Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 8

“Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso”

“Khalanibe Oganiza Bwino Ndipo Khalani Maso”

“Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso.”​—1 PET. 5:8.

NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto

ZIMENE TIPHUNZIRE a

1. Kodi Yesu anauza ophunzira ake chiyani zokhudza nthawi ya mapeto, nanga anawachenjeza chiyani?

 KUTATSALA masiku ochepa kuti Yesu aphedwe, ophunzira ake 4 anamufunsa kuti: “Chizindikiro . . . cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mat. 24:3) Ophunzirawo ayenera kuti ankafuna kudziwa chomwe chidzawathandize kudziwa nthawi yomwe Yerusalemu ndi kachisi wake zidzawonongedwe. Poyankha Yesu sanangolankhula za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake, koma analankhulanso zokhudza “mapeto a nthawi ino,” omwe ifeyo tikukhalamo. Ponena za nthawi ya mapeto Yesu anati: “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha.” Kenako anachenjeza ophunzira ake onse kuti ‘akhale tcheru’ ndiponso ‘akhale maso.’​—Maliko 13:32-37.

2. N’chifukwa chiyani zinali zofunika kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi akhalebe maso?

2 Akhristu a Chiyuda m’nthawi ya atumwi ankafunika kukhala maso kuti apulumuke. Yesu anauza otsatira ake zomwe zikanawathandiza kudziwa kuti Yerusalemu ndi kachisi wake zatsala pang’ono kuwonongedwa. Iye anati: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira.” Pa nthawiyo iwo ankafunika kumvera chenjezo la Yesu loti “adzayambe kuthawira kumapiri.” (Luka 21:20, 21) Amene anamvera chenjezoli anapulumuka pamene Aroma anawononga Yerusalemu.

3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

3 Panopa tikukhala m’nthawi ya mapeto a dziko loipali. Choncho nafenso tiyenera kukhalabe oganiza bwino komanso kukhala maso. Munkhaniyi tikambirana chimene chingatithandize kukhalabe oganiza bwino tikamaona zochitika za m’dzikoli. Tionanso zimene tingachite kuti tizisamala ndi zomwe timachita komanso mmene tingagwiritsire ntchito bwino nthawi yatsalayi.

MUZIKHALA OGANIZA BWINO MUKAMAONA ZOCHITIKA ZA M’DZIKO

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi mmene zochitika za m’dzikoli zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo?

4 Pali zifukwa zabwino zotichititsa kukhala ndi chidwi ndi mmene zochitika za m’dzikoli zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anatchula zinthu zosiyanasiyana zomwe zimatithandiza kudziwa kuti mapeto a dziko la Satanali ali pafupi. (Mat. 24:3-14) Mtumwi Petulo anatilimbikitsa kuti tizichita chidwi ndi mmene maulosi akukwaniritsidwira n’cholinga choti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba. (2 Pet. 1:19-21) Buku lomalizira la m’Baibulo limayamba ndi mawu akuti: “Chivumbulutso choperekedwa ndi Yesu Khristu, chimene Mulungu anamupatsa, kuti aonetse akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.” (Chiv. 1:1) Choncho timachita chidwi kwambiri ndi zomwe zikuchitika m’dzikoli kuti tione mmene zikukwaniritsira maulosi a m’Baibulo. Ndipo timafunitsitsa kukambirana ndi ena zochitika zimenezi.

Pokambirana ulosi wa m’Baibulo, kodi tiyenera kupewa chiyani, nanga tizichita chiyani? (Onani ndime 5) b

5. Kodi tiyenera kupewa kuchita chiyani, nanga tizichita chiyani? (Onaninso zithunzi.)

5 Tikamakambirana maulosi a m’Baibulo tizipewa kufotokoza za m’maganizo mwathu. Chifukwa chiyani? Chifukwa sitimafuna kulankhula chilichonse chimene chingasokoneze mgwirizano mumpingo. Mwachitsanzo, mwina tingamve olamulira a mayiko akufotokoza zimene angachite kuti athetse vuto linalake komanso kubweretsa mtendere ndi chitetezo. M’malo mongofotokoza maganizo athu kuti zimenezi zikukwaniritsa ulosi wa pa 1 Atesalonika 5:3, tiyenera kufotokoza mogwirizana ndi mfundo zimene zafalitsidwa posachedwapa. Tikamanena zinthu mogwirizana ndi zimene zili m’mabuku a gulu la Yehova, timathandiza kuti mpingo upitirize kukhala wogwirizana komanso ukhale “ndi maganizo amodzi.”​—1 Akor. 1:10; 4:6.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa 2 Petulo 3:11-13?

6 Werengani 2 Petulo 3:11-13. Mtumwi Petulo anatithandiza kuti tizikhala ndi maganizo oyenera tikamawerenga maulosi a m’Baibulo. Anatilimbikitsa kuti ‘tizikumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Chifukwa chiyani? Osati chifukwa choti tikungofuna kudziwa “tsiku ndi ola” limene Yehova adzamenye nkhondo ya Aramagedo. Koma chifukwa chakuti tikufuna kugwiritsa ntchito nthawi yomwe yatsalayi kuti tikhale anthu ‘akhalidwe loyera ndipo tizichita ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’ (Mat. 24:36; Luka 12:40) M’mawu ena tinganene kuti timafuna kuchita zoyenera komanso kuonetsetsa kuti tikuchita khama potumikira Yehova chifukwa chakuti timamukonda kwambiri. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumasamala ndi zimene timachita.

KODI KUKHALA OSAMALA NDI MMENE TIMACHITIRA ZINTHU KUMATANTHAUZA CHIYANI?

7. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timasamala ndi mmene timachitira zinthu? (Luka 21:34)

7 Yesu anauza ophunzira ake kuti ayenera kukhala osamala osati ndi zochitika za m’dzikoli zokha komanso ndi mmene amachitira zinthu. Mfundo imeneyi ikuonekera bwino pa chenjezo lomwe anapereka pa Luka 21:34. (Werengani.) Palembali Yesu anati: “Samalani.” Munthu amene akusamala, amakhala tcheru ndi zinthu zomwe zingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova ndipo amayesetsa kuzipewa. Akamachita zimenezi amapitiriza kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kumukonda.​—Miy. 22:3; Yuda 20, 21.

8. Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo otani kwa Akhristu?

8 Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azisamala ndi zimene amachita. Mwachitsanzo, anauza Akhristu a ku Efeso kuti: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru.” (Aef. 5:15, 16) Nthawi zonse Satana amayesetsa kuti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho Baibulo limatilangiza kuti tipitirize “kuzindikira chifuniro cha Yehova” n’cholinga choti tidziteteze ku misampha yake.​—Aef. 5:17.

9. Kodi tingadziwe bwanji zimene Yehova amafuna kuti tizichita?

9 Baibulo silitchula zinthu zonse zomwe zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Nthawi zonse timafunika kusankha tokha zochita pa nkhani zomwe sizinafotokozedwe mwachindunji m’Malemba. Kuti tisankhe zinthu mwanzeru timafunika kudziwa kapena kuti kuzindikira “chifuniro cha Yehova.” Tingachite zimenezo ngati nthawi zonse timaphunzira komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu. Tikamayesetsa kumvetsa chifuniro cha Yehova komanso kukhala ndi “maganizo a Khristu,” m’pamenenso timayenda “ngati anzeru” ngakhale kuti tilibe malamulo otiuza zochita pa nkhani iliyonse. (1 Akor. 2:14-16) Nthawi zina zimakhala zosavuta kudziwa zinthu zoyenera kuzipewa, koma nthawi zina zimakhala zovuta.

10. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tiyenera kupewa?

10 Zinthu zina zimene tiyenera kupewa ndi monga kukopana, kuledzera, kudya kwambiri, kulankhula mawu omwe angakhumudwitse ena komanso kuonera zosangalatsa zachiwawa, zolaula ndi zinthu zina zotere. (Sal. 101:3) Mdani wathu Mdyerekezi nthawi zonse amafunafuna mipata yoti awononge ubwenzi wathu ndi Yehova. (1 Pet. 5:8) Ngati sitingakhale maso, Satana angadzale m’mitima mwathu mbewu za nsanje, chinyengo, dyera, chidani, kudzikuza komanso mkwiyo. (Agal. 5:19-21) Poyamba zinthu zimenezi zingaoneke ngati zosaopsa. Koma ngati sitingachitepo kanthu mwamsanga kuzizula mumtima mwathu, zingapitirize kukula ngati chomera chakupha ndipo zingayambitse mavuto.​—Yak. 1:14, 15.

11. Kodi ndi vuto lina losaonekera liti lomwe tiyenera kupewa, nanga n’chifukwa chiyani?

11 Vuto lina losaonekera ndi kugwirizana ndi anthu oipa. Taganizirani zochitika ngati izi. Tiyerekeze kuti mumagwira ntchito ndi munthu yemwe si Mkhristu mnzanu. Pofuna kuthandiza mnzanuyo kuti aziona moyenera a Mboni za Yehova, mukuyesetsa kukhala okoma mtima komanso kumuthandiza. Komanso nthawi zambiri akakupemphani kuti mukadyere limodzi chakudya cha masana mumavomera. Posapita nthawi, mwayamba kumachita zimenezi pafupipafupi. Kenako mnzanuyo wayamba kumalankhula nkhani zosayenera zomwe poyamba mukudana nazo. M’kupita kwa nthawi mwafika pongozizolowera moti simukudana nazonso. Kenako tsiku lina mnzanuyo wakupemphani kuti mukaweruka mukamwere limodzi chakumwa ndipo mwavomera. Pang’ono ndi pang’ono mwayamba kuona kuti mukugwirizana kwambiri ndi mnzanuyo. Zikatere, kodi mukuganiza kuti pangatenge nthawi yaitali bwanji kuti muyambe kutengera zochita zake? N’zoona kuti timafuna kukomera mtima komanso kulemekeza anthu onse. Koma tizikumbukira kuti timatengera zochita za anthu amene timacheza nawo kwambiri. (1 Akor. 15:33) Tikamasamala ndi mmene timachitira zinthu monga mmene Yesu anatilangizira, tidzapewa kugwirizana ndi anthu amene satsatira mfundo za Yehova. (2 Akor. 6:15) Tidzaona vuto lomwe lingakhalepo ndipo tidzalipewa.

MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO NTHAWI YANU

12. Kodi ophunzira a Yesu ankafunika kuchita chiyani poyembekezera kuti mapeto afike?

12 Ophunzira a Yesu sankafunika kumangokhala pamene ankayembekezera kuti mapeto afike. Iye anawapatsa ntchito yoti azigwira. Anawalamula kuti azilalikira uthenga wabwino “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:6-8) Imeneyitu inali ntchito yaikulu kwambiri. Iwo ankagwiritsa ntchito bwino nthawi yawo pamene ankadzipereka pogwira ntchitoyi.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu? (Akolose 4:5)

13 Werengani Akolose 4:5. Kuti tizisamala ndi mmene timachitira zinthu, tiyenera kuganizira mmene timagwiritsira ntchito nthawi yathu. “Zinthu zosayembekezereka” zingagwere tonsefe. (Mlal. 9:11) Mwachitsanzo tingathe kumwalira mosayembekezereka.

Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu? (Onani ndime 14-15)

14-15. Kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito bwino nthawi yathu? (Aheberi 6:11, 12) (Onaninso chithunzi.)

14 Tingagwiritse ntchito bwino nthawi yathu pomachita chifuniro cha Yehova, komanso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. (Yoh. 14:21) Tiyenera kukhala “olimba, osasunthika, okhala ndi zochita zambiri nthawi zonse mu ntchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) Tikamachita zimenezi, mapeto akafika, kaya ndi mapeto a moyo wathu kapena a dziko loipali, sitidzanong’oneza bondo kuti sitinachite zambiri potumikira Yehova.​—Mat. 24:13; Aroma 14:8.

15 Masiku ano, Yesu akupitiriza kutsogolera ophunzira ake pamene akulalikira za Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Iye akukwaniritsa zomwe analonjeza. Kudzera m’gulu la Yehova, Yesu amatiphunzitsa mmene tingamalalikirire komanso amatipatsa zonse zotithandiza pogwira ntchitoyi. (Mat. 28:18-20) Timachita mbali yathu tikamagwira mwakhama ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu komanso kukhalabe maso pamene tikuyembekezera kuti Yehova awononge dziko loipali. Tikamatsatira malangizo a pa Aheberi 6:11, 12, chiyembekezo chathu chidzakhala “chotsimikizika mpaka mapeto.”​—Werengani.

16. Kodi ndife otsimikiza mtima kuchita chiyani?

16 Yehova anakhazikitsa tsiku ndi nthawi yomwe adzawononge dziko lolamuliridwa ndi Satanali. Tsikulo likadzafika, Yehova sadzalephera kukwaniritsa maulosi onse omwe analemba m’Mawu ake. Nthawi zina tingamaone ngati mapeto akuchedwa. Komabe tsiku la Yehova ‘silidzachedwa.’ (Hab. 2:3) Choncho tiyeni tikhale otsimikiza mtima kuti ‘tidzadikirira Yehova’ komanso kusonyeza kuti ‘tikuyembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso chathu.’​—Mika 7:7.

NYIMBO NA. 139 Yerekezerani Kuti Muli M’dziko Latsopano

a Munkhaniyi tikambirana zimene zingatithandize kukhalabe oganiza bwino komanso kupitirizabe kukhala maso. Kuwonjezera pamenepo, tionanso zimene tingachite kuti tizisamala ndi zimene timachita komanso mmene tingagwiritsire ntchito bwino nthawi yathu.

b MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: (Pamwamba) Banja likuonera nkhani. Kenako pambuyo pa misonkhano akuuza ena maganizo awo pa za tanthauzo la zomwe amaonerazo. (M’munsi) Banja likuonera lipoti la Bungwe Lolamulira kuti limvetse mmene ulosi wina wa m’Baibulo wafotokozedwera chaposachedwapa. Akugawira ena mabuku othandiza pophunzira Baibulo ochokera kwa kapolo wokhulupirika.