Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova

Abulahamu Anali “Bwenzi” la Yehova

“Iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga, iwe Yakobo amene ndakusankha, mbewu ya bwenzi langa Abulahamu.”—YES. 41:8.

NYIMBO: 91, 22

1, 2. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti anthu angathe kukhala mabwenzi a Mulungu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

MUNTHU aliyense amafuna kukondedwa pa moyo wake wonse. Ndipo sikuti timangofunikira chikondi chimene chimakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi. Timafuna kukondana ndiponso kugwirizana ndi anthu osiyanasiyana. Koma anthufe timafunika kukondedwa ndi Yehova kuposa wina aliyense. Anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova popeza ndi Wamphamvuyonse, wosaoneka komanso amakhala kumwamba. Koma Akhristufe sitikhala ndi maganizo amenewa.

2 Baibulo limasonyeza kuti anthu ena anali mabwenzi a Mulungu, ndipo mmodzi mwa anthuwa anali Abulahamu. (Werengani Yakobo 2:23.) Tingachite bwino kuganizira zimene anthuwa anachita kuti akhale mabwenzi a Mulungu. Tikutero chifukwa kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri. Koma kodi zinatheka bwanji kuti Abulahamu akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova? Nkhani inagona pa chikhulupiriro. Ndipotu Baibulo limati Abulahamu anali ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’ (Aroma 4:11) M’nkhaniyi tikambirana mmene chikhulupiriro chinathandizira Abulahamu kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Ndiyeno tonsefe tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatsanzire bwanji Abulahamu polimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova?’

KODI ZINATHEKA BWANJI KUTI ABULAHAMU AKHALE BWENZI LA YEHOVA?

3, 4. (a) Kodi Mulungu anauza Abulahamu kuti achite zotani? (b) N’chifukwa chiyani Abulahamu anali wokonzeka kupereka nsembe Isaki?

3 Pa nthawi ina, mwina Abulahamu ali ndi zaka 125 anali pa ulendo wodutsa m’njira ya m’mapiri. [1] Pa ulendowu Abulahamu anali ndi mwana wake Isaki yemwe anali ndi zaka 25. Isaki ananyamula nkhuni ndipo Abulahamu ananyamula mpeni komanso zoyatsira moto. Ulendowu unali wovuta kwambiri kwa Abulahamu. Koma osati chifukwa choti anali wokalamba, popeza pa nthawiyi anali adakali ndi mphamvu. Unali wovuta chifukwa Yehova anali atamuuza kuti akapereke nsembe mwana wakeyo.—Gen. 22:1-8.

4 Zimene Yehova anauza Abulahamu kuti achitezi, zikanasonyeza ngati Abulahamu analidi ndi chikhulupiriro cholimba kapena ayi. Anthu ena amanena kuti Mulungu anasonyeza nkhanza pouza Abulahamu kuti apereke mwana wake nsembe. Amatinso Abulahamu ankangomvera Mulungu n’chimbulimbuli osadziwa zimene akuchita. Koma anthuwa amanena zimenezi chifukwa alibe chikhulupiriro komanso sadziwa kuti chikhulupiriro chenicheni ndi chiyani. (1 Akor. 2:14-16) Si zoona kuti Abulahamu ankangomvera Mulungu n’chimbulimbuli. M’malomwake ankamvera chifukwa anali ndi chikhulupiriro cholimba. Ankadziwa kuti Atate wake wakumwamba sangamupemphe kuti achite zinthu zimene zingapangitse kuti avutike mpaka kalekale. Abulahamu ankadziwa kuti akamvera Yehova, Yehovayo adzamudalitsa komanso kudalitsa mwana wake. Koma kodi zinatheka bwanji kuti iye akhale ndi chikhulupiriro chimenechi? Ndi chifukwa cha zimene ankadziwa komanso zomwe anakumana nazo pa moyo wake.

5. Kodi n’kutheka kuti Abulahamu anaphunzira bwanji za Yehova, nanga zimene anaphunzirazo zinamuthandiza bwanji?

5 Zimene ankadziwa. Abulahamu anakulira mumzinda wa Akasidi wa Uri, womwe anthu ake ankalambira mafano. Nawonso bambo ake ankalambira mafano. (Yos. 24:2) Komabe Abulahamu anaphunzira za Yehova. Ndiye kodi anaphunzira bwanji? Baibulo silinena, komabe limasonyeza kuti Abulahamu anali mu m’badwo wa 9 kuchokera pa Semu yemwe anali mwana Nowa. Semu ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo anakhala ndi moyo mpaka pamene Abulahamu anali ndi zaka 150. Semu ayenera kuti anaphunzitsa anthu a m’banja lake za Yehova. Sitikudziwa ngati Abulahamu anaphunzira za Yehova kuchokera kwa Semu. Komabe chimene tikudziwa n’chakuti, Abulahamu anamva za Yehova ndipo anayamba kumukonda kwambiri komanso kumukhulupirira.

6, 7. Kodi zimene zinachitika pa moyo wa Abulahamu zinamuthandiza bwanji kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba?

6 Zimene anakumana nazo pa moyo wake. Kodi ndi zinthu ziti zimene zinathandiza Abulahamu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba? Zinthu zimene munthu wadziwa zikamukhudza mtima, zimamupangitsa kuti achite zinazake. Choncho zimene Abulahamu anaphunzira zokhudza Mulungu zinachititsa kuti ayambe kukonda ndiponso kulemekeza kwambiri “Yehova Mulungu Wam’mwambamwamba, amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Gen. 14:22) Apa ndiye kuti Abulahamu anayamba “kuopa Mulungu” ndipo khalidweli linamuthandiza kuti akhale naye pa ubwenzi wolimba ndiponso kuti azimumvera.—Aheb. 5:7; Sal. 25:14.

7 Mulungu anauza Abulahamu ndi Sara kuti achoke mumzinda wa Uri n’kupita kudziko lina. Kumeneko anayenera kumakhala m’mahema moyo wawo wonse. Koma Abulahamu anamvera ndipo izi zinachititsa kuti Mulungu azimuteteza komanso kumudalitsa. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Abulahamu anachita mantha kuti mwina aphedwa ndi kulandidwa mkazi wake chifukwa anali wokongola kwambiri. Komabe Abulahamu sanalole kuti maganizowa amusokoneze n’kusiya kumvera Yehova. Choncho kangapo konse, Yehova anateteza Abulahamu ndi Sara mozizwitsa kuti izi zisachitike. (Gen. 12:10-20; 20:2-7, 10-12, 17, 18) Zimenezi zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha Abulahamu.

8. Kodi n’chiyani chingatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova?

8 Zimene tingaphunzire zokhudza Mulungu komanso zomwe tingakumane nazo pa moyo, zingatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Abulahamu ankangodziwa zinthu zochepa chabe zimene zili m’Baibulo, koma ifeyo tili ndi Baibulo lonse. (Dan. 12:4; Aroma 11:33) M’Mawu a Mulungu muli zinthu zambiri zimene zingatithandize kuti timudziwe bwino Mulungu n’kuyamba kumulemekeza komanso kumukonda kwambiri. Zikatere timayamba kumumvera ndipo kenako timaona kuti zinthu zikutiyendera bwino. Timaonanso kuti amatidalitsa, kutipatsa mphamvu ndiponso malangizo ake amatiteteza. Timazindikira kuti tikamamutumikira ndi mtima wonse timakhala osangalala komanso ndi mtendere wamumtima. (Sal. 34:8; Miy. 10:22) Tikamaphunzirabe za Mulungu komanso kuona zimene akutichitira pa moyo wathu, timayamba kumukhulupirira kwambiri ndipo ubwenzi wathu ndi iye umalimba.

KODI ABULAHAMU ANATANI KUTI UBWENZI WAKE NDI YEHOVA UPITIRIRE?

9, 10. (a) Kodi pamafunika chiyani kuti ubwenzi ukhale wolimba? (b) Kodi Abulahamu anachita chiyani kuti ubwenzi wake ndi Yehova upitirire?

9 Kukhala ndi mnzanu wapamtima ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. (Werengani Miyambo 17:17.) Komabe ubwenzi suli ngati chinthu chimene ungagule, kuchigwiritsa ntchito kamodzi kenako n’kuchisiya penapake mpaka kuchita fumbi. M’malomwake ubwenzi uli ngati mbewu imene imafunika kuithirira ndi kuisamalira kuti izikula bwino. Abulahamu ankachita zinthu zomwe zinkathandiza kuti ubwenzi wake ndi Yehova upitirire. Kodi ankachita chiyani?

10 Abulahamu sankaona kuti zinthu zabwino zimene anali atachita kale zinali zokwanira kuti ubwenzi wake ndi Yehova upitirire. Pamene iye ndi banja lake ankapita ku Kanani, ankadalirabe Yehova kuti azimutsogolera ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono. Kutatsala chaka chimodzi kuti Isaki abadwe ndipo Abulahamu ali ndi zaka 99, Yehova anamuuza kuti amuna onse a m’banja lake adulidwe. Kodi ananyinyirika n’kuyamba kupeza njira zoti asachite zimene Yehova anamuuzazi? Ayi, koma anakhulupirira Mulungu ndipo anamvera “tsiku lomwelo.”—Gen. 17:10-14, 23.

11. N’chifukwa chiyani Abulahamu anada nkhawa za Sodomu ndi Gomora, ndipo Yehova anamuthandiza bwanji?

11 Abulahamu ankamvera Yehova ngakhale pa zinthu zazing’ono ndipo izi zinathandiza kuti ubwenzi wawo ukhale wolimba. Ankamasuka kuuza Yehova za mumtima mwake moti ankatha kumufunsa mafunso omwe ankamuthetsa nzeru. Mwachitsanzo, atamva kuti Mulungu awononga mzinda wa Sodomu ndi wa Gomora anada nkhawa kuti mwina anthu abwino akhoza kuwonongedwanso. N’kutheka kuti ankadera nkhawa Loti yemwe ankakhala ku Sodomu. Choncho Abulahamu anafunsa Mulungu mafunso okhudza zimenezi. Koma anafunsa modzichepetsa kwambiri komanso mosonyeza kuti ankakhulupirira zoti Mulungu ndi “Woweruza wa dziko lonse lapansi.” Yehova anayankha Abulahamu moleza mtima n’kumuthandiza kuona kuti iye ndi Mulungu wachifundo, amaona mumtima ndipo poweruza sangawononge anthu olungama.—Gen. 18:22-33.

12, 13. (a) Kodi zimene Abulahamu ankadziwa ndiponso zomwe anakumana nazo zinamuthandiza bwanji? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Abulahamu ankakhulupirira kwambiri Yehova?

12 Kunena zoona zimene Abulahamu ankadziwa zokhudza Yehova ndiponso zimene anakumana nazo pa moyo wake zinamuthandizadi kwambiri kuti akhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehovayo. Choncho pamene Yehova anamupempha kuti apereke mwana wake Isaki nsembe, Abulahamu sanavutike kumvera chifukwa ankamudziwa bwino Yehova. Tsopano tiyeni tipitirize kukambirana za ulendo wa Abulahamu pamene ankadutsa njira ya m’mapiri a ku Moriya. Kodi iye ankaganiza kuti Yehova wasintha moti wayamba nkhanza ndipo alibenso chifundo? Ayi, Abulahamu sanaganize zimenezi m’pang’ono pomwe. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

13 Abulahamu anauza antchito ake amene anayenda nawo kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambira, tikupezani.” (Gen. 22:5) Kodi apa Abulahamu ankatanthauza chiyani? Kodi ankanamiza antchito akewo kuti Isaki abweranso, pomwe ankadziwa kuti akukamupereka nsembe? Ayi, Baibulo limatithandiza kudziwa zimene Abulahamu ankaganiza. (Werengani Aheberi 11:19.) Iye “anadziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa [Isaki] kwa akufa.” Izi zikusonyeza kuti Abulahamu ankakhulupirira kuti akufa adzaukitsidwa. Paja Yehova anachititsa kuti iyeyo ndi Sara abereke mwana ngakhale kuti anali atakalamba kwambiri. (Aheb. 11:11, 12, 18) Abulahamu ankadziwa kuti palibe zimene Yehova sangakwanitse kuchita. Choncho sankakayikira kuti ngakhale atapereka mwana wakeyo nsembe, Yehova amuukitsa kuti akwaniritse zonse zimene analonjeza. N’chifukwa chake Abulahamu anatchedwa ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’

14. (a) Kodi inuyo mumakumana ndi mavuto ati potumikira Yehova? (b) Kodi chitsanzo cha Abulahamu chingakuthandizeni bwanji?

14 N’zoona kuti Mulungu satipempha kuchita zinthu ngati zimenezi masiku ano. Komabe amafuna kuti tizimumvera ngakhale pamene tikuona kuti n’zovuta kapena sitikumvetsa chifukwa chake. Kodi ndi zinthu ziti zimene Mulungu amafuna kuti tizichita, zomwe inuyo mumaona kuti ndi zovuta? Mwachitsanzo, anthu ena amavutika kulalikira. Mwina ndi amanyazi ndipo zimawavuta kulalikira kwa anthu osawadziwa. Pomwe ena zimawavuta kuti asachite nawo zinthu zina akakhala kusukulu kapena kuntchito poopa kuoneka osiyana. (Eks. 23:2; 1 Ates. 2:2) Kodi inunso nthawi zina mumaona kuti zimene Yehova akufuna kuti muchite ndi zovuta ngati zimene anauza Abulahamu? Ngati ndi choncho, nkhani ya Abulahamuyi ingakuthandizeni. Tikamaganizira kwambiri za chikhulupiriro cha anthu okhulupirika akale, tingayambe kuwatsanzira komanso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova.—Aheb. 12:1, 2.

TIMAPEZA MADALITSO AMBIRI TIKAKHALA PA UBWENZI NDI YEHOVA

15. N’chiyani chikusonyeza kuti Abulahamu sananong’oneze bondo chifukwa chomvera Yehova?

15 Kodi mukuganiza kuti Abulahamu ananong’oneza bondo chifukwa chomvera Yehova? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti Baibulo limati: “Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali ndi wokhutira.” (Gen. 25:8) Abulahamu anamwalira ali ndi zaka 175. Koma akaganizira zimene anachita pa moyo wake, ankaona kuti anali ndi moyo wosangalatsa komanso wabwino. Pa moyo wake wonse ankamvera Yehova ndipo anali naye pa ubwenzi wolimba. Komabe mawu akuti Abulahamu anakhala ndi moyo “wautali ndi wokhutira,” sakutanthauza kuti sankafunanso kukhala ndi moyo.

16. Kodi Abulahamu adzasangalala ndi zinthu ziti m’Paradaiso?

16 Baibulo limati Abulahamu ankayembekezera “mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.” (Aheb. 11:10) Iye ankakhulupirira kuti tsiku lina adzaona mzinda umenewu, kapena kuti Ufumu wa Mulungu, ukulamulira dziko lonse. Abulahamu ayenera kuti adzasangalala kwambiri kukhala m’Paradaiso padzikoli n’kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova. Adzasangalalanso akadzadziwa kuti chitsanzo chake chathandiza anthu a Yehova kwa zaka zambirimbiri. Komanso adzadziwa kuti zimene zinachitika ndi Isaki pamene ankafuna kumupereka nsembe, zinkaimira zinthu zina zofunika kwambiri. (Aheb. 11:19) Adzadziwanso kuti chisoni chimene anamva pamene ankakonzekera kupereka nsembe Isaki, chinathandiza anthu kumvetsa mmene Yehova anamvera pamene anapereka nsembe Mwana wake Yesu. (Yoh. 3:16) Nkhani ya Abulahamu imatithandiza kwambiri kuti tiziyamikira chikondi chachikulu chimene Mulungu ndiponso Yesu anasonyeza popereka dipo.

17. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani, nanga tidzakambirana zotani m’nkhani yotsatira?

17 Tonsefe tiziyesetsa kutsanzira chikhulupiriro cha Abulahamu. Tikamaphunzira za Yehova ndiponso kukhala okhulupirika kwa iye, timaona kuti amatithandiza ndiponso kutidalitsa. (Werengani Aheberi 6:10-12.) Tiyeni tiziyesetsa kuchita zonse zimene tingathe kuti tikhalebe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova mpaka kalekale. M’nkhani yotsatira, tidzakambirana za anthu enanso atatu amene anali pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

^ [1] (ndime 3) Poyamba Abulahamu ankadziwika kuti Abulamu ndipo mkazi wake anali Sarai. Koma m’nkhaniyi, tiziwatchula ndi mayina amene Mulungu anawapatsa akuti Abulahamu ndi Sara.