Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 48

NYIMBO NA. 97 Mawu a Mulungu Amatithandiza Kukhala ndi Moyo

Yesu Anapereka Chakudya Modabwitsa

Yesu Anapereka Chakudya Modabwitsa

“Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pangʼono.”​—YOH. 6:35.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tikambirana nkhani yopezeka mu Yohane chaputala 6, pomwe Yesu anachulukitsa mkate ndi nsomba n’kudyetsa anthu ambiri. Tionanso zimene tikuphunzirapo.

1. Kodi kale mkate unali wofunika bwanji?

 KALE mkate unali chakudya chomwe anthu ambiri ankadya. (Gen. 14:18; Luka 4:4) Mkate unali wofunika kwambiri moti nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “mkate” ponena za chakudya. (Mat. 6:11; Mac. 20:7) Pa maulendo ena awiri amene Yesu anachita zodabwitsa anagwiritsanso ntchito mkate. (Mat. 16:9, 10) Imodzi mwa nkhanizi imapezeka mu Yohane chaputala 6. Tiyeni tikambirane nkhaniyi n’kuona zimene tikuphunzirapo masiku ano.

2. Kodi ndi pa nthawi iti pomwe anthu ambiri ankafunikira chakudya?

2 Atumwi atamaliza kulalikira, anakwera boti limodzi ndi Yesu n’kupita tsidya lina la Nyanja ya Galileya kuti akapume. (Maliko 6:7, 30-32; Luka 9:10) Iwo anapita kudera lina lopanda anthu ku Betisaida. Koma pasanapite nthawi yaitali gulu la anthu linafika. Yesu sanawanyalanyaze. M’malomwake iye anayamba kuwaphunzitsa zokhudza Ufumu komanso kuchiritsa odwala. Kutayamba kuda, iwo anayamba kuganizira mmene anthuwo angapezere chakudya. N’kutheka kuti ena anali ndi chakudya chochepa koma ambiri ankafunika kupita kumidzi kukagula chakudya. (Mat. 14:15; Yoh. 6:4, 5) Kodi Yesu anatani?

ANAPANGA ZODABWITSA KUTI ANTHU APEZE CHAKUDYA

3. Kodi Yesu anati chiyani ataona kuti anthu ambiri akufunika chakudya? (Onaninso chapachikuto.)

3 Yesu anauza atumwi ake kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.” (Mat. 14:16) Zimenezi zinali zovuta chifukwa panali amuna pafupifupi 5,000. Tikaphatikiza akazi ndi ana, ndiye kuti payenera kuti panali anthu pafupifupi 15,000 oti awadyetse. (Mat. 14:21) Andireya anati: “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda 5 ya mkate wa balere ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire chigulu cha anthu chonsechi?” (Yoh. 6:9) Mikate ya balere ndi imene anthu ambiri ankadya ndipo nsombazo ziyenera kuti zinali zouma komanso zothira mchere. Koma chakudya chimene mnyamatayo anali nacho chinali chosakwanira kwa gulu lonselo.

Yesu anaphunzitsa anthu komanso kuwapatsa zimene ankafunikira (Onani ndime 3)


4. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya pa Yohane 6:11-13? (Onaninso zithunzi.)

4 Pofuna kuthandiza anthuwo, Yesu anawauza kuti akhale pa udzu m’magulu. (Maliko 6:39, 40; werengani Yohane 6:11-13.) Kenako timawerenga kuti Yesu anapemphera kwa Atate wake pothokoza chifukwa cha chakudyacho. Zinali zomveka kuti Yesu athokoze Mulungu chifukwa ndi amene amapereka chakudya. Apatu Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwa tonsefe kuti tizipemphera kaye tisanayambe kudya, kaya tili pagulu kapena kwatokha. Kenako Yesu anapereka chakudyacho kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Iwo anadya n’kukhuta mpaka chakudya china chinatsala ndipo Yesu ananena kuti chisatayidwe. Iye analamula kuti zotsalazo azisonkhanitse mwina kuti zidzagwiritsidwe ntchito pa nthawi ina. Apa Yesu anatipatsanso chitsanzo kuti tisamawononge zinthu. Ngati ndinu makolo, mungachite bwino kuphunzira nkhaniyi ndi ana anu n’kuona zimene tikuphunzirapo pa nkhani ya pemphero, kuchereza komanso kupatsa.

Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimatsanzira Yesu popemphera ndisanayambe kudya?’ (Onani ndime 4)


5. Kodi anthu anatani Yesu atachita zodabwitsa, nanga iye anachita chiyani?

5 Anthu ankachita chidwi ndi mmene Yesu ankaphunzitsira komanso mmene ankachitira zodabwitsa. Mose analonjeza kuti Mulungu adzapereka mneneri wapadera ndipo n’kutheka kuti anthu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Yesu ndi mneneri ameneyo?’ (Deut. 18:15-18) Anthu ayenera kuti ankaganiza kuti Yesu angakhale mtsogoleri wabwino moti angathe kupereka chakudya kwa mtundu wonsewo. Choncho anthu ambiri ankafuna “kubwera kudzamugwira kuti amuveke ufumu.” (Yoh. 6:14, 15) Yesu akanalola zimenezi akanalowerera ndale za Ayuda omwe ankalamuliridwa ndi Aroma. Choncho iye sanalole. Baibulo limanena kuti iye ‘anachoka nʼkupita kuphiri.’ Iye sanayambe kulowerera ndale ngakhale kuti anthu ena ankamukakamiza. Apatu iye anapereka chitsanzo chabwino kwa ifeyo.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufuna kutsanzira Yesu? (Onaninso chithunzi.)

6 N’zoonekeratu kuti ena sangatiuze kuti tichulukitse chakudya kapena kuchiritsa anthu modabwitsa. Sangatiuzenso kuti tikhale mfumu kapena wolamulira. Komabe angatilimbikitse kuti tichite nawo zandale povota kapena kuthandiza winawake yemwe akuona kuti angasinthe zinthu. Koma Yesu ndi chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye anakana kulowerera ndale ndipo pa nthawi ina ananena kuti, “Ufumu wanga si wamʼdzikoli.” (Yoh. 17:14; 18:36) Masiku ano, Akhristu ayenera kutsanzira Yesu. Mofanana ndi Yesu, timakhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu, timauza ena za Ufumuwu ndipo timaupempherera. (Mat. 6:10) Kodi tikuphunziranso chiyani pa zimene Yesu anachita popereka chakudya modabwitsa?

Yesu anapereka chitsanzo posalowerera ndale za Ayuda kapena Aroma (Onani ndime 6)


“TANTHAUZO LA MITANDA YA MKATE”

7. Kodi Yesu anachita chiyani, nanga atumwi anatani ataona zimenezo? (Yohane 6:16-20)

7 Yesu atadyetsa gulu la anthu, anauza atumwi ake kuti abwerere ku Kaperenao pa boti ndipo iye anapita kuphiri pofuna kupewa gulu la anthu omwe amafuna kumuveka ufumu. (Werengani Yohane 6:16-20.) Atumwiwo ali panyanja mphepo inayamba ndipo panali mafunde aakulu. Kenako Yesu anabwera akuyenda pamadzi. Ndipo anaitana Petulo kuti nayenso ayende pamadzipo. (Mat. 14:22-31) Yesu atangofika m’botilo mphepo ija inasiya. Zitatero ophunzirawo anadabwa kwambiri ndipo ananena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” a (Mat. 14:33) N’zochititsa chidwi kuti iwo ananena zimenezi pambuyo poti Yesu wayenda pamadzi ngakhale kuti anali atachita chodabwitsa podyetsa gulu la anthu lija. Maliko anawonjezeranso mfundo yakuti: “[Atumwiwo] anadabwa kwambiri. Chifukwa choti sanamvetse tanthauzo la mitanda ya mkate ija, iwo ankavutikabe kuti amvetse zinthu zonse.” (Maliko 6:50-52) Iwo anali asanazindikirebe kuti Yehova anali atapatsa Yesu mphamvu zochitira zodabwitsa zambiri. Pambuyo pake Yesu anafotokozanso zokhudza mkate ndipo tiyeni tione zimene tikuphunzirapo.

8-9. N’chifukwa chiyani gulu la anthu linkafunafuna Yesu? (Yohane 6:26, 27)

8 Gulu la anthu limene Yesu analidyetsa lija linkangofuna kupeza chakudya. Kodi iwo anachita zotani? Ataona kuti Yesu ndi atumwi ake achoka, anakwera maboti ochokera ku Tiberiyo ndipo anapita ku Kaperenao komwe Yesu anali. (Yoh. 6:22-24) Kodi iwo anachita zimenezi n’cholinga choti akamve zambiri zokhudza Ufumu? Ayi. Iwo ankangoganizira za chakudya chomwe anawapatsa. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

9 Taonani zimene zinachitika iwo atamupeza Yesu ku Kaperenao. Yesu anawauza mosapita m’mbali kuti iwo anabwera chifukwa chakuti ankangofuna chakudya. Iye anawauza kuti ngakhale kuti ‘anadya mikate nʼkukhuta,’ koma chimenecho chinali “chakudya chimene chimawonongeka.” Choncho anawalimbikitsa kuti ayenera kuyesetsa kupeza “chakudya chomwe chimabweretsa moyo wosatha.” (Werengani Yohane 6:26, 27.) Yesu ananena kuti Atate wake amapereka chakudya chimenecho. Mfundo yoti chakudya chingathandize munthu kupeza moyo wosatha iyenera kuti inali yodabwitsa kwa anthuwo. Ndi chakudya chamtundu wanji chomwe chikanachita zimenezi, nanga anthuwo akanatani kuti achipeze?

10. Kodi ndi zinthu ziti ‘zimene Mulungu amafuna kuti anthu azichita’ kuti adzapeze moyo wosatha?

10 N’kutheka kuti Ayudawo ankaganiza kuti ayenera kuchita zinazake kuti alandire chakudyacho. Mwina iwo ankaganiza kuti akuyenera kumachita zimene Chilamulo cha Mose chimanena. Koma Yesu anawauza kuti: “Zimene Mulungu akufuna kuti muzichita ndi zakuti muzisonyeza chikhulupiriro mwa amene anamutuma.” (Yoh. 6:28, 29) Kukhulupirira yemwe Mulungu anamutuma n’kofunika kuti munthu “akhale ndi moyo wosatha.” Ndipotu Yesu anali atanenapo zimenezi m’mbuyomo. (Yoh. 3:16-18, 36) Komanso pambuyo pake anafotokozanso zambiri pa nkhani ya mmene tingapezere moyo wosatha.​—Yoh. 17:3.

11. Kodi Ayuda anasonyeza bwanji kuti ankangofuna kupeza chakudya? (Salimo 78:24, 25)

11 Ayudawo sanavomereze mfundo yatsopano yomwe Yesu anaphunzitsa yokhudza ‘zimene Mulungu ankafuna kuti iwo azichita.’ Iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo muchita chizindikiro chotani kuti ife tichione nʼkukukhulupirirani?” (Yoh. 6:30) Ayudawo anafotokoza kuti m’nthawi ya Mose makolo awo analandira mana chomwe chinali ngati chakudya chawo cha tsiku ndi tsiku. (Neh. 9:15; werengani Salimo 78:24, 25.) N’zoonekeratu kuti iwo ankangoganizira zopeza chakudya basi. Sanafunse Yesu kuti awafotokozere zomwe ankatanthauza pomwe anatchula za “chakudya chenicheni chochokera kumwamba” ngati mana, chomwe chikanawathandiza kukhala ndi moyo. (Yoh. 6:32) Iwo ankaganizira kwambiri zimene angapeze moti ananyalanyaza choonadi chimene Yesu ankafuna kuwaphunzitsa. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi?

ZIMENE TIYENERA KUONA KUTI N’ZOFUNIKA KWAMBIRI

12. Kodi Yesu anasonyeza kuti chofunika kwambiri ndi chiyani?

12 Pali phunziro lofunika kwambiri lomwe tingapeze mu Yohane chaputala 6. Chofunika kwambiri ndi kuganizira zimene zingatithandize kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kumbukirani kuti Yesu anatchulanso mfundo imeneyi pamene Satana ankamuyesa. (Mat. 4:3, 4) Ndipo pa ulaliki wa paphiri iye anatsindikira kufunika kozindikira zosowa zathu zauzimu. (Mat. 5:3) Choncho tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene ndimachita pa moyo wanga zimasonyeza kuti ndimaona kuti chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu osati kupeza zimene ndimalakalaka?’

13. (a) N’chifukwa chiyani si zolakwika kusangalala ndi chakudya? (b) Kodi Paulo anatichenjeza za chiyani? (1 Akorinto 10:6, 7, 11)

13 Si zolakwika kupempherera zinthu zimene timafunikira komanso kusangalala nazo tikazipeza. (Luka 11:3) Baibulo limanena kuti ndi bwino kuti ‘munthu adye, amwe ndi kusangalala chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama’ popeza izi “nʼzochokera mʼdzanja la Mulungu woona.” (Mlal. 2:24; 8:15; Yak. 1:17) Komabe tiyenera kusamala kuti tisamaone zinthu zimenezi ngati zofunika kwambiri pa moyo wathu. Paulo anafotokozanso bwino mfundo imeneyi pamene analembera Akhristu a Chiyuda. Iye anafotokoza zimene zinachitikira Aisiraeli kuphatikizapo zomwe zinachitika pafupi ndi phiri la Sinai. Anachenjeza Akhristu kuti ‘asamalakelake zinthu zoipa ngati mmene [Aisiraeli] anachitira.’ (Werengani 1 Akorinto 10:6, 7, 11.) Aisiraeli analola kuti dyera lawo lolakalaka chakudya lichititse zinthu zimene Yehova anawapatsa modabwitsa kukhala “zinthu zoipa.” (Num. 11:4-6, 31-34) Komanso pamene ankalambira mwana wa ng’ombe iwo anasonyeza kuti chomwe chinali chofunika kwambiri kwa iwo ndi kudya, kumwa komanso kusangalala. (Eks. 32:4-6) Paulo anatchula zimenezi pomwe ankachenjeza Aisiraeli omwe ankayembekezera kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E. Ifenso tikukhala m’nthawi ya mapeto, choncho tingachite bwino kuganizira malangizo a Paulowa.

14. Pa nkhani ya chakudya, kodi tikuyembekezera zotani m’dziko la tsopano?

14 Pamene Yesu anatiuza kuti tizipempherera “chakudya chimene tikufunikira lero,” anatiuzanso kuti tizipemphera kuti zofuna za Mulungu “zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.” (Mat. 6:9-11) Kodi n’chiyani chimabwera m’maganizo mwanu mukamva zimenezi? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amafuna kuti padziko lapansi padzakhale chakudya chabwino. Lemba la Yesaya 25:6-8 limasonyeza kuti mu Ufumu wa Mulungu, padzikoli padzakhala chakudya chochuluka komanso chabwino. Lemba la Salimo 72:16 limanena kuti: “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.” Kodi mumadziyerekezera mukugwiritsa ntchito tiriguyu kuphika chakudya chimene mumachikonda kapena kuyesa kuphika zakudya zina zomwe simunaphikepo? Kuwonjezera pamenepo, mungadzalime minda yanuyanu ya mpesa n’kumadya zipatso zake. (Yes. 65:21, 22) Ndipo aliyense padzikoli adzakhala ndi zinthu ngati zimenezi.

15. Kodi anthu amene adzaukitsidwe adzaphunzitsidwa chiyani? (Yohane 6:35)

15 Werengani Yohane 6:35. Taganizirani za anthu amene anadya mkate ndi nsomba zimene Yesu anawapatsa. Ena mwa iwo mudzakumana nawo akadzaukitsidwa. Ngakhale kuti m’mbuyomo sanasonyeze chikhulupiriro, iwo akhoza kudzaukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29) Anthu amenewa adzadziwa zimene Yesu ankatanthauza pomwe anati: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo. Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pangʼono.” Iwo adzafunika kukhulupirira kuti Yesu anapereka moyo wake monga dipo chifukwa cha iwo. Pa nthawiyo padzakhalanso ntchito yophunzitsa anthu amene adzaukitsidwe komanso ana amene adzabadwe. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito yophunzitsayi. Kuthandiza anthu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova kudzakhala kosangalatsa kwambiri kuposa kudya chakudya chabwino.

16. Kodi tidzaphunzira chiyani munkhani yotsatira?

16 Munkhaniyi takambirana mfundo zina za mu Yohane chaputala 6. Koma pali zambiri zokhuza “moyo wosatha” zimene Yesu anaphunzitsa. Ayuda ankafunika kumvetsera mwatcheru ndipo ifenso tiyenera kuchita zimenezo. Munkhani yotsatira, tipitiriza kukambirana mfundo za mu Yohane chaputala 6.

NYIMBO NA. 20 Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yosangalatsayi, onani buku lakuti, Yesu​—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo patsamba 131, komanso lakuti, Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo patsamba 185.