Funso Losavuta Limene Aliyense Angathe Kufunsa
Mary ndi mwamuna wake John a amakhala m’dziko lina lomwe kumabwera anthu ambiri ochokera ku Philippines kudzagwira ntchito. Iwo amakhala ndi mwayi wolalikira uthenga wabwino kwa anthu amenewa. Pa nthawi ya mliri wa COVID-19, Mary anayambitsa maphunziro a Baibulo, osati ndi anthu a m’dziko limene amakhala lokha, komanso a m’mayiko ena. Kodi anachita bwanji zimenezi?
Mary ankafunsa anthu omwe ankaphunzira nawo Baibulo kuti, “Kodi pali aliyense amene mukumudziwa amene angakonde kuphunzira Baibulo?” Akananena kuti inde, ankawapempha ngati angamuthandize kuti adziwane nawo. Nthawi zambiri kufunsa funso losavutali kunkakhala ndi zotsatirapo zabwino. Tikutero chifukwa anthu amene amakonda Mawu a Mulungu nthawi zambiri amafuna kuuza achibale ndi anzawo zimene akuphunzira. Ndiye kodi kufunsa funso limeneli kunali ndi zotsatirapo zotani?
Munthu wina amene Mary ankaphunzira naye dzina lake Jasmin, anamuthandiza kupeza anthu ena 4 kuti aziphunzira nawo. Mmodzi wa ophunzirawo dzina lake Kristine ankasangalala kwambiri ndi phunzirolo ndipo anapempha Mary kuti aziphunzira naye kawiri pamlungu. Mary atamufunsa Kristine ngati pali anthu enanso amene angakonde kuti aziphunzira Baibulo, iye anayankha kuti, “Inde, pali anzanga ena ndipo ndiwafotokozera za inu.” Patangopita milungu yochepa, Kristine anathandiza Mary kuti aziphunzira ndi anzake ena 4. Pambuyo pake Kristine anathandiza Mary kudziwananso ndi anzake ena omwe nawonso ankadziwitsanso anzawo kuti akhoza kumaphunzira Baibulo.
Kristine ankafunanso kuti achibale ake ku Philippines aphunzire zokhudza Baibulo. Choncho anakambirana ndi mwana wake wamkazi dzina lake Andrea kuti nayenso ayambe kuphunzira. Poyamba Andrea ankaganiza kuti Mboni za Yehova ndi chipembedzo chachilendo, samakhulupirira Yesu komanso amangogwiritsa ntchito chipangano chakale. Koma atangophunzira kamodzi kokha anazindikira kuti zimene ankaganizazo sizinali zoona. Nthawi zonse akamaphunzira ankakonda kunena kuti, “Ngati Baibulo likunena zimenezi, ndiye kuti ndi zoona.”
Patapita nthawi, Andrea anafotokozera Mary zokhudza anzake ena awiri komanso mnzake wina wakuntchito omwe ankafuna kuphunzira Baibulo. Komanso Mary sankadziwa kuti akamaphunzira, azakhali a Andrea dzina lawo a Angela, omwe anali osaona, ankamvetsera. Ndiye tsiku lina azakhaliwo anauza Andrea kuti amuuze Mary kuti nawonso akufuna aziphunzira. Iwo ankasangalala ndi zimene ankaphunzira. Mwezi usanathe, anali ataloweza mavesi ambiri ndipo ankafuna kuti aziphunzira ka 4 pa mlungu. Andrea anathandiza azakhali akewo kuti azichita nawo misonkhano nthawi zonse kudzera pa vidiyokomfelensi.”
Mary atazindikira kuti mwamuna wa Kristine dzina lake Joshua akumakhala chapafupi pa nthawi ya phunzilolo, anamufunsa ngati angakonde kukhala nawo paphunzilolo. Joshua anayankha kuti, “Chabwino, koma ndizingomvetsera. Musandifunse funso lililonse, mukandifunsa ndichokapo.” Pamene inkatha 5 minitsi, iye anali atafunsa mafunso ambiri kuposa Kristine ndipo anayamba kufuna kuti aziphunzira Baibulo.
Funso losavuta lomwe Mary ankafunsa linachititsa kuti akhale ndi maphunziro a Baibulo ambiri. Popeza kuti maphunzirowa anali ambiri, Mary anakonza zoti ophunzira ena aziphunzira ndi a Mboni a kwawoko. Iye anali atayambitsa maphunziro a Baibulo okwana 28 m’mayiko 4.
Jasmin, wophunzira woyamba yemwe watchulidwa munkhaniyi anabatizidwa mu April 2021. Kristine anabatizidwa mu May 2022 ndipo anabwerera ku Philippines kuti akakhale ndi banja lake. Ophunzira enanso awiri omwe Mary anawapeza kudzera mwa Kristine anabatizidwanso. Azakhali a Andrea aja anabatizidwa patangopita miyezi yochepa ndipo panopa ndi mpainiya wokhazikika. Mwamuna wa Kristine, Joshua ndi mwana wake wamkazi, Andrea komanso ophunzira ena ambiri akupitirizabe kuphunzira Baibulo ndipo akuyesetsa kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.
M’nthawi ya atumwi uthenga wabwino unafalikira mwamsanga chifukwa anthu ankalalikira kwa achibale ndi anzawo. (Yoh. 1:41, 42a; Mac. 10:24, 27, 48; 16:25-33) Ndiye bwanji osakonza zoti mufunse amene mumaphunzira nawo Baibulo kapena anthu ena achidwi funso limeneli lakuti, “Kodi pali aliyense amene mukumudziwa yemwe angakonde kuphunzira Baibulo?” N’kutheka kuti mungayambitse maphunziro a Baibulo ambiri chifukwa chongofunsa funso losavuta limeneli, lomwe aliyense angathe kufunsa.
a Mayina ena asinthidw