Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 51

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu ndi Chiyembekezo Chathu Ndipo Timakudalirani

Yehova Amakumbukira Misozi Yathu Yonse

Yehova Amakumbukira Misozi Yathu Yonse

“Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa. Kodi misozi yanga sinalembedwe mʼbuku lanu?”​—SAL. 56:8.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona kuti Yehova amadziwa mmene timamvera tikakumana ndi mavuto ndipo amatipatsa zinthu zimene zingatilimbikitse.

1-2. Kodi ndi zinthu ngati ziti zomwe zingachititse kuti tigwetse misozi?

 PA NTHAWI inayake aliyense analirapo. Pakachitika zinazake zosangalatsa, timatha kugwetsa misozi yachisangalalo. Mwina mungagwetse misozi chifukwa cha zinthu zinazake zofunika kapena zapadera zimene zakuchitikirani, monga kubadwa kwa mwana, kukumbukira zinazake zosangalatsa kapenanso mukakumana ndi mnzanu amene munaonana naye kalekale.

2 Koma nthawi zambiri timalira chifukwa chokhumudwa ndi zinazake zimene zatichitikira. Mwachitsanzo, tingalire ngati munthu wina watikhumudwitsa kwambiri. Tingalirenso chifukwa choti tikudwala matenda aakulu kapena munthu amene timamukonda wamwalira. Pa nthawi ngati zimenezi, tingamve ngati mmene anamvera Yeremiya, Yerusalemu atawonongedwa ndi Ababulo. Yeremiya anati: “Maso anga akungotuluka misozi ngati mitsinje. . . . Maso anga akungotuluka misozi ndipo sikusiya.”​—Maliro 3:48, 49.

3. Kodi Yehova amamva bwanji akaona atumiki ake akuvutika? (Yesaya 63:9)

3 Yehova amadziwa kuchuluka kwa nthawi zimene takhala tikulira chifukwa cha mavuto amene timakumana nawo. Baibulo limatiuza kuti amadziwa mtumiki wake aliyense akakumana ndi vuto komanso amamva akamamupempha kuti amuthandize. (Sal. 34:15) Sikuti Yehova amangoona kapena kutimvetsera. Koma mofanana ndi kholo lachikondi, iye amakhudzidwa akamaona ana ake akulira, ndipo amafunitsitsa kuwathandiza.​—Werengani Yesaya 63:9.

4. Kodi tikambirana zitsanzo ziti, nanga zikutiphunzitsa chiyani zokhudza Yehova?

4 M’mawu ake Yehova amatifotokozera mmene anamvera komanso mmene anathandizira atumiki ake atagwetsa misozi. Tingaone zimenezi pa zomwe zinachitikira Hana, Davide ndi Mfumu Hezekiya. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iwo alire? Nanga Yehova anatani atamupempha kuti awathandize? Kodi zitsanzo zawo zingatilimbikitse bwanji tikamagwetsa misozi chifukwa cha chisoni, kusakhulupirika kwa ena kapena tikathedwa nzeru ndi zinazake?

KULIRA CHIFUKWA CHA CHISONI

5. Kodi Hana ankamva bwanji chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo?

5 Hana ankakumana ndi mavuto omwe ankachititsa kuti alire. Limodzi mwa mavutowo linali lakuti anali m’banja la mitala ndipo mkazi mnzake dzina lake Penina ankamunyoza. Kuwonjezera pamenepo Hana anali wosabereka, pomwe Penina anali ndi ana. (1 Sam. 1:1, 2) Ndiye Penina ankanyoza Hana chifukwa choti analibe ana. Kodi inuyo mungamve bwanji zoterezi zitakuchitikirani? Hana zinkamupweteka kwambiri mumtima moti “ankalira ndipo sankadya” komanso “anali wokhumudwa kwambiri.”​—1 Sam. 1:6, 7, 10.

6. Kodi Hana anatani kuti alimbikitsidwe?

6 Kodi n’chiyani chinamuthandiza Hana? Chimodzi mwa zinthu zomwe zinamuthandiza ndi kupita kuchihema komwe anthu ankalambirako Mulungu. Ali kumeneko, mwina chapafupi ndi khomo lolowera m’bwalo la chihema, “anayamba kupemphera kwa Yehova uku akulira kwambiri.” Iye anayamba kupempha Yehova kuti: ‘Muone kuvutika kwa ine kapolo wanu nʼkundikumbukira.’ (1 Sam. 1:10b, 11) Hana anafotokozera Yehova mmene ankamvera m’pemphero. Yehova ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri kuona mwana wake wokondedwayu akulira.

7. Kodi Hana analimbikitsidwa bwanji atafotokozera Yehova mmene ankamvera?

7 Kodi Hana anamva bwanji atapemphera kwa Yehova komanso atalimbikitsidwa ndi Eli yemwe anali mkulu wa ansembe? Baibulo limati: “Ndiyeno anachoka nʼkupita kukadya ndipo nkhope yake sinkaonekanso ya nkhawa.” (1 Sam. 1:17, 18) Ngakhale kuti vuto lakelo silinathe, Hana anayambanso kumva bwino. Iye anatulira Yehova nkhawa zake zonse. Yehova anaona mavuto ake, anamva kulira kwake komanso anamudalitsa pomupatsa mwana.​—1 Sam. 1:19, 20; 2:21.

8-9. Mogwirizana ndi Aheberi 10:24, 25, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizipezeka pamisonkhano? (Onaninso chithunzi.)

8 Zimene tikuphunzirapo. Kodi mukukumana ndi mavuto omwe amakuchititsani kuti nthawi zina muzigwetsa misozi? Mwina muli ndi chisoni chifukwa cha imfa ya wachibale kapena mnzanu. Mwachibadwa, pa nthawi ngati zimenezi timangofuna kukhala patokha. Koma mofanana ndi Hana yemwe analimbikitsidwa atapita kuchihema, inunso mungalimbikitsidwe mutapita kumisonkhano ngakhale pamene simukumva bwino. (Werengani Aheberi 10:24, 25.) Mukamamvetsera malemba olimbikitsa akuwerengedwa pamisonkhano, Yehova angakuthandizeni kuti muziganizira zinthu zabwino osati zoipa zimene zikukuchitikirani. Zimenezi zingatithandize kuti tizimvako bwino ngakhale pamene vuto lathulo silinasinthe.

9 Kumisonkhano timachezanso ndi abale ndi alongo athu omwe ndi achifundo, omwe amatimvetsa komanso amatikonda. Zimenezi zimachititsa kuti tiyambe kumva bwino. (1 Ates. 5:11, 14) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mpainiya wina wapadera yemwe mkazi wake anamwalira. Iye anati: “Ndimalirabe mpaka pano. Nthawi zina ndimakhala pakona n’kumangolira. Koma misonkhano yathu imandilimbikitsa kwambiri. Mawu okoma mtima komanso ndemanga zimene abale ndi alongo amapereka kumisonkhano, zimanditonthoza. Ngakhale kuti ndinali ndi nkhawa ndikafika kumisonkhano ndimayamba kumva bwino.” Kumisonkhano, Yehova angagwiritse ntchito abale ndi alongo anthu kuti atithandize.

Akhristu anzathu akhoza kutilimbikitsa (Onani ndime 8-9)


10. Kodi tingatsanzire bwanji Hana tikakhumudwa kwambiri?

10 Hana analimbikitsidwanso atafotokozera Yehova mmene ankamvera. Inunso ‘mukamutulira Yehova nkhawa zanu zonse,’ musamakayikire kuti akuthandizani. (1 Pet. 5:7) Mlongo wina yemwe mwamuna wake anaphedwa ndi akuba anati: “Ndinkangomva ngati mtima wanga wasweka tizidutswatizidutswa ndipo sindingachirenso. Koma ndikapemphera kwa Atate wanga wachikondi Yehova ndimayamba kumva bwino. Nthawi zina ndinkasowa mawu oti ndinene m’pemphero koma ankandimvetsa. Ndikakhala ndi nkhawa kwambiri ndinkapemphera kuti andipatse mtendere. Ndikatero, nthawi yomweyo mtima ndi maganizo anga zinkakhala m’malo ndipo ndinkakwanitsa kuchita zinthu zina.” Mukamufotokozera Yehova nkhawa zanu, amakhudzidwa akaona misozi yanu ndipo amamvetsa mmene mukumvera. Ngakhale kuti vuto lanulo silingathe, Yehova angakutonthozeni komanso kukuthandizani kuti mukhale ndi mtendere wa mumtima. (Sal. 94:19; Afil. 4:6, 7) Iye adzakudalitsani chifukwa cha kupirira kwanu.​—Aheb. 11:6.

KULIRA CHIFUKWA CHA KUSAKHULUPIRIKA KWA ANTHU ENA

11. Kodi Davide ankamva bwanji chifukwa cha zimene anthu ena ankamuchitira?

11 Pa moyo wake, Davide ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe ankamuchititsa kulira. Anthu ena ankadana naye ndipo ena omwe ankawakhulupirira anamukhumudwitsa. (1 Sam. 19:10, 11; 2 Sam. 15:10-14, 30) Pa nthawi ina iye analemba kuti: “Ndafooka chifukwa cha kuusa moyo kwanga. Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa ndi misozi, ndimalira ndipo misozi imadzaza pabedi panga.” N’chifukwa chiyani Davide ankamva chonchi? Iye anati: “Chifukwa cha anthu onse amene akundizunza.” (Sal. 6:6, 7) Anthu ena ankamuchitira zoipa kwambiri moti misozi yake inkangotsika ngati madzi.

12. Mogwirizana ndi Salimo 56:8, kodi Davide sankakayikira chiyani?

12 Ngakhale kuti Davide anakumana ndi mavuto ambiri, sankakayikira kuti Yehova amamukonda. Iye analemba kuti: “Chifukwa Yehova adzamva mawu a kulira kwanga.” (Sal. 6:8) Pa nthawi ina Davide analankhula mawu ochititsa chidwi opezeka pa Salimo 56:8. (Werengani.) Mawu amenewa amasonyeza bwino mmene Yehova amatikondera. Davide ankamva ngati kuti Yehova akusunga misozi yake m’botolo kapena akuilemba m’buku. Davide sankakayikira kuti Yehova ankaona komanso kukumbukira mavuto ake. Ankakhulupirira kuti Atate wake wachikondi akudziwa zimene akukumana nazo komanso mmene zikumukhudzira.

13. Kodi tizikumbukira chiyani ena akatikhumudwitsa? (Onaninso chithunzi.)

13 Zimene tikuphunzirapo. Kodi mtima ukukupwetekani chifukwa chakuti munthu amene munkamudalira wakukhumudwitsani kapena wachita zinthu zosakhulupirika? Mwinanso mukuvutika maganizo chifukwa banja lanu kapena chibwenzi chanu chatha mosayembekezereka, kapenanso munthu amene mumamukonda wasiya kutumikira Yehova. M’bale wina yemwe mkazi wake anachita chigololo n’kumuthawa, ananena kuti: “Sindinakhulupirire kuti zimenezi zandichitikira. Ndinakhumudwa kwambiri moti ndinkangodziona ngati wachabechabe.” Ngati mukuvutika chifukwa chakuti munthu wina anachita zosakhulupirika kapena anakukhumudwitsani, mungalimbikitsidwe kudziwa kuti Yehova sadzakusiyani. M’bale uja ananena kuti: “Ndazindikira kuti anthu akhoza kutikhumudwitsa koma Yehova ndi Thanthwe lathu. Kaya zinthu zili bwanji iye amatithandiza nthawi zonse. Iye samasiya atumiki ake okhulupirika.” (Sal. 37:28) Tizikumbukiranso kuti chikondi cha Yehova chimaposa cha munthu wina aliyense. N’zoona kuti kusakhulupirika kwa ena kungakhale kopweteka kwambiri, komabe Yehova samasintha mmene amationera. Amationabe kuti ndife a mtengo wapatali. (Aroma 8:38, 39) Choncho apa mfundo ndi yakuti kaya munthu watikhumudwitsa bwanji, Atate wathu wakumwamba amatikondabe.

Buku la Masalimo limatitsimikizira kuti Yehova amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka (Onani ndime 13)


14. Kodi lemba la Salimo 34:18 limatilimbikitsa bwanji?

14 Ngati ena achita zosakhulupirika tingalimbikitsidwenso ndi mawu a Davide apa Salimo 34:18. (Werengani.) Buku lina linanena kuti anthu amene “akudzimvera chisoni mumtima mwawo” angakhalenso anthu amene “amaona kuti m’tsogolomu mulibe chabwino chilichonse.” Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu amene amamva choncho? Mofanana ndi kholo lachikondi lomwe limatonthoza mwana wake akakhala ndi nkhawa, Yehova amakhala nafe pafupi. Iye amatisonyeza chifundo ndipo amakhala wokonzeka kutithandiza tikakhumudwa chifukwa cha kusakhulupirika kwa ena. Iye ndi wokonzeka kulimbikitsa anthu a mtima wosweka komanso amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.​—Yes. 65:17.

KULIRA CHIFUKWA CHA KUTHEDWA NZERU

15. Kodi Hezekiya anakumana ndi zotani zomwe zinamuchititsa kulira kwambiri?

15 Mfumu Hezekiya ya ku Yuda ili ndi zaka 39 inadwala matenda aakulu. Mneneri Yesaya anamuuza uthenga wochokera kwa Yehova wonena kuti afa ndi matenda akewo. (2 Maf. 20:1) Hezekiya ayenera kuti ankaona kuti palibenso chabwino. Iye atamva uthenga wokhumudwitsawu analira kwambiri ndipo anapemphera kwa Yehova mochonderera.​—2 Maf. 20:2, 3.

16. Kodi Yehova anathandiza bwanji Hezekiya?

16 Yehova anakhudzidwa ndi kulira kwa Hezekiya ndipo mokoma mtima anamuuza kuti: “Ndamva pemphero lako ndipo ndaona misozi yako. Ndikuchiritsa.” Kudzera mwa Yesaya, Yehova analonjeza kuti adzatalikitsa moyo wa Hezekiya komanso kupulumutsa Yerusalemu m’manja mwa Asuri.​—2 Maf. 20:4-6.

17. Kodi Yehova amatithandiza bwanji ngati tikudwala matenda aakulu? (Salimo 41:3) (Onaninso chithunzi.)

17 Zimene tikuphunzirapo. Kodi mukuvutika chifukwa cha matenda aakulu omwe mukuona kuti simungachire? Muzipemphera kwa Yehova ngakhale mukugwetsa misozi. Baibulo limatitsimikizira kuti Yehova yemwe ndi “Bambo wachifundo chachikulu ndiponso Mulungu amene amatitonthoza pa vuto lililonse,” adzatitonthoza pa mayesero anthu onse. (2 Akor. 1:3, 4) Masiku ano sitingayembekezere kuti Yehova atichotsera mavuto athu onse koma tingamudalire kuti atithandiza. (Werengani Salimo 41:3.) Iye angagwiritse ntchito mzimu woyera kuti atipatse mphamvu, nzeru komanso mtendere wa mumtima kuti tizipirira. (Miy. 18:14; Afil. 4:13) Amatilimbikitsanso potipatsa chiyembekezo chakuti adzathetsa matenda onse.​—Yes. 33:24.

Yehova adzayankha mapemphero anthu potipatsa mphamvu, nzeru komanso mtendere wa mumtima (Onani ndime 17)


18. Kodi ndi lemba liti lomwe mumaona kuti limakutonthozani mukakumana ndi vuto lalikulu? (Onani bokosi lakuti “ Mawu Olimbikitsa Omwe Angatitonthoze.”)

18 Hezekiya analimbikitsidwa ndi mawu a Yehova. Ifenso tingalimbikitsidwe ndi Mawu a Mulungu. Yehova anasunga m’Baibulo mawu amene amatikhazika mtima pansi tikakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (Aroma 15:4) Mlongo wina wa ku West Africa atapezeka ndi khansa, ankangokhalira kulira. Iye anati: “Lemba lomwe linandilimbikitsa kwambiri ndi la Yesaya 26:3. Ngakhale kuti palibe zimene tingachite pa mayesero amene timakumana nawo, vesili limanditsimikizira kuti Yehova angandithandize kupeza mtendere wa mumtima womwe ungandithandize kudziwa zochita ndikakumana ndi mayeserowo.” Mukakumana ndi vuto lalikulu ndipo mukusowa mtengo wogwira, kodi pali lemba limene limakulimbikitsani?

19. Kodi tikuyembekezera chiyani m’tsogolomu?

19 Tili m’masiku omaliza enieni ndipo tikuyembekezera kuti zinthu zomwe zimatichititsa kuti tizilira ziziwonjezeka. Koma mogwirizana ndi zimene takambirana pa chitsanzo cha Hana, Davide, ndi Mfumu Hezekiya, Yehova amaona misozi yathu ndipo zimamukhudza tikamalira. Yehova amakumbukira misozi yathu. Choncho tikamakumana ndi zinthu zomwe zikuchititsa kuti tizida nkhawa, tizimuuza mmene tikumvera m’pemphero. Tisamakonde kudzipatula kwa abale ndi alongo anthu mumpingo. Ndipo tizipitiriza kupeza mawu olimbikitsa m’Baibulo. Tisamakayikire kuti tikapitiriza kupirira Yehova adzatidalitsa. Tizikhulupiriranso lonjezo losangalatsa lakuti posachedwapa iye adzapukuta misozi yathu yomwe imabwera chifukwa cha chisoni, kusakhulupirika kwa ena komanso chifukwa cha kuthedwa nzeru. (Chiv. 21:4) Pa nthawiyo, tizidzangogwetsa misozi yobwera chifukwa cha chisangalalo.

NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”