Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 51

Tili ndi Chiyembekezo Chomwe Sichitikhumudwitsa

Tili ndi Chiyembekezo Chomwe Sichitikhumudwitsa

“Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa.”—AROMA 5:5.

NYIMBO NA. 142 Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi n’chiyani chinathandiza Abulahamu kuti akhale ndi chiyembekezo?

 YEHOVA analonjeza Abulahamu yemwe anali mnzake kuti mitundu yonse ya padziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa mbadwa yake. (Gen. 15:5; 22:18) Popeza Abulahamu ankakhulupirira kwambiri Mulungu, sankakayikira kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwa. Ngakhale zinali choncho, Abulahamu anali ndi zaka 100 ndipo mkazi wake zaka 90, koma banja lokhulupirikali linalibe mwana. (Gen. 21:​1-7) Koma Baibulo limati: “Abulahamu anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri . . . mogwirizana ndi zimene zinanenedwa.” (Aroma 4:18) Inu mukudziwa kuti zimene Abulahamu ankayembekezerazi zinakwaniritsidwa. Iye anabereka mwana wamwamuna dzina lake Isaki, yemwe anamuyembekezera kwa nthawi yaitali. Kodi n’chiyani chinamuthandiza Abulahamu kuti asamakayikire zimene Mulungu anamulonjeza?

2. N’chifukwa chiyani Abulahamu sankakayikira kuti zimene Yehova anamulonjeza zidzakwaniritsidwa?

2 Chifukwa chakuti anali pa ubwenzi ndi Yehova, Abulahamu “sankakayikira kuti zimene Mulungu analonjeza,” zidzakwaniritsidwa. (Aroma 4:21) Yehova anasangalala ndi Abulahamu, ndipo anamutchula kuti anali wolungama chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro. (Yak. 2:23) Monga mmene lemba la Aroma 4:18 limasonyezera, Abulahamu anali ndi chikhulupiriro komanso chiyembekezo. Tiyeni tikambirane zimene mtumwi Paulo ananena zokhudza chiyembekezo, mogwirizana ndi zimene zili mu Aroma 5.

3. Kodi Paulo akufotokoza zotani zokhudza chiyembekezo?

3 Paulo anafotokoza chifukwa chake tingakhale otsimikiza kuti ‘chiyembekezo chathu sichitikhumudwitsa.’ (Aroma 5:5) Zimene ananena zimatithandizanso kumvetsa mmene Akhristufe tingakhalire ndi chiyembekezo champhamvu. Tikamakambirana zimene zili pa Aroma 5:​1-5, muziganizira mmene zinthu zilili kwa inuyo. Mukamachita zimenezo, muona kuti pamene nthawi ikudutsa, chiyembekezo chanu chikhala chikuwonjezereka. Kukambirana nkhaniyi kukuthandizaninso kuona zimene mungachite kuti chiyembekezo chanu chiwonjezereke kuposa panopa. Tsopano tiyeni tikambirane za chiyembekezo chabwino kwambiri chimene Paulo ananena kuti sichitikhumudwitsa.

CHIYEMBEKEZO CHABWINO KWAMBIRI

4. Kodi Paulo akufotokoza zotani pa Aroma 5:​1, 2?

4 Werengani Aroma 5:​1, 2. Paulo analembera mawu amenewa Akhristu a ku Roma. Abale ndi alongo kumeneko anali ataphunzira za Yehova ndi Yesu, anali ndi chikhulupiriro komanso anali atakhala Akhristu. Choncho Mulungu ‘anawaona kuti ndi olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,’ ndipo anawadzoza ndi mzimu woyera. Iwo analidi ndi chiyembekezo chabwino kwambiri.

5. Kodi odzozedwa ali ndi chiyembekezo chotani?

5 Pambuyo pake Paulo analembera Akhristu odzozedwa a ku Efeso za chiyembekezo chimene Mulungu anawapatsa. Chiyembekezo chimenecho chinkaphatikizapo “zinthu . . . zimene walonjeza kwa oyera.” (Aef. 1:18) Polembera Akhristu a ku Kolose, Paulo anasonyezanso kumene iwo adzalandirire zimene ankayembekezera. Iye anati iwo anali ndi ‘chiyembekezo chodzalandira zinthu zimene anawasungira kumwamba.’ (Akol. 1:​4, 5) Choncho chiyembekezo cha Akhristu odzozedwa n’chakuti adzaukitsidwa n’kukakhala ndi moyo wosatha kumwamba, komwe akalamulire limodzi ndi Khristu.—1 Ates. 4:​13-17; Chiv. 20:6.

M’bale F. W. Franz anafotokoza kuti Akhristu odzozedwa amakhulupirira kwambiri kuti zimene akuyembekezera zidzachitikadi (Onani ndime 6)

6. Kodi m’bale wina wodzozedwa anafotokoza zotani zokhudza chiyembekezo chake?

6 Akhristu odzozedwa amasangalala ndi chiyembekezo chawochi. Mmodzi mwa iwo, yemwe ndi M’bale Frederick Franz, anafotokoza mmene ankamvera chifukwa cha chiyembekezochi, ndipo anati: “Chiyembekezo chathu n’chotsimikizirika ndipo chidzakwaniritsidwa kwa aliyense wa a 144,000, omwe ndi kagulu ka nkhosa. Zimene tikuyembekezerazi zidzakhala zabwino kwambiri kuposa mmene tikuganizira.” Atatumikira Mulungu kwa zaka zambiri, mu 1991, M’bale Franz ananenanso kuti: “Sitinaleke kuona kufunika kwa chiyembekezo chimenechi. Timachiyamikira mowonjezeraka kwa nthawi yonse yomwe tiyenera kuyembekezera. Ndi chinthu choyenera kuchiyembekezera ngakhale kwa zaka mamiliyoni. Ndimakonda kwambiri chiyembekezochi kuposa ndi kale lonse.”

7-8. Kodi atumiki ambiri a Yehova ali ndi chiyembekezo chotani? (Aroma 8:​20, 21)

7 Anthu ambiri omwe amalambira Yehova masiku ano ali ndi chiyembekezo chosiyana ndi chimenechi. Iwo ali ndi chiyembekezo chofanana ndi chimene Abulahamu anali nacho, chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu. (Aheb. 11:​8-10, 13) Paulo analemba za zinthu zabwino zomwe anthu omwe ali ndi chiyembekezochi adzalandire. (Werengani Aroma 8:​20, 21.) Mutaphunzira koyamba za zinthu zimene Baibulo limalonjeza ponena za m’tsogolo, kodi n’chiyani chinakusangalatsani kwambiri? Kodi inali mfundo yakuti tsiku lina mudzakhala wangwiro ndipo simudzakhalanso wochimwa? Kapena kodi munasangalala mutadziwa kuti anthu omwe mumawakonda adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo m’paradaiso? Chifukwa cha “chiyembekezo” chimene Mulungu wapereka, mukuyembekezera zinthu zabwino zambiri.

8 Kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, tili ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chomwe chimatichititsa kuti tizisangalala. Ndipotu tikhoza kumakhulupirira kwambiri zimene tikuyembekezera. Zimene Paulo analemba pambuyo pake zingatithandize kudziwa mmene tingachitire zimenezi. Tiyeni tione zimene iye analemba zokhudza chiyembekezo chathu. Kuchita zimenezi kutithandiza kuti tisamakayikire ngakhale pang’ono kuti zimene tikuyembekezera zidzakwaniritsidwa.

CHIYEMBEKEZO CHIMAWONJEZEREKA

Akhristu onse amayembekezera kukumana ndi mavuto enaake (Onani ndime 9-10)

9-10. Kodi chitsanzo cha Paulo chikusonyeza kuti Akhristu akuyembekezera chiyani? (Aroma 5:3) (Onaninso zithunzi.)

9 Werengani Aroma 5:3. Lembali likusonyeza kuti chiyembekezo chathu chimakula tikakumana ndi mavuto. Mwina zimenezi zikukudabwitsani. Zoona n’zakuti otsatira onse a Khristu amayembekezera kukumana ndi mavuto. Taganizirani zimene zinachitikira Paulo. Polembera Akhristu a ku Tesalonika, iye anati: “Pamene tinali nanu limodzi, tinkakuuziranitu kuti tidzakumana ndi mavuto ndipo monga mmene mukudziwira, zimene tinkakuuzanizo ndi zimene zachitikadi.” (1 Ates. 3:4) Ndipo kwa Akhristu a ku Korinto, iye analemba kuti: “Abale, tikufuna muzidziwa za mavuto amene tinakumana nawo, . . . tinalibe chiyembekezo choti tikhala ndi moyo.”—2 Akor. 1:8; 11:​23-27.

10 Masiku anonso Akhristu angakumane ndi mavuto enaake. (2 Tim. 3:12) Nanga bwanji inuyo? Kodi mwakumana ndi mavuto chifukwa chokhulupirira komanso kutsatira Yesu? Mwina mumanyozedwa ndi anzanu kapena achibale. Mwinanso amakuchitirani nkhanza. Kodi mumakumana ndi mavuto kuntchito chifukwa choyesetsa kuchita zinthu moona mtima? (Aheb. 13:18) Kodi mumatsutsidwa ndi akuluakulu a boma chifukwa chouza ena za chiyembekezo chanu? Kaya tikumane ndi mavuto otani, Paulo anati tiyenera kukhalabe osangalala. Chifukwa chiyani?

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala otsimikiza kupirira mayesero alionse?

11 Tikhoza kumasangalalabe ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto, chifukwa timadziwa kuti mavutowo angatithandize kukhala ndi khalidwe lina lofunika. Lemba la Aroma 5:3 limati “mavuto athu amachititsa kuti tipirire.” Akhristu onse adzakumana ndi mavuto, choncho ayenera kukhala opirira. Tiyenera kukhala otsimikiza kupirira mavuto aliwonse omwe tingakumane nawo. Tikatero m’pamene tingadzaone kukwaniritsidwa kwa zimene tikuyembekezera. Sitikufuna kukhala ngati anthu omwe anali m’maganizo a Yesu pamene ankanena za mbewu zimene zinagwera pamwala. Poyamba iwo analandira mawu mosangalala, koma ‘atakumana ndi masautso kapena kuyamba kuzunzidwa,’ anabwerera m’mbuyo. (Mat. 13:​5, 6, 20, 21) N’zoona kuti kukumana ndi mayesero kapena kuzunzidwa si kosangalatsa, koma tikapirira timapeza madalitso ndipo timapitiriza kutumikira Mulungu.

12. Kodi tikapirira mayesero timapeza madalitso otani?

12 Mtumwi Yakobo anafotokoza madalitso omwe timapeza tikamapirira mayesero. Iye analemba kuti: “Lolani kuti kupirirako kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda cholakwa pa mbali iliyonse, kapena kuti mukhale ndi makhalidwe onse abwino.” (Yak. 1:​2-4) Yakobo analemba ngati kuti kupirira kuli ndi ntchito yoti kugwire. Kodi ndi ntchito iti yomwe kupirira kumagwira? Kungatithandize kuti tizisonyeza kwambiri makhalidwe monga kuleza mtima, chikhulupiriro komanso kudalira Mulungu. Koma kupirira kumatithandizanso m’njira ina yofunika kwambiri.

13-14. Kodi kupirira kumatithandiza bwanji, nanga zimenezi zikugwirizana bwanji ndi chiyembekezo? (Aroma 5:4)

13 Werengani Aroma 5:4. Paulo ananena kuti kupirira “kumachititsa kuti tikhale ovomerezeka.” Tikapirira mayesero timakhala ovomerezeka kwa Yehova. Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amasangalala tikamakumana ndi mayesero kapena mavuto. M’malomwake, Mulungu amasangalala ndi ifeyo. Kupirira kwathu kumachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu. Amenewatu ndi madalitso aakulu kwambiri.—Sal. 5:12.

14 Kumbukirani kuti Abulahamu anapirira mayesero ndipo Mulungu anasangalala naye. Yehova ankamuona kuti ndi mnzake, ndipo anamutchula kuti ndi wolungama. (Gen. 15:6; Aroma 4:​13, 22) Zimenezi zingatichitikirenso ifeyo. Sikuti Mulungu amasangalala ndi kuchuluka kwa zimene timachita pomutumikira kapena maudindo omwe tili nawo. Iye amasangalala nafe chifukwa chakupirira kwathu mokhulupirika. Ndipotu tonsefe tingathe kupirira posatengera msinkhu wathu, mmene zinthu zilili kapenanso luso lathu. Kodi pali mayesero omwe mukupirira mokhulupirika panopa? Ngati ndi choncho, zikulimbikitsani kudziwa kuti Mulungu akusangalala nanu. Kudziwa kuti Mulungu akusangalala nafe kungatithandize kuti chiyembekezo chathu chikhale champhamvu.

CHIYEMBEKEZO CHAMPHAMVU

15. Kodi Paulo anatchulanso mfundo ina iti, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zingadabwitse anthu ena?

15 Monga mmene Paulo anafotokozera, Yehova amasangalala nafe tikamapirira mayesero. Taonani mmene Paulo anapitirizira kufotokoza: “Kukhala ovomerezeka kwa Mulungu kumachititsa kuti tikhale ndi chiyembekezo. Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa.” (Aroma 5:​4, 5) Zimenezi zingadabwitse anthu ena. Chifukwa chiyani? Chifukwa poyamba, monga mmene lemba la Aroma 5:2 likusonyezera, Paulo ananena kuti Akhristu a ku Roma anali kale ndi chiyembekezo, chiyembekezo cholandira ulemerero wa Mulungu. Choncho wina angafunse kuti, ‘Ngati Akhristuwo anali kale ndi chiyembekezo, n’chifukwa chiyani Paulo akubwerezanso kutchula za chiyembekezo?’

Nthawi ikamapita, chiyembekezo chimene munali nacho chimawonjezereka ndipo mumakhulupirira kwambiri kuti zimene mukuyembekezerazo zidzachitika (Onani ndime 16-17)

16. Kodi zimatani kuti munthu ayambe kukhala ndi chiyembekezo? (Onaninso zithunzi.)

16 Tingamvetse zimene Paulo ankatanthauza tikaganizira mfundo yakuti chiyembekezo chimawonjezereka. Mwachitsanzo, kodi mukukumbukira mmene munamvera mutawerenga kwa nthawi yoyamba za zinthu zosangalatsa zomwe timawerenga m’Mawu a Mulungu, zomwe tikuyembekezera? Mwina munkaganiza kuti lonjezo lakuti anthu adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso ndi maloto chabe. Koma mutayamba kuphunzira zambiri zokhudza Yehova komanso malonjezo ake opezeka m’Baibulo, munayamba kukhulupirira kwambiri kuti zimenezi zidzachitikadi.

17. Kodi chiyembekezo chimawonjezereka bwanji munthu akadzipereka komanso kubatizidwa?

17 Ngakhale pamene munadzipereka komanso kubatizidwa, munapitiriza kuphunzira komanso kukula mwauzimu, ndipo chiyembekezo chanu chinapitiriza kukula. (Aheb. 5:13–6:1) N’kutheka kuti zimene zili pa Aroma 5:​2-4 zakhala zikukuchitikirani. Mwakhala mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana koma mwawapirira, ndipo mwaona Yehova akusangalala nanu. Popeza simukayikira kuti Mulungu amakukondani, panopa muli ndi chifukwa chachikulu choyembekezerera zimene walonjeza. Chiyembekezo chanu chakhala champhamvu kwambiri kuposa mmene zinalili poyamba. Mumaona kuti zimene mukuyembekezera ndi zenizeni ndipo zimakukhudzani kwambiri. Chiyembekezocho chimakuthandizani pa mbali iliyonse ya moyo wanu, ndipo chakuthandizani kusintha mmene mumachitira zinthu ndi anthu a m’banja lanu, zimene mumasankha komanso mmene mumagwiritsira ntchito nthawi yanu.

18. Kodi Yehova akutitsimikizira chiyani?

18 Mtumwi Paulo anatchulanso mfundo ina yofunika kwambiri pa nkhani ya chiyembekezo chomwe timakhala nacho pambuyo pokhala ovomerezeka kwa Mulungu. Iye anatitsimikizira kuti zimene tikuyembekezera zidzakwaniritsidwa. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zimenezi? Mouziridwa, Paulo anatsimikizira Akhristu kuti: “Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu amasonyeza kuti amatikonda pogwiritsa ntchito mzimu woyera umene amatipatsa.” (Aroma 5:5) Tili ndi zifukwa zokwanira zotichititsa kukhala ndi chiyembekezo chomwe Yehova anatipatsachi.

19. Kodi sitiyenera kukayikira chiyani pa nkhani ya zimene tikuyembekezera?

19 Taganizirani zimene Yehova analonjeza Abulahamu komanso mmene anasonyezera kuti ankasangalala naye n’kumutchula kuti mnzake. Zimene Abulahamu ankayembekezera zinakwaniritsidwa. Baibulo limati: “Abulahamu atasonyeza kuleza mtima, analandira lonjezo limeneli.” (Aheb. 6:15; 11:​9, 18; Aroma 4:​20-22) Iye sanagwiritsidwe mwala. Inunso mungakhale otsimikiza kuti ngati mupitiriza kukhalabe okhulupirika, mudzalandira zimene mukuyembekezera. Chiyembekezo chanu ndi chenicheni ndipo chingakuthandizeni kukhala osangalala, osati kukukhumudwitsani. (Aroma 12:12) Paulo analemba kuti: “Mulungu amene amapereka chiyembekezo akuthandizeni kukhala osangalala kwambiri komanso kukhala ndi mtendere wonse pamene mukumukhulupirira, kuti mukhale ndi chiyembekezo champhamvu mothandizidwa ndi mzimu woyera.”—Aroma 15:13.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

a Munkhaniyi tikambirana zimene tikuyembekezera m’tsogolo, komanso chifukwa chake tingakhulupirire kuti zidzakwaniritsidwa. Chaputala 5 cha Aroma chitithandiza kuona kusiyana kwa chiyembekezo chomwe tili nacho panopa ndi chimene tinali nacho titangophunzira kumene choonadi.