Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 8

Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Tikakumana ndi Mayesero

Zimene Tingachite Kuti Tizisangalalabe Tikakumana ndi Mayesero

“Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana.”​—YAK. 1:2.

NYIMBO NA. 111 Tili ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. Mogwirizana ndi Mateyu 5:11, kodi tiziona bwanji mayesero amene timakumana nawo?

YESU analonjeza otsatira ake kuti adzapeza chimwemwe chenicheni. Koma anachenjezanso kuti onse amene amamukonda adzakumana ndi mayesero. (Mat. 10:22, 23; Luka 6:20-23) Timakhala osangalala chifukwa chokhala ophunzira a Khristu. Koma kodi timamva bwanji ngati anthu a m’banja lathu akutitsutsa chifukwa choti tikutumikira Yehova, akuluakulu a boma akamatizunza komanso anzathu a kuntchito kapena kusukulu akamatikakamiza kuti tichite zinthu zoipa? Kunena zoona zochitika ngati zimenezi zingatichititse kuti tizida nkhawa.

2 Anthu ambiri amaona kuti kuzunzidwa si chifukwa chimene chingawapangitse kukhala osangalala. Komatu izi ndi zimene mawu a Mulungu amanena. Mwachitsanzo, mtumwi Yakobo analemba kuti m’malo moti tizida nkhawa tikakumana ndi mayesero, tizisangalala. (Yak. 1:2, 12) Komanso Yesu ananena kuti tizisangalala pamene tikuzunzidwa. (Werengani Mateyu 5:11.) Ndiye kodi tingatani kuti tizisangalala pamene tikukumana ndi mayesero? Tingaphunzire zambiri tikaganizira mfundo zina zimene zili m’kalata imene Yakobo analembera Akhristu oyambirira. Choyamba, tiyeni tione mavuto ena omwe Akhristuwa ankakumana nawo.

KODI AKHRISTU OYAMBIRIRA ANKAKUMANA NDI MAYESERO OTANI?

3. Kodi chinachitika n’chiyani Yakobo atangokhala wophunzira wa Yesu?

3 Patangopita kanthawi kochepa kuchokera pamene Yakobo, mchimwene wake wa Yesu anakhala wophunzira, Akhristu ku Yerusalemu anayamba kuzunzidwa. (Mac. 1:14; 5:17, 18) Ndipo wophunzira Sitefano ataphedwa, Akhristu ambiri anathawa mumzindawo ndipo “anabalalikira m’zigawo za Yudeya ndi Samariya,” ndipo ena anakafika mpaka kumadera akutali ngati ku Kupuro ndi ku Antiokeya. (Mac. 7:58–8:1; 11:19) Kunena zoona, ophunzirawo anakumana ndi mavuto ambiri. Komabe kulikonse kumene iwo ankapita, ankalalikira uthenga wabwino mofunitsitsa ndipo anakhazikitsa mipingo m’madera ambiri omwe anali pansi pa ufumu wa Roma. (1 Pet. 1:1) Koma pambuyo pa zimenezi Akhristuwo anakumananso ndi mavuto ena ambiri.

4. Kodi ndi mavuto enanso ati omwe Akhristu oyambirira anakumana nawo?

4 Akhristu oyambirira anakumana ndi mayesero osiyanasiyana. Mwachitsanzo, cha m’ma 50 C.E., mfumu Kalaudiyo analamula kuti Ayuda achoke ku Roma. Choncho Ayuda omwe anakhala Akhristu anakakamizika kusiya nyumba zawo n’kusamukira kumadera ena. (Mac. 18:1-3) Cha m’ma 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu anzake ankatonzedwa poyera poikidwa m’ndende komanso kulandidwa katundu. (Aheb. 10:32-34) Mofanana ndi anthu onse, Akhristu nawonso ankapirira mavuto osiyanasiyana ngati umphawi komanso matenda.​—Aroma 15:26; Afil. 2:25-27.

5. Kodi tikambirana mafunso ati?

5 Pamene Yakobo ankalemba kalata yake chisanafike chaka cha 62 C.E., ankadziwa bwino mavuto amene abale ndi alongo ake ankakumana nawo. Yehova anauzira mtumwi Yakobo kuti alembere Akhristuwa malangizo amene akanawathandiza kuti apitirizebe kukhala osangalala ngakhale pamene akukumana ndi mayesero. Tiyeni tikambirane zimene zili m’kalata imene Yakobo analemba, n’kuyankha mafunso otsatirawa: Kodi Yakobo ankanena za kusangalala kotani? Kodi n’chiyani chingachititse kuti Mkhristu asiye kusangalala? Nanga kodi nzeru, chikhulupiriro komanso kulimba mtima zingatithandize bwanji kuti tizisangalalabe ngakhale titakumana ndi mayesero aliwonse?

N’CHIYANI CHIMACHITITSA KUTI MKHRISTU AZISANGALALA?

Mofanana ndi lawi la nyale yagalasi lomwe limakhala lotetezeka, chimwemwe chimene Yehova amapereka chimayakabe mumtima mwa Mkhristu (Onani ndime 6)

6. Mogwirizana ndi Luka 6:22, 23, n’chifukwa chiyani Mkhristu angakhalebe wosangalala akamakumana ndi mayesero?

6 Anthu ambiri amaganiza kuti angakhale osangalala ngati ali ndi thanzi labwino, ndalama zambiri komanso banja losangalala. Komatu chimwemwe chimene Yakobo ankanena ndi limodzi mwa makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa ndipo sichidalira mmene zinthu zilili pa moyo wa munthu. (Agal. 5:22) Mkhristu angakhale ndi chimwemwe kapena kuti wosangalala, akadziwa kuti akusangalatsa Yehova komanso kutsatira chitsanzo cha Yesu. (Werengani Luka 6:22, 23; Akol. 1:10, 11) Chimwemwe chimene chimakhala mumtima mwa Mkhristu chili ngati lawi la nyale yagalasi lomwe limakhala lotetezeka. Lawilo limayakabe ngakhale kukuomba mphepo kapena kukugwa mvula. Chimwemwe chimenechi chimakhalapobe ngakhale tidwale kapena tikhale ndi ndalama zochepa. Ndipo sichitha ngakhale pamene anthu ena kapena a m’banja lathu akutinyoza kapena kutitsutsa. M’malo mokhala okhumudwa, chimwemwe chathu chimawonjezereka nthawi iliyonse imene anthu ena akufuna kutilanda chimwemwecho. Mayesero amene timakumana nawo chifukwa cha chikhulupiriro chathu ndi amene amatsimikizira kuti ndifedi ophunzira a Khristu. (Mat. 10:22; 24:9; Yoh. 15:20) N’chifukwa chake Yakobo analemba kuti: “Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayesero osiyanasiyana.”​—Yak. 1:2.

N’chifukwa chiyani mayesero amayerekezeredwa ndi moto umene amagwiritsa ntchito popanga zitsulo kuti zikhale zolimba? (Onani ndime 7) *

7-8. N’chifukwa chiyani chikhulupiriro chathu chimalimba tikamakumana ndi mayesero?

7 Yakobo anafotokoza chifukwa chinanso chimene chimachititsa Akhristu kukhala ofunitsitsa kupirira ngakhale mayesero aakulu. Iye anati: “Chikhulupiriro chanu chikayesedwa, chimabala kupirira.” (Yak. 1:3) Mayesero tingawayerekezere ndi moto umene amagwiritsa ntchito popanga chitsulo kuti chikhale cholimba. Chitsulocho chimaikidwa pamoto ndipo chikazizira chimakhala cholimba kwambiri. Mofanana ndi zimenezi, tikapirira mayesero chikhulupiriro chathu chimalimba. N’chifukwa chake Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupirira kumalize kugwira ntchito yake, kuti mukhale okwanira ndi opanda chilema m’mbali zonse.” (Yak. 1:4) Tikamaona kuti mayesero akutithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba, tingathe kuwapirira mosangalala.

8 M’kalata yake, Yakobo anatchulanso zinthu zina zimene zingachititse kuti tisamasangalale. Kodi zinthu zake ndi ziti, nanga tingalimbane nazo bwanji?

ZIMENE TINGACHITE KUTI MAYESERO ASATILEPHERETSE KUKHALA OSANGALALA

9. N’chifukwa chiyani nzeru ndi zofunika tikakumana ndi mayesero?

9 Vuto limene limakhalapo: Kulephera kudziwa zoyenera kuchita. Tikakumana ndi mayesero timafuna kuti Yehova atithandize kuti tisankhe zimene iye angasangalale nazo, zimene zingathandize abale ndi alongo athu komanso zimene zingatithandize kupitirizabe kukhala okhulupirika. (Yer. 10:23) Timafunika nzeru kuti tidziwe zoyenera kuchita komanso kulankhula, anthu ena akamatitsutsa. Ngati sitikudziwa zoyenera kuchita tikakumana ndi mavuto enaake, tikhoza kutaya mtima ndipo zimenezi zingachititse kuti tisamasangalale.

10. Kodi lemba la Yakobo 1:5, limatiuza kuti tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze nzeru?

10 Zimene tingachite: Tizipempha Yehova kuti atipatse nzeru. Kuti tikwanitse kupirira mayesero athu mosangalala, choyamba tiyenera kupemphera kwa Yehova kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kusankha bwino zochita. (Werengani Yakobo 1:5.) Ndiye kodi tiyenera kutani ngati tikuona kuti sanayankhe pemphero lathu mwamsanga? Yakobo ananena kuti tiyenera ‘kumapemphabe’ kwa Mulungu. Yehova sakwiya nazo tikamapitirizabe kumupempha kuti atipatse nzeru ndipo samatinyoza. M’malomwake Atate wathu wakumwamba amatipatsa “mowolowa manja” tikamapempha kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kuti tipirire mayesero. (Sal. 25:12, 13) Yehova amaona mayesero amene tikukumana nawo, amakhudzidwa tikamavutika komanso ndi wokonzeka kutithandiza. Zimenezitu zimatithandiza kukhala osangalala. Koma kodi Yehova amatipatsa bwanji nzeru?

11. Kodi tiyenera kuchitanso chiyani kuti tipeze nzeru?

11 Yehova amatipatsa nzeru kudzera m’Mawu ake. (Miy. 2:6) Kuti tipeze nzeru zimenezi, tiyenera kumaphunzira Mawu a Mulungu komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo. Koma kuphunzira kokha sikokwanira, tiyenera kugwiritsira ntchito nzeru za Mulungu pa moyo wathu potsatira malangizo ake. Yakobo analemba kuti: “Muzichita zimene mawu amanena, osati kungomva chabe.” (Yak. 1:22) Tikamatsatira malangizo a Mulungu timakhala anthu amtendere, ololera komanso achifundo. (Yak. 3:17) Makhalidwe amenewa amatithandiza kuti tizipirira mayesero aliwonse amene tingakumane nawo koma n’kumakhalabe osangalala.

12. N’chifukwa chiyani ndi zofunika kuti tizilidziwa bwino Baibulo?

12 Mawu a Mulungu ali ngati galasi ndipo amatithandiza kudziwa zimene tiyenera kukonza komanso mmene tingachitire zimenezi. (Yak. 1:23-25) Mwachitsanzo, pambuyo pophunzira Mawu a Mulungu tikhoza kuzindikira kuti tikufunika kukhala oleza mtima. Yehova angatithandize kuti tizichita zinthu modekha anthu akatikhumudwitsa kapena tikakumana ndi mavuto enaake. Kuchita zinthu modekha kungathandize kuti tithe kulimbana ndi mavuto amene takumana nawo. Izi zili choncho chifukwa timachita zinthu moganiza bwino ndipo timasankha zochita mwanzeru. (Yak. 3:13) Choncho n’zofunika kwambiri kuti tizilidziwa bwino Baibulo.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira pa zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo?

13 Nthawi zina timaphunzira zinthu zoyenera kupewa tikalakwitsa zinazake. Komatu imeneyi si njira yabwino yophunzirira zinthu. Munthu wanzeru amaphunzira pa zimene ena anachita bwino kapena zimene analakwitsa. N’chifukwa chake Yakobo anatilimbikitsa kuganizira zitsanzo za anthu a m’Baibulo monga Abulahamu, Rahabi, Yobu komanso Eliya. (Yak. 2:21-26; 5:10, 11, 17, 18) Atumiki a Yehova okhulupirikawa anapirira mayesero amene akanawachititsa kuti asamasangalale. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti nafenso Yehova angatithandize kuti tizipirira mosangalala mayesero amene tingakumane nawo.

14-15. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthetsa kukayikira kulikonse kumene tingakhale nako?

14 Vuto limene limakhalapo: Kukayikira zimene timakhulupirira. Nthawi zina anthufe zingativute kumvetsa mfundo inayake ya m’Baibulo kapenanso Yehova sangayankhe mapemphero athu m’njira imene timayembekezera. Zikatere tingayambe kukayikira zimene timakhulupirira. Ngati sitingachitepo kanthu, kukayikira kumeneku kungawononge chikhulupiriro chathu komanso ubwenzi wathu ndi Yehova. (Yak. 1:7, 8) Zimenezi zingachititse kuti tisiye kukhulupirira zimene tikuyembekezera m’tsogolo.

15 Mtumwi Paulo anayerekezera chiyembekezo chathu cham’tsogolo ndi nangula. (Aheb. 6:19) Nangula amathandiza kuti sitima iime malo amodzi panyanja pakachita mafunde komanso kuti isatengeke ndi mphepo n’kukaomba miyala. Komatu nangula amakhala wothandiza ngati tcheni chake chili cholimba. Mofanana ndi mmene dzimbiri limachititsira kuti tcheni cha nangula chikhale chosalimba, nakonso kukayikira kumachititsa kuti chikhulupiriro chathu chifooke. Choncho munthu amene amakayikira akakumana ndi mavuto amasiya kukhulupirira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Ndiye munthu akasiya kukhulupirira sakhalanso ndi chiyembekezo. N’chifukwa chake Yakobo ananena kuti munthu wokayikira “ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo ndi lowindukawinduka.” (Yak. 1:6) Munthu wotereyu sangakhale wosangalala ngakhale pang’ono.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati tikukayikira zimene timakhulupirira?

16 Zimene tingachite: Tizithetsa kukayikira ndipo tizilimbitsa chikhulupiriro chathu. Tikayamba kukayikira tizichitapo kanthu mwamsanga. Mu nthawi ya mneneri Eliya anthu a Yehova anayamba kukayikira zimene ankakhulupirira. Eliya anawauza kuti: “Kodi mukayikakayika mpaka liti? Ngati Yehova ali Mulungu woona m’tsateni, koma ngati Baala ndiye Mulungu woona tsatirani ameneyo.” (1 Maf. 18:21) Zimenezi ndi zimene ifenso tiyenera kuchita masiku ano. Tiyenera kufufuza kuti tipeze umboni wotitsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu, Baibulo ndi Mawu ake komanso kuti a Mboni za Yehova ndi anthu ake. (1 Ates. 5:21) Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tisiye kukayikira komanso tilimbitse chikhulupiriro chathu. Tingapemphenso akulu kuti atithandize kuthetsa zimene tikukayikirazo. Tiyenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuti tipitirizebe kutumikira Yehova mosangalala.

17. Kodi chingachitike n’chiyani ngati titasiya kukhala olimba mtima?

17 Vuto limene limakhalapo: Kufooka. Mawu a Mulungu amati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miy. 24:10) Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “ukafooka” angatanthauzenso “kusiya kuchita zinthu molimba mtima.” Munthu akasiya kuchita zinthu molimba mtima amasiyanso kukhala wosangalala.

18. Kodi kupirira kumatanthauza chiyani?

18 Zimene tingachite: Tizidalira Yehova kuti atithandize kuchita zinthu molimba mtima kuti tipirire. Timafunika kuchita zinthu molimba mtima kuti tipirire mayesero. (Yak. 5:11) Mawu amene Yakobo anagwiritsa ntchito ponena za “kupirira,” akutipangitsa kuganiza za munthu amene waima malo amodzi osasuntha. Tingayerekezere ndi msilikali amene waimabe molimba mtima pamalo ake ndipo sakusuntha kapena kuthawa pamene mdani wake akubwera moopseza.

19. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha mtumwi Paulo?

19 Mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yochita zinthu molimba mtima komanso kupirira. Nthawi zina iye ankafooka koma ankatha kupirira chifukwa ankadalira Yehova kuti azimupatsa mphamvu. (2 Akor. 12:8-10; Afil. 4:13) Ifenso tingapeze mphamvu komanso kuchita zinthu molimba mtima ngati modzichepetsa timazindikira kuti timafunika Yehova kuti atithandize.​—Yak. 4:10.

TINGAPITIRIZE KUKHALA OSANGALALA TIKAKHALA PA UBWENZI NDI MULUNGU

20-21. Kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?

20 Tingakhale otsimikiza kuti mayesero amene timakumana nawo si chilango chochokera kwa Yehova. Yakobo ananena kuti: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yak. 1:13) Tikatsimikizira kuti zimene Yakobo ananenazi ndi zoona, timakhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi.​—Yak. 4:8.

21 Yehova “sasintha.” (Yak. 1:17) Iye anathandiza Akhristu a m’nthawi ya atumwi pa mayesero amene ankakumana nawo ndipo amatithandizanso masiku ano. Tizipempha Yehova mochokera pansi pamtima kuti atithandize kupeza nzeru, chikhulupiriro komanso kuti atithandize kukhala olimba mtima. Iye adzayankha mapemphero athu. Tikatero tidzakhala otsimikiza kuti iye adzatithandiza kukhalabe osangalala pamene tikupirira mayesero amene tikukumana nawo.

NYIMBO NA. 128 Tipirire Mpaka Mapeto

^ ndime 5 Buku la Yakobo lili ndi malangizo ofunika omwe angatithandize tikakumana ndi mayesero. Munkhaniyi tikambirana ena mwa malangizo amene Yakobo anapereka. Malangizo amenewa angatithandize kuti tizipirira tikakumana ndi mavuto n’kumakhalabe osangalala pamene tikutumikira Yehova.

^ ndime 59 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Apolisi amanga m’bale kunyumba kwake. Mkazi ndi mwana wake akuona pamene iwo akumutenga. Pamene m’baleyo ali kundende, abale ndi alongo abwera kunyumba kwake ndipo akuchita kulambira kwa pabanja ndi mkazi ndi mwana wake. Mayi ndi mwana wakeyo akumapemphera kwa Yehova pafupipafupi kuti awapatse mphamvu zotha kupirira mayesero amene akumana nawo. Yehova wawapatsa mtendere wamumtima ndipo wawathandiza kukhala olimba mtima. Zotsatira zake n’zakuti chikhulupiriro chawo chalimba kwambiri, zomwe zawathandiza kuti azipirira mosangalala.