Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kukula Mwauzimu

Pitirizani Kukula Mwauzimu

“Pitirizani kuyenda mwa mzimu.”​—AGAL. 5:16.

NYIMBO: 22, 75

1, 2. Kodi m’bale wina anazindikira kuti ali ndi vuto liti pa moyo wake wauzimu, nanga anakonza bwanji zinthu?

ROBERT anabatizidwa ali wachinyamata koma sankakonda kwenikweni choonadi. Iye anati: “Sikuti ndinkachimwa koma ndinkangochita zinthu mwamwambo. Ndinkaoneka ngati wolimba mwauzimu chifukwa ndinkapezeka pamisonkhano yonse ndipo nthawi zina ndinkachita upainiya. Koma ndinkasowa chinachake.”

2 Robert sanazindikire vuto lake mpaka pamene anakwatira. Iye ndi mkazi wake ankakonda kufunsana mafunso okhudza nkhani za m’Baibulo. Mkazi wake anali wolimba mwauzimu ndipo sankavutika kuyankha mafunsowo koma iyeyo ndiye zinkamuvuta moti ankachita manyazi. Robert anati: “Zinkangokhala ngati m’mutu mwanga mulibe chilichonse. Ndiye ndinadziuza kuti, ‘Ngati ndikufunadi kukhala mutu wa mkazi wanga ndiyenera kusintha.’” M’baleyu anasinthadi ndipo anati: “Ndinayamba kuphunzira kwambiri Baibulo ndipo ndinayamba kuona kugwirizana pakati pa nkhani zake. Ndinayamba kulimvetsa bwino koma chofunika kwambiri n’chakuti ubwenzi wanga ndi Yehova unalimba.”

3. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Robert? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Robert? Kungodziwa mfundo zina za m’Baibulo komanso kupezeka pamisonkhano si umboni wakuti ndife anthu auzimu. Mwina n’kutheka kuti takula ndithu mwauzimu koma ngati titadzifufuza bwinobwino tikhoza kupeza zinthu zina zimene tiyenera kusintha. (Afil. 3:16) Choncho munkhaniyi tikambirana mafunso atatu amene angatithandize kuti tipitirize kukula mwauzimu. Mafunso ake ndi awa: (1) N’chiyani chingatithandize kudzifufuza kuti tione ngati tilidi anthu auzimu? (2) Kodi tingatani kuti tipitirize kukula mwauzimu? (3) Kodi kukhala olimba mwauzimu kungatithandize bwanji posankha zochita?

TIYENERA KUDZIFUFUZA

4. Kodi malangizo a pa Aefeso 4:23, 24 ndi opita kwa ndani?

4 Anthufe titayamba kutumikira Yehova tinasintha zinthu zambiri pa moyo wathu. Kusinthaku kunapitirizabe ngakhale titabatizidwa. Paja Baibulo limatiuza kuti: “Mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.” (Aef. 4:23, 24.) Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti “mukhale atsopano” angamasuliridwenso kuti “mupitirize kukhala atsopano.” Choncho popeza tonsefe si angwiro, tiyenera kupitiriza kusintha zinthu zina. Ngakhale anthu amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri ayenera kuchita khama kuti akhalebe auzimu.​—Afil. 3:12, 13.

5. Kodi tingadzifunse mafunso ati podzifufuza?

5 Kuti tipitirize kukula mwauzimu tiyenera kudzifufuza moona mtima. Kaya ndife achinyamata kapena achikulire, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti ndikusintha n’kukhala munthu wolimba mwauzimu? Kodi ndikumatsanzira kwambiri Khristu? Nanga zimene ndimachita ndikakhala kumisonkhano zimasonyeza kuti moyo wanga wauzimu uli bwanji? Kodi zimene ndimakonda kukambirana ndi anthu ena zimasonyeza kuti ndimalakalaka chiyani? Nanga zimene ndimachita pa nkhani yophunzira Baibulo, kavalidwe komanso kudzikongoletsa zimasonyeza kuti ndine munthu wotani? Kodi ndimatani ndikapatsidwa malangizo kapena ndikakumana ndi mayesero? Nanga kodi ndasintha kuchoka pongodziwa mfundo zoyambirira n’kufika pokhala Mkhristu wolimba mwauzimu? (Aef. 4:13) Kuganizira zimene tingayankhe pa mafunso amenewa kungatithandize kudziwa ngati tikukula mwauzimu.

6. N’chiyani chingatithandizenso kuti tidziwe ngati tilidi anthu auzimu?

6 Anzathu akhoza kutithandizanso kudziwa ngati tilidi anthu auzimu. Mtumwi Paulo ananena kuti munthu wakuthupi sazindikira kuti zochita zake n’zolakwika pamaso pa Mulungu. Koma munthu wauzimu amadziwa maganizo a Yehova komanso kuti zochita za anthu akuthupi n’zolakwika. (1 Akor. 2:14-16; 3:1-3) Akulu amene ali ndi maganizo a Khristu amazindikira ngati munthu wayamba kukhala ndi maganizo olakwika ndipo amamuthandiza. Ndiye kodi akatipatsa malangizo timatsatira? Tikamatsatira malangizo awo timasonyeza kuti tikufunitsitsa kukula mwauzimu.​—Mlal. 7:5, 9.

TIZIYESETSA KUKHALA MUNTHU WAUZIMU

7. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kungodziwa Baibulo si kokwanira kuti munthu akhale wauzimu?

7 Tisaiwale kuti kungodziwa Baibulo si kokwanira kuti munthu akhale wauzimu. Paja Mfumu Solomo ankadziwa zambiri zokhudza Yehova ndipo mawu ake ena anaikidwa m’Baibulo. Koma pamapeto pake analephera kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. (1 Maf. 4:29, 30; 11:4-6) Ndiye kodi tiyenera kuchita chiyani kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo? Ndi bwino kuyesetsa kuti tipitirize kukula mwauzimu. (Akol. 2:6, 7) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

8, 9. (a) N’chiyani chingatithandize kuti tikhale okhazikika m’chikhulupiriro? (b) Kodi cholinga chathu pophunzira ndi kusinkhasinkha chiyenera kukhala chiyani? (Onani chithunzi choyambirira.)

8 Paulo analimbikitsa Akhristu oyambirira kuti ‘ayesetse mwakhama kuti akhale okhwima mwauzimu.’ (Aheb. 6:1) Ndiye kodi ifeyo tingatsatire bwanji malangizo a Paulowa? Chinthu china chofunika kwambiri n’kuphunzira buku lakuti Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’? Munthu akaphunzira buku lonseli amatha kuona mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. Ngati mwamaliza kuphunzira bukuli, mungachite bwino kuphunziranso mabuku ena amene angalimbitse chikhulupiriro chanu. (Akol. 1:23) Mungachitenso bwino kuganizira kwambiri zimene mukuphunzira n’kupempha Yehova kuti akuthandizeni kuzitsatira.

9 Cholinga chathu pophunzira chizikhala choti tikhale ndi mtima wofuna kusangalatsa Yehova komanso kumvera malamulo ake. (Sal. 40:8; 119:97) Tiyeneranso kuyesetsa kukana zinthu zimene zingatibwezeretse m’mbuyo mwauzimu.​—Tito 2:11, 12.

10. Kodi achinyamata angachite chiyani kuti akule mwauzimu?

10 Ngati ndinu wachinyamata, kodi muli ndi zolinga zauzimu? M’bale wina wa pa Beteli akapita kumsonkhano amapeza mpata wocheza ndi anthu amene akufuna kubatizidwa. Ambiri mwa anthuwo amakhala achinyamata. Ndiye amawafunsa zolinga zauzimu zimene ali nazo. Ambiri amasonyeza kuti akufuna kuchita zambiri potumikira Yehova, mwina kuchita utumiki wa nthawi zonse kapena kupita kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri. Koma achinyamata ena amasowa choyankha. Mwina achinyamata oterewa amaona kuti sakufunika kukhala ndi zolinga zauzimu. Ngati ndinu wachinyamata, muyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimangochita zinthu zauzimu chifukwa choti n’zimene makolo anga amafuna kuti ndizichita? Kodi ineyo pandekha ndikuyesetsa kuti ndikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu?’ Koma kunena zoona, si achinyamata okha amene ayenera kukhala ndi zolinga zauzimu. Zili choncho chifukwa zolinga zauzimu zimathandiza mtumiki wa Yehova aliyense kuti akhale wolimba mwauzimu.​—Mlal. 12:1, 13.

11. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikule mwauzimu? (b) Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chimene tiyenera kutengera pa nkhaniyi?

11 Tikazindikira zinthu zina zimene sitichita bwino tiyenera kuyesetsa kuti tisinthe. Kukhala munthu wauzimu n’kofunika kwambiri chifukwa kupanda kutero sitingadzapulumuke. (Aroma 8:6-8) Yehova sayembekezera kuti tizichita zinthu popanda kulakwitsa chilichonse ndipo amatipatsa mzimu wake woyera kuti uzitithandiza. Komabe ifeyo patokha tiyenera kuchita khama. Pofotokoza lemba la Luka 13:24, M’bale John Barr amene anali m’Bungwe Lolamulira ananena kuti: “Anthu ambiri amalephera kulowa pakhomo lopapatiza chifukwa sachita khama kwambiri kuti akhale amphamvu mwauzimu.” Tiyenera kukhala ngati Yakobo amene sanasiye kulimbana ndi mngelo mpaka pamene anamudalitsa. (Gen. 32:26-28) N’zoona kuti kuwerenga Baibulo n’kosangalatsa koma ndi losiyana ndi mabuku amene timawerenga pongofuna kusangalala. Tikamawerenga Baibulo, tiyenera kuchita khama kuti tipeze mfundo zamtengo wapatali zimene zingatithandize.

12, 13. (a) N’chiyani chingatithandize kuti titsatire malangizo a pa Aroma 15:5? (b) Kodi chitsanzo cha Petulo komanso malangizo ake zingatithandize bwanji? (c) Kodi inuyo mungatani kuti mukule mwauzimu? (Onani bokosi lakuti “ Zimene Mungachite Kuti Mukule Mwauzimu.”)

12 Tikamachita khama kuti tikule mwauzimu, mzimu woyera umatipatsa mphamvu kuti tisinthe maganizo athu. Pang’ono ndi pang’ono timayamba kukhala ndi maganizo amene Khristu anali nawo. (Aroma 15:5) Mzimu ungatithandizenso kuti tisiye kulakalaka zinthu zoipa n’kumakhala ndi makhalidwe amene amasangalatsa Mulungu. (Agal. 5:16, 22, 23) Tikaona kuti tidakali ndi kamtima kolakalaka chuma kapena zinthu zina zolakwika tisataye mtima. Tizingopitiriza kupempha mzimu woyera ndipo Yehova adzatithandiza kuti tiziika maganizo athu pa zinthu zoyenera. (Luka 11:13) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mtumwi Petulo. Maulendo angapo analephera kuchita zinthu ngati munthu wolimba mwauzimu. (Mat. 16:22, 23; Luka 22:34, 54-62; Agal. 2:11-14) Koma sanagwe mphwayi. Pang’ono ndi pang’ono Yehova anamuthandiza kukhala ndi maganizo a Khristu. Nafenso tikhoza kuchita chimodzimodzi.

13 Pa nthawi ina, Petulo anatchula makhalidwe amene tiyenera kukhala nawo. (Werengani 2 Petulo 1:5-8.) Tikamayesetsa mwakhama kuti tikhale ndi makhalidwe monga kudziletsa, kupirira komanso kukonda abale, tidzatha kukula kwambiri mwauzimu. Choncho ndi bwino kudzifunsa tsiku lililonse kuti, ‘Kodi lero ndingatani kuti ndikule mwauzimu?’

KUTSATIRA MFUNDO ZA M’BAIBULO PA MOYO WATHU

14. Kodi kukhala munthu wauzimu kungatithandize bwanji tsiku ndi tsiku?

14 Kukhala ndi maganizo a Khristu kungatithandize kuti zolankhula zathu ndiponso zochita zathu kusukulu kapena kuntchito zizikhala zabwino. Kungatithandizenso kuti tizisankha zinthu mwanzeru tsiku lililonse. Ndipo zimene tingasankhe zingasonyeze kuti timatsatiradi Khristu. Munthu amene ali ndi maganizo a Khristu salola kuti chilichonse chisokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Akakumana ndi mayesero, chimene chimabwera m’mutu mwamsanga ndi kukana. Asanasankhe zochita amayamba wadzifunsa kuti: ‘Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene ingandithandize kusankha bwino? Kodi akanakhala Khristu akanatani pamenepa? Nanga ndi ziti zimene ndingasankhe kuti ndisangalatse Yehova?’ Kuti tizitha kuchita zimenezi, tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo. M’chitsanzo chilichonse tiziona mfundo ya m’Malemba imene ingatithandize kusankha zochita mwanzeru.

15, 16. Kodi kukhala ndi maganizo a Khristu kungatithandize bwanji posankha (a) mwamuna kapena mkazi? (b) anthu ocheza nawo?

15 Posankha mwamuna kapena mkazi. Mfundo ya m’Baibulo yothandiza ili pa 2 Akorinto 6:14, 15. (Werengani.) Mawu a Paulo palembali akusonyezeratu kuti munthu wauzimu sangagwirizane ndi munthu wakuthupi kapena kuti wokonda za m’dziko. Ndiye kodi munthu angatsatire bwanji mfundo imeneyi posankha mwamuna kapena mkazi?

16 Anthu ocheza nawo. Mfundo ya m’Malemba yothandiza ili pa 1 Akorinto 15:33. (Werengani.) Munthu wauzimu sangamacheze ndi anthu amene angamufooketse mwauzimu. Kodi ndi mafunso ati amene angatithandize kugwiritsa ntchito mfundo imeneyi? Funso lina ndi lakuti, kodi mfundoyi ingandithandize bwanji pocheza ndi anthu pa intaneti? Nanga ndingatani ngati munthu wosamudziwa wapempha kuti ndichite naye masewera enaake pa intaneti?

Kodi zimene ndimasankha zingandithandize kukula mwauzimu? (Onani ndime 17)

17-19. Kodi kukhala munthu wauzimu kungatithandize bwanji (a) kupewa zinthu zachabechabe? (b) kukhala ndi zolinga zabwino? (c) kupewa mikangano?

17 Zinthu zimene zingatifooketse mwauzimu. Paulo anapereka chenjezo kwa Akhristu anzake pa Aheberi 6:1. (Werengani.) Kodi “ntchito zakufa” zimene tiyenera kupewa ndi ziti? Ndi zinthu zilizonse zachabechabe zimene sizingatithandize kukula mwauzimu. Mfundo imeneyi ikhoza kutithandiza kupeza mayankho pa mafunso monga: Kodi zimene ndikufuna kuchita zingandithandize mwauzimu kapena ndi zachabechabe? Kodi ndi nzeru kuti ndiyambe kuchita nawo bizinezi imeneyi? N’chifukwa chiyani sindiyenera kulowa m’magulu ofuna kusintha zinthu m’dziko?

Kodi zimene ndimasankha zingandithandize kukhala ndi zolinga zabwino? (Onani ndime 18)

18 Zolinga zauzimu. Mawu a Yesu pa ulaliki wapaphiri angatithandize kuti tikhale ndi zolinga zoyenera. (Mat. 6:33) Munthu wauzimu amakhala ndi zolinga zauzimu. Kuganizira mfundo imeneyi kungatithandize kuyankha mafunso ngati awa: Kodi ndi bwino kuti ndipite kuyunivesite? Kodi ndi nzeru kuvomera mwayi wa ntchito umene ndikupatsidwawu?

Kodi zimene ndimasankha zingandithandize ‘kukhala mwamtendere’ ndi anthu? (Onani ndime 19)

19 Kusemphana maganizo. Malangizo amene Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Roma angatithandize pa nkhani imeneyi. (Aroma 12:18) Akhristufe tiyenera kuyesetsa kuti tizikhala “mwamtendere ndi anthu onse.” Ndiye kodi timatani ngati tasemphana maganizo ndi munthu wina? Kodi timaumirira maganizo athu kapena timadziwika kuti ndife anthu okonda mtendere?​—Yak. 3:18.

20. N’chifukwa chiyani inuyo mukufunitsitsa kukula mwauzimu?

20 Apa tangokambirana zitsanzo zochepa zosonyeza kuti kuganizira mfundo za m’Malemba kungathandize kuti tizisankha zinthu ngati anthu auzimu. Kukhala munthu wauzimu kumathandiza kuti tizikhala osangalala. Robert amene tamutchula kumayambiriro uja anati: “Nditalimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova ndinakhala mwamuna wabwino komanso bambo wabwino. Ndinayambanso kukhala wosangalala.” Tikamayesetsa kuti tikule mwauzimu nafenso tikhoza kupeza madalitso ngati amenewa. Tikakhala anthu auzimu tidzakhala osangalala panopa komanso tidzapeza “moyo weniweniwo” m’tsogolo.​—1 Tim. 6:19.