Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

Galimoto Yodziwika Kwambiri Yokhala ndi Zokuzira Mawu

Galimoto Yodziwika Kwambiri Yokhala ndi Zokuzira Mawu

“Ku Brazil kunali galimoto imodzi yokhala ndi zokuzira mawu imene a Mboni ankaigwiritsa ntchito polalikira ndipo anthu ambiri ankaidziwa.”—Ananena zimenezi ndi a Nathaniel A. Yuille mu 1938.

KU BRAZIL ntchito yolalikira sinkayenda bwino kwenikweni m’zaka za m’ma 1930. Koma mu 1935, a Nathaniel Yuille ndi akazi awo a Maud analembera kalata M’bale Joseph F. Rutherford, amene ankatsogolera ntchito yolalikira padziko lonse. A Nathaniel ndi akazi awo anali apainiya ndipo analemba kuti akhoza kukatumikira kulikonse. Pa nthawiyi a Nathaniel anali ndi zaka 62 ndipo anali atapuma pa ntchito yawo ya zomangamanga.

Ndiyeno iwo ndi akazi awo anawatumiza ku Brazil ndipo a Nathaniel anakakhala mtumiki wa nthambi. Asanasamuke, anali wotsogolera utumiki mumpingo wawo mumzinda wa San Francisco ku California m’dziko la United States. Ankaonetsetsa kuti ntchito yolalikira ikuyenda bwino ndipo ankagwiritsa ntchito zipangizo zokuzira mawu polalikira. Zimene ankadziwazi ndiponso mtima wawo wodzipereka zinawathandiza kuti azitsogolera bwino zinthu atapita ku Brazil komwe kuli anthu olankhula zilankhulo zambiri.

A Nathaniel ndi akazi awo anafika ku Brazil mu 1936. Iwo anapitanso ndi mpainiya wina dzina lake Antonio P. Andrade kuti azikamasulira zimene akunena. Anatenganso magalamafoni 35 komanso galimoto yokhala ndi zokuzira mawu. Dziko la Brazil ndi la nambala 5 pa mayiko aakulu kwambiri padziko lonse ndipo pa nthawiyo m’dzikoli munali ofalitsa 60 okha. Komabe magalamafoni ndi galimotoyi, zinathandiza kuti athe kulalikira anthu ambiri pa zaka zochepa.

Patatha mwezi umodzi kuchokera pamene a Nathaniel ndi akazi awo anafika ku Brazil, ofesi ya nthambi inakonza msonkhano waukulu woyamba m’dzikoli ndipo unachitikira mumzinda wa São Paulo. Abale anagwiritsa ntchito galimoto yokhala ndi zokuzira mawu ija poitanira anthu ku nkhani ya onse yapamsonkhanowo ndipo anthu 110 anafika. Msonkhanowo unalimbikitsa kwambiri ofalitsa ndipo anayamba kudzipereka kwambiri pa ntchito yolalikira. Anaphunzira kulalikira pogwiritsa ntchito makadi komanso mabuku. Ankagwiritsanso ntchito galamafoni ndipo anthu ankatha kumvetsera uthenga womwe unajambulidwa m’Chingelezi, Chijeremani, Chihangare, Chipolishi, Chisipanishi komanso kenako m’Chipwitikizi.

Galimotoyi inathandiza kuti anthu ambiri a ku Brazil amve uthenga wabwino

Mu 1937, anachitanso msonkhano ku São Paulo, Rio de Janeiro ndi ku Curitiba. Misonkhanoyi inathandizanso kwambiri pa ntchito yolalikira. Anthu amene anabwera pamsonkhanowu ankapita kukalalikira kunyumba za anthu ndipo ankagwiritsanso ntchito galimoto ija. M’bale José Maglovsky, amene pa nthawiyi anali mnyamata, anati: “Tinkaika mabuku ndi magazini pakashelefu ndipo kenako tinkaulutsa uthenga kudzera pa galimoto yokhala ndi zokuzira mawu. Ndiyeno anthu akabwera kudzaona zimene zikuchitika, tinkawalalikira.”

Anthu anabatizidwira m’mitsinje ndipo kumitsinjeyi kunkapezekanso anthu ambiri omwe ankabwera kudzasamba. Nkhani ya ubatizo ya M’bale Rutherford yomwe inajambulidwa inkaulutsidwa kudzera pa galimotoyo ndipo inkamasuliridwa m’Chipwitikizi. Anthu ankachita chidwi ndipo ankafika pafupi ndi galimotoyo kudzamvetsera nkhaniyo. Kenako anthu ankabatizidwa kwinaku akumvetsera nyimbo za Ufumu zomwe zinajambulidwa m’Chipolishi. Abale ndi alongo ankaimba nawo nyimbozi m’zilankhulo zawo. Buku Lapachaka la 1938 linati: “Zimenezi zikutikumbutsa zomwe zinachitika pamwambo wa Pentekosite pamene aliyense anamva uthenga m’chilankhulo chake.”

Misonkhanoyi itatha, Lamlungu lililonse ankagwiritsanso ntchito galimoto ija kuulutsa nkhani za m’Baibulo. Ankachita zimenezi kumapaki, m’madera okhala anthu, kumafakitale amumzinda wa São Paulo ndiponso m’matauni ena apafupi. Komanso mwezi uliwonse ankapita pa galimoto ija kukaulutsa nkhani kumalo ena komwe kunkakhala anthu 3, 000 odwala khate. Malowa anali pa mtunda wa makilomita 97 kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa São Paulo. Patapita nthawi kuderali kunakhazikitsidwa mpingo. Ngakhale kuti anthu amumpingowu ankavutika ndi matendawa, anapempha boma kuti apite kumalo ena komwe kunkakhalanso anthu odwala khate kuti akawauze uthenga wolimbikitsa wa m’Baibulo.

Kuyambira mu 1938, ku Brazil kunayambanso kupezeka nkhani zojambulidwa m’Chipwitikizi. Pa tsiku lokumbukira anthu omwe anamwalira, anthu ambiri ankapita kumanda ndipo abale ankapita ndi galimoto ija kumanda osiyanasiyana kukaulutsa nkhani zomwe zinajambulidwa. Nkhani zake zinali ndi mutu wakuti, “Kodi Akufa Ali Kuti?,” “Yehova” komanso “Chuma.” Anthu oposa 40,000 anamvetsera nkhanizi.

Atsogoleri achipembedzo ankakwiya ndi uthenga womwe abale ankalalikira ndipo nthawi zambiri ankakakamiza akuluakulu a boma kuti aletse abalewo kugwiritsa ntchito galimoto yokhala ndi zokuzira mawu ija. Mlongo Yuille anafotokoza kuti pa nthawi ina wansembe anauza gulu la anthu kuti lipite kumene kunali galimoto ija kuti likasokoneze. Koma pamalowa panabweranso meya wa mzindawo komanso akuluakulu a polisi ndipo anamvetsera nkhani yonse. Nkhaniyo itatha, meyayo analandira mabuku athu. Ndiyeno gulu la anthu lija linangochoka osachita chilichonse. Ngakhale kuti abale ankakumana ndi mavuto amenewa, Buku Lapachaka la 1940 linanena kuti m’chaka cha 1939, ku Brazil “zinthu zinayenda bwino kwambiri pa nkhani yotumikira Mulungu komanso kulengeza dzina lake.”

Galimoto yokhala ndi zokuzira mawu imene banja la a Yuille linapititsa ku Brazil inathandiza kwambiri kuti ntchito yolalikira iyambe kuyenda bwino m’dzikoli. Galimoto imeneyi inali yodziwika kwambiri ndipo inathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wa m’Baibulo. Galimotoyi inagulitsidwa mu 1941 komabe panopa ku Brazil kuli a Mboni ambiri ndipo akupitiriza kulalikira kwa anthu a m’dzikoli.—Nkhaniyi yachokera ku Brazil.