Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizitsanzira Atumiki a Yehova Amene Anali Okhulupirika

Tizitsanzira Atumiki a Yehova Amene Anali Okhulupirika

“Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.”—SAL 18:25.

NYIMBO: 63, 43

1, 2. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Mulungu? (Onani chithunzi pamwambapa.)

PA NTHAWI ina, Sauli ndi asilikali ake 3,000 anali m’chipululu cha Yudeya ndipo ankasakasaka Davide kuti amuphe. Tsiku lina usiku, Davide ndi anthu ake anafika pamalo amene Mfumu Sauli ndi asilikali ake ankagona. Anapeza onse ali m’tulo ndipo Davide ndi Abisai anayenda monyang’ama mpaka kukafika pamene Sauli anagona. Kenako Abisai anauza Davide kuti: “Ndilole chonde, ndimubaye ndi kumukhomerera pansi ndi mkondo kamodzi kokha, sindichita kubwereza kawiri.” Koma zimene Davide anayankha zinali zodabwitsa kwambiri. Iye anati: “Ayi, usamuphe. Kodi ndani anatambasula dzanja lake ndi kupha wodzozedwa wa Yehova, n’kukhala wopanda mlandu? . . . Kwa ine, n’zosatheka! Sindingachite zimenezi pamaso pa Yehova. Sindingatambasule dzanja langa ndi kukantha wodzozedwa wa Yehova.”—1 Sam. 26:8-12.

2 Davide ankadziwa zimene ankayenera kuchita kuti akhale wokhulupirika kwa Yehova. Ankaona kuti ayenera kulemekeza Sauli ndipo sayenera kumupha. Zili choncho chifukwa Sauli anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Masiku anonso Mulungu amafuna kuti atumiki ake azikhala ‘okhulupirika’ kwa iye komanso azilemekeza anthu audindo.—Werengani Salimo 18:25.

3. Kodi Abisai anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Davide?

3 Abisai ankalemekeza Davide chifukwa ankadziwa kuti Mulungu anamusankha kuti adzakhale mfumu. Koma Davide atakhala mfumu, anachita machimo aakulu. Anachita chigololo ndi mkazi wa Uriya ndipo kenako anauza Yowabu kuti akaonetsetse kuti Uriya waphedwa kunkhondo. (2 Sam. 11:2-4, 14, 15; 1 Mbiri 2:16) Popeza Abisai anali mchimwene wake wa Yowabu, n’kutheka kuti anadziwa za nkhaniyi. Komabe iye anapitiriza kulemekeza Davide. Komanso Abisai sanagwiritse ntchito molakwika udindo wake monga mtsogoleri wa asilikali n’kuganiza zolanda ufumu. M’malomwake anateteza Davide kwa adani ake.—2 Sam. 10:10; 20:6; 21:15-17.

4. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Davide anali wokhulupirika kwa Yehova? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

4 Davide anali wokhulupirika kwa Yehova moyo wake wonse. Ali mnyamata, analimba mtima n’kukapha Goliyati amene ankanyoza Yehova komanso anthu ake. (1 Sam. 17:23, 26, 48-51) N’zoona kuti atakhala mfumu anachita chigololo komanso kupha munthu. Koma Yehova atatumiza mneneri Natani kuti akamudzudzule, iye anavomereza kulakwa kwake ndipo analapa. (2 Sam. 12:1-5, 13) Iye atakalamba anasonyezabe kuti anali wokhulupirika kwa Mulungu. Mwachitsanzo, anapereka zinthu zambiri zoti zithandize pomanga kachisi wa Yehova. (1 Mbiri 29:1-5) Ngakhale kuti Davide anachita machimo aakulu, sanasiye kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. (Sal. 51:4, 10; 86:2) M’nkhaniyi tikambirana zinthu zina zimene Davide komanso anthu ena a m’nthawi yake anachita. Zimenezi zitithandiza kuona zimene tingachite kuti tizikhala okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense. Tikambirananso makhalidwe amene angatithandize kuchita zimenezi.

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUTI NDIFE OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA?

5. Kodi tikuphunzira chiyani pa zinthu zolakwika zimene Abisai ankafuna kuchita?

5 Abisai anaganiza zoti aphe Sauli chifukwa ankafuna kukhala wokhulupirika kwa Davide. Koma Davide anamuletsa chifukwa ankadziwa kuti si bwino “kupha wodzozedwa wa Yehova.” (1 Sam. 26:8-11) Apa tikuphunzirapo kuti tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense. Mfundo za m’Malemba zingatithandize kuchita zimenezi.

6. Ngakhale kuti timafuna kukhala okhulupirika kwa achibale athu komanso anzathu , n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala?

6 Kukhulupirika kumayambira mumtima, koma Baibulo limanena kuti mtima ndi wonyenga. (Yer. 17:9) Chifukwa cha zimenezi, tingafune kukhala okhulupirika kwa anthu amene timawakonda ngakhale atakhala kuti akuchita zoipa. Choncho ngati munthu amene timamukonda wasiya kutumikira Mulungu, tizikumbukira kuti tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense.—Werengani Mateyu 22:37.

7. Kodi mlongo wina anachita chiyani kuti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu?

7 Tingasonyeze kuti ndife okhulupirika kwa Yehova pamene munthu wa m’banja lathu wachotsedwa mumpingo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Anne. [1] Mayi ake amene anali ochotsedwa, anamuimbira foni n’kumupempha kuti akufuna kupita kunyumba kwake kuti akacheze naye. Mayiwo anadandaula kuti achibale awo sacheza nawonso. Anne anawamvera chisoni mayi akewo komabe anawauza kuti adzawayankha powalembera kalata. Asanalembe kalatayo, anaganizira mfundo zina za m’Baibulo. (1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 9-11) M’kalatayo, anawafotokozera mayiwo mwaulemu kuti iwowo ndi amene anachititsa kuti achibale awo asamacheze nawonso chifukwa anachimwa ndipo sanalape. Anne anauza mayi akewo kuti: “Ngati mukufuna kukhalanso osangalala, muyenera kubwerera kwa Yehova.”—Yak. 4:8.

8. Kodi ndi makhalidwe ati amene angatithandize kukhala okhulupirika kwa Mulungu?

8 M’nthawi ya Davide, panalinso atumiki a Mulungu omwe anali odzichepetsa, okoma mtima ndiponso olimba mtima. Tiyeni tione mmene makhalidwewa angatithandizire kukhala okhulupirika kwa Yehova.

TIYENERA KUKHALA ODZICHEPETSA

9. N’chifukwa chiyani Abineri ankafuna kupha Davide?

9 Pamene Davide anabweretsa mutu wa Goliati kwa Mfumu Sauli, Yonatani ndiponso mkulu wa asilikali dzina lake Abineri analipo ndipo anaona zimenezi. Yonatani anayamba kugwirizana kwambiri ndi Davide ndipo anakhala wokhulupirika kwa iye. (1 Sam. 17:57–18:3) Koma Abineri sanachite zimenezi. M’malomwake pa nthawi ina anathandiza Sauli kusaka Davide n’cholinga choti amuphe. (Sal. 54:3; 1 Sam. 26:1-5) Onse awiri Yonatani ndi Abineri ankadziwa kuti Mulungu anali atasankha Davide kuti akhale mfumu ya Isiraeli. Koma Sauli atamwalira, Abineri sanakhale kumbali ya Davide. Iye anakhala kumbali ya mwana wa Sauli dzina lake Isiboseti ndipo ankafuna kuti akhale mfumu. Kenako Abineri anagonanso ndi mdzakazi wa Mfumu Sauli ndipo n’kutheka kuti anachita zimenezi chifukwa chofuna kuti akhale mfumu. N’chifukwa chiyani Abineri anachita zinthu mosiyana kwambiri ndi Yonatani? Yonatani anali wokhulupirika kwa Yehova ndiponso wodzichepetsa pomwe Abineri analibe makhalidwe amenewa.—2 Sam. 2:8-10; 3:6-11.

10. N’chiyani chikusonyeza kuti Abisalomu anali wosakhulupirika kwa Mulungu?

10 Nayenso Abisalomu, yemwe anali mwana wa Davide, anali wosakhulupirika kwa Mulungu chifukwa sanali wodzichepetsa. Iye ankafuna kukhala mfumu choncho “anadzipangira galeta lokokedwa ndi mahatchi, ndipo amuna 50 anali kuthamanga patsogolo pake.” (2 Sam. 15:1) Anakopanso Aisiraeli ambiri kuti akhale kumbali yake. Mofanana ndi Abineri, Abisalomu ankafunanso kupha Davide, ngakhale kuti ankadziwa zoti Yehova anasankha Davideyo kuti akhale mfumu ya Isiraeli.—2 Sam. 15:13, 14; 17:1-4.

11. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Abineri, Abisalomu ndiponso Baruki anachita?

11 Ngati munthu ndi wodzikuza ndipo akufunitsitsa kukhala ndi udindo, zimamuvuta kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. N’zoona kuti munthu amene amakonda kwambiri Yehova sangachite zinthu zoipa ngati zimene Abineri ndi Abisalomu anachita. Komabe tikayamba kufunitsitsa kukhala ndi chuma kapena ntchito yapamwamba, tikhoza kuchita zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Pa nthawi ina Baruki, yemwe anali mlembi wa Yeremiya, analola zinthu ngati zimenezi kumusokoneza potumikira Yehova. Ndiyeno Mulungu anamuuza kuti: “Taona! Zimene ndamanga, ndikuzigwetsa, ndipo zimene ndabzala, ndikuzizula. Ndichita zimenezi m’dziko lonse. Koma iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna.” (Yer. 45:4, 5) Baruki anamvera malangizo amenewa. Ifenso tingachite bwino kutsatira malangizowa chifukwa posachedwapa Mulungu awononga dziko loipali.

12. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti tikamatsatira zofuna zathu sitingakhale okhulupirika kwa Yehova.

12 M’bale wina wa ku Mexico dzina lake Daniel anayenera kusankha kukhala wokhulupirika kwa Yehova kapena kutsatira zofuna zake. Iye ankafuna kukwatira mtsikana amene sankatumikira Yehova. Daniel anati: “Ndinkalemberana nayebe makalata ngakhale nditayamba upainiya. Koma kenako ndinadzichepetsa n’kuuza mkulu wina za vuto langali. Iye anandithandiza kuona kuti ndiyenera kusiya kulembera mtsikanayo ngati ndikufuna kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Ndinapempherera nkhaniyi mobwerezabwereza ndipo nthawi zina ndinkalira kwambiri. Koma kenako ndinathetsa chibwenzicho ndipo ndinayamba kusangalala kwambiri potumikira Yehova.” Patapita nthawi, Daniel anakwatira mlongo amene amakonda Yehova ndipo panopa ndi woyang’anira dera.

TIKAKHALA OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA TIMACHITA ZINTHU MOKOMA MTIMA

Mukadziwa kuti mnzanu wachita tchimo lalikulu, kodi mungamuuze kuti apite kwa akulu n’cholinga choti amuthandize? (Onani ndime 14)

13. Kodi Natani anatani kuti akhalebe wokhulupirika kwa Mulungu komanso kwa Davide?

13 Kukhala okhulupirika kwa Yehova kungatithandize kukhalanso okhulupirika kwa anthu ena. Mwachitsanzo, mneneri Natani anali wokhulupirika kwa Yehova komanso kwa Davide. Koma Davide atachita chigololo ndiponso kukonza zoti mwamuna wa mkaziyo aphedwe, Yehova anatumiza Natani kukamudzudzula. Natani analimba mtima n’kukadzudzula Davide ndipo anachita zimenezi mwanzeru komanso mokoma mtima. Iye anafotokoza fanizo lonena za munthu wolemera amene analanda nkhosa ya munthu wosauka. Natani anachita izi kuti Davide azindikire kukula kwa machimo ake. Davide atapsa mtima ndi zimene munthu wolemerayo anachita, Natani anati: “Munthu ameneyo ndiwe!” Izi zinathandiza Davide kuti azindikire zoti wachimwa kwambiri.—2 Sam. 12:1-7, 13.

14. Kodi mungakhale bwanji wokhulupirika kwa Yehova komanso kwa mnzanu kapena wachibale wanu?

14 Inunso mungakhale wokhulupirika kwa Yehova ndiponso kwa anthu ena powachitira zinthu mokoma mtima. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mwadziwa kuti Mkhristu wina wachita tchimo lalikulu? Mwina mungafune kubisa tchimo lakelo pofuna kukhala wokhulupirika kwa munthuyo, makamaka ngati ndi wachibale kapena mnzanu wapamtima. Koma si bwino kuchita zimenezi chifukwa tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense. Choncho mofanana ndi Natani, muyenera kumvera Yehova komanso kuchita zinthu mokoma mtima pofuna kuthandiza mnzanuyo. Mungamuuze kuti akafotokozere akulu za tchimo lakelo kuti amuthandize. Ngati papita nthawi ndipo munthuyo sanauze akulu, inuyo muyenera kuwauza. Mukachita zimenezi mungasonyeze kuti ndinu wokhulupirika kwa Yehova komanso wokoma mtima kwa mnzanuyo. Akulu adzayesetsa kumuthandiza ndi mzimu wofatsa kuti akhalenso pa ubwenzi ndi Yehova.—Werengani Levitiko 5:1; Agalatiya 6:1.

TIYENERA KUKHALA OLIMBA MTIMA KUTI TIKHALE OKHULUPIRIKA KWA MULUNGU

15, 16. N’chifukwa chiyani Husai anafunika kulimba mtima kuti akhale wokhulupirika kwa Mulungu?

15 Husai anali mnzake wokhulupirika wa Mfumu Davide. Pamene anthu ankafuna kuika Abisalomu kuti akhale mfumu, Husai anafunika kulimba mtima kuti akhalebe wokhulupirika kwa Davide komanso kwa Mulungu. Ankadziwa kuti Abisalomu walowa mu Yerusalemu limodzi ndi asilikali ake ndipo Davide wathawa mumzindawo. (2 Sam. 15:13; 16:15) Ndiye kodi Husai anatani? Kodi anasiya Davide n’kuyamba kutsatira Abisalomu? Ayi. Ngakhale kuti Davide anali wokalamba ndipo anthu ambiri ankafuna kumupha, Husai anakhalabe wokhulupirika kwa iye chifukwa anali mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Choncho anapita kukakumana ndi Davide kuphiri la Maolivi.—2 Sam. 15:30, 32.

16 Ndiyeno Davide anapempha Husai kubwerera ku Yerusalemu kuti akanamizire kukhala kumbali ya Abisalomu. Anapempha zimenezi chifukwa ankafuna kuti Abisalomu ayambe kumvera malangizo a Husai m’malo momvera Ahitofeli. Husai anamvera Davide ngakhale kuti izi zinaika moyo wake pa ngozi. Zimenezi zinasonyezanso kuti anali wokhulupirika kwa Yehova. Davide anapempha Yehova kuti athandize Husai ndipo anamuthandizadi. Tikutero chifukwa chakuti Abisalomu anayamba kumvera malangizo a Husai m’malo momvera Ahitofeli.—2 Sam. 15:31; 17:14.

17. N’chifukwa chiyani nthawi zina timafunika kukhala olimba mtima kuti tikhalebe okhulupirika?

17 Nafenso nthawi zina timafunika kuchita zinthu molimba mtima kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova. Tiyenera kuchita zimenezi ngati anzathu akuntchito, achibale kapena akuluakulu a boma akufuna kuti tichite zinthu zosemphana ndi mfundo za Mulungu. Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Japan dzina lake Taro ankayesetsa kumvera makolo ake kuyambira ali mwana. Iye ankachita zimenezi chifukwa chofunitsitsa kuwasangalatsa. Koma Taro atayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova, makolo ake sanasangalale. Choncho zinali zovuta kwambiri kuti awauze zoti akufuna kuyamba kumasonkhana ndi a Mboni. Komabe analimba mtima n’kuwauza. Taro anati: “Makolo anga anakwiya kwambiri moti kwa zaka zambiri sankandilola kuti ndipite kunyumba kwawo kukawaona. Ndinkapempha Mulungu kuti andithandize kukhala wolimba mtima kuti ndisasinthe zimene ndinasankhazo. Panopa makolo anga anasintha ndipo amandilola kupita kunyumba kwawo.”—Werengani Miyambo 29:25.

18. Kodi nkhaniyi yakuthandizani bwanji inuyo?

18 Ifenso tingakhale osangalala kwambiri tikakhala okhulupirika kwa Yehova ngati mmene anachitira Davide, Yonatani, Natani ndiponso Husai. Koma tizipewa kuchita zimene Abineri ndi Abisalomu anachita. N’zoona kuti ndife ochimwa ndipo timalakwitsa zinthu zina. Komabe tiyeni tiziyesetsa kukhala okhulupirika kwa Yehova kuposa kwa wina aliyense.

^ [1] (ndime 7) Mayina ena asinthidwa.