Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 5

“Mutu wa Mwamuna Aliyense ndi Khristu”

“Mutu wa Mwamuna Aliyense ndi Khristu”

“Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.”​—1 AKOR. 11:3.

NYIMBO NA. 12 Yehova ndi Mulungu Wamkulu

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingakhudze mmene mwamuna amachitira zinthu ndi mkazi komanso ana ake?

KODI mukuganiza kuti kukhala mutu kumatanthauza chiyani? Mmene amuna ena amachitira zinthu ndi akazi awo komanso ana awo, zimangosonyeza kuti amachita zinthu potengera chikhalidwe cha kwawo kapenanso mmene analeredwera. Mlongo wina wa ku Europe dzina lake Yanita ananena kuti: “Kumene ndimakhala, anthu amakhulupirira kuti akazi ndi otsika poyerekezera ndi amuna ndipo ayenera kuonedwa ngati antchito.” Ndipo m’bale wina wa ku United States dzina lake Luke anati: “Abambo ena amaphunzitsa ana awo aamuna kuti maganizo aakazi sakhala othandiza, choncho sayenera kuwamvetsera akamalankhula.” Koma maganizo amenewa ndi osiyana ndi zimene Yehova amafuna kuti amuna azichita. (Yerekezerani ndi Maliko 7:13.) Ndiye kodi mwamuna angatani kuti akhale mutu wa banja wabwino?

2. Kodi mwamuna yemwe ndi mutu wa banja ayenera kudziwa chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

2 Kuti akhale mutu wa banja wabwino, choyamba mwamuna ayenera kumvetsa zimene Yehova amafuna kuti iye azichita. Amafunikanso kudziwa chifukwa chake Yehova anakonza zakuti ena azitsogolera anzawo komanso zimene angachite kuti azitsanzira Yehova ndi Yesu. N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kudziwa zimenezi? Zili choncho chifukwa Yehova anapereka udindo wotsogolera m’banja kwa mwamuna, ndipo amafuna kuti azigwiritsa ntchito udindowu moyenera.​—Luka 12:48b.

KODI KUKHALA MUTU KUMATANTHAUZA CHIYANI?

3. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Baibulo limanena pa 1 Akorinto 11:3?

3 Werengani 1 Akorinto 11:3. Vesili likusonyeza zimene Yehova anakonza pa nkhani yotsogolera m’banja lake lakumwamba komanso lapadziko lapansi. Kukhala mutu kumaphatikizapo zinthu ziwiri izi: kukhala ndi mphamvu komanso udindo. Yehova ndi “mutu,” ndipo iye ndi amene ali ndi mphamvu zonse. Popeza amatha kupereka mphamvu komanso udindo kwa ana ake omwe akuphatikizapo angelo ndi anthu, Yehova amayembekezera kuti iwo agwiritsa ntchito bwino udindo kapena mphamvu zawo moyenera. (Aroma 14:10; Aef. 3:14, 15) Yehova wapereka kwa Yesu udindo wotsogolera mpingo, ndipo amayembekezera kuti iye azigwiritsa ntchito bwino udindo wake potitsogolera. (1 Akor. 15:27) Waperekanso kwa mwamuna udindo wotsogolera mkazi ndi ana ake, ndipo iye ndi Yesu amayembekezera kuti mwamuna azigwiritsa ntchito bwino udindowu.​—1 Pet. 3:7.

4. Kodi Yehova ndi Yesu ali ndi mphamvu zochita chiyani?

4 Popeza kuti Yehova ndi mutu wa banja lake lakumwamba komanso padziko lapansi, iye ali ndi mphamvu zopanga malamulo oti ana ake azitsatira komanso kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa. (Yes. 33:22) Nayenso Yesu yemwe ndi mutu wampingo, ali ndi mphamvu zopanga malamulo komanso kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa.​—Agal. 6:2; Akol. 1:18-20.

5. Kodi mwamuna yemwe ndi mutu wa banja ali ndi udindo wotani, nanga udindowo uli ndi malire ati?

5 Mofanana ndi Yehova komanso Yesu, mwamuna ali ndi udindo wosankha zochita zokhudza banja lake. (Aroma 7:2; Aef. 6:4) Komabe udindo wake uli ndi malire. Mwachitsanzo, malamulo amene amapanga ayenera kukhala ogwirizana ndi mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu. (Miy. 3:5, 6) Komanso mwamuna alibe udindo wopangira malamulo anthu ena omwe si a m’banja lake. (Aroma 14:4). Ndipo ana ake akakula n’kuchoka pakhomo, anawo amapitirizabe kumulemekeza koma iye sapitiriza kuwatsogolera monga mutu wawo.​—Mat. 19:5.

N’CHIFUKWA CHIYANI YEHOVA ANAKONZA ZOTI ENA AZIKHALA NDI UDINDO WOTSOGOLERA?

6. N’chifukwa chiyani Yehova anakonza zoti ena azikhala ndi udindo wotsogolera?

6 Yehova anakonza zoti ena azikhala ndi udindo wotsogolera chifukwa choti amakonda banja lake lonse. Choncho udindo wotsogolera ndi mphatso yochokera kwa iye. Kukhala ndi ena oti azitsogolera kumathandiza kuti m’banja la Yehova, zinthu zizichitika mwamtendere komanso mwadongosolo. (1 Akor. 14:33, 40) Zikanakhala kuti Yehova sanakonze kuti ena azitsogolera anzawo, m’banja lake mukanakhala chisokonezo ndipo zimenezi zikanachititsa kuti onse m’banjali asamasangalale. Mwachitsanzo, zikanakhala zovuta kudziwa amene ayenera kusankha zochita komanso amene angatsogolere pochita zimene asankhazo.

7. Mogwirizana ndi Aefeso 5:25, 28, kodi Yehova amafuna kuti amuna azichitira nkhanza kapena kupondereza akazi awo?

7 Ngati zimene Mulungu anakonza kuti mwamuna azitsogolera m’banja zili zabwino, n’chifukwa chiyani akazi ambiri masiku ano amaona kuti amuna awo amawapondereza komanso kuwachitira nkhanza? Zimenezi zili choncho chifukwa amuna ambiri amanyalanyaza mfundo za Yehova zimene mabanja ayenera kutsatira, ndipo m’malomwake amasankha kutsatira mfundo zachikhalidwe komanso miyambo yawo. Nthawi zina chifukwa chodzikonda, iwo amachitira nkhanza akazi awo pofuna kungosangalala. Mwamuna akhoza kumazunza mkazi wake n’cholinga choti azidziona kuti ndi wofunika kwambiri kapenanso kuti anthu ena azimuona kuti ndi “mwamuna weniweni.” Iye akhoza kumaganiza kuti sangakakamize mkazi wake kuti azimukonda, koma akhoza kumuchititsa kuti azimuopa. Angamachite zimenezi n’cholinga choti mkaziyo azichita zilizonse zimene mwamunayo akufuna. * Amuna amene amaganiza komanso kuchita zinthu zimenezi amalakwitsa chifukwa akazi ayenera kupatsidwa ulemu ndipo kulephera kuwalemekeza n’kosemphana ndi zimene Yehova amafuna.​—Werengani Aefeso 5:25, 28.

KODI MWAMUNA ANGATANI KUTI AKHALE MUTU WA BANJA WABWINO?

8. Kodi mwamuna angatani kuti akhale mutu wa banja wabwino?

8 Mwamuna angakhale mutu wabwino akamatsanzira mmene Yehova ndi Yesu amachitira pa nkhani yotsogolera. Tiyeni tione makhalidwe awiri amene Yehova ndi Yesu amasonyeza komanso mmene mwamuna angasonyezere makhalidwewa pochita zinthu ndi mkazi komanso ana ake.

9. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa?

9 Kudzichepetsa. Yehova ndi wanzeru kuposa wina aliyense. Komabe, iye amamvetsera maganizo a atumiki ake. (Gen. 18:23, 24, 32) Iye amalola amene akuwatsogolera kufotokoza maganizo awo. (1 Maf. 22:19-22) Yehova ndi wangwiro, koma samayembekezera kuti anthufe tizichita zinthu popanda kulakwitsa kalikonse. M’malomwake, iye amathandiza atumiki ake omwe si angwiro kuti zinthu ziziwayendera bwino. (Sal. 113:6, 7) Ndipotu Baibulo limafotokoza kuti Yehova ndi “m’nthandizi” wathu. (Sal. 27:9; Aheb. 13:6) Mfumu Davide ananena kuti anakwanitsa kugwira ntchito yaikulu imene anapatsidwa chifukwa chakuti Yehova ndi wodzichepetsa ndipo anamuthandiza.​—2 Sam. 22:36.

10. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa?

10 Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Iye anasambitsa mapazi a ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankamuona kuti ndi Ambuye. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova analola kuti nkhaniyi ilembedwe m’Baibulo? Mosakaikira iye ankafuna kuti aliyense kuphatikizapo amuna omwe ndi mitu ya mabanja azitsatira zimenezi. Ndipotu Yesu ananena kuti: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yoh. 13:12-17) Ngakhale kuti iye anali ndi udindo waukulu, sankafuna kuti ena azimutumikira. M’malomwake iye ndi amene ankatumikira ena.​—Mat. 20:28.

Mwamuna angasonyeze kuti ndi wodzichepetsa komanso amakonda anthu a m’banja lake, akamagwira nawo ntchito zapakhomo komanso powathandiza kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova (Onani ndime 11 ndi 13)

11. Kodi mwamuna yemwe ndi mutu wa banja angaphunzire chiyani kwa Yehova ndi Yesu pa nkhani yokhala wodzichepetsa?

11 Zimene tikuphunzirapo. Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja, angasonyeze kuti ndi wodzichepetsa m’njira zambiri. Mwachitsanzo, iye sayembekezera kuti mkazi ndi ana ake azichita zinthu mosalakwitsa chilichonse. Iye amamvetsera maganizo a anthu a m’banja lake ngakhale pamene maganizo awo akusiyana ndi maganizo ake. Marley, yemwe amakhala ku United States, ananena kuti: “Nthawi zina ine ndi mwamuna wanga timakhala ndi maganizo osiyana. Koma ndimaona kuti iye amandiyamikira komanso kundilemekeza chifukwa akandifunsa maganizo anga, amawaganizira mosamala asanasankhe zochita.” Kuwonjezera pamenepo, mwamuna wodzichepetsa amakhala wofunitsitsa kugwira ntchito za pakhomo ngakhale kuti m’dera limene amakhala, anthu ambiri amaganiza kuti ntchito zapakhomo ndi za akazi. Zimenezitu zingakhale zovuta kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Mlongo wina dzina lake Rachel ananena kuti: “Kudera limene ndimachokera, mwamuna akamathandiza mkazi wake kutsuka mbale kapena kukonza m’nyumba, achibale komanso anthu oyandikana nawo nyumba amakayikira ngati alidi ‘mwamuna weniweni.’ Iwo amaganiza kuti mwamuna woteroyo mkazi wake sangamamumvere.” Ngati kudera limene mumakhala anthu ambiri ali ndi maganizo amenewa, muzikumbukira kuti Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake, ngakhale kuti imeneyi inkaonedwa kuti ndi ntchito ya akapolo. Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja wabwino safuna kuti ena azimuona kuti ndi wamphamvu kapena wofunika kwambiri. M’malomwake iye amafuna kuti mkazi ndi ana ake azisangalala. Kuwonjezera pa kudzichepetsa, kodi ndi khalidwe linanso liti limene mwamuna amene ndi mutu wa banja wabwino ayenera kukhala nalo?

12. Kodi chikondi chimachititsa Yehova ndi Yesu kuchita chiyani?

12 Chikondi. Chilichonse chimene Yehova amachita, amachichita chifukwa cha chikondi. (1 Yoh. 4:7, 8) Iye anatipatsa Mawu ake Baibulo komanso gulu lake chifukwa choti amatikonda ndiponso amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Iye amatithandiza kuti tiziona kuti ndife otetezeka, potitsimikizira kuti amatikonda. Yehova amaonetsetsanso kuti tili ndi zinthu zofunika pa moyo. Ndipo “amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.” (1 Tim. 6:17) Tikalakwitsa zinazake, iye amatidzudzula, koma sasiya kutikonda. Ndipo chifukwa chotikonda, iye anatipatsa dipo. Nayenso Yesu amatikonda kwambiri, moti analolera kupereka moyo wake chifukwa cha ife. (Yoh. 3:16; 15:13) Choncho palibe chimene chingalepheretse Yehova ndi Yesu kusonyeza chikondi kwa anthu amene ndi okhulupirika kwa iwo.​—Yoh. 13:1; Aroma 8:35, 38, 39.

13. N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kukonda banja lake? (Onaninso bokosi lakuti “ Kodi Mwamuna Yemwe Wangokwatira Kumene Angatani Kuti Mkazi Wake Azimulemekeza?”)

13 Zimene tikuphunzirapo. Chilichonse chimene mwamuna yemwe ndi mutu wa banja amachita ayenera kuchichita chifukwa cha chikondi. N’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kuli kofunika kwambiri? Mtumwi Yohane anafotokoza kuti: “Amene sakonda m’bale wake [kapena banja lake], amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.” (1 Yoh. 4:11, 20) Choncho mwamuna yemwe amakonda banja lake ndipo akufuna kutsanzira Yehova ndi Yesu, amayesetsa kuthandiza anthu a m’banjalo kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, kuwathandiza kuti aziona kuti ndi otetezeka komanso amawapezera zofunika pa moyo. (1 Tim. 5:8) Iye amaphunzitsa ana ake komanso kuwapatsa chilango ngati pakufunika kutero. Nthawi zonse amasankha zochita zimene zingalemekeze Yehova komanso kuthandiza banja lake. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zimenezi ndipo tiona zomwe mwamuna yemwe ndi mutu wabanja angachite kuti azitsanzira Yehova ndi Yesu.

ZIMENE MUTU WA BANJA UYENERA KUCHITA

14. Kodi mwamuna angatani kuti azithandiza anthu a m’banja lake kukhala pa ubwenzi ndi Yehova?

14 Kuthandiza anthu a m’banja lake kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Potsanzira Atate wake, Yesu ankaonetsetsa kuti akuthandiza otsatira ake kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Mat. 5:3, 6; Maliko 6:34) Mofanana ndi zimenezi, mwamuna ayenera kuona kuti chinthu chofunika kwambiri ndikuthandiza anthu a m’banja lake kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. (Deut. 6:6-9) Iye amachita zimenezi poonetsetsa kuti anthu a m’banja lake akuwerenga komanso kuphunzira Mawu a Mulungu, kupezeka pamisonkhano, kulalikira uthenga wabwino komanso kuwathandiza kuti apitirize kukonda kwambiri Yehova.

15. Kodi mwamuna angathandize bwanji anthu a m’banja lake kuti aziona kuti ndi otetezeka?

15 Kuthandiza anthu a m’banja lake kuti aziona kuti ndi otetezeka. Yehova anauza Yesu kuti amamukonda anthu ena akumva. (Mat. 3:17) Yesu anasonyezanso kuti amakonda otsatira ake kudzera m’zochita komanso zolankhula zake. Nawonso otsatira ake anamuuza kuti amamukonda. (Yoh. 15:9, 12, 13; 21:16) Mwamuna angasonyeze kuti amakonda mkazi ndi ana ake mwa zochita zake, monga kuphunzira nawo limodzi Baibulo. Ayeneranso kumawayamikira n’kumawauza kuti amawakonda. Ndipo ngati n’kotheka azichitanso zimenezi pamaso pa anthu ena.​—Miy. 31:28, 29.

Kuti azisangalatsa Yehova, mwamuna ayenera kupezera anthu a m’banja lake zinthu zofunika pa moyo (Onani ndime 16)

16. Kodi ndi chinthu chinanso chiti chimene mwamuna yemwe ndi mutu wa banja ayenera kuchita, nanga ayenera kupewa chiyani?

16 Kupezera anthu a m’banja lake zinthu zofunika pa moyo. Yehova ankapatsa Aisiraeli zinthu zofunika pa moyo ngakhale pamene ankawalanga chifukwa choti sanamumvere. (Deut. 2:7; 29:5) Masiku anonso iye amatipatsa zimene timafunikira. (Mat. 6:31-33; 7:11) Mofanana ndi Atate wake nayenso Yesu anadyetsa anthu amene ankamutsatira. (Mat. 14:17-20) Komanso anachiritsa anthu ambiri amene ankadwala. (Mat. 4:24) Kuti azisangalatsa Yehova, mwamuna ayenera kupezera anthu a m’banja lake zinthu zofunika pa moyo. Komabe iye ayenera kukhala wosamala pa nkhani imeneyi. Iye safunika kutanganidwa kwambiri ndi ntchito pofuna kusamalira banja lake, mpaka kufika polephera kuthandiza anthu a m’banja lakewo kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kulephera kuwathandiza kuti aziona kuti ndi otetezeka.

17. Kodi Yehova ndi Yesu amatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani yotiphunzitsa komanso kutipatsa uphungu?

17 Kuphunzitsa anthu a m’banja lake. Yehova amatiphunzitsa komanso kutipatsa malangizo n’cholinga choti zinthu zizitiyendera bwino. (Aheb. 12:7-9) Mofanana ndi Atate wake, nayenso Yesu amaphunzitsa mwachikondi anthu amene amawatsogolera. (Yoh. 15:14, 15) Iye amaperekanso uphungu koma mokoma mtima. (Mat. 20:24-28) Amadziwa kuti si ife angwiro ndipo nthawi zina timalakwitsa.​—Mat. 26:41.

18. Kodi mwamuna yemwe ndi mutu wa banja wabwino amakumbukira chiyani?

18 Mwamuna yemwe amatsanzira Yehova ndi Yesu amakumbukira kuti anthu a m’banja lake si angwiro. Iye ‘samapsera mtima’ mkazi wake komanso ana ake. (Akol. 3:19) M’malomwake iye amagwiritsa ntchito mfundo ya pa Agalatiya 6:1 ndipo amawalangiza ndi “mzimu wofatsa” pokumbukira kuti nayenso si wangwiro. Mofanana ndi Yesu, iye amadziwa kuti njira yabwino yophunzitsira anthu a m’banja lake ndi kudzera m’zochita zake.​—1 Pet. 2:21.

19-20. Kodi Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja angatsanzire bwanji Yehova ndi Yesu posankha zochita?

19 Kusankha zochita zokomera banja lonse. Yehova amasankha zinthu zimene zingakhale zabwino kwa onse. Mwachitsanzo, Iye anatilenga osati n’cholinga chofuna kupeza zinazake, koma kuti nafenso tizisangalala ndi moyo. Ndipotu palibe akanamukakamiza kupereka Mwana wake chifukwa cha machimo athu. Koma mwakufuna kwake iye anachita zimenezi kuti atithandize. Nayenso Yesu ankasankha zinthu zimene zinkathandiza ena. (Aroma 15:3) Mwachitsanzo, pa nthawi ina iye atatopa anasankha kupitirizabe kuphunzitsa anthu m’malo mopita kukapuma.​—Maliko 6:31-34.

20 Mwamuna yemwe ndi mutu wa banja wabwino amadziwa kuti chimodzi mwa zinthu zovuta kwambiri ndi kusankha mwanzeru zinthu zokhudza banja lake ndipo saiona mopepuka nkhani imeneyi. Iye amapewa kusankha zinthu mopupuluma kapena potengera mmene akumvera pa nthawiyo. M’malomwake iye amalola kuti Yehova azimuphunzitsa kusankha bwino zochita. * (Miy. 2:6, 7) Akamachita zimenezi amaganizira zimene zingathandizenso ena, osati iye yekha.​—Afil. 2:4.

21. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

21 Yehova wapereka kwa amuna omwe ndi mitu ya mabanja udindo waukulu kwambiri, ndipo amayembekezera kuti iwo achita zonse zomwe angathe kuti aukwaniritse. Koma mwamuna akamayesetsa kutsanzira Yehova ndi Yesu, angathe kukhala mutu wa banja wabwino. Nayenso mkazi wake akamayesetsa kukwaniritsa udindo wake, banja lawo likhoza kukhala losangalala. Koma kodi mkazi ayenera kuona bwanji udindo wa mwamuna wake monga mutu? Nanga ndi mavuto otani amene angakumane nawo? Nkhani yotsatirayi idzayankha mafunso amenewa.

NYIMBO NA. 16 Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa

^ ndime 5 Mwamuna akakwatira, amakhala mutu wa banja lake. Munkhaniyi tikambirana zimene kukhala mutu kumatanthauza, chifukwa chake Yehova anakonza zoti ena azikhala ndi udindo wotsogolera komanso zimene amuna angaphunzire kwa Yehova ndi Yesu. Munkhani yotsatira, tidzaona zimene amuna ndi akazi angaphunzire kwa Yesu komanso anthu ena otchulidwa m’Baibulo. Ndipo munkhani yachitatu, tidzakambirana zimene abale angachite kuti azigwiritsa ntchito moyenera udindo wawo mumpingo.

^ ndime 7 Nthawi zina mabuku, mafilimu kapena masewero, amasonyeza kuti palibe vuto ngati mwamuna atamachitira nkhanza kapena kuzunza mkazi wake. Maganizo amenewa amachititsa kuti anthu ambiri aziona kuti sikulakwa kuti mwamuna azipondereza mkazi wake.

^ ndime 20 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani yokhudza kusankha bwino zochita, onani nkhani yakuti “Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2011, tsamba 13-17.