Muzipewa Mzimu Wodzikonda
ANTHU ambiri m’dzikoli amaona kuti ndi ofunika kupatsidwa ulemu wapadera, ufulu komanso kuchitiridwa zinthu m’njira yapadera. Koma ngakhale atapeza zonsezi, iwo amaonabe kuti n’zosakwanira. Anthu amene amakhala ndi maganizo amenewa amakhala odzikonda komanso osayamika ndipo ndi zimene Baibulo linanena kuti anthu azidzachita m’masiku otsiriza.—2 Tim. 3:2.
Ndipotu anthu akhala akusonyeza mzimu wodzikondawu kuyambira kale. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Adamu ndi Hava, omwe ankafuna kuti azisankha okha chabwino ndi choipa, ndipo zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu. Chitsanzo china ndi Mfumu Uziya ya ku Yuda yemwe ankaganiza kuti akhoza kupereka nsembe zofukiza kukachisi, koma iye sankayenera kuchita izi. (2 Mbiri 26:18, 19) Mofanana ndi zimenezi, Afarisi ndi Asaduki ankakhulupirira kuti Mulungu ayenera kumawakonda mwapadera chifukwa chakuti anali mbadwa za Abulahamu.—Mat. 3:9.
Popeza kuti tazunguliridwa ndi anthu odzikonda, tikhoza kuyamba kutengera zochita zawo. (Agal. 5:26) Tikhoza kumaganiza kuti ndife oyenera kupatsidwa mwayi winawake kapena kuchitiridwa zinthu m’njira yapadera. Kodi tingatani kuti tipewe maganizo amenewa? Choyamba, tiyenera kudziwa maganizo a Yehova pa nkhaniyi. Tiyeni tikambirane mfundo ziwiri za m’Baibulo zomwe zingatithandize.
Yehova ndi amene amasankha zimene tiyenera kukhala nazo. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
-
M’banja, mwamuna amayenera kulemekezedwa ndi mkazi wake ndipo mkazi amayenera kukondedwa ndi mwamuna wake. (Aef. 5:33) Iwo sayenera kusonyeza kwa munthu wina chikondi chimene chimayenera kukhalapo pakati pa awiriwo. (1 Akor. 7:3) Makolo amafuna kuti ana awo aziwamvera ndipo anawo amayembekezera kuti makolowo aziwakonda komanso kuwathandiza.—2 Akor. 12:14; Aef. 6:2.
-
Mumpingo, tiyenera kulemekeza akulu omwe amagwira ntchito yawo mwakhama. (1 Ates. 5:12) Komabe akuluwo alibe mphamvu yolamulira abale ndi alongo awo.—1 Pet. 5:2, 3.
-
Mulungu amafuna kuti anthu azipereka misonkho ku boma komanso azilemekeza amene akulamulira.—Aroma 13:1, 6, 7.
Mwachikondi, Yehova amatipatsa zambiri kuposa zimene timafunikira. Chifukwa choti ndife ochimwa, sitinkafunikira kukhala ndi moyo. (Aroma 6:23) Koma chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika, Yehova amatipatsa madalitso ambiri. (Sal. 103:10, 11) Iye amatipatsa madalitso onsewa osati chifukwa chakuti ndife oyenera kupatsidwa madalitsowa, koma chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.—Aroma 12:6-8; Aef. 2:8.
ZIMENE TINGACHITE KUTI TIZIPEWA MZIMU WODZIKONDA
Tizisamala kuti tisatengere maganizo a anthu a m’dzikoli. Mosadziwa tingayambe kumaganiza kuti timafunika kupatsidwa zambiri kuposa ena. Yesu anasonyeza mmene zingakhalire zosavuta kukhala ndi maganizo amenewa, pomwe anafotokoza fanizo la antchito omwe anapatsidwa dinari imodzi monga malipiro a ntchito yawo. Antchito ena anayamba kugwira ntchito m’mawa kwambiri ndipo anagwira ntchito tsiku lonse padzuwa. Pamene ena anangogwira ntchito kwa ola limodzi. Gulu loyambali linkaganiza kuti liyenera kupatsidwa malipiro ambiri chifukwa cha ntchito imene anagwirayo. (Mat. 20:1-16) Pofotokoza fanizoli, Yesu anasonyeza kuti otsatira ake ayenera kukhala okhutira ndi zimene Yehova wafuna kuwapatsa.
Muzikhala oyamikira ndipo musamayembekezere kuti ena akuchitireni zinthu. (1 Ates. 5:18) Tizitsanzira mtumwi Paulo yemwe sanapemphe abale ake a ku Korinto kuti amupatse zinthu zofunika pa moyo ngakhale kuti akanatha kutero. (1 Akor. 9:11-14) Tiziyamikira zilizonse zimene ena atipatsa ndipo tisamachite kuwalamula kuti atipatse.
Muzikhala odzichepetsa. Munthu akayamba kudziganizira kuposa mmene ayenera kudziganizirira, amayamba kuona kuti ayenera kupatsidwa zambiri kuposa zimene ayenera kupatsidwa. Kudzichepetsa n’kumene kungatithandize kupewa kukhala ndi maganizo olakwikawa.
Mneneri Danieli ndi chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzichepetsa. Iye akanatha kumaona kuti ayenera kuchitiridwa zinthu m’njira yapadera kapena kupatsidwa mwayi winawake chifukwa cha banja limene anachokera, maonekedwe, nzeru komanso luso lake. (Dan. 1:3, 4, 19, 20) Koma Danieli anakhalabe wodzichepetsa ndipo khalidwe limeneli linachititsa kuti Yehova azimukonda kwambiri.—Dan. 2:30; 10:11, 12.
Tiyeni tizipewa mzimu wodzikonda womwe anthu ambiri ali nawo m’dzikoli. M’malomwake, tiziyamikira madalitso aliwonse omwe Yehova amatipatsa chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.