Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi “angelo ochita kusankhidwa” otchulidwa pa 1 Timoteyo 5:21 ndi ndani?

Mtumwi Paulo analembera kalata Timoteyo, yemwe anali mkulu mnzake, ndipo anati: “Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu ndiponso angelo ochita kusankhidwa, kuti uzitsatira malangizo amenewa popanda tsankho kapena kukondera.”​—1 Tim. 5:21.

Choyamba, tiyeni tikambirane za angelo omwe sali m’gulu angelo ochita kusankhidwali. N’zoonekeratu kuti iwo sangakhale a 144,000. Pamene Paulo ankalembera Timoteyo kalatayi, Akhristu odzozedwa anali asanayambe kuukitsidwira kumwamba. Pa nthawiyo, atumwi komanso odzozedwa ena anali asanakhale zolengedwa zauzimu choncho iwo sangakhale “angelo ochita kusankhidwa” amenewa.​—1 Akor. 15:50-54; 1 Ates. 4:13-17; 1 Yoh. 3:2.

Komanso ‘angelo ochita kusankhidwawa’ sangakhale angelo omwe sanamvere Mulungu pa nthawi yachigumula. Angelo amenewa anakhala kumbali ya Satana ndipo anakhala ziwanda komanso adani a Yesu. (Gen. 6:2; Luka 8:30, 31; 2 Pet. 2:4) M’tsogolomu, iwo adzaikidwa m’ndende kwa zaka 1,000 ndipo pambuyo pake adzawonongedwa pamodzi ndi Mdyerekezi.​—Yuda 6; Chiv. 20:1-3, 10.

“Angelo ochita kusankhidwa,” omwe Paulo anatchula, ayenera kuti ndi angelo okhulupirika amene ali kumbali ya “Mulungu ndi Khristu Yesu.”

Kumwamba kuli angelo masauzande ambiri omwe ndi okhulupirika. (Aheb. 12:22, 23) Koma sitiyenera kuganiza kuti iwo amagwira ntchito zofanana pa nthawi imodzi. (Chiv. 14:17, 18) Kumbukirani kuti pa nthawi ina mngelo mmodzi anapatsidwa ntchito yowononga asilikali a Asuri okwana 185,000. (2 Maf. 19:35) Angelo ambiri anapatsidwa ntchito ‘yodzachotsa mu Ufumu [wa Yesu] zinthu zonse zopunthwitsa ndiponso anthu osamvera malamulo.’ (Mat. 13:39-41) Angelo enanso adzagwira ntchito ‘yosonkhanitsa osankhidwa ake’ kumwamba. (Mat. 24:31) Ndipo ena analamulidwa kuti ‘azititeteza m’njira zathu zonse.’​—Sal. 91:11; Mat. 18:10; Yerekezerani ndi Mateyu 4:11; Luka 22:43.

“Angelo ochita kusankhidwa” otchulidwa pa 1 Timoteyo 5:21 ayenera kuti ndi angelo amene anapatsidwa ntchito zapadera zothandiza mipingo. M’chaputalachi, Paulo anapereka malangizo anzeru omwe angathandize akulu kuti azigwira bwino ntchito yawo, zomwe zingachititse kuti anthu mumpingo aziwalemekeza. Akulu ayenera kugwira ntchito zawo ‘mopanda tsankho kapena kukondera’ ndipo sayenera kusankha zinthu kapena kuweruza mopupuluma. Chifukwa chachikulu chomwe chiyenera kuchititsa akulu kutsatira malangizo ouziridwa a Paulo ndi chakuti iwo amagwira ntchito za mumpingo “pamaso pa Mulungu ndi Khristu ndiponso angelo ochita kusankhidwa.” Choncho n’zoonekeratu kuti angelo ena amagwira ntchito zothandiza mpingo monga kuteteza atumiki a Mulungu, kuwathandiza pa ntchito yolalikira komanso kuuza Yehova mmene zinthu zikuyendera.​—Mat. 18:10; Chiv. 14:6.