Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 50

Yehova Anakonza Zoti Tikhale ndi Ufulu

Yehova Anakonza Zoti Tikhale ndi Ufulu

“Muzilengeza ufulu kwa anthu onse okhala m’dzikolo.”—LEV. 25:10.

NYIMBO NA. 22 Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) Kodi m’mayiko ena anthu amachita chikondwerero chotani? (Onani bokosi lakuti “ Kodi N’chiyani Chinkachitika pa Chaka cha Ufulu?”) (b) Kodi Yesu anatchula za chiyani pa Luka 4:16-18?

M’MAYIKO ena, anthu amachita chikondwerero chapadera pa chaka cha 50 chimene mfumu kapena mfumukazi yakhala ikulamulira. Anthu amatha kuchita chikondwererocho kwa tsiku limodzi, mlungu umodzi kapena kwa nthawi yaitali. Koma pa mapeto pake chimatha ndipo chisangalalo chimene anthu anali nacho chimaiwalika.

2 Munkhaniyi, tikambirana chikondwerero chabwino kwambiri chomwe chimaposa chikondwerero chimene Aisiraeli ankachita kwa chaka chathunthu pa zaka 50 zilizonse. Chikondwererochi chinkathandiza Aisiraeli kuti akhale pa ufulu. Kukambirana za chikondwererochi n’kothandiza chifukwa chimatikumbutsa zimene Yehova anakonza kuti atipatse ufulu wosatha. Yesu anatchula za ufulu umenewu ndipo tikusangalala nawo ngakhale panopa.​—Werengani Luka 4:16-18.

Aisiraeli ankasangalala pa Chaka cha Ufulu chifukwa chakuti akapolo ankabwerera kwawo (Onani ndime 3) *

3. Malinga ndi Levitiko 25:8-12, kodi Chaka cha Ufulu chinkathandiza bwanji Aisiraeli?

3 Kuti timvetse bwino ufulu umene Yesu anatchula, tiyeni tikambirane za Chaka cha Ufulu chimene Mulungu anakonzera anthu ake akale. Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Chaka cha 50 chizikhala chopatulika, ndipo muzilengeza ufulu kwa anthu onse okhala m’dzikolo. Chizikhala Chaka cha Ufulu kwa inu, ndipo aliyense wa inu azibwerera kumalo ake ndi kubanja lake.” (Werengani Levitiko 25:8-12.) Munkhani yapita ija tinakambirana mmene lamulo la Sabata linkathandizira Aisiraeli. Koma kodi Chaka cha Ufulu chinkawathandiza bwanji? Tiyerekeze kuti munthu wina anakongola ndalama zambiri moti anafunika kugulitsa malo ake kuti alipire ngongoleyo. Pa Chaka cha Ufulu, munthuyo ankafunika kubwezeredwa malowo. Zikatero munthuyo ‘ankabwerera kumalo ake,’ ndipo malowo ankakhala cholowa cha ana ake. Nthawi zina, munthu ankafunika kugulitsa mwana wake kapena kudzigulitsa yekha kuti akhale kapolo pofuna kulipira ngongole. Pa Chaka cha Ufulu, kapoloyo ankafunika ‘kubwerera ku banja lake.’ Choncho palibe amene ankakhala kapolo mpaka kalekale. Izitu zikusonyeza kuti Yehova amakonda kwambiri anthu ake.

4-5. Kodi kudziwa za Chaka cha Ufulu kungatithandize bwanji masiku ano?

4 Kodi Chaka cha Ufulu chinkathandiza Aisiraeli m’njira ina iti? Yehova ananena kuti: “Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsa ndithu m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako.” (Deut. 15:4) Izitu ndi zosiyana kwambiri ndi zimene zikuchitika masiku ano chifukwa anthu olemera akulemeralemerabe pomwe osauka akusaukirasaukirabe.

5 Akhristufe sititsatira Chilamulo cha Mose. Choncho sititsatira lamulo la Chaka cha Ufulu lokhudza kumasula akapolo, kukhululukira ngongole komanso kubwezera anthu malo awo. (Aroma 7:4; 10:4; Aef. 2:15) Komabe kudziwa za Chaka cha Ufulu kungatithandizenso ifeyo. Tikutero chifukwa tingakhale ndi ufulu umene ungatikumbutse zimene Yehova anakonzera Aisiraeli.

YESU ANALENGEZA ZA UFULU

6. Kodi anthufe tifunika kumasulidwa ku ukapolo uti?

6 Tonsefe tifunika kumasulidwa ku ukapolo wa uchimo womwe ndi woipa kwambiri. Uchimowu umachititsa kuti tizikalamba, kudwala komanso kufa. Ambiri amaona umboni wa zimenezi akadziyang’anira pagalasi kapena akapita kuchipatala. Timakhumudwanso tikachita machimo enaake. Mtumwi Paulo ananena kuti anali ‘kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zake.’ Ananenanso kuti: “Munthu wovutika ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likufa imfa imeneyi?”​—Aroma 7:23, 24.

7. Kodi Yesaya analosera za chiyani pa nkhani ya ufulu?

7 Chosangalatsa n’chakuti Mulungu anakonza njira yotimasulira ku ukapolo wa uchimo. Yesu ndi amene ali ndi udindo waukulu pothandiza anthu kuti amasuke. Zaka zoposa 700 Yesu asanabwere padzikoli, mneneri Yesaya analosera za ufulu waukulu kuposa umene Aisiraeli ankakhala nawo pa Chaka cha Ufulu. Iye analemba kuti: “Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine, pakuti Yehova wandidzoza kuti ndikanene uthenga wabwino kwa anthu ofatsa. Wandituma kuti ndikamange zilonda za anthu osweka mtima, ndikalengeze za ufulu kwa anthu ogwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.” (Yes. 61:1) Kodi ndi ndani anakwaniritsa ulosiwu?

8. Kodi ndi ndani anakwaniritsa ulosi wa Yesaya wonena za kumasula anthu kuti akhale pa ufulu?

8 Ulosiwu unayamba kukwaniritsidwa Yesu atayamba utumiki wake. Iye atapita kusunagoge wa kwawo ku Nazareti anawerenga mawu a Yesayawa kwa Ayuda amene anasonkhana. Yesu ananena kuti iyeyo anakwaniritsa mawu akuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu, ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.” (Luka 4:16-19) Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosiwu?

ANTHU OYAMBIRIRA KUKHALA PA UFULU

Yesu ananena za ufulu musunagoge wa ku Nazareti (Onani ndime 8-9)

9. Kodi anthu ambiri a nthawi ya Yesu ankalakalaka ufulu wotani?

9 Ufulu umene Yesaya analosera, umenenso Yesu anauwerenga, unayamba nthawi ya Yesu. Iye anatsimikizira mfundo imeneyi pamene ananena kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.” (Luka 4:21) Anthu ambiri amene anamva zimene Yesu anawerengazi ayenera kuti ankalakalaka atamasulidwa ku ulamuliro wa Aroma. Mwina anali ndi maganizo ofanana ndi anthu awiri amene ananena kuti: “Ife tinali kuyembekezera kuti munthu ameneyu ndi amene adzapulumutse Isiraeli.” (Luka 24:13, 21) Koma tikudziwa kuti Yesu sanauze otsatira ake kuti aukire ulamuliro wankhanza wa Aroma. M’malomwake, anawalangiza kuti azipereka “zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” (Mat. 22:21) Ndiye kodi Yesu anabweretsa bwanji ufulu pa nthawiyo?

10. Kodi Yesu anathandiza anthu kuti amasulidwe ku zinthu ziti?

10 Mwana wa Mulungu anabwera kudzathandiza anthu kuti akhale pa ufulu m’njira ziwiri. Choyamba, Yesu anamasula anthu ku zinthu zolakwika zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa. Pa nthawiyo, Ayuda ambiri anali pa ukapolo wotsatira miyambo ndi zikhulupiriro zabodza. (Mat. 5:31-37; 15:1-11) Atsogoleri achipembedzowo anali ngati akhungu. Iwo anakana Mesiya komanso zimene ankaphunzitsa choncho anakhalabe mumdima komanso machimo awo sanakhululukidwe. (Yoh. 9:1, 14-16, 35-41) Zinthu zolondola zomwe Yesu ankaphunzitsa komanso chitsanzo chake chabwino, zinathandiza anthu ofatsa kudziwa zimene angachite kuti amasulidwe mwauzimu.​—Maliko 1:22; 2:23–3:5.

11. Kodi njira yachiwiri imene Yesu anabweretsera ufulu ndi iti?

11 Kodi njira yachiwiri imene Yesu anabweretsera ufulu inali yotani? Iye anamasula anthu ku ukapolo wa uchimo umene anatengera kwa Adamu. Chifukwa cha nsembe ya Yesu, Mulungu amatha kukhululukira anthu amene amakhulupirira dipo n’kumachita zinthu zosonyeza chikhulupirirocho. (Aheb. 10:12-18) Yesu ananena kuti: “Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.” (Yoh. 8:36) Ufulu umenewu ndi waukulu kuposa umene Aisiraeli ankakhala nawo pa Chaka cha Ufulu. Mwachitsanzo, munthu amene anamasulidwa pa chaka chimenechi sakanapewa imfa ndipo akanatha kukhalanso kapolo.

12. Kodi anthu oyamba kukhala pa ufulu umene Yesu ananena anali ndani?

12 Pa Pentekosite mu 33 C.E., Yehova anadzoza ndi mzimu woyera atumwi ndiponso amuna ndi akazi ena okhulupirika. Iye anayamba kuwaona ngati ana ake oti adzalamulire ndi Yesu kumwamba. (Aroma 8:2, 15-17) Iwo anali oyamba kukhala pa ufulu umene Yesu anautchula musunagoge wa ku Nazareti. Anthu amenewa anamasulidwa ku ukapolo wotsatira zinthu zabodza zimene atsogoleri achipembedzo ankaphunzitsa komanso makhalidwe awo osemphana ndi Malemba. Mulungu anayambanso kuwaona kuti amasuka ku uchimo ndi imfa. Chaka cha Ufulu chophiphiritsira chimene chinayamba mu 33 C.E., pamene otsatira a Khristu anadzozedwa, chidzatha pa mapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu. Kodi chidzachitike n’chiyani pofika nthawi imeneyo?

ANTHU ENA MAMILIYONI ADZAKHALA PA UFULU

13-14. Kuwonjezera pa odzozedwa, kodi ndi anthu ena ati amene angapeze ufulu umene Yesu ananena?

13 Masiku ano, anthu mamiliyoni ochokera m’mitundu yonse ali m’gulu la “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Mulungu sanawasankhe kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Koma Baibulo limasonyeza kuti akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Kodi inunso mukuyembekezera zimenezi?

14 Ngakhale panopa, nanunso mukupeza madalitso amene odzozedwa ali nawo. Mwachitsanzo, kukhulupirira nsembe ya Yesu kumathandiza kuti machimo anu akhululukidwe. Izi zimathandiza kuti mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso mukhale ndi chikumbumtima choyera. (Aef. 1:7; Chiv. 7:14, 15) Mulinso pa ufulu chifukwa choti mwamasulidwa ku ukapolo wotsatira zikhulupiriro zabodza. Paja Yesu ananena kuti: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:32) N’zosangalatsa kwambiri kukhala pa ufulu umenewu.

15. Kodi tikuyembekezera ufulu uti, nanga ndi madalitso ati amene tingapeze?

15 Koma pali ufulu waukulu kwambiri umene tikuyembekezera. Posachedwapa, Yesu adzachotsa zipembedzo zonyenga komanso maboma achinyengo. Mulungu adzapulumutsa “khamu lalikulu” la anthu amene amamutumikira kuti apeze madalitso osaneneka m’dziko latsopano. (Chiv. 7:9, 14) Anthu ambirimbiri adzaukitsidwa n’kupatsidwa mwayi woti amasulidwe ku uchimo umene tinatengera kwa Adamu.​—Mac. 24:15.

16. Kodi anthu adzamasulidwa bwanji m’tsogolomu?

16 Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, Yesu ndi mafumu anzake adzathandiza anthu onse kuti akhale angwiro. Nthawi imeneyi idzakhala ngati Chaka cha Ufulu ku Isiraeli. Anthu onse padzikoli amene amatumikira Yehova mokhulupirika adzamasulidwa ku uchimo n’kukhala angwiro.

M’dziko latsopano, tizidzagwira ntchito yabwino komanso yosangalatsa (Onani ndime 17)

17. Kodi pa Yesaya 65:21-23 pali ulosi wotani wokhudza anthu a Mulungu? (Onani chithunzi chapachikuto.)

17 Pa Yesaya 65:21-23 (Werengani.) pali ulosi wonena mmene moyo udzakhalire padzikoli. Pa nthawiyo palibe amene adzakhale wosowa zochita. Baibulo limasonyeza kuti anthu a Mulungu azidzagwira ntchito zosangalatsa komanso zothandiza. Pamapeto pa zaka 1,000 zimenezi, chilengedwechi “chidzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”​—Aroma 8:21.

18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti tidzasangalala kwambiri m’tsogolomu?

18 Munkhaniyi taona kuti Yehova anakonza zoti Aisiraeli azigwira ntchito komanso kupuma. Ndi mmene zidzakhalirenso ndi anthu ake mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Tidzakhala ndi nthawi yokwanira yolambira Mulungu. Paja kulambira Mulungu n’kumene kumatithandiza kuti tizisangalala panopa ndipo ndi mmene zidzakhalirenso m’dziko latsopano. Anthu onse okhulupirika adzasangalala kwambiri mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu chifukwa chakuti adzakhala ndi ntchito zosangalatsa komanso azidzatumikira Mulungu momasuka.

NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

^ ndime 5 Yehova anakonza njira yapadera yothandizira Aisiraeli kuti azikhala pa ufulu. Iye anakonza zoti pazikhala Chaka cha Ufulu. Akhristufe sititsatira Chilamulo cha Mose, koma kuphunzira za Chaka cha Ufulu kungatithandize kwambiri. Munkhaniyi tiona kuti Chaka cha Ufulu chimatikumbutsa zimene Yehova watikonzera komanso mmene zinthuzo zingatithandizire.

^ ndime 61 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Pa Chaka cha Ufulu, anthu amene anali akapolo ankamasulidwa n’kubwerera kwawo.