Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumayendera Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Mowa?

Kodi Mumayendera Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Mowa?

MOSAKAYIKIRA, mumayamikira mphatso zosiyanasiyana zomwe Yehova watipatsa, kuphatikizapo mphatso ya ufulu wosankha mmene mungasangalalire ndi mphatsozi. N’zochititsa chidwi kuti Baibulo limafotokoza kuti vinyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo limati: “Chakudya chimachititsa kuti anthu aziseka, ndipo vinyo amachititsa kuti moyo ukhale wosangalatsa.” (Mlal. 10:19; Sal. 104:15) Koma mwina mwaonapo anthu ena akukumana ndi mavuto chifukwa cha mowa. Kuwonjezera apo, anthu padziko lonse amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mowa. Ndiye kodi n’chiyani chingathandize Akhristu kuti azisankha zochita mwanzeru pa nkhaniyi?

Posatengera kumene timakhala kapena chikhalidwe chathu, tikafuna kusankha zochita pa nkhaniyi ndi bwino kuyendera malangizo a Yehova osati a anthu amene atizungulira. Tikatero, tidzakhala anthu osangalala.

Mwina mumaonanso kuti anthu ambiri m’dzikoli amamwa kwambiri komanso pafupipafupi. Ena amamwa mowa chifukwa amati umawathandiza kumva bwino. Pomwe ena amamwa kuti aiwale mavuto awo. M’madera ena, munthu yemwe amamwa mowa wambiri amaonedwa ngati wotsogola kapena wamphamvu.

Koma Akhristu timatsatira malangizo anzeru ochokera kwa Mlengi wathu wachikondi. Mwachitsanzo, iye amatichenjeza za mavuto amene amabwera chifukwa chomwa mowa kwambiri. Mwina munawerenga lemba la Miyambo 23:​29-35, lomwe limafotokoza bwino zokhudza munthu woledzera komanso mavuto amene amakumana nawo. a Mkulu wina wa Chikhristu ku Europe, dzina lake Daniel amakumbukira mmene moyo wake unalili asanakhale Mkhristu. Iye anati: “Ndinkamwa mowa kwambiri ndipo izi zinachititsa kuti ndizikumana ndi mavuto ambiri moti mpaka pano zimandipwetekabe ndikamaziganizira.”

Kodi Akhristu angagwiritsire ntchito bwanji ufulu wawo wosankha kuti apewe mavuto amene amabwera chifukwa chomwa mowa kwambiri? Chomwe chingathandize, ndi kulola kuti malangizo a Mulungu azitsogolera maganizo komanso zochita zathu.

Tiyeni tsopano tikambirane zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mowa komanso zolinga zomwe anthu ena amakhala nazo akamamwa mowa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA PA NKHANI YA MOWA

Mawu a Mulungu saletsa kumwa mowa mosapitirira malire. Ndipotu Baibulo limavomereza kuti kumwa vinyo kumakhala kosangalatsa. Limati: “Ukadye chakudya chako mokondwera ndipo ukamwe vinyo wako ndi mtima wosangalala.” (Mlal. 9:7) Nthawi zina, Yesu komanso atumiki a Yehova ena okhulupirika ankamwa vinyo.—Mat. 26:​27-29; Luka 7:34; 1 Tim. 5:23.

Komabe Mawu a Mulungu amafotokoza momveka bwino kusiyana pakati pa kumwa mowa pang’ono ndi kuledzera. Amanena kuti: “Musamaledzere ndi vinyo.” (Aef. 5:18) Amanenanso kuti anthu omwe ndi “zidakwa . . . sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.” (1 Akor. 6:10) N’zoona kuti Yehova amadana ndi kumwa mowa kwambiri komanso kuledzera. Choncho m’malo mongotsatira chikhalidwe chathu, tiyenera kutsatira mfundo zomwe zingasangalatse Mulungu.

Anthu ena amaganiza kuti akhoza kumwa mowa wambiri koma osaledzera. Komatu zimenezi ndi zoopsa kwambiri. Malemba amanena kuti kukhala ‘kapolo wa vinyo wambiri’ kungachititse munthu kulakwitsa zinthu ndiponso kuchimwira Yehova. (Tito 2:3; Miy. 20:1) Yesu ananenanso kuti “kumwa kwambiri” kungalepheretse munthu kukalowa m’dziko latsopano. (Luka 21:​34-36) Ndiye kodi n’chiyani chingathandize Mkhristu kupewa mavuto amene amabwera chifukwa chomwa mowa kwambiri?

MUZIGANIZIRA MMENE MUMAMWERA MOWA KOMANSO ZIFUKWA ZOMWE MUMAMWERA

Kumangoyendera zimene anthu a chikhalidwe chathu amachita pa nkhani ya mowa n’koopsa. Akhristu amayesetsa kusangalatsa Yehova pa nkhani ya zakudya komanso zakumwa. Baibulo limatikumbutsa kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa, kapena kuchita china chilichonse, muzichita zinthu zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akor. 10:31) Tiyeni tsopano tikambirane mafunso komanso mfundo za m’Baibulo zimene tiyenera kuziganizira.

Kodi ndimamwa mowa n’cholinga choti ena azindikonda? Lemba la Ekisodo 23:​2, limanena kuti: ‘Tisamachite zinthu pongotsatira gulu la anthu.’ Apa Yehova ankachenjeza Aisiraeli kuti asamatsanzire anthu omwe sankachita zinthu zomusangalatsa. Malangizo amenewa ndi othandizanso kwa Akhristu masiku ano. Tikamangoyendera maganizo a anzathu pa nkhani ya mowa, tikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova ndiponso kulephera kutsatira mfundo zake.—Aroma 12:2.

Kodi ndimamwa kuti anthu aziona kuti ndine wamphamvu? M’zikhalidwe zina, anthu amaona kuti palibe vuto kumwa mowa kwambiri komanso pafupipafupi. (1 Pet. 4:3) Koma taonani mawu anzeru opezeka pa 1 Akorinto 16:​13, lembali limati: “Khalani maso, khalani ndi chikhulupiriro cholimba, khalani olimba mtima ndipo khalani amphamvu.” Ndiye kodi mowa ungathandizedi munthu kukhala wamphamvu? Ayi, si zoona. Mowa umachititsa munthu kufooka moti saganiza bwino. Choncho kumwa mowa wambiri kumasonyeza kuti munthu ndi wofooka osati wamphamvu. Lemba la Yesaya 28:​7, limafotokoza za munthu amene wasochera chifukwa cha mowa, limanena kuti amayenda modzandira ndipo sangasankhe zinthu mwanzeru.

Mphamvu zenizeni zimachokera kwa Yehova ndipo munthu wamphamvu ‘amakhala maso komanso amakhala ndi chikhulupiriro cholimba.’ (Sal. 18:32) Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kukhalabe maso komanso kumasankha zochita mwanzeru kuti tisawononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Yesu ali padziko lapansi anasonyeza kuti ndi wamphamvu ndipo anthu ambiri ankamulemekeza chifukwa choti ankachita zinthu zoyenera komanso anali wolimba mtima.

Kodi ndimamwa mowa kuti ndiiwale mavuto anga? Munthu wina yemwe analemba masalimo, anauziridwa kulemba kuti: “Nkhawa zitandichulukira, [inu Yehova] munanditonthoza komanso kundisangalatsa.” (Sal. 94:19) Mukakhala ndi nkhawa muzidalira Yehova osati mowa. Mungachite zimenezi popemphera pafupipafupi kwa Yehova. Ambirinso amaona kuti kupempha malangizo kwa anzawo olimba mwauzimu kumakhala kothandiza. Kunena zoona, munthu akamamwa mowa n’cholinga choti aiwale mavuto, zimafooketsa maganizo ake ndiponso zimamulepheretsa kuchita zinthu zoyenera. (Hos. 4:11) Daniel amene tamutchula koyambirira uja, ananena kuti: “Ndinkavutika kwambiri ndi nkhawa komanso ndinkadziimba mlandu. Ndinkaledzera kuti ndiiwale mavuto amenewa koma ankangowonjezereka ndipo anthu anasiya kucheza nane komanso sankandilemekeza.” Ndiye kodi n’chiyani chinathandiza Daniel? Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndiyenera kudalira Yehova osati mowa. Pamapeto pake ndinakwanitsa kupirira mavuto anga ndiponso kuthana nawo.” Apa mfundo ndi yakuti Yehova akhoza kutithandiza nthawi ina iliyonse ngakhale pamene tikuona kuti tilibiretu mtengo wogwira.—Afil. 4:​6, 7; 1 Pet. 5:7.

Ngati nthawi zina mumamwa mowa, mungachite bwino kudzifufuza pogwiritsa ntchito mafunso awa, ‘Kodi mnzanga kapena munthu wa m’banja langa anadandaulapo za kamwedwe kanga?’ Ngati ndi choncho, umenewo ungakhale umboni wakuti mwayamba chizolowezi cholakwika koma inuyo simukudziwa. ‘Kodi panopa ndikumamwa kwambiri kuposa kale? Zimenezi zingasonyeze kuti ngakhale kuti panopa munthuyo si chidakwa, koma akuyamba kukhala chidakwa. ‘Kodi zimandivuta kukhala osamwa mowa kwa masiku ochepa kapena ambiri?’ Ngati ndi choncho, ndiye kuti chizolowezi cha kumwa mowa chamera mizu kapena mwayamba uchidakwa. Zimenezi zingatanthauze kuti mukufunika kuthandizidwa ndi akatswiri kuti musiye kumwa mowa.

Poganizira mavuto omwe amabwera chifukwa cha kumwa mowa, Akhristu ena amasankha kusamwa mowa ngakhale pang’ono. Ena amasankha kuti asamamwe chifukwa sakonda kakomedwe kake. Ngati mnzanu anasankha kuti asamamwe mowa, mungamusonyeze kukoma mtima polemekeza zomwe wasankhazo popanda kumuweruza.

Anthu ena amaona kuti kudziikira malire n’kumene kumathandiza. Mkhristu angadziikire malire a kuchuluka kwa mowa umene angamamwe. Apo ayi, angadziikire lamulo pa nthawi imene azimwa, kuti mwina azimwa kamodzi pa mlungu kapena kumwa pang’ono pa nthawi ya chakudya. Enanso amasankha mtundu wa mowa umene ayenera kumamwa. Mwachitsanzo angasankhe kumangomwa vinyo kapena mowa wochepa mphamvu osati wamphamvu kwambiri. Samamwa mowa wamphamvu ngakhale utasakanizidwa ndi zakumwa zina. Munthu akadziikira malire pa nkhani ya kumwa, zimakhala zosavuta kuti asawapitirire. Ngati Mkhristu wolimba mwauzimu anadziikira malamulo pa nkhaniyi n’kumawatsatira, sayenera kudera nkhawa zimene ena aziganiza.

Posankha zochita pa nkhani ya mowa, tiyenera kuganiziranso anthu ena. Lemba la Aroma 14:​21, limanena kuti: “Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita chilichonse chimene chimakhumudwitsa m’bale wako.” (Aroma 14:21) Kodi tingatsatire bwanji malangizo amenewa? Tiyenera kumasonyeza chikondi. Ngati mukuona kuti kumwa mowa kungakhumudwitse munthu winawake, chikondi chingakulimbikitseni kuti musamwe pa nthawiyo. Mukatero mumasonyeza kuti mumaganizira komanso kulemekeza anthu ena. Mumasonyezanso kuti sikuti mumangofuna zopindulitsa inuyo basi koma zopindulitsanso ena.—1 Akor. 10:24.

Boma limathanso kupereka malamulo pa nkhani ya mowa, amene Akhristu ayeneranso kuwatsatira. Malamulowo angakhale okhudza zaka zimene munthu ayenera kuyamba kumwa kapena oletsa kumwa ngati ukuyendetsa galimoto kapena kugwiritsa ntchito mashini ena ake.—Aroma 13:​1-5.

Yehova anatilemekeza potipatsa ufulu wosankha zochita pamene tikusangalala ndi mphatso zosiyanasiyana zimene watipatsa. Zimenezi zikuphatikizapo ufulu wosankha zimene tikufuna kudya kapena kumwa. Tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira ufulu umene tapatsidwawu pochita zinthu zimene zingalemekeze Atate wathu wakumwamba.

a Bungwe lina loona za umoyo ku United States, linanena kuti kumwa mowa kwambiri kumabweretsa mavuto monga kupha anthu, kudzipha, nkhanza zokhudza kugonana, kuzunza mwamuna kapena mkazi wako, khalidwe lotayirira pa nkhani ya kugonana komanso kupita padera.