Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Pamene Satana anauza Hava kuti sadzafa akadya chipatso cha mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa, kodi ankanena za mfundo imene yafala masiku ano yakuti mzimu wa munthu suufa?
Zikuoneka kuti ayi. Mdyerekezi sanauze Hava kuti ngati atadya chipatso chimene Mulungu analetsa, thupi lake likanafa koma mzimu wake ukanakakhalabe ndi moyo. Pamene Satana ankalankhula ndi Hava pogwiritsa ntchito njoka, ananena kuti Hava akadya chipatso cha mtengowo, ‘sadzafa.’ Satana ankatanthauza kuti Hava sakanafa koma akanakhala ndi moyo wabwino kwambiri padziko lapansi popanda kulamuliridwa ndi Mulungu.—Gen. 2:17; 3:3-5.
Ngati mfundo yabodza yakuti mzimu wa munthu suufa sinayambire mu Edeni, ndiye kuti inayamba bwanji? Sitikudziwa bwinobwino. Koma zimene tikudziwa ndi zakuti kulambira konyenga konse kunatha pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa. Palibe mfundo zabodza zimene zinatsala chifukwa anthu amene anapulumuka anali Nowa ndi banja lake basi ndipo ankalambira Yehova.
Choncho mfundo ya masiku ano yakuti mzimu suufa iyenera kuti inayamba pambuyo pa Chigumula. Pamene Mulungu anasokoneza zilankhulo ku Babele, anthu anabalalikira “padziko lonse lapansi.” (Gen. 11:8, 9) Ndipo kumene anapita ayenera kuti anapitiriza kufalitsa mfundo yabodza yakuti mzimu wa munthu suufa. Kaya bodzali linayambira pati, zomwe tikudziwa ndi zakuti Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “tate wake wa bodza,” ndi amene analiyambitsa ndipo amasangalala kuti lafala kwambiri.—Yoh. 8:44.