NKHANI YOPHUNZIRA 8
Kodi Malangizo Amene Mumapereka ‘Amasangalatsa Mtima’?
“Mafuta ndi zofukiza zonunkhira n’zimene zimasangalatsa mtima, chimodzimodzinso kukoma kwa mnzako chifukwa cha malangizo ake ochokera pansi pa mtima, kumasangalatsa mtima.”—MIY. 27:9.
NYIMBO NA. 102 “Muthandize Ofookawo”
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. Kodi m’bale wina anaphunzira chiyani pa nkhani yopereka malangizo?
ZAKA zambiri zapitazo, akulu awiri anakayendera mlongo wina yemwe kwa kanthawi sankapita kumisonkhano. Mkulu amene anayamba kulankhula anamuonetsa mlongoyo malemba angapo okhudza kufunika kosonkhana. Ankaganiza kuti amulimbikitsa koma pamene iye ndi mkulu mnzakeyo ankatsanzika mlongoyo anati: “Abale inu simukudziwa mavuto amene ndikukumana nawo.” Abalewo anangomupatsa mlongoyo malangizo osamufunsa kaye mavuto amene akukumana nawo komanso mmene zinthu zinali pa moyo wake. Izi zinachititsa kuti mlongoyo aone kuti malangizo omwe anamupatsawo ndi osathandiza.
2 Poganizira zomwe zinachitika, mkulu amene anali woyamba kulankhulapo uja unanena kuti: “Pa nthawiyo ndinkaganiza kuti mlongoyo anali wamwano. Koma nditaganizira mofatsa, ndinaona kuti ndinangomuonetsa malemba oyenera, m’malo momufunsa mafunso oyenera monga akuti, ‘Kodi mwakhala mukukumana ndi zotani?’ ‘Ndingakuthandizeni bwanji?’” Mkuluyo anaphunzira mfundo yofunika kwambiri pa zimene zinachitikazi. Panopa iye ndi m’busa wabwino amene amachitira ena chifundo komanso kuwathandiza.
3. Kodi ndi ndani angapereke malangizo mumpingo?
3 Monga abusa, akulu ali ndi udindo wopereka malangizo ngati pakufunika kutero. Komabe nthawi zina anthu enanso mumpingo angafunike kupereka malangizo. Mwachitsanzo, m’bale kapena mlongo angapatse mnzake malangizo ochokera m’Baibulo. (Sal. 141:5; Miy. 25:12) Kapena mlongo wachikulire angalangize “akazi achitsikana” pa nkhani ngati zomwe zatchulidwa pa Tito 2:3-5. Komanso makolo nthawi ndi nthawi amafunika kupereka malangizo kwa ana awo. Choncho ngakhale kuti mfundo za munkhaniyi zikukhudza kwambiri akulu, tonsefe tingapindule tikamaganizira njira zomwe tingaperekere malangizo kuti akhale othandiza, olimbikitsa komanso ‘osangalatsa mtima.’—Miy. 27:9.
4. Kodi munkhaniyi tikambirana chiyani?
4 Munkhaniyi tikambirana mafunso 4 pa nkhani yokhudza kupereka malangizo. (1) Kodi tizikhala ndi zolinga zotani tikamapereka malangizo? (2) Kodi pakufunikiradi kupereka malangizo? (3) Kodi ndi ndani ayenera kupereka malangizo? (4) Kodi mungatani kuti muzipereka malangizo othandiza?
KODI TIZIKHALA NDI ZOLINGA ZOTANI?
5. N’chifukwa chiyani anthu siziwavuta kulandira malangizo omwe mkulu wapereka chifukwa cha chikondi? (1 Akorinto 13:4, 7)
5 Akulu amakonda abale ndi alongo awo. Nthawi zina iwo amasonyeza chikondi chimenechi popereka malangizo kwa munthu yemwe wayamba kuyenda panjira yolakwika. (Agal. 6:1) Komabe asanalankhule ndi munthuyo, mkulu angaganizire zinthu zina zokhudza chikondi zomwe mtumwi Paulo anafotokoza. Iye anati: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima. . . . Chimakwirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapirira zinthu zonse.” (Werengani 1 Akorinto 13:4, 7.) Kuganizira kwambiri mavesi a m’Baibulo amenewa, kungathandize mkulu kuti afufuze zolinga zake popereka malangizo komanso kukhala ndi maganizo oyenera akamapereka malangizowo. Munthu yemwe akupatsidwa malangizoyo akazindikira kuti mkuluyo amamukonda, zingakhale zosavuta kuti awalandire.—Aroma 12:10.
6. Kodi mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chabwino chiti?
6 Mtumwi Paulo monga mkulu anapereka chitsanzo chabwino. Mwachitsanzo, iye sanazengereze kupereka malangizo kwa abale a ku Tesalonika pomwe ankafunika kutero. Komabe m’makalata omwe anawalembera, Paulo ankayamba ndi kuwayamikira chifukwa cha chikhulupiriro, ntchito zachikondi, komanso kupirira kwawo. Iye ankaganiziranso mmene zinthu zinalili pa moyo wawo, ndipo mokoma mtima anawatsimikizira kuti ankadziwa za mavuto amene ankakumana nawo komanso kuti ankapirira akamazunzidwa. (1 Ates. 1:3; 2 Ates. 1:4) Anawauzanso kuti iwo anali chitsanzo chabwino kwa Akhristu ena. (1 Ates. 1:8, 9) Iwo ayenera kuti anasangalala kwambiri chifukwa chakuti Paulo anawayamikira. N’zosakayikitsa kuti Paulo ankakonda kwambiri abale akewa. N’chifukwa chake m’makalata ake onse opita kwa Akhristu a ku Tesalonika anatha kuwapatsa malangizo owafika pamtima.—1 Ates. 4:1, 3-5, 11; 2 Ates. 3:11, 12.
7. N’chifukwa chiyani anthu ena zingawavute kulandira malangizo?
7 Kodi n’chiyani chingachitike ngati sitinapereke malangizo m’njira yoyenera? Mkulu wina wodziwa zambiri ananena kuti: “Anthu ena salandira malangizo osati chifukwa choti malangizowo si abwino koma chifukwa choti sanaperekedwe mwachikondi.” Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene ananenazi? Malangizo savuta kuwalandira ngati aperekedwa chifukwa cha chikondi osati chifukwa chokwiya.
KODI PAKUFUNIKIRADI KUPEREKA MALANGIZO?
8. Kodi mkulu ayenera kudzifunsa mafunso ati asanapereke malangizo?
8 Akulu ayenera kuchita zinthu modekha pa nkhani yopereka malangizo. Asanapereke malangizo, mkulu ayenera kudzifunsa kaye kuti: ‘Kodi ndikuyeneradi kulankhulapo chilichonse? Kodi ndatsimikizira kuti zimene munthuyu akuchita n’zolakwika? Kodi pali lamulo lililonse la m’Baibulo limene laphwanyidwa? Kapena kodi ndikungosiyana naye mmene ndimaonera zinthu?’ Akulu amachita zinthu mwanzeru popewa kukhala ‘opupuluma m’mawu awo.’ (Miy. 29:20) Ngati mkulu sali wotsimikiza kuti pakufunikadi kupereka malangizo kwa winawake, angafunse mkulu wina kuti amuthandize kuona ngati zimene munthuyo wachita zikusemphanadi ndi mfundo za m’Malemba.—2 Tim. 3:16, 17.
9. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Paulo pa nkhani yokhudza zovala ndi kudzikongoletsa? (1 Timoteyo 2:9, 10)
9 Taganizirani izi: Tiyerekeze kuti mkulu akudera nkhawa ndi zimene Mkhristu wina amasankha pa nkhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa. Mkuluyo angadzifunse kuti, ‘Kodi pali mfundo iliyonse ya m’Malemba imene ingandichititse kulankhulapo?’ Pofuna kupewa kulankhula za m’maganizo mwake, iye angafunse maganizo kwa mkulu wina kapena Mkhristu wolimba mwauzimu. Kenako angafufuzire limodzi malangizo a Paulo okhudza zovala ndi kudzikongoletsa. (Werengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) Paulo anafotokoza mfundo zina zikuluzikulu zosonyeza kuti Mkhristu ayenera kuvala moyenera, mwaulemu komanso moganiza bwino. Koma sanatchule zimene munthu ayenera kuvala ndi zimene sayenera kuvala. Iye ankazindikira kuti Mkhristu aliyense payekha ali ndi ufulu wosankha zinthu zimene amakonda zomwe sizisemphana ndi mfundo za m’Malemba. Choncho akafuna kuona ngati pakufunika kupereka malangizo kapena ayi, akulu angachite bwino kuona ngati zimene munthu wasankha zikusonyeza kuti akuchita zinthu mwaulemu komanso moganiza bwino.
10. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani kuti tizilemekeza zimene ena amasankha?
10 Tingachite bwino kumakumbukira kuti Akhristu awiri olimba mwauzimu angasankhe zinthu ziwiri zosiyana koma zonsezo n’kukhala zovomerezeka. Sitiyenera kukakamiza Akhristu anzathu kuti azichita zimene ifeyo tikuona kuti n’zolondola.—Aroma 14:10.
KODI NDI NDANI AYENERA KUPEREKA MALANGIZO?
11-12. Ngati pakufunika kupereka malangizo, kodi mkulu angadzifunse mafunso ati, nanga n’chifukwa chiyani?
11 Ngati zikuoneka kuti winawake akufunika kupatsidwa malangizo, funso lina lofunika kuliganizira ndi lakuti, Kodi ndi ndani ayenera kupereka malangizowo? Ngati mkazi kapena mwana wa m’bale akufunika kupatsidwa malangizo, mkulu angachite bwino kufunsa mutu wa banja yemwe mwina angafune kuti asamalire nkhaniyo yekha. * Kapenanso mwamuna yemwe ndi mutu wa banja angafune kukhalapo pamene mkulu akupereka malangizo. Ndipo monga mmene tinaonera mu ndime 3, nthawi zina zimakhalanso bwino kuti mlongo wachikulire apereke malangizo kwa mlongo wachitsikana.
12 Palinso mfundo ina yofunika kuiganizira. Mkulu angadzifunse kuti, ‘Kodi ndine woyenera kupereka malangizowa, kapena zingakhale bwino kwambiri ataperekedwa ndi munthu wina?’ Mwachitsanzo, ngati munthu wina amavutika ndi maganizo odziona kuti ndi wosafunika, angalandire bwino malangizo kuchokera kwa mkulu yemwe anakumana ndi vuto ngati lakelo. N’zodziwikiratu kuti mkulu woteroyo angapereke malangizowo mwachifundo ndipo zimene anganene, munthu winayo sangavutike kuzivomereza. Komabe akulu onse ali ndi udindo wolimbikitsa abale ndi alongo awo kuti azisintha zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. Choncho chofunika kwambiri ndi kupereka malangizo ngakhale kuti mkulu amene akupereka malangizoyo sanakumanepo ndi vuto limene munthuyo wakumana nalo.
KODI MUNGATANI KUTI MUZIPEREKA MALANGIZO OTHANDIZA?
13-14. N’chifukwa chiyani mkulu ayenera kumvetsera kaye asanapereke malangizo?
13 Muzikhala okonzeka kumvetsera. Mkulu akamakonzekera kuti akapereke malangizo ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndikudziwa zotani zokhudza m’baleyo? Kodi n’chiyani chikumuchitikira pa moyo wake? Kodi mwina akukumana ndi mavuto omwe ineyo sindikuwadziwa? Kodi chimene akufunikira kwambiri panopa n’chiyani?’
14 Aliyense amene akufuna kupereka malangizo angachite bwino kuganizira mfundo ya pa Yakobo 1:19. Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” Mkulu angaganize kuti akudziwa mfundo zonse zokhudza nkhaniyo, koma kodi akudziwadi zonse? Lemba la Miyambo 18:13 limatikumbutsa kuti: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.” Choncho zingakhale bwino kuti munthuyo afotokoze yekha mmene zinthu zilili. Mkulu ayenera kumvetsera asanayambe kulankhula. Kumbukirani phunziro limene mkulu amene watchulidwa kumayambiriro kwa nkhaniyi anapeza. Iye anazindikira kuti m’malo mongoyamba kufotokoza mfundo zimene anakonzekera, anafunika kufunsa mlongoyo mafunso ngati awa: “Kodi mwakhala mukukumana ndi zotani?” “Ndingakuthandizeni bwanji?” Ngati akulu atamayesetsa kupeza mfundo zonse, n’zosakayikitsa kuti angathandize komanso kulimbikitsa kwambiri abale ndi alongo awo.
15. Kodi akulu angagwiritse ntchito bwanji mfundo ya pa Miyambo 27:23?
15 Muzidziwa bwino nkhosa. Monga mmene taonera kumayambiriro kwa nkhaniyi, kupereka malangizo othandiza kumaphatikizapo zambiri osati kungowerenga malemba angapo kapena kunena mfundo zina. Abale ndi alongo athu amafunika aziona kuti timawakonda, kuwamvetsa komanso kuti tikufunitsitsa kuwathandiza. (Werengani Miyambo 27:23.) Akulu ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti azigwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo awo.
16. Kodi n’chiyani chingathandize akulu kuti azipereka malangizo othandiza?
16 Akulu ayenera kupewa kuchititsa abale ndi alongo kuganiza kuti amangofuna kulankhula nawo pa nthawi yokhayo imene akufunika kuwapatsa malangizo. M’malomwake nthawi zonse amalankhula ndi abale ndi alongo powasonyeza kuti amawaganizira akamakumana ndi mavuto. Mkulu wina wodziwa zambiri ananena kuti: “Mukamachita zimenezi mudzakhala nawo pa ubwenzi wabwino kwambiri. Choncho zingadzakhale zosavuta kupereka malangizo pakadzafunika kutero.” Zikatero munthu amene akupatsidwa malangizoyo adzawalandira mosavuta.
17. Kodi ndi pa nthawi iti pamene mkulu amafunikira kwambiri kukhala woleza mtima komanso wokoma mtima?
17 Muzikhala oleza mtima komanso okoma mtima. Kuleza mtima ndiponso kukoma mtima n’kofunika kwambiri makamaka ngati munthu akukana kulandira malangizo a m’Baibulo. Mkulu ayenera kuyesetsa kuti asamakwiye ngati malangizo amene wapereka sakutsatiridwa nthawi yomweyo. Ponena za Yesu, ulosi unaneneratu kuti: “Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa.” (Mat. 12:20) Choncho akamapemphera payekha, mkulu angapemphe Yehova kuti adalitse munthu amene akufunika kupatsidwa malangizoyo komanso kuti amuthandize kumvetsa chifukwa chake akufunikira malangizowo ndi kuwatsatira. Nthawi zina m’bale amene akupatsidwa malangizoyo angafunike nthawi yokwanira kuti aganizire zimene wauzidwa. Ngati mkulu ali woleza mtima komanso wokoma mtima, munthu amene akumuthandizayo sadzasokonedwa ndi mmene malangizowo akuperekedwera, m’malomwake adzaganizira kwambiri malangizo amene akupatsidwawo. Komabe nthawi zonse malangizowo ayenera kukhala ochokera m’Mawu a Mulungu.
18. (a) Kodi tiyenera kukumbukira mfundo iti tikamafuna kupereka malangizo? (b) Mogwirizana ndi chithunzi chimene chili pamwambapa, kodi makolowo akukambirana chiyani?
18 Muziphunzirapo kanthu pa zimene mwalakwitsa. Popeza kuti si ife angwiro, sitingatsatire bwinobwino malangizo onse amene takambirana munkhaniyi. (Yak. 3:2) Tingalakwitse zinthu zina, koma zimenezo zikachitika tiziphunzirapo kanthu pa zimene talakwitsazo. Abale ndi alongo athu akaona kuti timawakonda, sizidzawavuta kuti atikhululukire ngati titalankhula kapena kuchita zinthu zimene zawakhumudwitsa. —Onaninso bokosi lakuti, “ Mawu kwa Makolo.”
KODI TAPHUNZIRA CHIYANI?
19. Kodi tingatani kuti malangizo amene tikupereka azisangalatsa mtima wa abale ndi alongo athu?
19 Monga mmene taonera, si zophweka kupereka malangizo othandiza. Si ife angwiro, chimodzimodzinso anthu amene timawapatsa malangizo. Muzikumbukira mfundo zimene takambirana munkhaniyi. Muzionetsetsa kuti mukupereka malangizo muli ndi zolinga zoyenera. Muzitsimikiziranso ngati malangizo akufunika kuperekedwa komanso ngati inuyo muli oyenera kupereka malangizowo. Musanapereke malangizo muzifunsa mafunso komanso kumvetsera mwatcheru kuti mumvetse zimene munthuyo akukumana nazo. Muziyesa kuona zinthu mmene munthuyo akuzionera. Muzichita zinthu modekha ndipo muzigwirizana kwambiri ndi abale ndi alongo anu. Kumbukirani kuti cholinga chathu sikungopereka malangizo amene ndi othandiza koma amenenso ‘angasangalatse mtima.’—Miy. 27:9.
NYIMBO NA. 103 Abusa Ndi Mphatso za Amuna
^ ndime 5 Si nthawi zonse pamene zimakhala zophweka kupereka malangizo. Ndiye kodi tingatani kuti tiziwapereka m’njira yoti akhale othandiza komanso olimbikitsa kwa ena? Nkhaniyi ithandiza makamaka akulu kuti azipereka malangizo kwa ena mowafika pamtima.
^ ndime 11 Onani nkhani yakuti, “Udindo Umene Akulu Ali Nawo Mumpingo” mu Nsanja ya Olonda ya February 2021.