Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 53

Akhristu Achinyamata, Kodi Mungatani Kuti Mukhale Olimba Mwauzimu?

Akhristu Achinyamata, Kodi Mungatani Kuti Mukhale Olimba Mwauzimu?

“Uchite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.”​—1 MAF. 2:2.

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga Khala Wanzeru”

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi mwamuna wa Chikhristu ayenera kuchita chiyani kuti zinthu zimuyendere bwino?

 MFUMU Davide analangiza Solomo kuti: “Uchite zinthu mwamphamvu ndipo ukhale wolimba mtima.” (1 Maf. 2:​1-3) Abale onse masiku ano, angachite bwino kutsatira malangizo amenewa. Kuti akwanitse kuchita zimenezi, ayenera kuphunzira kumvera malamulo a Mulungu komanso kutsatira mfundo za m’Baibulo pa zochita zawo zonse. (Luka 2:52) N’chifukwa chiyani Akhristu achinyamata ayenera kuyesetsa kuti akule mwauzimu?

2-3. N’chifukwa chiyani wachinyamata ayenera kuyesetsa kuti akhale wolimba mwauzimu?

2 Mwamuna wa Chikhristu amakhala ndi maudindo ofunika kwambiri m’banja ndiponso mumpingo. Mosakayikira, inu Akhristu achinyamata muyenera kuti munaganizirapo za maudindo omwe mudzakhale nawo m’tsogolo. Mwina muli ndi cholinga chochita utumiki wa nthawi zonse, kukhala mtumiki wothandiza ndipo kenako kudzakhala mkulu mumpingo. Mwinanso mukufuna kudzakwatira n’kudzakhala ndi ana. (Aef. 6:4; 1 Tim. 3:1) Kuti zimenezi zitheke komanso zinthu zizikuyenderani bwino, muyenera kukula mwauzimu. b

3 Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mukule mwauzimu? Pali maluso ena ofunika amene muyenera kukhala nawo. Ndiye mungachite chiyani panopa kuti mukonzekere maudindo amene mudzakhale nawo m’tsogolo?

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUKULE MWAUZIMU

Kutsanzira makhalidwe abwino a Yesu kungakuthandizeni kuti mukule mwauzimu (Onani ndime 4)

4. Kodi mungapeze kuti anthu abwino oti muziwatsanzira? (Onaninso chithunzi.)

4 Muzisankha anthu abwino oti muziwatsanzira. M’Baibulo muli zitsanzo zabwino zambiri zimene achinyamata angatengere. Anthu akalewa ankakonda Mulungu ndipo anali ndi maudindo osiyanasiyana posamalira anthu ake. Mukhozanso kupeza zitsanzo zabwino za Akhristu olimba mwauzimu m’banja lanu ndiponso mumpingo. (Aheb. 13:7) Komanso muli ndi chitsanzo changwiro cha Yesu Khristu. (1 Pet. 2:21) Mukamaphunzira mosamala za anthu amenewa, muziganiziranso makhalidwe abwino amene anali nawo. (Aheb. 12:​1, 2) Kenako muziona zomwe mungachite kuti muwatsanzire.

5. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti mukhale oganiza bwino, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika? (Salimo 119:9)

5 Muzikhala ‘oganiza bwino.’ Munthu woganiza bwino amaganizira kaye asanasankhe zochita. Choncho yesetsani kuti mukhale ndi luso limeneli. N’chifukwa chiyani tikutero? M’dzikoli, muli achinyamata ambiri amene amangoyendera nzeru zawo kapena omwe amangochita zinthu motengeka maganizo. (Miy. 7:7; 29:11) Komanso zinthu ngati TV, mafilimu ndi intaneti zikhoza kusokoneza maganizo ndi zochita zanu. Ndiye kodi mungatani kuti mukhale oganiza bwino? Choyamba, muyenera kuphunzira mfundo za m’Baibulo ndi kumaganizira ubwino wake. Ndiyeno muzigwiritsa ntchito mfundo zimenezo posankha kuchita zinthu zimene zingasangalatse Yehova. (Werengani Salimo 119:9.) Kukhala ndi luso limeneli, kudzakuthandizani kwambiri kuti mukule mwauzimu. (Miy. 2:​11, 12; Aheb. 5:14) Tiyeni tikambirane mmene kuganiza bwino kungakuthandizireni pa nkhani ziwiri izi: (1) pochita zinthu ndi alongo ndipo (2) posankha zovala komanso mmene muyenera kuonekera.

6. Kodi kuganiza bwino kungathandize bwanji wachinyamata kuti azilemekeza alongo?

6 Kuganiza bwino kungakuthandizeni kuti muzilemekeza akazi. Palibe cholakwika ngati m’bale wachinyamata akufuna kudziwana bwino ndi mlongo wina. Komabe wachinyamata woganiza bwino sangalankhule, kulemba kapena kuchita chilichonse chimene chingakope mtsikana, pokhapokha ngati akufunadi kudzakwatirana naye. (1 Tim. 5:​1, 2) Ndipo ngati ali pachibwenzi ndi mlongo, angateteze mbiri ya mlongoyo popewa kukhala awiriwiri popanda owaperekeza.—1 Akor. 6:18.

7. Kodi kuganiza bwino kungathandize bwanji wachinyamata kuti azisankha bwino pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa?

7 Njira ina imene wachinyamata angasonyezere kuti ndi woganiza bwino, ndi zimene amasankha pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa. Nthawi zambiri mafashoni amapangidwa kapena kulimbikitsidwa ndi anthu amene salemekeza Yehova kapena a makhalidwe oipa. Mafashoni omwe amapangawo, amakhala a zovala zothina kapena zochititsa amuna kuoneka ngati akazi. Koma Mkhristu amene akukula mwauzimu amasankha zovala motsatira mfundo za m’Baibulo komanso chitsanzo cha anthu abwino mumpingo. Iye angadzifunse kuti: ‘Kodi zovala zanga zimasonyeza kuti ndine woganiza bwino komanso woganizira ena? Kodi kavalidwe kanga kamathandiza anthu kuzindikira mosavuta kuti ndinadzipereka kuti ndizitumikira Mulungu?’ (1 Akor. 10:​31-33; Tito 2:6) Wachinyamata woganiza bwino amakhala wolemekezeka pamaso pa abale ndi alongo komanso Mulungu.

8. Kodi wachinyamata angatani kuti akhale wodalirika?

8 Muzikhala odalirika. Wachinyamata wodalirika, amakwaniritsa maudindo ake mokhulupirika. (Luka 16:10) Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi. Iye sankachita zinthu mosasamala kapena mosaikirapo mtima. M’malomwake anachita zinthu zonse zomwe Yehova anamutuma, ngakhale pamene kuchita zimenezi kunali kovuta. Yesu ankakonda anthu makamaka ophunzira ake, ndipo mofunitsitsa anapereka moyo wake chifukwa cha iwo. (Yoh. 13:1) Potsanzira Yesu, muzigwira mwakhama ntchito iliyonse yomwe mwapatsidwa. Ngati simukudziwa mmene mungachitire zinthu zina, muyenera kukhala odzichepetsa ndi kumapempha abale olimba mwauzimu kuti akuthandizeni. Musamakhutire ndi kungochita zochepa chabe. (Aroma 12:11) M’malomwake, muzimaliza ntchito yonse imene mwapatsidwa ngati “mukuchitira Yehova, osati anthu.” (Akol. 3:23) Komabe, muzikumbukira kuti si inu angwiro choncho muzidziwa malire anu n’kumavomereza zimene mwalakwitsa.—Miy. 11:2.

MUZIPHUNZIRA MALUSO AMENE ANGAKUTHANDIZENI PA MOYO WANU

9. N’chifukwa chiyani wachinyamata ayenera kuphunzira maluso amene angamuthandize?

9 Kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu muyenera kuphunzira maluso amene angakuthandizeni. Malusowa angakuthandizeni kuti mukwaniritse bwino maudindo anu mumpingo, mupeze ntchito kuti muzipeza zofunika pa moyo wanu kapena wa banja lanu komanso kuti muzigwirizana ndi anthu ena. Tiyeni tikambirane ena mwa maluso amenewa.

Kudziwa kuwerenga komanso kulemba bwino kungakuthandizeni inuyo komanso mpingo (Onani ndime 10-11)

10-11. Kodi wachinyamata amene waphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino angapindule bwanji, nanga angathandize bwanji mpingo? (Salimo 1:​1-3) (Onaninso chithunzi.)

10 Muziphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. Baibulo limanena kuti munthu amene amawerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku n’kumawaganizira mozama, amakhala wosangalala ndipo zinthu zimamuyendera bwino. (Werengani Salimo 1:​1-3.) Munthu akamawerenga Baibulo tsiku lililonse, amadziwa maganizo a Yehova ndipo izi zimamuthandiza kuti aziganiza bwino komanso azitsatira mfundo za m’Malemba. (Miy. 1:​3, 4) Mumpingo mumafunika anthu ngati amenewa. N’chifukwa chiyani tikutero?

11 Abale ndi alongo athu amafuna kuthandizidwa ndi amuna odziwa kuphunzitsa komanso kupereka malangizo ochokera m’Baibulo. (Tito 1:9) Ngati mumawerenga komanso kulemba bwino, mukhoza kukonzekera ndemanga komanso nkhani zimene zingapindulitse anthu ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Mungathenso kulemba notsi zothandiza pamene mukuphunzira Baibulo panokha, kumvetsera nkhani za pamisonkhano yampingo, yadera ndiponso yachigawo. Notsi zimenezi zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso kulimbikitsa anthu ena.

12. N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzilankhula bwino ndi anthu?

12 Muziphunzira kulankhula bwino ndi anthu. Mwamuna wa Chikhristu ayenera kuphunzira kulankhula bwino ndi anthu. Munthu amene amalankhula bwino ndi anthu, amamvetsera kuti azindikire zimene zili m’maganizo mwa anthu komanso kuti adziwe mmene akumvera. (Miy. 20:5) Iye amatha kuzindikira zinthu zina chifukwa cha mmene mawu akumvekera, mmene nkhope ikuonekera komanso mmene munthu akuchitira zinthu. Komatu simungadziwe zinthu ngati zimenezi ngati simucheza ndi anthu. Ngati nthawi zonse mumalankhula ndi anthu pogwiritsa ntchito zipangizo zamakono, monga polemba ma imelo kapena mameseji, simungakhale ndi luso lolankhula ndi anthu pamasom’pamaso. Choncho, muziyesetsa kumapeza nthawi yocheza ndi anthu pamasomp’amaso.—2 Yoh. 12.

Ndi bwino kuphunzira luso limene lingakuthandizeni kudzapeza ntchito (Onani ndime 13)

13. Kodi wachinyamata ayenera kuphunziranso chiyani? (1 Timoteyo 5:8) (Onaninso chithunzi.)

13 Muzitha kudzisamalira nokha. Mwamuna wolimba mwauzimu amafunika azipeza zofunika pa moyo wake komanso wa anthu a m’banja lake. (Werengani 1 Timoteyo 5:8.) M’mayiko ena, achinyamata amaphunzira ntchito kuchokera kwa bambo awo kapena wachibale wina. Koma m’mayiko ena, achinyamata amaphunzira ntchito kapena luso linalake akakhala kusekondale. Kaya zinthu zili bwanji kwanuko, muyenera kuphunzira luso limene lingakuthandizeni kudzapeza ntchito. (Mac. 18:​2, 3; 20:34; Aef. 4:28) Muzidziwika kuti ndinu munthu wakhama, amene sasiya ntchito mpaka ataimaliza. Mukatero, mukhoza kupeza ntchito ndipo sangakuchotseni. Makhalidwe komanso maluso takambiranawa ndi ofunikanso kwa mwamuna wa Chikhristu kuti adzakwaniritse bwino maudindo ake m’tsogolo. Tsopano tiyeni tikambirane ena mwa maudindo amenewa.

MUZIKONZEKERA MAUDINDO ANU A M’TSOGOLO

14. Kodi wachinyamata angakonzekere bwanji kuti adzachite utumiki wa nthawi zonse?

14 Utumiki wa nthawi zonse. Abale ambiri olimba mwauzimu, anayamba utumiki wa nthawi zonse ali achinyamata. Upainiya umathandiza wachinyamata kuti azitha kugwira bwino ntchito ndi anthu osiyanasiyana. Umathandizanso munthu kuti azipanga bajeti yabwino n’kumaitsatira. (Afil. 4:​11-13) Upainiya wothandiza ndi poyambira pabwino kuti munthu achite utumiki wa nthawi zonse. Ambiri amachita upainiya wothandiza kwa kanthawi kuti akonzekere kudzachita upainiya wokhazikika. Upainiya umapatsa munthu mwayi wochita mautumiki wosiyanasiyana a nthawi zonse, monga kugwira nawo ntchito zomangamanga kapena kutumikira pa Beteli.

15-16. Kodi wachinyamata angatani kuti ayenerere kutumikira mumpingo?

15 Mtumiki wothandiza kapena mkulu. Amuna a Chikhristu ayenera kukhala ndi cholinga choti ayenerere kutumikira abale ndi alongo awo mumpingo ngati akulu. Baibulo limanena kuti amuna amene akuyesetsa kuti akhale ndi udindo umenewu “akufuna ntchito yabwino.” (1 Tim. 3:1) M’bale asanakhale mkulu, amafunika akhale kaye mtumiki wothandiza. Atumiki othandiza amathandiza akulu m’njira zambiri. Akulu ndi atumiki othandiza amatumikira abale ndi alongo awo modzichepetsa ndiponso amagwira nawo ntchito yolalikira mwakhama. Abale achinyamata akhoza kuyenerera kukhala atumiki othandiza ngakhale ali ndi zaka za pakati pa 17 ndi 19. Ndipo mtumiki wothandiza amene akuchita bwino, akhoza kukhala mkulu atangokwanitsa zaka 20.

16 Kodi mungatani kuti muyenerere maudindo amenewa? Baibulo limatchula mfundo zimene zingakuthandizeni ndi makhalidwe amene muyenera kukhala nawo. Mfundo zimenezi zagona pa kukonda Yehova, banja lanu komanso mpingo. (1 Tim. 3:​1-13; Tito 1:​6-9; 1 Pet. 5:​2, 3) Choncho yesetsani kuti mumvetse mfundo iliyonse. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti muyenerere. c

Yehova amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi ndi ana ake ndiponso aziwapezera zofunika pa moyo, azikhala mnzawo wapamtima ndipo koposa zonse, aziwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehovayo (Onani ndime 17) )

17. Kodi wachinyamata angakonzekere bwanji kuti adzakhale mwamuna komanso mutu wa banja wabwino? (Onaninso chithunzi.)

17 Mwamuna ndiponso mutu wa banja. Mogwirizana ndi mawu a Yesu, amuna ena a Chikhristu amasankha kukhala wosakwatira. (Mat. 19:12) Koma ngati mungasankhe kukwatira, mudzakhala ndi udindo winanso owonjezereka. Mudzakhala mwamuna komanso mutu wa banja. (1 Akor. 11:3) Yehova amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake ndipo azimupezera zofunika pa moyo, azikhala mnzake wapamtima komanso azimuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehovayo. (Aef. 5:​28, 29) Makhalidwe komanso maluso omwe takambirana mu nkhaniyi, monga kuganiza bwino, kulemekeza akazi komanso kukhala odalirika, angakuthandizeni kuti mukhale mwamuna wabwino. Ndipo mudzakhala okonzeka kukwaniritsa maudindo anu monga mwamuna komanso mutu wabanja.

18. Kodi wachinyamata angakonzekere bwanji kuti adzakhale bambo wabwino?

18 Bambo. Mukadzakwatira, mukhoza kudzakhala ndi ana. Ndiye kodi mungaphunzire chiyani kwa Yehova pa nkhani yokhala bambo wabwino? Pali zambiri zimene mungaphunzire. (Aef. 6:4) Yehova ankauza Mwana wake Yesu kuti amamukonda ndiponso kuti amamusangalatsa kwambiri. (Mat. 3:17) Nanunso mukadzakhala ndi ana, muzidzawauza pafupipafupi kuti mumawakonda. Nthawi zonse muzidzawayamikira akachita zabwino. Abambo amene amatsanzira Yehova, amathandiza ana awo kuti akule mwauzimu. Mungakonzekere udindo umenewu posamalira mwachikondi anthu a m’banja lanu ndiponso a mumpingo. Komanso pouza anthu ena kuti mumawakonda ndiponso kuwayamikira. (Yoh. 15:9) Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kukonzekera bwino udindo wanu wa m’tsogolo monga mwamuna komanso bambo. Ndipo panopa mudzakhala munthu wamtengo wapatali pamaso pa Yehova, m’banja lanu komanso mumpingo.

KODI MUYENERA KUCHITA CHIYANI PANOPA?

Abale ambiri achinyamata omwe anaphunzitsidwa mfundo za m’Malemba n’kumazitsatira, amakula mwauzimu (Onani ndime 19-​20)

19-20. N’chiyani chingathandize achinyamata kuti akule mwauzimu? (Onani chithunzi chapachikuto.)

19 Abale achinyamata, dziwani kuti kukula mwauzimu sikumangochitika pakokha. Muyenera kusankha anthu abwino oti muziwatsanzira, kukhala oganiza bwino, kukhala odalirika, kuphunzira maluso amene angakuthandizeni komanso kukonzekera maudindo anu a m’tsogolo.

20 Mwina nthawi zina mungamaone kuti ndi zovuta mukaganizira zonse zimene muyenera kuchita. Komatu mukhoza kukwanitsa. Kumbukirani kuti Yehova ndi wokonzeka kukuthandizani. (Yes. 41:​10, 13) Nawonso abale ndi alongo anu mumpingo, adzakuthandizani. Mukadzakula n’kukhala Mkhristu wolimba mwauzimu, moyo wanu udzakhala wabwino komanso wosangalatsa. Abale achinyamatanu, timakukondani kwambiri. Yehova akudalitseni pamene mukuyesetsa kuti mukule mwauzimu.—Miy. 22:4.

NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo

a Amuna olimba mwauzimu akufunika mumpingo. Mu nkhaniyi, tikambirana zimene achinyamata angachite kuti akhale Akhristu olimba mwauzimu.

b Onani “Tanthauzo la Mawu Ena” mu nkhani yapitayi.

c Onani mutu 5 ndi 6, m’buku lakuti Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova.