Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muzitumikirabe Yehova Mosangalala?

Kodi Mungatani Kuti Muzitumikirabe Yehova Mosangalala?

KODI tsiku losangalatsa kwambiri pa moyo ndi liti? Kodi ndi tsiku la ukwati wanu kapena limene mwana wanu woyamba anabadwa? Kapena ndi tsiku limene munabatizidwa? Ambiri amaona kuti tsiku limene anabatizidwa ndi losangalatsa komanso lofunika kwambiri. Abale ndi alongo ayenera kuti anasangalalanso kwambiri kukuonani mukulengeza poyera kuti mumakonda Mulungu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, maganizo anu onse ndiponso mphamvu zanu zonse.—Maliko 12:30.

Muyenera kuti kuyambira pamene munabatizidwa, mwachita zinthu zambiri zosangalatsa potumikira Yehova. Komabe atumiki a Mulungu ena asiya kutumikira Yehova mosangalala. Kodi n’chiyani chimachititsa zimenezi? Nanga ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kuti tizitumikirabe Yehova mosangalala?

N’CHIFUKWA CHIYANI ENA SAKUSANGALALANSO POTUMIKIRA YEHOVA?

Uthenga wa m’Baibulo wakuti posachedwapa Yehova awononga dziko loipali n’kubweretsa dziko latsopano umatithandiza kuti tizisangalala. Komanso lemba la Zefaniya 1:14 limati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.” Komabe ngati tayembekezera nthawi yaitali kuposa mmene tinkaganizira, tingasiye kutumikira Yehova mosangalala komanso mwakhama.—Miy. 13:12.

Koma kusonkhana ndiponso kucheza ndi Akhristu anzathu kumatithandiza kuti tizitumikirabe Yehova mosangalala. Mwina makhalidwe abwino a anthu a Yehova ndi amene anatikopa kuti tiyambe kutumikira Mulungu. (1 Pet. 2:12) Koma nthawi zina Mkhristu wina mumpingo angapatsidwe chilango chifukwa chosatsatira mfundo za m’Baibulo. Zikatere ena angakhumudwe n’kusiya kutumikira Yehova mosangalala.

Tikayamba kufunafuna chuma tingasiyenso kutumikira Yehova mosangalala. Dziko la Satanali limachititsa anthu kuganiza kuti ayenera kukhala ndi zinthu zambiri. Koma zinthuzo zimakhala zosafunika kwenikweni. Tizikumbukira mawu a Yesu akuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri, pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Choncho ngati tikuyesetsa kukhala ndi zinthu zambiri m’dzikoli sitingathe kutumikira Yehova mosangalala.

ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TIZITUMIKIRA YEHOVA MOSANGALALA

Anthu amene amakonda Yehova saona kuti kumutumikira n’kotopetsa. (1 Yoh. 5:3) Paja Yesu anati: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Goli la Yesu si lolemera ndipo limatithandiza kukhala osangalala. Ndipotu pali zinthu zambiri zimene zingatithandize kuti tizitumikira Yehova mosangalala. Tiyeni tsopano tikambirane zitatu mwa zinthu zimenezi.—Hab. 3:18.

Timatumikira Mulungu wachimwemwe amene anatipatsa moyo. (Mac. 17:28; 1 Tim. 1:11) Popeza Mulungu ndi amene anatilenga, tiyenera kumutumikira mosangalala. Tiyenera kuchita zimenezi kaya tangobatizidwa kumene kapena takhala tikumutumikira kwa nthawi yaitali.

A Héctor amakhalabe osangalala chifukwa amaganizira kwambiri za Ufumu komanso amalalikira mwakhama

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Héctor yemwe anali woyang’anira dera kwa zaka 40. Panopa m’baleyu ndi wokalamba koma akutumikirabe Yehova mwakhama. (Sal. 92:12-14) Ngakhale kuti a Héctor amalephera kuchita zambiri chifukwa choti akazi awo amadwaladwala, amatumikirabe Yehova mosangalala. Iwo anati: “Matenda a akazi anga akukulirakulira ndipo ndimayenera kuwasamalira. Komabe ndimayesetsa kuti ndizitumikirabe Yehova mosangalala. Ndimadziwa kuti Yehova ndiye anandipatsa moyo ndipo amafuna kuti tizisangalala. Choncho ndimaona kuti ndiyenera kumukonda kwambiri ndiponso kumutumikira ndi mtima wonse. Ndimayesetsa kugwira nawo ntchito yolalikira mwakhama komanso kuganizira kwambiri za Ufumu. Izi zimandithandiza kuti ndizikhalabe osangalala.”

Yehova anapereka mwana wake nsembe ndipo izi zimatithandiza kukhala osangalala. Paja Baibulo limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Choncho Yehova amatikhululukira machimo ndipo tikamakhulupirira nsembe ya dipo la Yesu tingathe kudzakhala ndi moyo wosatha. Tiyenera kuyamikira Yehova chifukwa cha zimene anatichitirazi. Izi zingatithandizenso kuti tizimutumikira mosangalala.

A Jesús anasintha zinthu zina pa moyo wawo ndipo akhala akutumikira Yehova mosangalala kwa zaka zambiri

M’bale wina wa ku Mexico dzina lake Jesús anati: “Poyamba ndinkangokhalira kugwira ntchito moti nthawi zina ndinkagwira mashifiti 5 molumikiza, ngakhale kuti abwana sankandikakamiza kuchita zimenezi. Ndinkachita izi pongofuna kupeza ndalama zambiri. Kenako ndinaphunzira za Yehova komanso zoti anapereka Mwana wake kuti adzatifere. Ndinkafunitsitsa kuti ndiyambe kumutumikira choncho ndinadzipereka kwa iye n’kubatizidwa. Ngakhale kuti ndinagwira ntchito kwa zaka 28, ndinaisiya n’kuyamba utumiki wa nthawi zonse.” Tsopano papita zaka zambiri m’baleyu akutumikira Yehova mosangalala.

Timayesetsa kupewa makhalidwe oipa ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tizisangalala. Kodi mukukumbukira zimene munkachita musanaphunzire za Yehova? Mtumwi Paulo anakumbutsa Akhristu a ku Roma kuti poyamba iwo ‘anali akapolo a uchimo.’ Koma anasintha n’kukhala “akapolo a chilungamo” ndipo anali ndi makhalidwe oyera amene akanawathandiza kuti adzapeze moyo wosatha. (Aroma 6:17-22) Ifenso timayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino, choncho timapewa mavuto amene amabwera chifukwa chochita zinthu monga chiwerewere kapena chiwawa. Izinso zimatithandiza kukhala osangalala.

“Ndimaona kuti nthawi yosangalatsa kwambiri pa moyo wanga ndi imene ndakhala ndikutumikira Yehova.”—A Jaime

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Jaime. Poyamba ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu komanso zinthu sizinachite kulengedwa. Ankakondanso kwambiri masewera a nkhonya. Koma kenako anayamba kupita kumisonkhano yathu ndipo anachita chidwi kwambiri ndi chikondi chimene anthu ankasonyezana. M’baleyu anapempha Yehova kuti amuthandize kuti ayambe kumukhulupirira. Iye anati: “Pang’ono ndi pang’ono ndinayamba kukhulupirira kuti kuli Mulungu. Ndinayambanso kuzindikira kuti iye ndi Atate wathu wachikondi komanso wachifundo. Ndimaona kuti ndimatetezeka kwambiri chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Ndikanapanda kusintha, mwina ndikanaphedwa ngati mmene zinakhalira ndi anzanga ena omwe ndinkachita nawo masewera a nkhonya. Ndimaona kuti nthawi yosangalatsa kwambiri pa moyo wanga ndi imene ndakhala ndikutumikira Yehova.”

MUSASIYE KUTUMIKIRA YEHOVA MOSANGALALA

Kodi tiyenera kuona bwanji zinthu pamene tikudikira kuti dziko loipali liwonongedwe? Tizikumbukira kuti tikuchita zimene Mulungu amafuna ndipo tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha. “Choncho tisaleke kuchita zabwino, pakuti pa nyengo yake tidzakolola tikapanda kutopa.” (Agal. 6:8, 9) Yehova angatithandize kuti tipitirize kumutumikira mosangalala ngakhale pamene takumana ndi mavuto. Angatithandizenso kuti tikhale ndi makhalidwe ofunika kuti tidzapulumuke pa “chisautso chachikulu.”—Chiv. 7:9, 13, 14; Yak. 1:2-4.

Mulungu amaona zimene timachita pomutumikira ndipo amadziwa kuti timamukonda. Choncho tisamakayikire kuti adzatidalitsa. Tikapitiriza kutumikira Yehova mosangalala tingakhale ndi maganizo ofanana ndi a Davide. Iye anati: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Choncho moyo wanga ukukondwera, ndipo ndidzakhala wosangalala. Komanso ndidzakhala wotetezeka.”—Sal. 16:8, 9.