NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) December 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa February 3–March 1, 2020.

Pali Nthawi Yogwira Ntchito ndi Nthawi Yopuma

Nkhaniyi itithandiza kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhani ya ntchito ndi kupuma ndipo chitsanzo chake ndi cha lamulo la Sabata limene Aisiraeli anapatsidwa.

Yehova Anakonza Zoti Tikhale ndi Ufulu

Chaka cha Ufulu chimatikumbutsa zimene Yehova anakonza zoti tikhale ndi ufulu.

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani Chilamulo chinkanena kuti ngati mwamuna anagwirira mtsikana wolonjezedwa kukwatiwa ali “kuthengo” ndipo anakuwa, mtsikanayo sankaimbidwa mlandu koma mwamunayo?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Pamene Satana anauza Hava kuti sadzafa akadya chipatso cha mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa, kodi ankanena za mfundo imene yafala masiku ano yakuti mzimu wa munthu suufa?

Kodi Mumamudziwa Bwino Yehova?

Kodi kumudziwa Yehova n’kutani, nanga tingaphunzire chiyani kwa Mose ndi Mfumu Davide pa nkhani yokhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

Makolo Ayenera Kuphunzitsa Ana Awo Kukonda Yehova

Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti azikonda Yehova komanso kumutumikira?

“Muziyamika pa Chilichonse”

Kukhala oyamikira kumatithandiza m’njira zambiri.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwasangalala powerenga nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda a posachedwapa? Tayesani kuyankha mafunso awa.

Mlozera Nkhani wa Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2019

Mlozera nkhani wa nkhani zonse zotuluka m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a 2019, ndipo zalembedwa motsatira mitu yake.