Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 7

NYIMBO NA. 51 Tinadzipereka kwa Mulungu

Zimene Tingaphunzire kwa Anaziri

Zimene Tingaphunzire kwa Anaziri

“Iye ndi woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake.”​—NUM. 6:8.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Tiona mmene chitsanzo cha Anaziri chingatithandizire kuti tikhale olimba mtima komanso odzimana potumikira Yehova.

1. Kuyambira kale, kodi atumiki a Yehova akhala akuchita chiyani posonyeza kuti amamukonda?

 KODI mumakonda kwambiri Yehova? N’zosachita kufunsa. Ndipo dziwani kuti si inu nokha amene mumamukonda. Kuyambira kale, anthu osawerengeka akhalanso akumukonda ngati mmene inuyo mumachitira. (Sal. 104:33, 34) Ambiri akhala akudzimana zinazake kuti azilambira Yehova. Izi ndi zimenenso Aisiraeli otchedwa Anaziri ankachita. Kodi iwo anali ndani, nanga tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chawo?

2. Kodi Anaziri anali ndani? (Numeri 6:1, 2) (b) N’chifukwa chiyani Aisiraeli ena ankapanga lonjezo lokhala Anaziri?

2 Mawu akuti “Mnaziri” ndi ochokera ku Chiheberi ndipo amatanthauza “Wopatulidwa” kapena “Wodzipereka.” Mawuwa amanena za Mwisiraeli wakhama amene ankadzimana zinthu zina n’cholinga choti azitumikira Yehova m’njira yapadera. Chilamulo cha Mose chinkalola kuti mwamuna kapena mkazi achite lonjezo lapadera kwa Yehova losankha kukhala Mnaziri kwa nthawi inayake. a (Werengani Numeri 6:1, 2.) Munthu amene wapanga lonjezoli ankafunika kutsatira malamulo enaake mosiyana ndi Aisiraeli anzake. Ndiye kodi n’chiyani chinkachititsa kuti Mwisiraeli apange lonjezoli? Ayenera kuti ankapanga lonjezoli chifukwa chokonda kwambiri Yehova komanso kuyamikira madalitso omwe ankamupatsa.​—Deut. 6:5; 16:17.

3. Kodi anthu a Yehova masiku ano amafanana bwanji ndi Anaziri?

3 Unaziri unatha Chilamulo cha Mose chitalowedwa m’malo ndi “chilamulo cha Khristu.” (Agal. 6:2; Aroma 10:4) Komabe mofanana ndi Anaziri, anthu a Yehova masiku ano amapitiriza kusonyeza kuti ndi ofunitsitsa kumutumikira ndi mtima wonse, moyo wawo wonse, maganizo awo onse komanso ndi mphamvu zawo zonse. (Maliko 12:30) Mofunitsitsa, timalonjeza zimenezi tikamadzipereka kwa Yehova. Kuti tikwaniritse lonjezoli, timafunika kuchita chifuniro cha Yehova komanso kudzimana zinthu zina. Tikamakambirana zimene Anaziri ankachita kuti akwaniritse lonjezo lawo, tiphunzira zimene ifenso tingachite kuti tizikwaniritsa lonjezo lathu. b (Mat. 16:24) Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

MUZIKHALA ODZIMANA

4. Mogwirizana ndi Numeri 6:3, 4, kodi Anaziri ankalolera kudzimana zinthu ngati ziti?

4 Werengani Numeri 6:3, 4. Anaziri sankayenera kumwa mowa kapena kudya zilizonse zochokera ku mphesa. Aisiraeli ena onse ankamwa komanso kudya zinthu ngati zimenezi chifukwa panalibe cholakwika ndi zinthuzi. Ndipotu Baibulo limafotokoza kuti “vinyo . . . amasangalatsa mtima wa munthu” ndipo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Sal. 104:14, 15) Koma mofunitsitsa, Anaziri ankalolera kudzimana zinthu ngati zimenezi. c

Kodi ndinu ofunitsitsa kudzimana zinazake ngati mmene ankachitira Anaziri? (Onani ndime 4-6)


5. Kodi Madián ndi Marcela analolera kusiya zinthu ziti, nanga n’chifukwa chiyani?

5 Mofanana ndi Anaziri, timadzimana zinthu zina kuti tizichita zambiri potumikira Yehova. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Madián ndi Marcela. d Banjali linkakhala moyo wawofuwofu. Madián ankagwira ntchito yabwino zomwe zinachititsa kuti azikhala m’nyumba yokongola. Komabe iwo ankafuna kuti azichita zambiri potumikira Yehova. Kuti zimenezi zitheke, anaganiza zosintha zinthu zina. Iwo anati: “Tinayamba kuchepetsa zinthu zomwe tinkagula. Tinagulitsa galimoto yathu ndipo tinasamukira m’nyumba yaing’ono.” Madián ndi Marcela anasankha zimenezi chifukwa ankafuna kuwonjezera utumiki wawo, osati chifukwa chakuti ndi zimene ankafunika kuchita. Iwo amasangalala kwambiri chifukwa cha zimene anasankha.

6. N’chifukwa chiyani Akhristu masiku ano amalolera kudzimana zinthu zina? (Onaninso chithunzi.)

6 Akhristu masiku ano amasangalala chifukwa cholera kusiya zinthu zina n’cholinga choti azikhala ndi nthawi yambiri yotumikira Yehova. (1 Akor. 9:3-6) Sikuti Yehova amayembekezera kuti tizidzimana zinthu zinazake, komanso zinthu zimene timalolera kudzimanazo pazokha si zolakwika. Mwachitsanzo, ena amalolera kusiya ntchito yabwino, nyumba ngakhalenso ziweto zimene amazikonda. Ambiri asankha kusakwatira msanga kapena kusakhala ndi ana. Ena amasankha kupita kumene kukufunikira olalikira ambiri ngakhale kuti izi zimachititsa kuti atalikirane ndi achibale awo. Mofunitsitsa, ambirife timalolera kusiya zinthu ngati zimenezi chifukwa chofuna kupatsa Yehova zinthu zabwino kwambiri. Musamakayikire kuti Yehova amasangalala kwambiri mukalolera kudzimana zinthu zina, kaya zazikulu kapena zazing’ono, n’cholinga choti muzimutumikira.​—Aheb. 6:10.

MUZIYESETSA KUKHALA OSIYANA NDI ENA

7. N’chiyani chinkachititsa kuti zikhale zovuta kwa Mnaziri kuti asunge lonjezo lake? (Numeri 6:5) (Onaninso chithunzi.)

7 Werengani Numeri 6:5. Anaziri ankalonjeza kuti sadzameta tsitsi lawo. Imeneyi inali njira yosonyezera kuti adzipereka kotheratu kwa Yehova. Mwisiraeli akakhala Mnaziri kwa nthawi yaitali, tsitsi lake linkatalika kwambiri moti anthu ena ankatha kuzindikira zimenezi. Aisiraeli ena akamalemekeza komanso kulimbikitsa Mnaziriyo, zinkakhala zosavuta kuti apitirize kukwaniritsa lonjezo lake. Koma n’zomvetsa chisoni kuti pa nthawi ina Aisiraeli sankalemekeza kapena kuthandiza Anaziri. M’nthawi ya mneneri Amosi, Aisiraeli ampatuko ‘ankapatsa Anaziri vinyo kuti amwe,’ ndipo n’kutheka kuti ankachita zimenezi pofuna kuwachititsa kuti aswe lonjezo lawo lopewa kumwa vinyo. (Amosi 2:12) Nthawi zina Mnaziri ankafunika kulimba mtima kwambiri kuti akwaniritse lonjezo lake n’kukhalabe wosiyana ndi ena.

Mnaziri yemwe ankakwaniritsa lonjezo lake ankalolera kukhala wosiyana ndi ena (Onani ndime 7)


8. Kodi zimene zinachitikira Benjamin zakulimbikitsani bwanji?

8 Mothandizidwa ndi Yehova, ifenso tingathe kulimba mtima n’kukhala osiyana ndi ena, ngakhale kuti mwachibadwa tingakhale amanyazi kapena amantha. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi wa Mboni wina wa zaka 10 wa ku Norway dzina lake Benjamin. Kusukulu kwawo kunali zochitika zomwe cholinga chake chinali kulimbikitsa anthu a ku Ukraine komwe kunali nkhondo. Ana a sukuluwo anauzidwa kuti aimbe nyimbo atavala zovala zokhala ndi mitundu ya mbendera ya ku Ukraine. Iye anakonza zokhala chapatali ndi pamene pankachitika zinthuzo n’cholinga choti asachite nawo. Komabe mphunzitsi wina anamuona ndipo anamuitana kuti: “Bwera kuno udzaimbe nawo, tonse tikudikira iweyo.” Molimba mtima Benjamin anapita kwa mphunzitsiyo n’kukamuuza kuti: “Sindichita nawo zionetsero zilizonse zandale, ndipo a Mboni za Yehova ambiri ali m’ndende chifukwa chokana kumenya nawo nkhondo.” Mphunzitsiyo anamvetsera zimene Benjamin anafotokoza ndipo anamulola kuti asachite nawo. Komabe anzake a m’kalasi anayamba kumufunsa chifukwa chake sanachite nawo zinthuzo. Benjamin anachita mantha kwambiri moti anatsala pang’ono kulira. Komabe molimba mtima kwambiri anabwerezera kalasi yonseyo zomwe anauza mphunzitsiyo. Pambuyo pake iye anauza makolo ake kuti anaona kuti Yehova anamuthandiza kuti alimbe mtima n’kufotokoza zimene amakhulupirira.

9. Kodi tingatani kuti tizisangalatsa mtima wa Yehova?

9 Chifukwa chakuti timasankha kuchita chifuniro cha Yehova, timakhala osiyana ndi anthu a m’dzikoli. Timafunika kulimba mtima kuti tizidziwikitse kuti ndife a Mboni za Yehova tikakhala kuntchito kapena kusukulu. Komanso pamene zochitika ndi makhalidwe a m’dzikoli zikuipiraipira, nthawi zina zingakhale zovuta kuti tizitsatira mfundo za m’Baibulo komanso kuuza ena uthenga wabwino. (2 Tim. 1:8; 3:13) Komabe tingachite bwino kumakumbukira kuti ‘timasangalatsa mtima wa [Yehova]’ tikapitiriza kukhala olimba mtima n’kumasonyeza kuti ndife osiyana ndi anthu omwe samutumikira.​—Miy. 27:11; Mal. 3:18.

MUZIIKA YEHOVA PAMALO OYAMBA

10. Kodi kutsatira lamulo la pa Numeri 6:6, 7 kunali kovuta bwanji kwa Anaziri?

10 Werengani Numeri 6:6, 7. Anaziri sankayenera kuyandikira munthu wakufa. N’kutheka kuti mukuganiza kuti imeneyi siinali nkhani yaikulu. Koma kalelo, zinkakhala zovuta kwa Mnaziri makamaka ngati amene wamwalirayo ndi wachibale wake wapafupi. Pa nthawiyo, miyambo ya maliro inkaphatikizapo kukhala pafupi ndi thupi la womwalirayo. (Yoh. 19:39, 40; Mac. 9:36-40) Koma lonjezo limene Mnaziri ankachita linkapangitsa kuti asatsatire miyambo ngati imeneyi. Ngakhale pochita zinthu ndi achibale pa nthawi yovuta yachisoniyo, Mnaziri ankasonyeza chikhulupiriro champhamvu posungabe lonjezo lake. Mosakayikira, Yehova ankalimbikitsa atumiki ake odziperekawa kuti athe kupirira mavuto omwe ankakumana nawo.

11. Kodi Mkhristu ayenera kukhala wotsimikiza kuchita chiyani akamachita zinthu ndi achibale ake? (Onaninso chithunzi.)

11 Monga Akhristu, sitimaona mopepuka lonjezo lathu lodzipereka kwa Yehova. Zimenezi zingakhudze zosankha komanso zochita zathu pa nkhani zokhudza achibale. Timayesetsa kukwaniritsa mosamala udindo wathu wa m’Malemba wosamalira achibale athu, koma sitilola kuti zofuna za achibale athuwo zitilepheretse kuchita zimene Yehova amafuna. (Mat. 10:35-37; 1 Tim. 5:8) Nthawi zina zimenezi zingachititse kuti tisankhe zinthu zomwe achibale athuwo sangasangalale nazo, koma zingasangalatse Yehova.

Kodi ndinu wofunitsitsa kuika chifuniro cha Yehova pamalo oyamba, ngakhale pa nthawi yovuta kwambiri? (Onani ndime 11) e


12. Pamene ankachita zinthu ndi mkazi wake, kodi Alexandru anachita chiyani, nanga sanachite chiyani?

12 Taganizirani zimene zinachitikira Alexandru ndi mkazi wake Dorina. Banjali litaphunzira Baibulo kwa chaka, Dorina anasiya kuphunzira ndipo ankafunanso kuti mwamuna wake asiye. Koma mwaulemu ndiponso modekha iye anamuuza kuti apitiriza kuphunzira. Dorina sanasangalale nazo ndipo anayesetsa kumukakamiza kuti asiye. Alexandru ankayesetsa kumvetsa mmene mkazi wake ankamvera koma sizinali zophweka kwa iye. Nthawi zina Dorina akamamulankhula mwaukali iye ankaona kuti mwina bola angosiya kuphunzira. Komabe Alexandru anapirira poika Yehova pamalo oyamba ndipo anapitiriza kukonda kwambiri komanso kulemekeza mkazi wakeyo. Pamapeto pake, chitsanzo chake chabwino chinathandiza kuti Dorina ayambirenso kuphunzira Baibulo ndipo patapita nthawi anabatizidwa.​—Onani pa jw.org vidiyo yakuti Alexandru ndi Dorina Vacar: Chikondi N’choleza Mtima Ndiponso N’chokoma Mtima pa gawo lakuti “Mfundo za M’Baibulo Zimasintha Anthu.”

13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova komanso anthu a m’banja lathu?

13 Yehova ndi amene anayambitsa banja ndipo amafuna kuti tizikhala ndi banja losangalala. (Aef. 3:14, 15) Ngati tikufuna kuti tizisangalaladi m’banja lathu tiyenera kumachita zimene Yehova amafuna. Musamakayikire kuti Yehova amasangalala ndi khama lomwe mumachita pomulambira komanso kusamalira anthu a m’banja lanu mwachikondi ndi mwaulemu.​—Aroma 12:10.

TIZILIMBIKITSA ENA KUTI AZIKHALA NGATI ANAZIRI

14. Kodi ndi anthu ati makamaka amene tiyenera kuwalimbikitsa ndi zolankhula zathu?

14 Masiku ano, onse amene amasankha kuti azilambira Yehova ayenera kukhala ofunitsitsa kumutumikira chifukwa chomukonda. Komabe nthawi zina kuchita zimenezi si kophweka. Kodi tingathandize bwanji ena kuti azichita zimenezi? Tiziwalimbikitsa ndi zolankhula zathu. (Yobu 16:5) Kodi pali ena mumpingo mwanu omwe asiya zinthu zina n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Yehova? Kodi mukudziwa achinyamata ena omwe molimba mtima akuyesetsa kuti akhale osiyana ndi anzawo kusukulu, ngakhale kuti kuchita zimenezo n’kovuta? Kodi pali ophunzira Baibulo kapena Akhristu ena omwe akuyesetsa kukhalabe okhulupirika ngakhale kuti akutsutsidwa ndi achibale awo? Tiyenera kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kulimbikitsa Akhristu anzathu okondedwawa powayamikira chifukwa choyesetsa kukhala odzimana komanso olimba mtima.​—Filim. 4, 5, 7.

15. Kodi ena amathandiza bwanji anthu omwe akuchita utumiki wanthawi zonse?

15 Nthawi zina tikhoza kuthandiza Akhristu anzathu omwe akuchita utumiki wanthawi zonse powapatsa zinthu zofunikira. (Miy. 19:17; Aheb. 13:16) Izi ndi zimene mlongo wina wachikulire yemwe amakhala ku Sri Lanka ankafunitsitsa kuchita. Atamuwonjezera ndalama zake za penshoni, anafuna kuthandiza alongo ena awiri achitsikana omwe ankachita upainiya kuti apitirize utumiki wawo, ngakhale kuti m’dziko mwawo munali mavuto azachuma. Choncho anaganiza zoti aziwapatsa ndalama mwezi uliwonse zolipirira mabilu a telefoni. Mlongoyutu anasonyeza mtima wabwino kwambiri.

16. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Anaziri?

16 Kunena zoona, tingaphunzire zambiri pa chitsanzo chabwino cha Anaziri. Komabe lonjezo la Mnaziri limatithandizanso kudziwa zinthu zina zokhudza Atate wathu wakumwamba, Yehova. Iye amadziwa kuti timafuna ndi mtima wonse kumusangalatsa, komanso kuti timafunitsitsa kudzimana zinthu zina n’cholinga choti tikwaniritse lonjezo lathu lomwe tinapanga podzipereka. Iye anatilemekeza potipatsa mwayi woti tizisonyeza patokha kuti timamukonda. (Miy. 23:15, 16; Maliko 10:28-30; 1 Yoh. 4:19) Lonjezo la Mnaziri limasonyeza kuti Yehova amaona komanso amayamikira kudzimana komwe timachita kuti timutumikire. Choncho tiyeni tikhale otsimikiza kuti tipitirizabe kutumikira Yehova komanso kuyesetsa kuchita zomwe tingathe pomupatsa zinthu zabwino kwambiri.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Anaziri ankasonyeza m’njira ziti kuti anali odzimana komanso olimba mtima?

  • Kodi tingalimbikitse bwanji ena masiku ano kuti azikhala ngati Anaziri?

  • Kodi lonjezo la Mnaziri likusonyeza bwanji kuti Yehova amayamikira zimene atumiki ake amachita pomulambira?

NYIMBO NA. 124 Tizikhulupirika Nthawi Zonse

a Ngakhale kuti Anaziri ochepa ankachita kusankhidwa ndi Yehova, Aisiraeli ambiri ankasankha okha kutumikira ngati Anaziri kwa kanthawi.​—Onani bokosi lakuti “ Anaziri Osankhidwa ndi Yehova.”

b Nthawi zina mabuku athu amayerekezera Anaziri ndi atumiki anthawi zonse. Komabe munkhaniyi, tiona mmene atumiki onse odzipereka a Yehova angachitire zinthu ngati Anaziri.

c Zikuoneka kuti Mnaziri sankapatsidwa zochita zina zake monga ngati ntchito n’cholinga choti akwaniritse lonjezo lake.

d Onani pa jw.org nkhani yakuti “Tinasankha Kukhala Moyo Wosalira Zambiri” pa gawo lakuti “Zochitika pa Moyo wa a Mboni za Yehova.”

e MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Ali padenga, Mnaziri akuonerera mwambo wamaliro wa wachibale wake. Chifukwa cha lonjezo lomwe anapanga, iye sangayandikire malirowo.