Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOTI NDIPHUNZIRE

Anthu Okhulupirika kwa Yehova Amakwaniritsa Zimene Alonjeza

Anthu Okhulupirika kwa Yehova Amakwaniritsa Zimene Alonjeza

Werengani Oweruza 11:30-40 kuti muone zimene mukuphunzira kwa Yefita ndi mwana wake wamkazi pa nkhani yokwaniritsa malonjezo.

Ganizirani nkhani yonse. Kodi Aisiraeli okhulupirika ankaona bwanji zimene amulonjeza Yehova? (Num. 30:2) Kodi Yefita ndi mwana wake wamkazi anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova?​—Ower. 11:9-11, 19-24, 36.

Fufuzani mozama. Kodi Yefita analonjeza chiyani nanga ankatanthauza chiyani? (w16.04 7 ¶12) Kodi Yefita ndi mwana wake anadzimana zinthu ziti kuti akwaniritse zimene analonjeza? (w16.04 7-8 ¶14-16) Kodi ndi zinthu ziti zimene Akhristu angalonjeze masiku ano?​—w17.04 5-8 ¶10-19.

Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘N’chiyani chingandithandize kukwaniritsa lonjezo lomwe ndinachita podzipereka kwa Yehova?’ (w20.03 13 ¶20)

  • ‘Kodi ndingadzimane zinthu ziti kuti ndizichita zambiri potumikira Yehova?’

  • ‘Kodi ndingatani kuti ndizikwaniritsa zimene ndinalonjeza mwamuna kapena mkazi wanga pamene tinkakwatirana?’ (Mat. 19:5, 6; Aef. 5:28-33)