Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 51

Kodi Mumamudziwa Bwino Yehova?

Kodi Mumamudziwa Bwino Yehova?

“Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani, pakuti simudzasiya ndithu anthu okufunafunani, inu Yehova.”—SAL. 9:10.

NYIMBO NA. 56 Inuyo Panokha Muzikonda Kwambiri Choonadi

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Kodi nkhani ya Angelito ikusonyeza kuti aliyense ayenera kuchita chiyani?

KODI makolo anu ndi a Mboni za Yehova? Ngati ndi choncho, dziwani kuti sangakulimbitsireni ubwenzi wanu ndi Yehova. Kaya makolo anu amatumikira Mulungu kapena ayi, munthu aliyense payekha amafunika kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova.

2 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Angelito. Iye anakulira m’banja la Mboni. Koma ali wamng’ono sanali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Iye anati: “Ndinkangotumikira Yehova chifukwa chakuti n’zimene anthu a m’banja lathu ankachita.” Kenako anaganiza zoyamba kuwerenga kwambiri Baibulo, kusinkhasinkha komanso kupemphera kwa Yehova pafupipafupi. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndikhoza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Atate wanga Yehova pokhapokha ngati ndamudziwa bwino.” Nkhani ya Angelito ingatichititse kufunsa kuti: Kodi kungodziwa Yehova kumasiyana bwanji ndi kumudziwa bwino? Nanga tingatani kuti timudziwe bwino?

3. Kodi kungodziwa Yehova kumasiyana bwanji ndi kumudziwa bwino?

3 Tinganene kuti munthu amadziwa Yehova ngati amadziwa dzina lake komanso zinthu zina zimene ananena kapena kuchita. Koma pamafunika zambiri kuti munthu amudziwe bwino. Tiyenera kupeza nthawi yophunzira za Yehova komanso makhalidwe ake abwino. Tikatero m’pamene timayamba kumvetsa zimene zimamuchititsa kunena kapena kuchita zinthu. Izi zingatithandize kuzindikira ngati amasangalala ndi zimene timaganiza, kusankha komanso kuchita.

4. Kodi kukambirana chitsanzo cha anthu otchulidwa m’Baibulo kungatithandize bwanji?

4 Anthu ena akhoza kutinyoza chifukwa choti tikufuna kutumikira Yehova ndipo akhoza kutitsutsa kwambiri tikayamba kusonkhana ndi anthu ake. Koma tikamadalira Yehova, iye sangatisiye. Kumudalira kungathandize kuti tikhale naye pa ubwenzi wosatha. Koma kodi n’zothekadi kumudziwa bwino Yehova? Inde. Chitsanzo cha anthu ngati Mose ndi Mfumu Davide chimatitsimikizira kuti zimenezi n’zotheka. Tiyeni tsopano tikambirane zimene anthu awiriwa anachita ndipo tiyankha mafunso awa: Kodi iwo anatani kuti adziwe bwino Yehova? Nanga tikuphunzira chiyani pa zimene anachita?

MOSE ANAONA “WOSAONEKAYO”

5. Kodi Mose anasankha kuchita chiyani?

5 Mose anasankha kutumikira Mulungu. Mose ali ndi zaka pafupifupi 40, anasankha kugwirizana ndi Aheberi, omwe anali anthu a Mulungu, m’malo motchedwa “mwana wa mwana wamkazi wa Farao.” (Aheb. 11:24) Iye analolera kuti asakhale ndi udindo wapamwamba koma agwirizane ndi Aheberi, omwe anali akapolo ku Iguputo. Zimenezi zikanachititsa kuti Farao, yemwe anali wolamulira wamphamvu komanso anthu ankamuona kuti anali mulungu, amukwiyire kwambiri. Apatu Mose anasonyeza chikhulupiriro cholimba. Iye ankadalira Yehova ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova moyo wake wonse.​—Miy. 3:5.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Mose?

6 Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mose? Tonsefe tiyeneranso kusankha zochita pa nkhani yotumikira Mulungu komanso kugwirizana ndi anthu ake. Mwina tingafunike kudzimana zinthu zina kuti tizitumikira Mulungu ndipo anthu amene sadziwa Yehova akhoza kutitsutsa. Koma tikamadalira Atate wathu wakumwamba, iye sangatisiye.

7-8. Kodi Mose anapitiriza kuphunzira za chiyani?

7 Mose anapitiriza kuphunzira za makhalidwe a Yehova komanso kuchita zimene amafuna. Mwachitsanzo, Mose atauzidwa kuti atsogolere Aisiraeli pochoka ku ukapolo, iye ankadzikayikira moti anauza Yehova mobwerezabwereza kuti sangakwanitse. Mulungu anamuchitira chifundo kwambiri, ndipo anamuthandiza. (Eks. 4:10-16) Chifukwa cha zimenezi, Mose anakwanitsa kupereka mauthenga amphamvu a chiweruzo kwa Farao. Iye anaona Yehova akugwiritsa ntchito mphamvu zake populumutsa Aisiraeli n’kuwononga Farao ndi anthu ake m’Nyanja Yofiira.​—Eks. 14:26-28; Sal. 136:15.

8 Mose atachoka ku Iguputo ndi Aisiraeli, iwo ankangokhalira kudandaula. Koma Mose anaona Yehova akuleza mtima kwambiri pochita zinthu ndi anthu amene anawamasula ku ukapolowa. (Sal. 78:40-43) Pa nthawi ina, Mose atapempha Yehova kuti asinthe maganizo ake, iye anasonyeza kudzichepetsa n’kusintha maganizowo.​—Eks. 32:9-14.

9. Malinga ndi Aheberi 11:27, kodi Mose anali pa ubwenzi wotani ndi Yehova?

9 Mose atachoka ku Iguputo ndi Aisiraeli, ubwenzi wake ndi Yehova unalimba kwambiri moti zinali ngati ankaona Atate wake wakumwambayo. (Werengani Aheberi 11:27.) Baibulo limasonyeza kuti ubwenzi wawo unali wolimba kwambiri chifukwa limanena kuti: “Yehova anali kulankhula ndi Mose pamasom’pamaso, mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake.”​—Eks. 33:11.

10. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti timudziwe bwino Yehova?

10 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Kuti timudziwe bwino Yehova, tiyenera kuphunzira za makhalidwe ake komanso kuchita zimene amafuna. Yehova amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Choncho tikamaphunzitsa anthu za Mulungu timakhala tikuchita zimene iye amafuna.

11. Kodi kuphunzitsa anthu za Yehova kumatithandiza bwanji kuti nafenso timudziwe bwino?

11 Nthawi zambiri tikamaphunzitsa anthu za Yehova ifenso timayamba kumudziwa bwino. Mwachitsanzo, timaona umboni wakuti Yehova ndi wachifundo akamatitsogolera kuti tipeze anthu amtima wabwino. (Yoh. 6:44; Mac. 13:48) Timaonanso mphamvu za Mawu a Mulungu zikuthandiza anthu amene timaphunzira nawo kuti asiye makhalidwe oipa n’kuyamba kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Komanso timaona umboni wakuti Mulungu ndi woleza mtima akamapatsa anthu am’gawo lathu mipata yambiri yoti aphunzire za iye n’kudzapulumuka.​—Aroma 10:13-15.

12. Malinga ndi Ekisodo 33:13, kodi Mose anapempha chiyani, nanga n’chifukwa chiyani anapempha zimenezi?

12 Mose ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi wofunika kwambiri. Ngakhale atachita zinthu zodabwitsa m’dzina la Mulungu, Mose anapempha Yehova kuti amuthandize kumudziwa bwino. (Werengani Ekisodo 33:13.) Iye anali ndi zaka za m’ma 80 pamene anapempha zimenezi, koma ankadziwa kuti panali zambiri zoti aphunzirebe zokhudza Atate wake wakumwamba.

13. Kodi njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi iti?

13 Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Kaya tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kuonabe kuti ubwenzi wathu ndi iye ndi wamtengo wapatali. Njira imodzi imene tingasonyezere kuti timayamikira ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi kupemphera kwa iye.

14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kupemphera kungatithandize kwambiri kumudziwa bwino Mulungu?

14 Anthu amagwirizana kwambiri akamakambirana momasuka. Choncho muzilimbitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu popemphera kwa iye pafupipafupi ndipo musamaope kumuuza zamumtima mwanu. (Aef. 6:18) Mlongo wina wa ku Turkey dzina lake Krista anati: “Nthawi iliyonse imene ndimapemphera kwa Yehova n’kuona akundithandiza, ndimayamba kumukonda kwambiri komanso kumudalira. Kuona mmene Yehova amayankhira mapemphero anga kwandithandiza kumuona kuti ndi Atate wanga komanso Mnzanga wapamtima.”

MUNTHU WAPAMTIMA WA YEHOVA

15. Kodi Yehova anafotokoza bwanji Mfumu Davide?

15 Mfumu Davide anabadwira mu mtundu umene unkalambira Yehova Mulungu. Koma sikuti iye ankangolambira Mulungu potsatira zimene anthu a m’banja lake ankachita. Iye payekha analimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova ndipo Yehovayo ankamukonda kwambiri. Mulungu anafika ponena kuti Davide anali ‘munthu wapamtima pake.’ (Mac. 13:22) Kodi zinatani kuti Davide ayambe kugwirizana kwambiri ndi Yehova?

16. Kodi Davide anaphunzira chiyani poona chilengedwe?

16 Davide anaphunzira za Yehova poona chilengedwe. Davide ali wamng’ono ankakhala nthawi yaitali akuweta nkhosa za bambo ake. N’kutheka kuti pa nthawi imeneyi m’pamene anayamba kuganizira kwambiri zinthu zimene Yehova analenga. Mwachitsanzo, iye akayang’ana kumwamba sankangoona nyenyezi basi. Ayenera kuti ankazindikiranso makhalidwe a amene analenga nyenyezizo. Davide anafika polemba kuti: “Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu. Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.” (Sal. 19:1, 2) Iye akaganizira mmene Yehova analengera anthu ankaona kuti Yehovayo ndi wanzeru kwambiri. (Sal. 139:14) Iye akaganizira zinthu zonse zimene Yehova wachita ankazindikira kuti ndi wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi Yehovayo.​—Sal. 139:6.

17. Kodi kuganizira kwambiri zinthu zam’chilengedwe kungatithandize kuphunzira chiyani?

17 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kuganizira kwambiri zinthu zam’chilengedwe. Tisamangokhala m’dziko lokongola limene Yehova anatilengera koma tizichitanso chidwi ndi zinthu zimene analenga. Tsiku lililonse tiziganizira zimene tingaphunzire zokhudza Yehova pa zinthu monga zomera, nyama komanso anthu. Tikatero, tsiku ndi tsiku tiziphunzira zinthu zambiri zokhudza Atate wathu. (Aroma 1:20) Zimenezi zidzathandiza kuti chikondi chathu kwa iye chiziwonjezereka tsiku lililonse.

18. Malinga ndi Salimo 18, kodi Davide anazindikira chiyani?

18 Davide anazindikira kuti Yehova akumuthandiza. Mwachitsanzo, Davide atapha mkango ndi chimbalangondo zimene zinkafuna kugwira nkhosa za bambo ake, anazindikira kuti Yehova ndi amene anamuthandiza. Iye atagonjetsa Goliyati, anaonanso kuti Yehova ndi amene ankamutsogolera. (1 Sam. 17:37) Atapulumuka pamene Sauli ankafuna kumupha, Davide anaonanso kuti Yehova ndi amene wamupulumutsa. (Sal. 18, timawu tapamwamba) Iye akanakhala wodzikuza bwenzi akudzitama pa zinthu zonsezi. Koma popeza Davide anali wodzichepetsa, anatha kuona kuti Yehova ndi amene ankamuthandiza.​—Sal. 138:6.

19. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Davide?

19 Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tisamangopempha Yehova kuti atithandize. Koma tizizindikiranso mmene akutithandizira. Tikamazindikira zimene sitingakwanitse, zingakhale zosavuta kuti tione mmene Yehova akutithandizira. Nthawi iliyonse imene taona kuti Yehova watithandiza, ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambiri. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wa ku Fiji dzina lake Isaac. Iye watumikira Yehova kwa nthawi yaitali ndipo ananena kuti: “Ndikaganizira za moyo wanga, ndimaona kuti Yehova wakhala akundithandiza kuyambira pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo mpaka panopa. Zimenezi zandithandiza kuti ndizimuona kuti ndi mnzanga weniweni.”

20. Kodi kudziwa bwino Yehova kunamuthandiza bwanji Davide, nanga tikuphunzirapo chiyani?

20 Davide ankatsanzira Yehova. Yehova anatilenga m’njira yoti tizitha kumutsanzira. (Gen. 1:26) Tikamaphunzira kwambiri za makhalidwe a Yehova m’pamene tingathe kumutsanzira bwino. Davide ankadziwa bwino Atate wake wakumwamba choncho zinali zosavuta kuti azimutsanzira pochita zinthu ndi anthu ena. Taganizirani zimene zinachitika Davide atachimwira Yehova pochita chigololo ndi Bati-seba komanso kuphetsa mwamuna wake. (2 Sam. 11:1-4, 15) Yehova anamuchitira chifundo chifukwa chakuti nayenso ankachitira chifundo anthu ena. Popeza Davide anali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, Aisiraeli ankamukonda kwambiri ndipo Yehova ankaona kuti iye ndi chitsanzo chabwino kwa mafumu ena onse.​—1 Maf. 15:11; 2 Maf. 14:1-3.

21. Malinga ndi Aefeso 4:24 ndi 5:1, kodi chingachitike n’chiyani tikamayesetsa ‘kutsanzira Mulungu’?

21 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani imeneyi? Tiyenera kuyesetsa ‘kutsanzira Mulungu.’ Tikamachita zimenezi zinthu zidzatiyendera bwino komanso tidzamudziwa kwambiri. Tikamatsanzira Yehova timasonyeza kuti ndifedi ana ake.​—Werengani Aefeso 4:24; 5:1.

TIZIYESETSA KUDZIWA BWINO YEHOVA

22-23. N’chiyani chingachitike tikamagwiritsa ntchito zomwe timaphunzira zokhudza Yehova?

22 Monga taonera, tikhoza kuphunzira za Yehova poona zimene analenga komanso pophunzira Baibulo. M’Baibulo muli nkhani zambiri za atumiki a Mulungu okhulupirika omwe tingawatsanzire monga Mose ndi Davide. Apatu tingati Yehova wachita mbali yake. Ifenso tikufunika kuchita mbali yathu poyesetsa kumudziwa bwino.

23 Anthufe tidzaphunzira za Yehova mpaka kalekale. (Mlal. 3:11) Chofunika si kungodziwa zinthu zambiri zokhudza Yehova koma kugwiritsa ntchito bwino zimene tikudziwazo. Tikamachita zimenezi komanso kutsanzira Atate wathu, tidzapitiriza kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Yak. 4:8) Yehova amatitsimikizira m’Mawu ake kuti sadzasiya anthu amene amayesetsa kumudziwa.

NYIMBO NA. 80 “Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

^ ndime 5 Anthu ambiri amadziwa kuti Mulungu aliko koma samudziwa bwino. Kodi kudziwa Yehova kumatanthauza chiyani? Nanga tingaphunzire chiyani kwa Mose ndi Mfumu Davide pa nkhani yolimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu? Munkhaniyi tikambirana mayankho a mafunso amenewa.