Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwawerenga mosamala magazini a chaka chino a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:
Kodi Yehova wapereka bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani ya mmene tiyenera kumachitira zinthu ndi akazi?
Yehova amachita nawo zinthu mopanda tsankho ndipo sakonda kwambiri amuna kuposa akazi. Amamvetsera akazi, amaganizira mmene akumvera komanso zimene zikuwadetsa nkhawa. Iye amawadalira n’kuwapatsa udindo wogwira ntchito yake.—w24.01, pp. 15-16.
Kodi tingatsatire bwanji mfundo ya pa Aefeso 5:7, yakuti: “Musamachite zimene iwo amachita”?
Mtumwi Paulo anatichenjeza kuti tisamawirizane ndi anthu amene angachititse kuti tisamamvere mfundo za Yehova. Anthu amene timagwirizana nawo si amene timacheza nawo pamasom’pamaso okha koma amenenso timacheza nawo pa intaneti.—w24.03, pp. 22-23.
Kodi tiyenera kupewa nkhani zabodza ziti?
Tiyenera kupewa nkhani zabodza zochokera kwa anzathu zimene sanazifufuze, zochokera m’mauthenga amene anthu ena angatitumizire komanso zochokera kwa anthu ampatuko amene amayesa kubisa zolinga zawo.—w24.04, p. 12.
Kodi ndi zinthu ziti zimene sitikudziwa nanga ndi zinthu ziti zimene tikudziwa pa nkhani ya mmene Yehova adzaweruzire Mfumu Solomo, anthu amene anafa ku Sodomu ndi Gomora komanso amene anafa pachigumula?
Sitikudziwa ngati Yehova anawaweruza kuti afe ndipo asadzaukitsidwe. Koma tikudziwa kuti iye amadziwa zonse ndipo ndi wachifundo chachikulu.—w24.05, tsa. 3-4.
Kodi mfundo yakuti Mulungu ndi “Thanthwe” imatitsimikizira za chiyani? (Deut. 32:4)
Yehova ndi malo othawirako otetezeka. Iye ndi wodalirika ndipo nthawi zonse amakwaniritsa malonjezo ake. Ndipo iye sasintha makhalidwe ake komanso zolinga zake.—w24.06, tsa. 26-28.
N’chiyani chingakuthandizeni kuti muzolowere mpingo watsopano?
Muzidalira Yehova, chifukwa angakuthandizeni ngati mmene anathandizira atumiki ake m’mbuyomu. Muzipewa kuyerekezera ndi mpingo wanu wakale. Muzichita nawo zinthu zambiri komanso muzipeza anzanu atsopano.—w24.07, tsa. 26-28.
Kodi tikuphunzira chiyani pa mafanizo opezeka muchaputala 25 cha Mateyu?
Fanizo la nkhosa ndi mbuzi limatilimbikitsa kukhala okhulupirika. Fanizo la anamwali 10 limatilimbikitsa kukhala maso komanso okonzeka. Ndipo fanizo la matalente limatilimbikitsa kukhala akhama.—w24.09, tsa. 20-24.
Kodi khonde la kachisi wa Solomo linali lalitali bwanji?
M’mipukuti ina, mawu a pa 2 Mbiri 3:4, amanena za “mikono 120,” zomwe zikutanthauza kuti linali lalitali mamita 53 kupita m’mwamba. Koma m’zolemba zina zodalirika lembali limati “mikono 20,” yomwe ndi mamita 9 kupita m’mwamba. Nambala yachiwiriyi ikuoneka kuti ingakhale yogwirizana ndi mmene makoma a kachisiyu analili.—w24.10, tsa. 31.
Kodi mawu akuti mtumiki wothandiza akhale ‘mwamuna wa mkazi mmodzi’ amatanthauza chiyani? (1 Tim. 3:12)
Ayenera kukwatira mkazi mmodzi yekha ndipo sayenera kuchita chiwerewere. Komanso sayenera kukopana ndi akazi ena.—w24.11, tsa. 19.
N’chifukwa chiyani sitinganene kuti lemba la Yohane 6:53 limasonyeza zimene ziyenera kuchitika pamwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye?
Pa Yohane 6:53 Yesu ananena kuti anthu ayenera kudya thupi lake ndi kumwa magazi ake. Iye ananena mawu amenewa ku Galileya mu 32 C.E. ndipo ankauza Ayuda amene ankafunika kumukhulupirira. Koma mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye anauyambitsa patapita chaka chimodzi ku Yerusalemu. Apa Yesu ankalankhula ndi anthu amene akalamulire nawo kumwamba.—w24.12, tsa. 10-11.