Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 8

NYIMBO NA. 130 Muzikhululuka

Kodi Tingatsanzire Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?

Kodi Tingatsanzire Bwanji Kukhululuka kwa Yehova?

“Mofanana ndi Yehova amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.”AKOL. 3:13.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tikhululukire munthu amene watilakwira.

1-2. (a) Kodi ndi pa nthawi iti pamene zingakhale zovuta kwambiri kukhululuka? (b) Kodi Denise anachita chiyani posonyeza kukhululuka?

 KODI zimakuvutani kukhululukira ena? Ambirife zimativuta makamaka ngati munthu walankhula kapena kuchita zinthu zimene zatipweteka kwambiri. Komabe n’zotheka kusiya kukwiya n’kumakhululuka. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Denise, a yemwe anasonyeza kukhululuka m’njira yapadera kwambiri. Mu 2017, Denise anapita ndi banja lake kukaona malo kulikulu lathu la Mboni za Yehova lomwe linali litangotsegulidwa kumene. Akubwerera kunyumba, dalaivala wina analephera kuwongolera bwino galimoto yake ndipo anagunda galimoto yawo. Ngoziyo itachitika Denise anakomoka. Atatsitsimuka, anamva kuti ana ake anavulala kwambiri komanso mwamuna wake Brian anafa pangoziyo. Poganizira zimene zinachitikazo, Denise anati: “Ndinakhumudwa ndipo zinandisokoneza kwambiri.” Pambuyo pake iye anamva kuti panalibe chilichonse chimene chinasokoneza dalaivalayo kuti achite ngoziyo ndipo analibe vuto lililonse lokhudza thanzi lake. Choncho anapempha Yehova kuti amuthandize kukhala ndi mtendere.

2 Dalaivala amene anawagundayo anatseguliridwa mlandu wopha munthu mwangozi ndipo zikanapezeka kuti ndi wolakwa, akanatsekeredwa m’ndende. Khoti linanena kuti chigamulo cha mlanduwo chinkadalira umboni umene Denise akanapereka. Denise anati: “Ndinkangomva ngati munthu wang’amba bala langa lomwe linasokedwa n’kuthirapo mchere wambiri chifukwa ndinkafunika kufotokozanso zinthu zoipa zomwe zinachitika.” Patangopita milungu yochepa, Denise anapita kukhoti kukapereka umboni pamaso pa munthu yemwe anachititsa kuti banja lawo likumane ndi mavuto aakulu. Ndiye kodi Denise ananena kuti chiyani? Iye anapempha woweruzayo kuti achitire chifundo dalaivalayo. b Atamaliza kulankhula, woweruzayo anagwetsa misozi ndipo anati: “ Pa zaka 25 zimene ndakhala ndikugwira ntchito imeneyi sindinamvepo zoterezi. Sindinaonepo wolakwiridwa akupempha kuti wolakwa achitiridwe chifundo. Sindinamvepo mawu osonyeza chikondi ndi kukhululuka ngati amenewa.”

3. N’chiyani chinamuthandiza Denise kuti akhululuke?

3 Kodi n’chiyani chinathandiza Denise kuti akhululuke? Iye anaganizira za kukhululuka kwa Yehova. (Mika 7:18) Tikamayamikira zimene Yehova anachita potikhululukira, zingatithandize kuti ifenso tizikhululukira ena.

4. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani? (Aefeso 4:32)

4 Yehova amafuna kuti tizikhululukira ena ndi mtima wonse ngati mmene iyenso amachitira. (Werengani Aefeso 4:32.) Iye amayembekezera kuti tizikhululukira anthu amene atilakwira. (Sal. 86:5; Luka 17:4) Munkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene zingatithandize kuti tizikhululuka ndi mtima wonse.

MUSAMANYALANYAZE MMENE MUKUMVERA

5. Mogwirizana ndi Miyambo 12:18, kodi timamva bwanji munthu wina akatilakwira?

5 Tingakhumudwe kwambiri chifukwa cha zimene wina walankhula kapena kuchita makamaka ngati munthuyo ndi mnzathu wapamtima kapena wachibale wathu. (Sal. 55:12-14) Nthawi zina ululu umene timamva umayerekezeredwa ndi kubayidwa ndi mpeni. (Werengani Miyambo 12:18.) Tingayesetse kunyalanyaza mmene tikumvera koma kuchita zimenezi kungafanane ndi kusiya mpeni pabala pomwepo. Mofanana ndi zimenezi, sitingayembekezere kuti tiyamba kumva bwino pongonyalanyaza mmene tikumvera.

6. Kodi nthawi zambiri timatani munthu wina akatilakwira?

6 Chinthu choyamba chimene nthawi zambiri timachita munthu akatikhumudwitsa ndi kukwiya. Baibulo limavomereza kuti tingathe kukwiya. Koma limatichenjeza kuti tisamalole kuti mkwiyo uzitilamulira. (Sal. 4:4; Aef. 4:26) Chifukwa chiyani? Chifukwa nthawi zambiri timachita zinthu potengera mmene tikumvera. Ndipo kukwiya sikukhala ndi zotsatirapo zabwino. (Yak. 1:20) Kumbukirani kuti kukwiya kumangochitika kokha, koma timachita kusankha kuti tikhalebe okwiya.

Kukwiya kumangochitika kokha, koma timachita kusankha kuti tikhalebe okwiya

7. Kodi nthawi zina timamvanso bwanji ena akatikhumudwitsa?

7 Tikachitiridwa zoipa, tingamve ululu m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Ann ananena kuti: “Ndili mwana, bambo anga anasiya mayi anga n’kukwatira wantchito yemwe ankandilera. Ndinkangodzimva kuti ndasiyidwa. Atabereka ana, ndinkangoona ngati anawo alanda malo anga. Ndinakula ndikumadzimva ngati munthu wosafunika.” Mlongo wina dzina lake Georgette anafotokoza mmene anamvera mwamuna wake atachita zosakhulupirika. Iye anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinadziwana tili ana. Tinkachitira limodzi upainiya. Ndiye ndinakhumudwa kwambiri.” Mlongo wina dzina lake Naomi ananena kuti: “Ndinali ndisanaganizirepo kuti mwamuna wanga angandikhumudwitse. Choncho ataulula kuti wakhala akuonera zolaula mobisa ndinkangodzimva kuti ndanamizidwa komanso ndachitiridwa zopanda chilungamo.”

8. (a) Kodi ndi zifukwa zina ziti zomwe zingatichititse kukhululukira ena? (b) Kodi kukhululuka kumatithandiza bwanji? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Mungatani Ngati Munthu Wina Wakukhumudwitsani Kwambiri?”)

8 Sitingathe kulamulira zimene ena angalankhule kapena kuchita. Koma tingathe kudzilamulira mmene tingachitire zinthu. Ndipotu njira yabwino imakhala kukhululuka. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa timakonda Yehova ndipo iye amafuna kuti tizikhululuka. Nthawi zambiri tingachite zinthu mosaganiza bwino komanso zingakhudze thanzi lathu. (Miy. 14:17, 29, 30) Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina dzina lake Christine. Iye anati: “Ndikakwiya kwambiri ndimalephera kusekerera. Ndimafika polephera kusankha zakudya zoyenera ndipo ndimalepheranso kugona mokwanira. Zimandivutanso kulamulira mmene ndikumvera zomwe zimakhudzanso kwambiri mmene ndimachitira zinthu ndi mwamuna wanga ndi anthu ena.”

9. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusunga chakukhosi?

9 Ngakhale munthu amene watilakwira sakufuna kupepesa, tingachepetsebe mavuto amene amakhalapo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Georgette yemwe tamutchula kale uja anati: “Banja ndi mwamuna wanga litatha ndinasiya kumukwiyira komanso kumusungira chakukhosi ngakhale kuti zinanditengera nthawi. Zotsatira zake n’zakuti ndinapezanso mtendere wa mumtima.” Tikasiya kusunga chakukhosi, timateteza mtima wathu kuti tisamakwiye pochita zinthu ndi ena. Tikatero timakhala kuti tadzichitira chinthu china chabwino kwambiri, chomwe ndi kusiya kuganizira zomwe zachitikazo n’kuyambiranso kusangalala. (Miy. 11:17) Koma bwanji ngati mukuona kuti simunakonzekebe kukhululuka?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI KUTI MUSIYE KUKWIYA

10. N’chifukwa chiyani timafunika kudzipatsa nthawi yokwanira kuti mtima wathu ukhale m’malo? (Onaninso zithunzi.)

10 Kodi mungatani kuti musapitirize kukwiya? Njira imodzi ndi kudzipatsa nthawi yokwanira kuti mtima wanu ukhale m’malo. Munthu amene wavulala akapatsidwa mankhwala pamafunika nthawi yokwanira kuti balalo lipole. Ifenso tingafunike nthawi yokwanira kuti tithe kukhululukira munthu kuchokera pansi pa mtima.—Mlal. 3:3; 1 Pet. 1:22.

Kuti bala lipole pamafunika kulisamalira ndiponso pamatenga nthawi. Ndi mmenenso zimakhalira munthu wina akatikhumudwitsa (Onani ndime 10)


11. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tizikhululuka?

11 Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhululukira ena. c Ann, yemwe tamutchula kale uja, anafotokoza mmene pemphero linamuthandizira. Iye anati: “Ndinapempha Yehova kuti akhululukire aliyense m’banja lathu chifukwa cha zinthu zosayenera zimene analankhula kapena kuchita. Kenako ndinalembera kalata bambo anga ndi akazi awo atsopano yowauza kuti ndawakhululukira.” Ann anavomereza kuti kuchita zimenezi si kunali kophweka. Koma iye anati: “Ndikuganiza kuti kutsanzira Yehova pokhala wokhululuka kuthandiza bambo anga ndi akazi awo kuti aphunzire zokhudza Yehova.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova m’malo mongoganizira mmene tikumvera? (Miyambo 3:5, 6)

12 Muzikhulupirira Yehova, osati kudalira mmene mukumvera. (Werengani Miyambo 3:5, 6.) Nthawi zonse Yehova amadziwa zomwe zili zabwino kwa ife. (Yes. 55:8, 9) Ndipo iye sangatiuze kuti tichite zinthu zimene zingativulaze. Choncho akamatilimbikitsa kuti tizikhululuka, timadziwa kuti kuchita zimenezo n’kothandiza kwa ifeyo. (Sal. 40:4; Yes. 48:17, 18) Koma ngati timangodalira mmene tikumvera sitingathe kukhululukira ena. (Miy. 14:12; Yer. 17:9) Naomi yemwe tamutchula kale uja ananena kuti: “Poyamba ndinkaona kuti sindiyenera kumukhululukira mwamuna wanga yemwe ankaonera zolaula. Ndinkaopa kuti ndikamukhululukira adzachitanso kapena sangadziwe mmene zandikhudzira. Komanso ndinkaganiza kuti Yehova akumvetsa mmene ndikumvera. Koma kenako ndinazindikira kuti ngakhale kuti Yehova amamvetsa mmene ndimamvera, sizitanthauza kuti amavomereza kuti tisamakhululukire ena. Iye amadziwa mmene zandikhudzira ndiponso kuti pangafunike nthawi yokwanira kuti ndisiye kukhala wokwiya, koma amafunanso kuti ndikhululuke.” d

MUZIGANIZIRA ZINTHU ZABWINO

13. Mogwirizana ndi Aroma 12:18-21, kodi tiyenera kuchita chiyani?

13 Kuti tikhululukire munthu amene watikhumudwitsa kwambiri pamafunika zambiri osati kungosiya kulankhula za zimene zachitikazo. Ngati amene watikhumudwitsayo ndi m’bale kapena mlongo wathu, cholinga chathu chizikhala kubwezeretsa mtendere. (Mat. 5:23, 24) Tizisankha kuti m’malo mokwiya, tizisonyeza chifundo ndipo m’malo mosunga chakukhosi, tizikhululuka. (Werengani Aroma 12:18-21; 1 Pet. 3:9) Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizichita zimenezi?

14. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

14 Tiyenera kuyesetsa kuti tiziona munthu yemwe watilakwira ngati mmene Yehova amamuonera. Yehova amasankha kuti aziona zabwino mwa anthu. (2 Mbiri 16:9; Sal. 130:3) Ngati tikufuna kuona zabwino mwa munthu, tingazipeze ndipo n’chimodzimodzinso ngati tikufuna kupeza zoipa mwa munthu. Tikamayesetsa kupeza zabwino mwa ena, zingakhale zosavuta kuti tiziwakhululukira. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Jarrod ananena kuti, “Ndimaona kuti sizimandivuta kukhululukira m’bale ndikayerekezera zomwe walakwitsa ndi zabwino zambiri zimene amachita.”

15. N’chifukwa chiyani kumuuza munthu kuti tamukhululukira n’kofunika?

15 Chinthu china chofunika kwambiri ndi kuuza munthu amene wakulakwirani kuti mwamukhululukira. Chifukwa chiyani? Taonani zimene Naomi, yemwe tamutchula kale uja ananena. Iye anati: “Mwamuna wanga anandifunsa kuti, ‘Kodi wandikhululukira?’ Nditatsegula pakamwa kuti ndizinena kuti, ‘Ndakukhululukira,’ ndinatsamwa. Ndiye ndinazindikira kuti sindinamukhululukire ndi mtima wonse. Patapita nthawi, ndinakwanitsa kulankhula mawu amphamvu amenewa akuti, ‘Ndakukhululukira.’ Ndinadabwa kwambiri ndi mmene anamvera ndipo nanenso ndinakhala ndi mtendere wamumtima. Kuchokera nthawi imeneyo, ndinayambiranso kumukhulupirira ndipo panopa timagwirizana kwambiri.”

16. Kodi mwaphunzira chiyani pa nkhani ya kukhululuka?

16 Yehova amafuna kuti tizikhululuka. (Akol. 3:13) Komabe, nthawi zina zingamativute kukhululukira ena. Koma tingakwanitse ngati timapewa kunyalanyaza mmene tikumvera n’kumayesetsa kuti tisapitirize kukwiya. Tikamachita zimenezi, tingapitirize kukhala ndi maganizo oyenera.—Onani bokosi lakuti “ Zinthu Zitatu Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muzikhululuka.”

MUZIGANIZIRA MMENE KUKHULULUKA KUMAKUTHANDIZIRANI

17. Kodi kukhululuka kumatithandiza bwanji?

17 Tili ndi zifukwa zambiri zotichititsa kuti tizikhululukira ena. Tiyeni tione zina mwa zifukwazi. Choyamba, timatsanzira komanso kusangalatsa Atate wathu wachifundo, Yehova. (Luka 6:36) Chachiwiri, timafuna kusonyeza kuyamikira kuti Yehova amatikhululukira mokoma mtima. (Mat. 6:12) Ndipo chachitatu, timakhala ndi thanzi labwino komanso timagwirizana kwambiri ndi anthu ena.

18-19. Kodi chimachitika n’chiyani tikakhululuka?

18 Tikamakhululukira ena, timapeza madalitso omwe sitimawayembekezera. Mwachitsanzo, taonani zimene zinachitikira Denise, yemwe tamutchula kale uja. Ngakhale kuti iye sankadziwa, munthu yemwe anachititsa ngozi uja anakonza zoti adziphe mlandu wake ukagamulidwa. Koma anakhudzidwa kwambiri ndi zimene Denise anachita pomukhululukira ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

19 Mwina nthawi zina ifenso zingativute kukhululukira munthu yemwe watilakwira. Komatu kukhululukira ena n’kothandiza kwambiri. (Mat. 5:7) Choncho, tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe kuti tizitsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira ena.

NYIMBO NA. 125 “Osangalala Ndi Anthu Achifundo”

a Mayina ena asinthidwa.

b Pa nkhani ngati imeneyi, Mkhristu aliyense ayenera kusankha yekha zimene angachite.

c Onani pa jw.org, mavidiyo a nyimbo akuti “Tizikhululukirana,” “Ndikhululuke” komanso “Tigwirizanenso.”

d Ngakhale kuti kuonera zolaula n’koipa komanso ndi tchimo, sikumachititsa kuti mwamuna kapena mkazi akhale ndi ufulu wothetsa banja lake mwa Malemba.