Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chimwemwe Ndi Khalidwe Limene Mulungu Amapereka

Chimwemwe Ndi Khalidwe Limene Mulungu Amapereka

PAFUPIFUPI munthu aliyense amafuna kukhala wachimwemwe. Koma popeza tikukhala m’masiku otsiriza, tonsefe timakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (2 Tim. 3:1) Anthu ambiri zimawavuta kukhala osangalala chifukwa chochitiridwa zopanda chilungamo, kudwala, kuferedwa, kusowa ntchito kapena mavuto ena. Ngakhale anthu amene amatumikira Mulungu nthawi zina amakhumudwa moti sakhala achimwemwe. Ngati zoterezi zakuchitikirani, kodi mungatani kuti mukhalenso achimwemwe?

Kuti tiyankhe funsoli, choyamba tiyenera kudziwa tanthauzo la chimwemwe komanso zimene zathandiza anthu ena kuti akhalebe achimwemwe ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Kenako tiona zimene tingachite kuti tipitirize kukhala achimwemwe komanso kuwonjezera chimwemwecho.

KODI CHIMWEMWE N’CHIYANI?

Kukhala wachimwemwe sikutanthauza kungosangalala kwa kanthawi basi. Mwachitsanzo, munthu akamwa mowa mpaka kuledzera amaona kuti akusangalala ndipo amangoseka zilizonse. Koma mowawo ukamuthera m’mutu amasiya kuseka ndipo amayambanso kukhala ndi nkhawa. Choncho sitinganene kuti munthu wotere amaseka chifukwa cha chimwemwe.​—Miy. 14:13.

Koma chimwemwe ndi khalidwe limene limachokera mumtima. Munthu amakhala ndi chimwemwe chifukwa chokhala ndi zinthu zabwino kapena kuyembekezera zinthu zosangalatsa. Sasiyanso kukhala wachimwemwe ngakhale pamene wakumana ndi mavuto. (1 Ates. 1:6) Munthu akhoza kukhumudwa ndi zinthu zina koma n’kumakhalabe wachimwemwe mumtima mwake. Mwachitsanzo, atumwi anakwapulidwa chifukwa chouza anthu zokhudza Khristu. Koma zitatero “anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala chifukwa chakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu.” (Mac. 5:41) N’zoona kuti sankasangalala chifukwa chokwapulidwa. Koma anali achimwemwe chifukwa choti anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu.

Munthu sabadwa ali wachimwemwe komanso sangathe kungopeza chimwemwe popanda kuchita chilichonse. Zili choncho chifukwa chimwemwe ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa. Choncho munthu amafunika kuthandizidwa ndi mzimu wa Mulungu kuti avale “umunthu watsopano” womwe umaphatikiza kukhala wachimwemwe. (Aef. 4:24; Agal. 5:22) Ndipo tikakhala achimwemwe timatha kupirira mavuto amene timakumana nawo.

ZITSANZO ZABWINO PA NKHANIYI

Cholinga cha Yehova chinali choti zinthu ziziyenda bwino padzikoli osati kuti tizikumana ndi mavuto. Komabe zinthu zoipa zimene anthu ena amachita sizichititsa kuti Yehova asakhale wachimwemwe. Paja Mawu ake amanena kuti: “Pokhala pake pali mphamvu ndi chimwemwe.” (1 Mbiri 16:27) Komanso zinthu zabwino zimene atumiki ake amachita ‘zimakondweretsa mtima wake.’​—Miy. 27:11.

Tikhoza kutsanzira Yehova tikamapewa kudandaula kwambiri ngati zinthu sizinachitike mmene tinkayembekezera. M’malo mosiya kukhala achimwemwe, tiyenera kuganizira kwambiri zinthu zabwino zimene tili nazo n’kumadikira moleza mtima nthawi imene zinthu zonse zidzakhale bwino. *

Baibulo limafotokoza za anthu ambiri amene anakhalabe achimwemwe ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Abulahamu. Iye anakhalabe wachimwemwe ngakhale pa nthawi imene moyo wake unali pa ngozi komanso pamene anthu ena ankamubweretsera mavuto. (Gen. 12:10-20; 14:8-16; 16:4, 5; 20:1-18; 21:8, 9) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kukhalabe wachimwemwe? Iye ankaganizira kwambiri chiyembekezo chake chodzakhala m’dziko latsopano n’kumalamuliridwa ndi Mesiya. (Gen. 22:15-18; Aheb. 11:10) Yesu anati: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa.” (Yoh. 8:56) Tingatsanzire Abulahamu tikamaganizira zinthu zabwino zimene tikuyembekezera m’tsogolo.​—Aroma 8:21.

Mofanana ndi Abulahamu, mtumwi Paulo komanso Sila ankaganizira zimene Mulungu analonjeza. Iwo anali ndi chikhulupiriro cholimba ndipo ankakhalabe achimwemwe ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, atakwapulidwa koopsa komanso kutsekeredwa mundende, “chapakati pa usiku, [iwo] anali kupemphera ndi kutamanda Mulungu poimba nyimbo, ndipo akaidi ena anali kuwamva.” (Mac. 16:23-25) Paulo ndi Sila ankalimbikitsidwa ndi zinthu zabwino zimene ankayembekezera komanso ankasangalala chifukwa chokhala ndi mwayi wozunzidwa chifukwa cha dzina la Khristu. Tingawatsanzire tikamaganizira ubwino wotumikira Mulungu mokhulupirika.​—Afil. 1:12-14.

Masiku anonso, pali abale ndi alongo ambiri amene amapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yokhalabe achimwemwe ngakhale pamene akukumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, mu November 2013, ku Philippines kunachitika mphepo yamkuntho komanso madzi anasefukira ndipo nyumba zoposa 1,000 za abale ndi alongo zinawonongeka. Nyumba ya m’bale wina dzina lake George inawonongekeratu mumzinda wa Tacloban koma iye anati: “Ngakhale kuti abale akumana ndi mavutowa, akusangalalabe. Ndikusowa mawu ofotokozera chimwemwe chathu.” Tikamaganizira kwambiri zinthu zabwino zimene Yehova watichitira n’kumakhala ndi mtima woyamikira, tikhoza kukhalabe achimwemwe ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene Yehova watipatsa zomwe zingatithandize kuti tikhale achimwemwe?

ZIFUKWA ZIMENE ZIMATICHITITSA KUKHALA ACHIMWEMWE

Chifukwa chachikulu kwambiri chimene chimatichititsa kukhala achimwemwe ndi ubwenzi wathu ndi Mulungu. Ndi mwayi waukulu kwambiri kudziwa Wolamulira chilengedwe chonse. Timayamikira kuti iye ndi Mulungu wathu, Atate wathu komanso Mnzathu wapamtima.​—Sal. 71:17, 18.

Timayamikiranso mphatso ya moyo komanso kuti tinalengedwa m’njira yoti tizisangalala ndi moyowo. (Mlal. 3:12, 13) Yehova watithandizanso kumvetsa cholinga chake chokhudza anthufe. (Akol. 1:9, 10) Choncho timadziwa cholinga cha moyo. Koma anthu ambiri sadziwa zimenezi. Paulo anatsindika mfundo imeneyi ponena kuti: “‘Palibe munthu amene anaonapo kapena kumvapo kapenanso kuganizapo zimene Mulungu wakonzera omukonda.’ Pakuti mwa mzimu wake, Mulungu anaululira ifeyo zinthu zimenezi.” (1 Akor. 2:9, 10) Kunena zoona timasangalala kwambiri chifukwa chodziwa cholinga cha Yehova.

Palinso zinthu zina zimene Yehova watichitira. Mwachitsanzo, anakonza zoti machimo athu azitha kukhululukidwa. (1 Yoh. 2:12) Watichitiranso chifundo potipatsa chiyembekezo chodzakhala m’dziko latsopano posachedwapa. (Aroma 12:12) Yehova watipatsanso gulu la abale ndi alongo omwe timasangalala kulambira nawo limodzi. (Sal. 133:1) Baibulo limatitsimikiziranso kuti Yehova amatiteteza kwa Satana ndi ziwanda zake. (Sal. 91:11) Tikamaganizira madalitso onse amene Mulungu watipatsawa, tikhoza kukhala achimwemwe kwambiri.​—Afil. 4:4.

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIKHALE ACHIMWEMWE KWAMBIRI

Kodi n’zotheka kuti Mkhristu amene ali kale wachimwemwe awonjezere chimwemwe chake? Yesu ananena kuti: “Ndalankhula zinthu izi kwa inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu, ndi kuti chimwemwe chanu chisefukire.” (Yoh. 15:11) Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti n’zotheka munthu kuwonjezera chimwemwe chake. Tingayerekezere zimenezi ndi moto. Kuti moto uyake kwambiri muyenera kuwonjezera nkhuni. N’chimodzimodzinso ndi chimwemwe. Kumbukirani kuti mzimu woyera ndi umene umatithandiza kukhala ndi chimwemwe. Choncho kuti tiwonjezere chimwemwe tiyenera kupitiriza kupempha Yehova kuti azitipatsa mzimu wakewo. Tiyeneranso kusinkhasinkha zimene timawerenga m’Baibulo, lomwe Mulungu anauzira pogwiritsa ntchito mzimu woyera.​—Sal. 1:1, 2; Luka 11:13.

Tingawonjezerenso chimwemwe chathu tikamachita zinthu zosangalatsa Yehova. (Sal. 35:27; 112:1) Zili choncho chifukwa tinalengedwa n’cholinga choti tizichita zimene Mulungu amafuna. Paja Baibulo limanena kuti: “Opa Mulungu woona ndi kusunga malamulo ake chifukwa zimenezi ndiye zimene munthu ayenera kuchita.” (Mlal. 12:13) Choncho tikamatumikira Yehova m’pamene timakhala achimwemwe kwambiri. *

UBWINO WOKHALA WACHIMWEMWE

Tikamayesetsa kukhala achimwemwe, tingapindule kwambiri. Mwachitsanzo, tikamatumikira Yehova mwachimwemwe ngakhale pamene takumana ndi mavuto, iye amasangalala nafe. (Deut. 16:15; 1 Ates. 5:16-18) Komanso kukhala ndi chimwemwe chenicheni kungatithandize kuti tizidzipereka kwambiri pa ntchito za Ufumu wa Mulungu m’malo moyesetsa kukhala ndi chuma. (Mat. 13:44) Tikamaona ubwino wodzipereka chonchi tikhoza kukhala achimwemwe kwambiri, tingapeze mtendere wamumtima komanso tingathandize anthu ena kuti azisangalala.​—Mac. 20:35; Afil. 1:3-5.

Munthu wina wa kuyunivesite ya Nebraska m’dziko la United States anachita kafukufuku wokhudza thanzi la anthu ndipo analemba kuti: “Ngati panopa ndinu wosangalala ndi mmene moyo wanu ulili, mudzatha kukhalabe wathanzi m’tsogolo.” Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.” (Miy. 17:22) Choncho mukamakhala wachimwemwe mukhoza kupewanso matenda ambiri.

Munkhaniyi taona kuti n’zotheka kukhala achimwemwe ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto. Komanso kuti tipeze chimwemwe tiyenera kukhala ndi mzimu woyera ndipo mzimuwo tingaulandire tikamapemphera, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kusinkhasinkha zimene taphunzirazo. Tingawonjezerenso chimwemwe chathu tikamaganizira madalitso athu, kutsanzira chikhulupiro cha ena komanso tikamayesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Tikamachita zonsezi tidzaona umboni wakuti lemba la Salimo 64:10 ndi loona. Lembali limati: “Wolungama adzakondwera mwa Yehova ndipo adzathawira kwa iye.”

^ ndime 10 Munkhani ina yam’tsogolo, yokhudza “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa,” tidzakambirana khalidwe la kuleza mtima.

^ ndime 20 Kuti mudziwe zinthu zina zimene zingakuthandizeni kukhala achimwemwe, onani bokosi lakuti “ Zinthu Zina Zothandiza Kuti Tikhale Achimwemwe.”