Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 50

NYIMBO NA. 135 Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga Khala Wanzeru”

Muzithandiza Ana Anu Kulimbitsa Chikhulupiriro Chawo

Muzithandiza Ana Anu Kulimbitsa Chikhulupiriro Chawo

“Muzindikire chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”​—AROMA 12:2.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona zinthu zina zimene zingathandize makolo kuti azikambirana momasuka ndi ana awo komanso mmene angawathandizire kuti azikhulupirira Mulungu ndi Baibulo.

1-2. Kodi makolo ayenera kuchita chiyani ngati mwana wawo akufunsa mafunso okhudza zimene timakhulupirira?

 AMBIRI angavomereze kuti kulera ana ndi ntchito yaikulu. Ngati ndinu kholo ndipo muli ndi mwana wamng’ono tikukuthokozani chifukwa choyesetsa kumuthandiza kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Deut. 6:6, 7) Mwana wanu akamakula adzayamba kufunsa mafunso ena ovuta okhudza zimene timakhulupirira komanso mfundo za m’Baibulo zokhudza makhalidwe abwino.

2 Poyamba mukhoza kumada nkhawa ndi mafunso amene mwana wanu akufunsa. Mwinanso mukhoza kuyamba kuona kuti chikhulupiriro chake chayamba kuchepa. Koma zoona n’zakuti mwana akamakula ayenera kumafunsa mafunso n’cholinga chakuti azitsimikizira zimene amakhulupirira. (1 Akor. 13:11) Choncho simuyenera kuchita mantha. Akamafunsa mafunso muziona kuti umenewo ndi mwayi womuthandiza kuti aziganiza bwino.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Munkhaniyi tikambirana zimene makolo angachite pothandiza ana awo kuti, (1) azitsimikizira zimene amakhulupirira, (2) aziyamikira mfundo zamakhalidwe abwino za m’Baibulo, komanso (3) azitha kufotokozera ena zimene amakhulupirira. Tionanso ubwino woti ana azifunsa mafunso komanso zimene makolo angachite pokambirana ndi ana awo zimene amakhulupirira.

MUZITHANDIZA ANA ANU KUTSIMIKIZIRA ZIMENE AMAKHULUPIRIRA

4. Kodi mwana wanu angadzifunse mafunso ati nanga n’chifukwa chiyani?

4 Makolo a Chikhristu amazindikira kuti kukhulupirira Mulungu si zimene mwana amatengera pobadwa. Inuyo simunabadwe mukukhulupirira Yehova. N’chimodzimodzinso ndi mwana wanu. Pakapita nthawi, iye akhoza kumadzifunsa mafunso ngati awa: ‘Ndingadziwe bwanji kuti kuli Mulungu? Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona?’ Ndipotu Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizigwiritsa ntchito luso la kuganiza,’ komanso ‘tizifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizira.’ (Aroma 12:1; 1 Ates. 5:21) Ndiye kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba?

5. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuti azikhulupirira Baibulo? (Aroma 12:2)

5 Muzithandiza mwana wanu kupeza umboni wotsimikizira kuti zimene Baibulo limaphunzitsa ndi zoona. (Werengani Aroma 12:2.) Mwana wanu akamafunsa mafunso muzipezerapo mwayi womuthandiza mmene angapezere mayankho pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira monga Watch Tower Publications Index komanso Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani. M’buku lofufuzira nkhanili, pansi pa mutu wakuti “Baibulo,” angayang’ane pa kamutu kakuti “Kuuziridwa ndi Mulungu” kuti apeze umboni wakuti Baibulo ndi “Mawu a Mulungu” osati chabe buku labwino lolembedwa ndi anthu. (1 Ates. 2:13) Mwachitsanzo, angafufuze zokhudza mzinda wakale wa Asuri wotchedwa Nineve. Kale anthu otsutsa Baibulo ankanena kuti mzinda wa Nineve kunalibe. Koma pofika m’ma 1850, anthu anafukula zinthu zakale za mumzindawu zomwe zinatsimikizira kuti Baibulo ndi lolondola. (Zef. 2:13-15) Kuti aone umboni wakuti kuwonongedwa kwa Nineve kunakwaniritsa ulosi wa m’Baibulo angawerenge nkhani yakuti “Kodi Mukudziwa?” mu Nsanja ya Olonda ya November 2021. Akamayerekezera zimene amaphunzira m’mabuku athu ndi zimene mabuku ena odalirika amanena, mwana wanu adzayamba kukhulupirira kwambiri zimene Baibulo limanena.

6. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kupeza umboni wakuti Baibulo ndi lolondola? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.)

6 Muzithandiza mwana wanu kuti aziganiza. Makolo ayenera kugwiritsa ntchito mwayi uliwonse kuti akambirane ndi mwana wawo zokhudza kukhulupirira Mulungu kapena Baibulo. Angachite zimenezi pamene apita kumalo osungirako zinthu zakale, kumalo ena ake okongola kapena akapita kukaona zinthu ku ofesi ya nthambi. Mwachitsanzo, mukapita kumalo osungirako zinthu zakale kapena kuona zinthuzo pa intaneti, mungagwiritse ntchito zinthu zakalezo pothandiza mwana wanu kuona kuti Baibulo ndi lolondola. Kodi mwana wanu amadziwa kuti dzina la Mulungu limapezeka pamwala wina wa ku Moabu womwe wakhalapo zaka pafupifupi 3,000? Mwala umenewu uli kumalo osungirako zinthu zakale ku Louvre ku Paris m’dziko la France. Mungathenso kukaona mwala wa ku Moabu woyerekezera ku Likulu Lapadziko Lonse la Mboni za Yehova ku Warwick ku New York. Mwala umenewu umasonyeza kuti Mfumu Mesa ya ku Mowabu inagalukira Isiraeli. Zimene ndi zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. (2 Maf. 3:4, 5) Ngati mwana wanu ataona umboni woti Baibulo ndi lolondola, chikhulupiriro chake chikhoza kulimba.​—Yerekezerani ndi 2 Mbiri 9:6.

Mungathandize mwana wanu kuti aziganiza bwino, pokambirana naye za zinthu zakale zimene zimatsimikizira kuti Baibulo ndi lolondola (Onani ndime 6)


7-8. (a) Kodi tingaphunzire chiyani pa zinthu zokongola zimene timaona m’chilengedwe? Perekani chitsanzo. (Onaninso chithunzi.) (b) Kodi ndi mafunso ati amene angathandize mwana wanu kuti azikhulupirira kuti kuli Mlengi?

7 Muzilimbikitsa mwana wanu kuti aziganizira zinthu za m’chilengedwe. Mukamayenda ndi mwana wanu m’tchire kapena m’munda, muzimuthandiza kuona kapangidwe kochititsa chidwi ka zinthu za m’chilengedwe. N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezo? Zimenezi zingamuthandize kuzindikira kuti amene anapanga zinthu zimenezi ndi wanzeru. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri asayansi akhala akuphunzira kapangidwe kozungulira ka zinthu zosiyanasiyana. Wasayansi wina dzina lake Nicola Fameli anafotokoza kuti zinthu zambiri zozungulira m’chilengedwechi zimapindika mozungulira maulendo ofanana. Kazunguliridwe kameneka kamatchedwa Fibonacci. Timaona kuzungulira kotereku m’zinthu zambiri za m’chilengedwe monga milalang’amba, chigoba cha nkhono masamba a zomera zina komanso mpendadzuwa. a

8 Mwana wanu akamaphunzira sayansi kusukulu akhoza kuzindikira kuti m’chilengedwechi muli malamulo amene amachititsa kuti zinthu zizioneka mosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mitengo yambiri imaoneka mofanana. Pamakhala thunthu, nthambi kenako masamba. Kaonekedwe kameneka kamapezekanso m’zinthu zina m’chilengedwe. Koma kodi ndi ndani amene anaika malamulo amene amathandiza kuti zinthu zizioneka zokongola chonchi? Nanga ndi ndani amene anazilenga? Pamene mwana wanu akuganizira mayankho a mafunso amenewa, m’pamenenso amayamba kukhulupirira kwambiri kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. (Aheb. 3:4) Pa nthawi ina mukhoza kumufunsa kuti, “Ngati Mulungu ndi amene anatilenga, kodi sizingakhale zomveka kuti iye ndi amene ayenera kutipatsa malangizo otithandiza kuti tizisangalala?” Kenako mungamuuze kuti malangizo amenewa amapezeka m’Baibulo.

NASA, ESA, and the Hubble Heritage (STScl/AURA)-ESA/Hubble Collaboration

Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zokongola zomwe timaona m’chilengedwe? (Onani ndime 7-8)


MUZITHANDIZA MWANA WANU KUYAMIKIRA MFUNDO ZAMAKHALIDWE ABWINO

9. Kodi n’chiyani chingachititse mwana wanu kufunsa funso lokhudza mfundo za makhalidwe abwino za m’Baibulo?

9 Ngati mwana wanu ali ndi mafunso okhudza mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino, muziganizira chifukwa chake wafunsa mafunsowo. Kodi wafunsa chifukwa chakuti amakayikira mfundo za m’Baibulozo, kapena vuto ndi loti sakudziwa mmene angafotokozere ena zimene amakhulupirira? Kaya wafunsa pa zifukwa ziti mungamuthandize kuti aziyamikira mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino pophunzira naye buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. b

10. Kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti aziganizira zimene angachite kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova?

10 Muzilimbikitsa mwana wanu kuti azifunitsitsa kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Mukamaphunzira Baibulo ndi mwana wanu muzimuthandiza kuganiza pogwiritsa ntchito mafunso ndi mafanizo opezeka m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. (Miy. 20:5) Phunziro 8 limayerekezera Yehova ndi mnzathu wabwino amene amatikumbutsa zinthu zimene zingatiteteze komanso kutithandiza. Pambuyo pokambirana naye lemba la 1 Yohane 5:3 mungamufunse kuti, “Kodi kudziwa kuti Yehova ndi mnzathu wabwino kungatithandize kuti tiziona bwanji zimene amatiuza kuti tizichita?” Funsoli lingaoneke ngati losavuta, koma lingamuthandize mwana wanu kuti aziona malamulo a Mulungu ngati umboni woti amatikonda.​—Yes. 48:17, 18.

11. Kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti aziyamikira mfundo za m’Baibulo? (Miyambo 2:10, 11)

11 Muzikambirana ndi mwana wanu mmene mfundo za m’Baibulo zingamuthandizire. Mukamawerenga Baibulo kapena lemba la tsiku, muzikambirana mmene mfundo za m’Baibulo zathandizira banja lanu. Kodi mwana wanu amaona ubwino wogwira ntchito mwakhama komanso kukhala oona mtima? (Aheb. 13:18) Mungamufotokozerenso mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira kuti tikhale athanzi komanso osangalala. (Miy. 14:29, 30) Kukambirana naye mfundo ngati zimenezi kungamuthandize kuti aziyamikira kwambiri mfundo za m’Baibulo.​—Werengani Miyambo 2:10, 11.

12. Kodi bambo wina amathandiza bwanji mwana wake kuti aziona kuti mfundo za m’Baibulo ndi zothandiza?

12 Bambo wina wa ku France dzina lake Steve, anafotokoza mmene iye ndi mkazi wake amathandizira mwana wawo dzina lake Ethan, kuti aziona kuti Yehova amatipatsa malamulo chifukwa chotikonda. Iwo anati: “Timamufunsa mafunso ngati akuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizimvera mfundo imeneyi? Kodi zimenezi zikusonyeza bwanji kuti amatikonda? Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitingatsatire mfundo imeneyi?’” Kukambirana mafunso ngati amenewa kunathandiza Ethan kuti azikonda mfundo za Yehova. Steve anawonjezera kuti: “Cholinga chathu ndi kuthandiza Ethan kuti aziona kuti nzeru za m’Baibulo ndi zabwino kwambiri kuposa za anthu.”

13. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuti azigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo? Perekani chitsanzo.

13 Muziphunzitsa mwana wanu mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo. Mungathe kuchita zimenezi pamene mwana wanu wauzidwa kuti awerenge buku linalake kusukulu. Zimene zili m’bukulo zingamasonyeze kuti anthu amene amachita chiwerewere kapena amene amakwiya kwambiri ndi oyenera kuwatsanzira. Mungalimbikitse mwanayo kuganizira ngati anthu amene akufotokozedwa m’bukuwo akutsatira mfundo za m’Baibulo. (Miy. 22:24, 25; 1 Akor. 15:33; Afil. 4:8) Zimenezi zingamuthandize kuti akalalikire aphunzitsi komanso anzake a m’kalasi pa nthawi imene akukambirana zimene zili m’bukulo.

MUZITHANDIZA MWANA WANU KUTI AZITHA KUFOTOKOZERA ENA ZIMENE AMAKHULUPIRIRA

14. Kodi ndi nkhani ziti zimene zikhoza kuchititsa mantha Mkhristu wachinyamata akakhala kusukulu, nanga n’chifukwa chiyani?

14 Nthawi zina Akhristu achinyamata amaopa kufotokozera ena zimene amakhulupirira. Mwina iwo angachite mantha anthu m’kalasi akayamba kufotokoza kuti zinthu zinachita kusintha. Mwina angamachite mantha chifukwa chakuti aphunzitsi awo amafotokoza ngati kuti zinthu zinachitadi kusintha. Ndiye ngati ndinu kholo kodi mungatani kuti muthandize mwana wanu kuti asamaope kufotokoza zomwe amakhulupirira?

15. Kodi n’chiyani chimene chingathandize Mkhristu wachinyamata kuti asamakayikire zimene amakhulupirira?

15 Muzithandiza mwana wanu kuti asamakayikire zimene amakhulupirira. Mwana wanu sayenera kuchita manyazi chifukwa chakuti amakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa. (2 Tim. 1:8) N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa palinso asayansi ambiri amene amakhulupirira kuti zamoyo sizinachite kusintha. Iwo amaona umboni woti pali winawake wanzeru amene analenga zinthu zodabwitsa za m’chilengedwe. Choncho iwo sagwirizana ndi zimene zimaphunzitsidwa kusukulu zakuti zamoyo zinachita kusintha. Mwana wanu akhoza kulimbitsa chikhulupiriro chake akamaganizira zifukwa zimene zinachititsa abale ndi alongo ena kukhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa. c

16. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuti azitha kufotokozera ena kuti kuli Mlengi? (1 Petulo 3:15) (Onaninso chithunzi.)

16 Muzithandiza mwana wanu kuti azitha kufotokozera ena chifukwa chake amakhulupirira kuti kuli Mlengi. (Werengani 1 Petulo 3:15.) Zingakhale zothandiza kuphunzira ndi mwana wanuyo nkhani zopeza pa jw.org zakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa​—Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa?” Ndiyeno mungakambirane ndi mwana wanuyo zifukwa zimene iyeyo akuona kuti zingathandize ena kudziwa kuti zinthu zinachita kulengedwa. Muyenera kumukumbutsa kuti sakuyenera kukangana ndi anzake akusukulu pokambirana nkhaniyi. Mulimbikitseni kuti azigwiritsa ntchito mfundo zosavuta ngati ena akufuna kuti akambirane naye. Mwachitsanzo, mnzake wakusukulu anganene kuti: “Ndimangokhulupirira zokhazo zimene ndaziona, ndipo sindinaonepo Mulungu.” Mkhristu wachinyamatayo angayankhe kuti: “Tiyerekeze kuti ukuyenda m’nkhalango kumalo kumene kulibeko anthu ndipo wapeza chitsime chabwinobwino. Kodi ungaganize chiyani? Ngati chitsimecho chikukupatsa umboni woti pali winawake wanzeru amene anachipanga, ndiye kuli bwanji zinthu zonse za m’chilengedwezi?”

Muzifotokoza momveka bwino komanso m’njira yosavuta mukamakambirana ndi anzanu akusukulu (Onani ndime 16-17) d


17. Kodi makolo angalimbikitse bwanji mwana wawo kuti azifunafuna mipata youza ena choonadi cha m’Baibulo? Perekani chitsanzo.

17 Muzilimbikitsa mwana wanu kuti azifunafuna mipata youza ena choonadi cha m’Baibulo. (Aroma 10:10) Mungayerekezere khama limene mwana wanu amafunika kuti aziuza ena zimene amakhulupirira ndi khama limene limafunika kuti munthu aphunzire kugwiritsa ntchito chida chinachake choimbira. Poyamba angafunike kuphunzira nyimbo yosavuta. Pakapita nthawi angayambe kuimba nyimbo ngakhale zovuta. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu wachinyamata angayambe ndi nkhani yosavuta pouza ena zimene amakhulupirira. Mwachitsanzo, iye angafunse mnzake wa kusukulu kuti: “Kodi ukudziwa kuti akatswiri opanga zinthu amatengera zinthu za m’chilengedwe? Ndikufuna ndikuonetse kavidiyo aka komwe ndi kosangalatsa.” Pambuyo pomuonetsa imodzi mwa mavidiyo akuti Kodi Zinangochitika Zokha? anganene kuti: “Kodi ndi ndani amene akuyenera kulemekezedwa pakati pa akatswiri amene amapanga zinthu potengera zinthu za m’chilengedwe ndi mwiniwake amene anapanga zinthu zachilengedwezo?” Kugwiritsa ntchito njira yosavuta imeneyi kungathandize mnzake wa kusukuluyo kukhala ndi chidwi chofuna kuphunzira zambiri.

PITIRIZANI KUTHANDIZA MWANA WANU KUTI AZILIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHAKE

18. Kodi makolo angathandize bwanji mwana wawo kuti azikhulupirira kwambiri Mulungu?

18 Tikukhala m’dziko limene anthu ake sakukhulupirira Yehova. (2 Pet. 3:3) Choncho makolo mukamaphunzira Baibulo ndi mwana wanu muzimulimbikitsa kuti aziphunzira nkhani zomwe zingamuthandize kuti azilemekeza Mawu a Mulungu komanso mfundo zake za makhalidwe abwino. Muzimuthandiza kuti aziganiza mozama pomufotokozera zinthu zodabwitsa zimene Yehova analenga. Muzimuthandizanso kuti aziganizira maulosi ochititsa chidwi a m’Baibulo amene anakwaniritsidwa kale. Koposa zonse muzipemphera ndi mwana wanu komanso kumupempherera. Mukamachita zimenezi, Yehova adzakudalitsani ndipo mudzathandiza mwana wanu kulimbitsa chikhulupiriro chake.​—2 Mbiri 15:7.

NYIMBO NA. 133 Lambirani Yehova Mudakali Achinyamata

a Kuti mudziwe zambiri onerani vidiyo ya Chingelezi pa jw.org yakuti The Wonders of Creation Reveal God’s Glory.

b Ngati mwana wanu anamaliza kuphunzira buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, mungabwereze naye mitu ina ya m’gawo 3 ndi 4 yomwe imafotokoza mfundo za m’Baibulo za makhalidwe abwino.

c Onani nkhani yakuti “Chifukwa Chimene Timakhulupirira Kuti Kuli Mlengi” mu Galamukani! ya September 2006, komanso kabuku kakuti Mmene Moyo Unayambira​—Mafunso 5 Ofunika Kwambiri.

d MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Wachinyamata wa Mboni akuonetsa vidiyo yakuti Kodi Zinangochitika Zokha? kwa mnzake wa kusukulu yemwe amachita chidwi ndi kandege kouluka kokha.