Mfundo Zothandiza Pophunzira
Muzifufuza Mfundo Zothandiza Zomwe Mungagwiritse Ntchito
Tikamawerenga Baibulo, tingathe kupeza mfundo zothandiza pofufuza zambiri zokhudza nkhani yomwe tikuwerenga. Ndiye kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri?
Muzifufuza mozama nkhani za m’Baibulo. Mwachitsanzo, muzifufuza kuti mudziwe amene analemba, amene ankawalembera komanso nthawi yomwe analemba zinthuzo. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawiyo, n’chiyani chinachitika asanalembe zinthuzo, nanga chinachitika n’chiyani pambuyo pake?
Muziganizira zimene mukuphunzirapo pofufuza mayankho a mafunso ngati awa: ‘Kodi anthu otchulidwawo ankamva bwanji? Kodi anasonyeza makhalidwe ati? N’chifukwa chiyani ndiyenera kutsanzira makhalidwewo kapena kuwapewa?’
Muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo mu utumiki kapenanso pochita zinthu ndi ena. Mukamachita zimenezi, mumasonyeza nzeru ya Mulungu, monga mmene Baibulo limanenera kuti: “Aliyense wanzeru aona zinthu zimenezi.”—Sal. 107:43.
-
Zokuthandizani: Muziona mmene nkhani za pamisonkhano ya mkati mwa mlungu pa gawo lakuti Chuma Chopezeka M’mawu a Mulungu, zimatithandizira kugwiritsa ntchito zimene taphunzira. Nthawi zambiri nkhanizi zimakhala ndi mafunso omwe tingadzifunse, mfundo zomwe tingaganizire komanso zithunzi.