo 118, lomwe anthu ena amanena kuti Davide ndi amene analemba. Musalimoli muli mawu ochonderera Yehova akuti: “Haa! Inu Yehova, chonde tipulumutseni. . . . Wodala ndi Iye wobwera m’dzina la Yehova.” Mwina mukukumbukira kuti anthu ananena mawu okhudza Mesiyawa pamene Yesu ankalowa mu Yerusalemu pa Nisani 9. (Sal. 118:25, 26; Mat. 21:7-9) Koma kodi Salimo 118 linalosera zotani zokhudza munthu amene adzauke kwa akufa patapita zaka zambirimbiri? Salimoli linaloseranso kuti: “Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.”​—Sal. 118:22.

“Omanga nyumba” anakana Mesiya (Onani ndime 7)

7. Kodi Ayuda anakana bwanji Yesu?

7 “Omanga nyumba,” kapena kuti atsogoleri achiyuda, anakana Mesiya. Sikuti anangokana kutsatira Yesu kapena kukhulupirira kuti anali Khristu. Ayuda ambiri anafika pofuna kumupha. (Luka 23:18-23) Ndipo iwo ndi amene anachititsa kuti Yesu aphedwe.

Yesu anaukitsidwa kuti akhale “mwala wofunika kwambiri wapakona” (Onani ndime 8 ndi 9)

8. N’chiyani chinachitika kuti Yesu akhale “mwala wofunika kwambiri wapakona”?

8 Ngati Yesu anakanidwa komanso kuphedwa, kodi akanakhala bwanji “mwala wofunika kwambiri wapakona”? Zimenezi zikanatheka pokhapokha ngati akanaukitsidwa. Nayenso Yesu ankadziwa zimenezi. Iye anafotokoza fanizo la alimi amene anamenya anthu omwe anatumizidwa ndi mwini munda. Zimene alimiwa anachita ndi zofanana ndi zomwe Aisiraeli ankachitira aneneri amene anatumizidwa ndi Mulungu. M’fanizoli mwini munda anafika potumiza mwana wake weniweni yemwe akanalandira mundawo monga cholowa. Koma kodi alimiwo anamulandira bwino? Ayi. Iwo anamupha mwanayo. Yesu atamaliza kufotokoza fanizoli anatchulanso mawu a ulosi a pa Salimo 118:22 aja. (Luka 20:9-17) Nayenso mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito mawu amenewa polankhula kwa ‘olamulira, akulu ndiponso alembi’ achiyuda omwe “anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu.” Petulo anawauza kuti: “Yesu Khristu Mnazareti uja, amene inu munamupachika pamtengo, . . . Mulungu anamuukitsa kwa akufa.” Kenako iye ananena mosapita m’mbali kuti: “Yesu ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’”​—Mac. 3:15; 4:5-11; 1 Pet. 2:5-7.

9. Kodi lemba la Salimo 118:22 linalosera za nkhani iti yofunika?

9 Mawu a pa Salimo 118:22 amene analosera za kuuka kwa munthu wakufa analembedwa zaka zambirimbiri zimenezi zisanachitike. Analosera kuti Mesiya adzakanidwa n’kuphedwa ndipo kenako adzaukitsidwa n’kukhala mwala wofunika kwambiri wapakona. Yesu ataphedwa anaukitsidwadi ndipo anapatsidwa udindo wofunika kwambiri wopulumutsa anthu.​—Mac. 4:12; Aef. 1:20.

10. (a) Kodi lemba la Salimo 16:10 linalosera za chiyani? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti lemba la Salimo 16:10 silinalosere za Davide?

10 Tiyeni tikambiranenso vesi lina limene linalosera za kuuka kwa akufa. Mawu ake analembedwa kudakali zaka zoposa 1,000 kuti nkhani yake ichitike. Nkhani imeneyi ikhoza kukutsimikizirani kuti lonjezo loti akufa adzauka likhoza kukwaniritsidwa ngakhale patapita zaka zambirimbiri. Mu Salimo 16, lomwe anthu amati Davide ndi amene analemba, muli mawu akuti: “Simudzasiya moyo wanga m’Manda. Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.” (Sal. 16:10) Apa Davide sankatanthauza kuti iyeyo sadzamwalira kapena kuti sadzakhala m’manda. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti Davide anakalamba n’kufa. Amasonyezanso kuti atafa “anagona limodzi ndi makolo ake, ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide.” (1 Maf. 2:1, 10) Ndiye kodi lemba la Salimo 16:10 linalosera za ndani?

11. Kodi ndi liti pamene Petulo anafotokoza lemba la Salimo 16:10?

11 Baibulo limatithandiza kuyankha funso limeneli. Petulo anafotokoza lemba la Salimo 16:10 kwa Ayuda komanso anthu ena amene analowa Chiyuda. Anachita zimenezi patapita zaka zoposa 1,000 kuchokera pamene salimoli linalembedwa, komanso pambuyo poti Yesu waphedwa n’kuukitsidwa. (Werengani Machitidwe 2:29-32.) Iye ananena kuti Davide anamwaliradi n’kuikidwa m’manda ndipo anthu amene ankamvetserawo ankadziwa bwino zimenezi. Baibulo silinena kuti anthuwo anatsutsa pamene Petulo ankanena kuti Davide “anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka” kwa Mesiya.

12. Kodi lemba la Salimo 16:10 linakwaniritsidwa bwanji, nanga zimenezi zimatithandiza bwanji kukhulupirira kuti akufa adzauka?

12 Petulo anatsindika mfundo imeneyi ponena mawu a Davide pa Salimo 110:1. (Werengani Machitidwe 2:33-36.) Iye anagwiritsa ntchito Malemba pothandiza anthuwo kuzindikira kuti Yesu anali “Ambuye ndi Khristu.” Ndipo anthuwo anavomerezanso kuti lemba la Salimo 16:10 linakwaniritsidwa pamene Yesu anaukitsidwa. Pa nthawi ina, mtumwi Paulo anakambirananso ndi Ayuda mumzinda wa Antiokeya wa ku Pisidiya pogwiritsa ntchito ulosi wa Davide wonena za Yesu. Anthuwo anachita chidwi kwambiri ndipo ankafuna kumva zambiri. (Werengani Machitidwe 13:32-37, 42.) Nafenso timalimbikitsidwa kudziwa kuti maulosi a m’Baibulo amenewa anakwaniritsidwa ngakhale kuti analembedwa kudakali nthawi yaitali zinthuzo zisanachitike.

NTHAWI YOUKITSIDWA

13. Kodi tingafunse mafunso ati pa nkhani ya kuuka kwa akufa?

13 Mfundo yoti lonjezo la kuukitsidwa likhoza kukwaniritsidwa patapita zaka zambirimbiri iyenera kutilimbikitsa kwambiri. Koma mwina tingafunse kuti: ‘Kodi zimenezi zikutanthauza kuti tidikira nthawi yaitali kwambiri kuti tidzaonane ndi anzathu amene anamwalira? Kodi anzathu amene anamwalira adzauka liti?’ Yesu anauza ophunzira ake kuti pali zinthu zina zimene iwowo sankazidziwa komanso sangathe kuzidziwa. Iye anawauzanso kuti pali “nthawi kapena nyengo zimene Atate waziika pansi pa ulamuliro wake.” (Mac. 1:6, 7; Yoh. 16:12) Koma izi sizikutanthauza kuti palibiretu mfundo zotithandiza kudziwa nthawi imene anthu adzauke.

14. Kodi kuuka kwa Yesu kumasiyana bwanji ndi kwa anthu ena amene anali ataukitsidwa kale?

14 Kuti tidziwe za nthawiyi, tiyeni tikambirane zimene Baibulo linalosera pa nkhani ya kuuka kwa akufa. Nkhani yoyamba komanso yofunika kwambiri ndi ya kuuka kwa Yesu. Iye akanapanda kuukitsidwa, tonsefe sitikanakhala ndi chiyembekezo chodzaonananso ndi anzathu amene anamwalira. Akufa amene anthu monga Eliya ndi Elisa anawaukitsa, anadzafanso ndipo matupi awo anawonongeka m’manda. Koma ponena za Yesu, Baibulo limati: “Khristu waukitsidwa kwa akufa, sadzafanso. Imfa sikuchitanso ufumu pa iye.” Iye ali kumwamba ndipo adzakhalabe “ndi moyo kwamuyaya.”​—Aroma 6:9; Chiv. 1:5, 18; Akol. 1:18; 1 Pet. 3:18.

15. Kodi mawu oti Yesu ndi “chipatso choyambirira” akutanthauza chiyani?

15 Yesu anali woyamba kuukitsidwa m’njira imeneyi ndipo kuuka kwake ndi kofunika kwambiri kuposa kuuka kwa munthu wina aliyense. (Mac. 26:23) Koma Baibulo linanena za anthu enanso amene adzaukitsidwe kupita kumwamba n’kukhala ndi matupi auzimu. Paja Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti adzakalamulira limodzi naye kumwamba. (Luka 22:28-30) Koma kuti alandire mphoto imeneyi, anafunika kufa kaye kenako n’kuukitsidwa ndi thupi lauzimu. Pa nkhani imeneyi, Paulo analemba kuti: “Khristu anaukitsidwa kwa akufa, n’kukhala chipatso choyambirira cha amene akugona mu imfa.” Kenako anasonyeza kuti padzakhala anthu enanso amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Choyamba Khristu, amene ndi chipatso choyambirira, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.”​1 Akor. 15:20, 23.

16. Kodi ndi mawu ati amene angatithandize kudziwa nthawi ya kuukitsidwa kwa opita kumwamba?

16 Mawu oti “pa nthawi ya kukhalapo kwake” angatithandize kudziwa nthawi ya kuukitsidwa kwa anthu opita kumwamba. Kwa zaka zambiri, a Mboni za Yehova akhala akufotokoza kuchokera m’Malemba kuti nthawi ya “kukhalapo” kwa Yesu inayamba mu 1914. Nthawiyi ikupitirira ndipo mapeto a dziko loipali ali pafupi kwambiri.

17, 18. N’chiyani chidzachitikire odzozedwa ena pa nthawi ya kukhalapo kwa Khristu?

17 Pa nkhani ya oukitsidwa kupita kumwamba, Baibulo limanenanso kuti: “Sitikufuna kuti mukhale osadziwa za amene akugona mu imfa . . . Pakuti ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa ndi kuukanso, ndiye kuti amenenso agona mu imfa kudzera mwa Yesu, Mulungu adzawasonkhanitsa kuti akhale naye limodzi . . . Ife amoyofe amene tidzakhalapo pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene agona mu imfa. Chifukwa Ambuye mwini adzatsika kumwamba, ndi mfuu yolamula . . . Ndipo amene anafa mwa Khristu adzauka choyamba. Pambuyo pake ife amoyo otsalafe, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa m’mitambo kukakumana ndi Ambuye m’mlengalenga, ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.”​—1 Ates. 4:13-17.

18 Malinga ndi lembali, kuuka koyamba kunayenera kuchitika pambuyo poti nthawi ya “kukhalapo” kwa Khristu yayamba. Odzozedwa amene adzakhalebe moyo pa nthawi ya chisautso chachikulu ‘adzatengedwa m’mitambo.’ (Mat. 24:31) Tinganene kuti anthu amene ‘adzatengedwewo’ ‘sadzagona mu imfa’ chifukwa chakuti sipadzadutsa nthawi yaitali ali akufa. Iwo ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza.’​—1 Akor. 15:51, 52.

19. Kodi Baibulo likamanena za “kuuka kwabwino kwambiri” limatanthauza chiyani?

19 Masiku ano, Akhristu ambiri si odzozedwa ndipo sanaitanidwe kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. M’malomwake akuyembekezera “tsiku la Yehova” pamene dziko loipali lidzawonongedwa. Palibe amene akudziwa deti limene tsikuli lidzafike koma pali umboni wotsimikizira kuti layandikira kwambiri. (1 Ates. 5:1-3) Pambuyo pa tsikuli, anthu ena adzaukitsidwa kuti akhale m’paradaiso padziko lapansi. Anthu amene adzaukewo adzakhala ndi mwayi wothandizidwa kuti akhale angwiro komanso apatsidwe moyo wosatha. Kumeneku kudzakhala “kuuka kwabwino kwambiri” chifukwa chakuti sizidzakhala ngati zimene zinachitika m’mbuyomu. Paja m’mbuyomo “akazi analandira akufa awo amene anauka” koma kenako oukawo anadzafanso.​—Aheb. 11:35.

20. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti anthu adzauka mwadongosolo m’dziko latsopano?

20 Ponena za anthu amene adzapite kumwamba, Baibulo limanena kuti iwo adzauka mwadongosolo, “aliyense pamalo ake.” (1 Akor. 15:23) Sitikukayikira kuti anthu ouka padzikoli adzaukanso mwadongosolo. Mfundo imeneyi ndi yochititsa chidwi koma imabweretsa mafunso ambiri. Kodi anthu amene adzafe Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu utatsala pang’ono kuyamba, ndi amene adzayambe kuuka n’cholinga choti adzalandiridwe ndi anthu amene akuwadziwa? Nanga kodi atumiki okhulupirika akale amene ali ndi luso lotha kutsogolera anthu adzauka msanga n’cholinga choti adzathandize anthu a Mulungu kukhala mwadongosolo m’dziko latsopano? Kodi anthu amene sanatumikirepo Yehova adzauka pa nthawi iti, nanga adzaukira kuti? Koma kodi pali chifukwa choti tiziswa mitu kuganizira kwambiri mafunso amenewa? Kunena zoona ndi bwino kungoyembekezera n’kudzaona zonse pa nthawiyo. Zidzakhalatu zochititsa chidwi kwambiri kuona mmene Yehova adzayendetsere zinthu pa nthawi imeneyo.

21. Kodi inuyo muli ndi chiyembekezo chiti pa nkhani ya kuuka kwa akufa?

21 Chofunika panopa n’kuyesetsa kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova amene watilonjeza kudzera mwa Yesu kuti anthu onse amene akuwakumbukira adzauka. (Yoh. 5:28, 29; 11:23) Posonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu youkitsa akufa, Yesu ananena kuti anthu monga Abulahamu, Isaki ndi Yakobo ‘ndi amoyo kwa iye.’ (Luka 20:37, 38) Panopa tili ndi zifukwa zomveka zolankhulira ngati Paulo amene ananena kuti: “Ine ndili ndi chiyembekezo mwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka” kwa akufa.​—Mac. 24:15.