Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwawerenga mosamala magazini a chaka chino a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
Kodi mawu akuti “kusintha maganizo” amatanthauza chiyani? (Aroma 12:2)
Satanthauza kuti tizingochita ntchito zabwino basi. M’malomwake, tiyenera kumafufuza umunthu wathu wamkati komanso kumasintha pamene pakufunikira kutero, n’cholinga choti zochita zathu zizigwirizana kwambiri ndi mfundo za Yehova.—w23.01, tsa. 8-9.
Kodi tingasonyeze bwanji kuganiza bwino tikamaona zochitika za m’dzikoli?
Tonsefe timachita chidwi ndi mmene zochitika za m’dzikoli zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo. M’malo mongofotokoza maganizo athu tiyenera kufotokoza mogwirizana ndi mfundo zimene zafalitsidwa posachedwapa. Tikamanena zinthu mogwirizana ndi zimene zili m’mabuku a gulu la Yehova, timathandiza kuti mpingo upitirize kukhala wogwirizana. (1 Akor. 1:10)—w23.02, tsa. 16.
Kodi kubatizidwa kwa Yesu kumasiyana bwanji ndi kwa otsatira ake?
Yesu sankafunika kudzipereka kwa Yehova chifukwa anabadwira mumtundu womwe unali wodzipereka kale kwa Mulungu. Iye sankafunika kulapa machimo kapena kupempha chikumbumtima choyera chifukwa anali wangwiro, kapena kuti wosachimwa.—w23.03, tsa. 5.
Tingathandize bwanji anthu ena kuti aziyankha pamisonkhano?
Tizipereka ndemanga zachidule kuti tipereke mpata kwa ena kuti ayankhepo. Tizipewa kutchula mfundo zambiri chifukwa ena angasowe zoti alankhulepo.—w23.04, tsa. 23.
Kodi mawu kuti “Msewu wa Chiyero” kapena kuti “Msewu Wopatulika” opezeka pa Yesaya 35:8 amatanthauza chiyani?
Msewu wophiphiritsawu unkaimira njira imene Ayuda anadutsa pochoka ku Babulo kubwerera kwawo. Nanga bwanji masiku ano? Kwa zaka zambiri chisanafike chaka cha 1919, ntchito yokonza msewu wauzimu inagwiridwa—panali kumasulira komanso kusindikiza Mabaibulo. Anthu a Mulungu akhala akuyenda pa “Msewu Wopatulika” kulowa m’paradaiso kuti akalandire madalitso amene Ufumu udzabweretse.—w23.05, tsa. 15-19.
Kodi pa Miyambo chaputala 9 timapezapo malangizo okhudza akazi awiri ati ophiphiritsa?
Chaputalachi chimanena kuti “mkazi wopusa” amaitana anthu kuti apite kumanda pomwe nzeru yeniyeni imayerekezedwa ndi mkazi amene amaitana anthu kuti azitsogoleredwa ndi kumvetsa zinthu n’kukapeza moyo. (Miy. 9:1, 6, 13, 18)—w23.06, tsa. 22-24.
Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa komanso wololera pochita zinthu ndi Loti?
Yehova anauza Loti kuti achoke ku Sodomu ndipo athawire kumapiri. Koma Loti atapempha kuti athawire ku Zoari, Mulungu anavomereza zimene anapemphazo.—w23.07, tsa. 21.
Kodi mkazi angatani ngati mwamuna wake amaonera zolaula?
Sayenera kudziimba mlandu. Aziyesa kuganizira kwambiri zokhudza ubwenzi wake ndi Yehova komanso nkhani za m’Baibulo za akazi amene anatonthozedwa atapemphera kwa Mulungu. Akhozanso kuthandiza mwamuna wake kupewa zinthu zimene zingamuchititse kuonera zolaula.—w23.08, tsa. 14-17.
Ngati munthu akutsutsa zimene timakhulupirira, kodi kuzindikira kungatithandize bwanji kuti tiyankhe mofatsa?
Tiziona kuti funsolo kapena kutsutsako ndi mwayi umene ungatithandize kudziwa zimene munthuyo amaganiza kapena zimene zikumudetsa nkhawa. Tikatero tikhoza kumuyankha mofatsa.—w23.09, tsa. 17.
Kodi tikuphunzira chiyani kwa Mariya pa nkhani yopeza mphamvu?
Mariya atamva kuti adzakhala mayi wa Mesiya, anapeza mphamvu kuchokera kwa anthu ena. Gabirieli ndi Elizabeti anamulimbikitsa pogwiritsa ntchito Malemba. Ifenso tikhoza kupeza mphamvu kuchokera kwa Akhristu anzathu.—w23.10, tsa. 15.
Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero athu?
Iye analonjeza kuti aziyankha mapemphero athu ndipo amawayankha mogwirizana ndi cholinga chake. (Yer. 29:12) Mapemphero athu akhoza kukhala ofanana koma Yehova n’kuyankha m’njira zosiyana.—w23.11, tsa. 21-22.
Lemba la Aroma 5:2 limanena za “chiyembekezo,” ndiye n’chifukwa chiyani chiyembekezo chikutchulidwanso pavesi 4?
Munthu akamva uthenga wabwino amakhala ndi chiyembekezo choti adzakhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. Koma akamakumana ndi mavuto n’kuwapirira ndiponso kuona kuti Yehova akusangalala naye, chiyembekezo chake chimakhala champhamvu ndipo zimene akuyembekezera zimamukhudza kwambiri.—w23.12, tsa. 12-13.