Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mungayankhe mafunso otsatirawa ochokera m’magazini a Nsanja ya Olonda a 2019?

Kodi lonjezo la Mulungu lakuti: “Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana” limatanthauza chiyani? (Yes. 54:17)

Sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatiteteza pamene “anthu ankhanza akuwomba” ngati mphepo. (Yes. 25:4, 5) Adani athu sangathe kutiwonongeratu.​—w19.01, tsa. 6-7.

Kodi zimene Mulungu anachita ndi Akanani komanso Aisiraeli osamvera zimasonyeza bwanji kuti iye ndi wachilungamo?

Mulungu anapereka chiweruzo kwa anthu amene ankachita chiwerewere kapena kupondereza akazi ndi ana. Koma anadalitsa anthu amene ankamumvera komanso kuchitira ena zinthu mwachilungamo.​—w19.02, tsa. 22-23.

Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tili pamalo amene munthu wosakhulupirira akupemphera?

Tikhoza kungokhala chete ndiponso kusonyeza ulemu koma osanena kuti “ame” kapena kugwirana manja ndi ena. Tikhozanso kupereka pemphero lathu chamumtima.​—w19.03, tsa. 31.

N’chifukwa chiyani kugwirira mwana ndi tchimo lalikulu?

Munthu amene wagwirira mwana amakhala kuti wachimwira mwanayo, mpingo, boma komanso Mulungu. Akulu ayenera kutsatira malamulo okanena ku boma ngati wina akuganiziridwa kuti wagwirira mwana.​—w19.05, tsa. 9-10.

Kodi mungasinthe bwanji mphamvu zoyendetsa maganizo anu?

Mfundo zothandiza ndi izi: Muzipemphera kwa Yehova. Muzisinkhasinkha n’cholinga choti muzidzifufuza. Muzisankhanso mwanzeru anthu ocheza nawo.​—w19.06, tsa. 11.

Kodi tingakonzekere bwanji kuzunzidwa?

Tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Tizikhulupirira kuti amatikonda ndipo sadzatisiya. Tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse komanso kupemphera pafupipafupi. Tisamakayikire madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse. Tiziloweza malemba amene timawakonda kwambiri komanso nyimbo zotamanda Mulungu.​—w19.07, tsa. 2-4.

Kodi tingathandize bwanji achibale athu kuti adzapulumuke?

Tiyenera kuwamvetsa, kukhala ndi khalidwe labwino, kukhala oleza mtima komanso kuchita zinthu mwaulemu.​—w19.08, tsa. 15-17.

Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjeza pa Mateyu 11:28, kodi timatsitsimulidwa bwanji?

Tili ndi oyang’anira achikondi, anzathu abwino komanso ntchito yabwino kwambiri.​—w19.09, tsa. 23.

Kodi Mulungu angatipatse bwanji mtima wofuna kuchita zinazake komanso mphamvu zochitira zinthuzo? (Afil. 2:13)

Tikamawerenga Mawu a Mulungu komanso kuwasinkhasinkha, Mulungu angatipatse mtima wofuna kuchita zofuna zake komanso mphamvu zochitira zinthuzo. Mzimu wake ungawonjezere luso limene tili nalo.​—w19.10, tsa. 21.

Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kusankha zochita mwanzeru?

Pali zinthu 5 izi: Tizifufuza mokwanira. Tizipempha Mulungu kuti atipatse nzeru. Tiziganizira zifukwa zake. Tizidziwa bwinobwino zimene tikufuna kuchita. Tizidziwa zimene tingakwanitse.​—w19.11, tsa. 27-29.

Kodi maganizo oti mzimu suufa anayamba ndi zimene Satana anauza Hava?

Zikuoneka kuti ayi. Satana anauza Hava kuti sadzafa osati thupi lake lidzafa koma mzimu wake udzakhalabe ndi moyo kwinakwake. Mfundo zilizonse zabodza sizinapitirire pambuyo pa Chigumula. Zikuoneka kuti kukhulupirira kuti mzimu suufa kunayamba nthawi inayake Mulungu asanabalalitse anthu omwe ankamanga nsanja ya Babele.​—w19.12, tsa. 15.