Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 52

Akhristu Achitsikana, Kodi Mungatani Kuti Mukhale Olimba Mwauzimu?

Akhristu Achitsikana, Kodi Mungatani Kuti Mukhale Olimba Mwauzimu?

“Nawonso akazi akhale. . . ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse.”—1 TIM. 3:11.

NYIMBO NA. 133 Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikule mwauzimu?

 Timadabwa kuona mmene mwana amakulira mofulumira kwambiri n’kukhala munthu wamkulu. Zimaoneka kuti kukula kumeneku kumangochitika pakokha. Koma kukula mwauzimu sikumachitika pakokha. b (1 Akor. 13:11; Aheb. 6:1) Kuti munthu akule mwauzimu amafunika kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timafunikanso mzimu woyera kuti utithandize kukhala ndi makhalidwe abwino, kukhala ndi luso lochitira zinthu bwino komanso kukonzekera maudindo athu am’tsogolo.—Miy. 1:5.

2. Kodi tikuphunzira chiyani pa Genesis 1:​27, nanga tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Polenga anthu, Yehova anawalenga mwamuna ndi mkazi. (Werengani Genesis 1:27.) Mwamuna ndi mkazi amaoneka mosiyana komanso amakhala osiyana m’njira zina. Mwachitsanzo, Yehova analenga amuna ndi akazi kuti azikwaniritsa maudindo osiyana. Choncho iwo amafunika kukhala ndi makhalidwe komanso maluso amene angawathandize kukwaniritsa bwino maudindo awowo. (Gen. 2:18) Munkhaniyi tikambirana zimene Akhristu achitsikana angachite kuti akhale olimba mwauzimu. Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene Akhristu achinyamata angachite.

MUZIKHALA NDI MAKHALIDWE AMENE AMASANGALATSA YEHOVA

Kutengera chitsanzo cha akazi okhulupirika monga Rabeka, Esitere ndi Abigayeli kungakuthandizeni kuti mukule mwauzimu (Onani ndime 3-4)

3-4. Kodi alongo achitsikana angapeze kuti zitsanzo zimene angatengere? (Onaninso chithunzi.)

3 Baibulo limatchula zitsanzo zambiri za akazi amene ankakonda Yehova komanso kumutumikira. (Onani pa jw.org nkhani yakuti “Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Akazi Otchulidwa M’Baibulo?”) Mogwirizana ndi lemba limene likutsogolera nkhani yathuyi, akaziwo anali “ochita zinthu mosapitirira malire” ndiponso “okhulupirika pa zinthu zonse.” Kuwonjezera pamenepo, Akhristu achitsikana angapeze mumpingo wawo alongo olimba mwauzimu amene angamawatsanzire.

4 Ngati ndinu mlongo wachitsikana, mungachite bwino kupeza alongo a Chikhristu olimba mwauzimu amene mungamawatsanzire. Muziona makhalidwe awo abwino. Kenako muziona mmene mungamasonyezere makhalidwe amenewo. Munkhaniyi, tikambirana makhalidwe atatu ofunika kwa akazi kuti akhale olimba mwauzimu.

5. N’chifukwa chiyani kudzichepetsa ndi kofunika kwambiri kwa mkazi wa Chikhristu yemwe ndi wolimba mwauzimu?

5 Kudzichepetsa ndi khalidwe lofunika kwambiri kuti Mkhristu akule mwauzimu. Mkazi wodzichepetsa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso anthu ena. (Yak. 4:6) Mwachitsanzo, mkazi amene amakonda Yehova amakhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo amene Yehova anapereka okhudza mutu wa banja ndi mutu wa mpingo. c1 Akor. 11:3.

6. Kodi alongo achitsikana angaphunzire chiyani kwa Rabeka pa nkhani ya kudzichepetsa?

6 Taganizirani chitsanzo cha Rabeka. Iye anali mkazi wanzeru komanso wosazengereza pochita zinthu kwa moyo wake wonse. (Gen. 24:58; 27:​5-17) Koma anali waulemu ndiponso wogonjera. (Gen. 24:​17, 18, 65) Inunso mukakhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo ngati Rabeka, mudzakhala chitsanzo chabwino m’banja lanu komanso mumpingo.

7. Kodi alongo achitsikana angaphunzire chiyani kwa Esitere pa nkhani ya kudziwa malire awo?

7 Kudziwa malire athu ndi khalidwe lina lofunika kwambiri kuti Mkhristu akhale wolimba mwauzimu. Baibulo limanena kuti “anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.” (Miy. 11:2) Esitere anali mtumiki wa Mulungu wokhulupirika yemwe ankadziwa malire ake. Khalidwe limeneli linamuthandiza kuti asachite zinthu modzikuza. Iye anamvetsera komanso kutsatira malangizo ochokera kwa Moredikayi, yemwe anali wachibale wake wamkulu. (Esitere 2:​10, 20, 22) Inunso mukhoza kusonyeza kuti mumadziwa malire anu mukamapempha malangizo ndiponso kuwatsatira.—Tito 2:​3-5.

8. Mogwirizana ndi 1 Timoteyo 2:​9, 10, kodi kudzichepetsa ndiponso kudziwa malire kungathandize bwanji mlongo wachitsikana kusankha mwanzeru pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa?

8 Esitere anasonyezanso kuzindikira malire ake m’njira ina. Iye anali “wooneka bwino ndiponso wokongola kwambiri” koma sankachita zinthu modzionetsera. (Esitere 2:​7, 15) Kodi chitsanzo cha Esitere chingathandize bwanji akazi a Chikhristu? Njira imodzi yafotokozedwa pa 1 Timoteyo 2:​9, 10. (Werengani.) Mtumwi Paulo analangiza akazi a Chikhristu kuti azivala mwaulemu ndiponso mwanzeru. Mawu a Chigiriki amene anawagwiritsa ntchito palembali amasonyeza kuti zovala za mkazi wa Chikhristu ziyenera kukhala zaulemu, komanso zosonyeza kuti amaganizira anthu ena. Timayamikira kwambiri alongo athu a Chikhristu chifukwa amayesetsa kuvala mwaulemu.

9. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Abigayeli?

9 Kuzindikira ndi khalidwe linanso limene alongo olimba mwauzimu amasonyeza. Kodi kuzindikira n’kutani? Kuzindikira kumatanthauza kutha kusiyanitsa pakati pa zoyenera ndi zolakwika ndiyeno n’kusankha zoyenerazo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Abigayeli. Mwamuna wake anasankha zinthu molakwika zomwe zikanachititsa kuti banja lawo lonse likumane ndi mavuto. Abigayeli anachitapo kanthu mwamsanga ndipo kuzindikira kwake kunapulumutsa anthu ambiri. (1 Sam. 25:​14-23, 32-35) Kuzindikira kumatithandiza kudziwa nthawi yoyenera kulankhula ndi nthawi yoyenera kukhala chete. Kuzindikira kumatithandizanso kuti tizisonyeza chidwi kwa anthu ena popanda kuwapatsa maganizo olakwika.—1 Ates. 4:11.

MUZIPHUNZIRA MALUSO AMENE ANGAKUTHANDIZENI PA MOYO WANU

Kodi kuphunzira kuwerenga ndi kulemba kwakuthandizani bwanji? (Onani ndime 11)

10-11. Kodi kuwerenga ndi kulemba bwino kungakuthandizeni bwanji inuyo komanso anthu ena? (Onaninso chithunzi.)

10 Mkazi wa Chikhristu amafunika kuphunzira maluso osiyanasiyana. Maluso ena amene mtsikana amaphunzira ali wamng’ono amamuthandiza kwa moyo wake wonse. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo.

11 Muziphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. M’zikhalidwe zina, anthu amaona kuti akazi sayenera kuphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. Komatu luso limeneli ndi lofunika kwa Mkhristu aliyense. d (1 Tim. 4:13) Choncho musalole chilichonse kukulepheretsani kuwerenga ndi kulemba bwino. Kodi maluso amenewa angakuthandizeni bwanji? Malusowa angakuthandizeni kuti mulembedwe ntchito n’kumapeza ndalama. Angakuthandizeni kuti muziphunzira Mawu a Mulungu n’kumaphunzitsanso anthu ena. Koposa zonse, lusoli limakuthandizani kuti mukhale pa ubwenzi wolimba kwambiri ndi Yehova chifukwa chakuti mumawerenga mawu ake n’kumawaganizira mozama.—Yos. 1:8; 1 Tim. 4:15.

12. Kodi lemba la Miyambo 31:26 lingakuthandizeni bwanji kuti muzilankhula bwino ndi anthu ena?

12 Muziphunzira kulankhula bwino ndi anthu. Akhristu amafunika kulankhula bwino ndi anthu. Pa nkhani imeneyi, Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anapereka malangizo akuti: “Munthu aliyense azikhala wokonzeka kumvetsera, aziganiza kaye asanalankhule.” (Yak. 1:19) Mukamamvetsera mosamala pamene ena akulankhula, mumasonyeza kuti mumaganizira anthu ena ndiponso kuwamvera chisoni. (1 Pet. 3:8) Ngati mukukayikira zoti mwamvetsa zimene munthu wina akunena kapena mmene akumvera mungachite bwino kumufunsa mafunso oyenera. Kenako muziganiza kaye musanalankhule. (Miy. 15:28) Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimene ndikufuna kulankhula ndi zoona komanso zolimbikitsa? Kodi zisonyeza ulemu komanso kukoma mtima? Muziphunzira kwa alongo olimba mwauzimu amene amalankhula bwino ndi anthu. (Werengani Miyambo 31:26.) Muziona mmene amalankhulira. Mukaphunzira kulankhula bwino ndi anthu, m’pamenenso muzigwirizana nawo kwambiri.

Mkazi amene waphunzira ntchito zapakhomo amathandiza kwambiri m’banja lake komanso mumpingo (Onani ndime 13)

13. Kodi mungatani kuti muphunzire ntchito zapakhomo? (Onaninso chithunzi.)

13 Muziphunzira ntchito zapakhomo. M’madera ambiri, akazi ndi amene amagwira ntchito zambiri zapakhomo. Mayi anu kapena mlongo wina wodziwa ntchito zapakhomo akhoza kukuphunzitsani. Mlongo wina dzina lake Cindy ananena kuti: “Chinthu chimodzi chofunika kwambiri chimene ndinaphunzira kwa mayi anga ndi chakuti kugwira ntchito mwakhama kumathandiza kuti uzisangalala. Kuphunzira ntchito monga kuphika, kuyeretsa, kusoka ndiponso kugula zinthu kunandithandiza kuti ndizisangalala komanso ndizichita zambiri potumikira Yehova. Mayi anga anandiphunzitsanzo kuti ndizilandira bwino alendo, ndipo izi zandithandiza kuti ndikumane ndi abale ndi alongo abwino kwambiri amene ndimatengera zitsanzo zawo. (Miy. 31:​15, 21, 22) Mkazi akakhala wakhama, wolandira bwino alendo komanso wodziwa ntchito zapakhomo amathandiza kwambiri m’banja komanso mumpingo.—Miy. 31:​13, 17, 27; Mac. 16:15.

14. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Crystal nanga muyenera kukumbukira chiyani?

14 Muziphunzira kukhala wokhutira. Kukhala wokhutira ndi khalidwe lina lofunika kwambiri kwa Akhristu olimba mwauzimu. (Afil. 4:11) Mlongo wina dzina lake Crystal ananena kuti: “Makolo anga anandilimbikitsa kusankha maphunziro amene angandithandize kupeza luso limene lingadzandithandize m’tsogolo. Bambo anga anandilimbikitsa kuchita maphunziro a zowerengetsa ndalama ndipo akundithandiza kwambiri.” Kuwonjezera pa kuphunzira maluso amene angakuthandizeni kuti mupeze ntchito, muyeneranso kuphunzira kupanga bajeti n’kumaitsatira. (Miy. 31:​16, 18) Muziika maganizo anu pa zinthu zauzimu, muzipewa ngongole zosayenera ndipo muzikhutira ndi moyo wosalira zambiri.—1 Tim. 6:8.

MUZIKONZEKERA MAUDINDO ANU AM’TSOGOLO

15-16. Kodi alongo osakwatiwa amathandiza bwanji anthu ena? (Maliko 10:​29, 30)

15 Kuphunzira maluso osiyanasiyana komanso kusonyeza makhalidwe abwino kudzakuthandizani kuti mudzakwaniritse bwino maudindo anu am’tsogolo. Tiyeni tikambirane zitsanzo za zinthu zina zimene mungachite.

16 Mukhoza kusankha kukhala osakwatiwa kwa nthawi inayake. Mogwirizana ndi mawu a Yesu, alongo ena amasankha kuti asakwatiwe ngakhale kuti m’chikhalidwe chawo anthu amalimbikitsa kukwatiwa. (Mat. 19:​10-12) Ena amakhala osakwatiwa pa zifukwa zosiyanasiyana. Dziwani kuti Yehova ndi Yesu saona kuti Akhristu amene sali pabanja ndi osafunika. Alongo ambiri osakwatiwa amachita zambiri m’mipingo padziko lonse. Chikondi chawo, komanso mtima woganizira anthu ena umawalimbikitsa kuti akhale alongo kapena amayi auzimu a anthu ambiri.—Werengani Maliko 10:​29, 30; 1 Tim. 5:2.

17. Kodi mlongo wachitsikana angakonzekere bwanji kuti ayambe utumiki wa nthawi zonse?

17 Mukhoza kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Akazi a Chikhristu amachita zambiri pa ntchito yolalikira padziko lonse. (Sal. 68:11) Kodi inuyo mungakonze zoti muyambe utumiki wa nthawi zonse? Mukhoza kuchita upainiya, kugwira nawo ntchito zomangamanga kapena kutumikira pa Beteli. Muzipempherera zolinga zimene muli nazo. Muzikambirana ndi anthu amene anakwaniritsa zolinga ngati zimenezo n’kuona zimene mungachite kuti nanunso muyenerere. Mukatero muzichita zinthu zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa zolingazo. Mukayamba utumiki wa nthawi zonse, zidzakuthandizani kuti muchite zambiri potumikira Yehova.

Ngati mukuganizira zokhala pabanja, muyenera kusankha mosamala kwambiri munthu wokwatirana naye (Onani ndime 18)

18. N’chifukwa chiyani mlongo ayenera kusamala kwambiri posankha mwamuna? (Onaninso chithunzi.)

18 Mungasankhe kukhala pabanja. Makhalidwe komanso maluso amene takambiranawa angakuthandizeni kuti mukhale mkazi wabwino. Komabe, muyenera kukhala wosamala kwambiri posankha munthu amene mukufuna kukwatirana naye. Chifukwa kusankha munthu wokwatirana naye ndi nkhani yaikulu kwambiri pa moyo wanu. Kumbukirani kuti mwamuna amene adzakukwatireni ndi amene adzakhale mutu wanu. (Aroma 7:2; Aef. 5:​23, 33) Choncho muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iye ndi Mkhristu wolimba mwauzimu? Kodi amaika zinthu zauzimu pamalo oyamba? Kodi amasankha zochita mwanzeru? Kodi amavomereza akalakwitsa zinazake? Kodi iye amalemekeza akazi? Kodi angandithandize kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu, kundipezera zofunika pa moyo komanso kukhala mnzanga wapamtima? Kodi amasamalira bwino maudindo ake? Mwachitsanzo, kodi kumpingo ali ndi udindo wotani, nanga amausamalira bwanji?’ (Luka 16:10; 1 Tim. 5:8) Dziwani kuti ngati mukufuna kupeza mwamuna wabwino inuyonso muyenera kukhala mkazi wabwino.

19. N’chifukwa chiyani tinganene kuti udindo wokhala “wothandiza” si wotsika?

19 Baibulo limanena kuti mkazi wabwino amakhala “womuthandiza” mwamuna wake komanso “mnzake womuyenerera.” (Gen. 2:18) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti mkazi ndi wotsika? Ayi! Mkazi ali ndi udindo wofunika kwambiri. Baibulo limanenanso kuti Yehova ndi wotithandiza. (Sal. 54:4; Aheb. 13:6) Mkazi amakhala wothandiza kwa mwamuna wake ngati amagwirizana naye pa zinthu zokhudza banja zimene mwamunayo wasankha. Popeza amakonda Yehova amayesetsa kuti mbiri ya mwamuna wake ikhale yabwino. (Miy. 31:​11, 12; 1 Tim. 3:11) Kuti mukonzekere udindo wanu wam’tsogolowu, muyenera kukonda kwambiri Yehova komanso kumathandiza anthu ena kunyumba kwanu ndiponso mumpingo.

20. Kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene mayi angachitire banja lake?

20 Mukhoza kudzakhala ndi ana. Mukadzakhala pabanja, inu ndi mwamuna wanu mukhoza kudzakhala ndi ana. (Sal. 127:3) Choncho ndi bwino kuganizira zimene zingafunike kuti mudzakhale mayi wabwino. Makhalidwe ndiponso maluso amene takambirana munkhaniyi angakuthandizeni kuti mudzakhale mkazi wabwino komanso mayi wabwino. Mukakhala achikondi, okoma mtima ndiponso oleza mtima, mudzathandiza banja lanu kukhala losangalala ndipo ana anu adzamva kuti ndi otetezeka komanso amakondedwa.—Miy. 24:3.

Alongo ambiri achitsikana amene anaphunzitsidwa mfundo za m’Malemba n’kumazitsatira amakula mwauzimu (Onani ndime 21)

21. Kodi timamva bwanji tikaganizira za alongo athu? Perekani chifukwa. (Onani chithunzi chapachikuto.)

21 Dziwani kuti timakukondani kwambiri alongo athu chifukwa cha zimene mumachitira Yehova komanso anthu ake. (Aheb. 6:10) Mumachita khama kuti mukhale ndi makhalidwe abwino ndiponso kukhala ndi maluso amene angakuthandizeni pa moyo wanu komanso wa anthu ena. Makhalidwe komanso maluso amenewa amakuthandizani kuti mukonzekere bwino maudindo anu am’tsogolo. Ndinu anthu a mtengo wapatali kwambiri m’gulu la Yehova.

NYIMBO NA. 137 Akazi a Chikhristu Okhulupirika

a Alongo athu achitsikananu, dziwani kuti timakukondani ndipo ndinu amtengo wapatali kwambiri mumpingo. Mukhoza kukula mwauzimu mukamayesetsa kuti mukhale ndi makhalidwe abwino, mukamaphunzira maluso othandiza komanso mukamakonzekera maudindo anu am’tsogolo. Mukatero mudzapeza madalitso ambiri potumikira Yehova.

b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Mkhristu wolimba mwauzimu amatsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu osati nzeru za anthu. Iye amatengera chitsanzo cha Yesu, amayesetsa kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso amasonyeza chikondi chenicheni kwa anthu ena.