Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 7

NYIMBO NA. 15 Tamandani Mwana Woyamba Kubadwa wa Yehova

Timapindula ndi Kukhululuka kwa Yehova

Timapindula ndi Kukhululuka kwa Yehova

“Inu mumakhululuka ndi mtima wonse.”SAL. 130:4.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona mawu angapo a m’Baibulo ofotokoza mwafanizo zimene Yehova amachita potikhululukira ndi mtima wonse komanso mmene tingasonyezere kuyamikira.

1. N’chifukwa chiyani zimakhala zovuta kudziwa zimene munthu akutanthauza akanena kuti watikhululukira?

 MAWU akuti, “ndakukhululukira” ndi okhazika mtima pansi makamaka ngati unalankhula kapena kuchita zinthu zomwe zakhumudwitsa winawake. Koma kodi mawu akuti “ndakukhululukira” amatanthauza chiyani? Kodi munthu amene tamukhumudwitsayo amakhala akunena kuti muzionanabe monga mabwenzi ngati poyamba? Kapena amakhala akungotanthauza kuti sakufuna kuti mukambiranenso za zimene zachitikazo? Anthu akamanena kuti akhululuka amakhala akutanthauza zinthu zosiyanasiyana.

2. Kodi Baibulo limafotokoza bwanji kukhululuka kwa Yehova? (Onaninso mawu a m’munsi.)

2 Mmene Yehova amatikhululukira anthu ochimwafe, n’zosiyana kwambiri ndi mmene timakhululukirana tokhatokha. Palibe amene angathe kukhululuka ngati mmene Yehova amachitira. Ponena za Yehova wolemba masalimo anati: “Inu mumakhululuka ndi mtima wonse, kuti anthu azikuopani.” a (Sal. 130:4) Choncho Yehova ‘amakhululuka ndi mtima wonse.’ Iye ndi chitsanzo chabwino chosonyeza zimene kukhululuka kumatanthauza. M’mavesi ena, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu a Chiheberi ofotokoza za kukhululuka amene amagwiritsidwa ntchito ponena za Yehova yekha, osati anthu.

3. Kodi kukhululuka kwa Yehova kumasiyana bwanji ndi kwa anthufe? (Yesaya 55:6, 7)

3 Yehova akakhululukira munthu amafufuta machimo onse a munthuyo ndipo amakhala nayenso pa ubwenzi ngati poyamba. Timayamikira kuti Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse komanso mobwerezabwereza.—Werengani Yesaya 55:​6, 7.

4. Kodi Yehova amatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la kukhululuka?

4 Popeza kukhululuka kwa Yehova ndi kosiyana ndi kwathu, kodi tingatani kuti timvetse tanthauzo la kukhululuka kwenikweni? Yehova amagwiritsa ntchito mafanizo pofuna kutithandiza kumvetsa kukhululuka kwake. Munkhaniyi tikambirana ena mwa mafanizo amenewo. Mafanizowo atithandiza kuona mmene Yehova amachotsera machimo n’kukonzanso ubwenzi umene wawonongeka. Kukambirana mafanizowa kutithandiza kuti tiziyamikira kwambiri Atate wathu wachifundo omwe amatikhululukira m’njira zambiri.

YEHOVA AMACHOTSA MACHIMO

5. Kodi chimachitika n’chiyani Yehova akakhululuka machimo athu?

5 M’Baibulo machimo amawayerekezera ndi katundu wolemera. Pofotokoza za machimo ake Mfumu Davide anati: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera.” (Sal. 38:4) Koma Yehova amakhululukira anthu amene alapa. (Sal. 25:18; 32:5) Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “kukhululuka” angatanthauze “kuchotsa” kapena “kunyamula.” Choncho Yehova ali ngati munthu wamphamvu yemwe mophiphiritsa amatichotsera machimo omwe amalemera paphewa lathu.

“Munandikhululukira” (Sal. 32:⁠5)


6. Kodi Yehova amataya machimo athu kutali bwanji?

6 Fanizo lina limasonyeza mmene Yehova amanyamulira machimo athu n’kukawasiya kutali ndi ife. Lemba la Salimo 103:12 limatiuza kuti: “Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa, Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.” Kum’mawa ndi kotalikirana kwambiri ndi kumadzulo. Malo awiriwa sangakumane. Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova amaika machimo athu kutali kwambiri ndi ife. Zimenezi zikutitsimikizira kuti Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse.

“Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa” (Sal. 103:12)


7. Kodi Baibulo limafotokoza bwanji zimene Yehova amachita ndi machimo athu? (Mika 7:18, 19)

7 Ngakhale kuti mophiphiritsa Yehova amachotsa machimo athu n’kuwaika kutali kwambiri ndi ife, kodi zimenezi zikutanthauza kuti amawakumbukirabe? Ayi. Ponena za Yehova Mfumu Hezekiya analemba kuti: “Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu,” kapenanso monga mmene mawu a m’munsi amanenera kuti, “Mwachotsa machimo anga onse kuti musawaonenso.” (Yes. 38:9, 17; mawu a m’munsi.) Mawuwa akusonyeza kuti Yehova amachotsa machimo a munthu amene walapa n’kukawataya kumalo amene sangawaonenso. Mawuwa angafotokozedwenso kuti: “Mwachititsa kuti [machimo anga] akhale ngati sanachitike n’komwe. Baibulo limapitiriza kufotokoza mfundoyi ndi mawu ena a fanizo opezeka pa Mika 7:18, 19. (Werengani.) Mavesiwa amafotokoza ngati kuti Yehova akuponya machimo athu m’nyanja pamalo ozama. Mosiyana ndi masiku ano, kale chinthu chikaponyedwa m’nyanja pamalo ozama sizinkatheka kuti munthu akachitengenso.

“Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.” (Yes. 38:⁠17)

“Machimo athu onse mudzawaponya mʼnyanja pamalo ozama” (Mika 7:19)


8. Kodi taphunzira chiyani pofika pano?

8 Mafanizowa akutithandiza kuona kuti Yehova akatikhululukira, timapepukidwa ku machimo athu. Monga mmene Davide ananenera, “osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa. Wosangalala ndi munthu amene Yehova sadzawerengera tchimo lake.” (Aroma 4:7, 8) Kumeneku ndiye kukhululuka ndi mtima wonse.

YEHOVA AMAFUFUTA MACHIMO

9. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mafanizo ati pofuna kutithandiza kumvetsa kukhululuka kwake?

9 Yehova amagwiritsa ntchito mafanizo ena pofuna kutithandiza kumvetsa mmene amafufutira machimo a anthu amene alapa pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo. Baibulo limanena kuti Yehova amatsuka kapena kuti kuyeretsa machimo. Zimenezi zimathandiza kuti wochimwayo akhale woyera. (Sal. 51:7; Yes. 4:4; Yer. 33:8) Yehova anafotokoza yekha zotsatirapo zake ndipo anati: “Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri, adzayera kwambiri. Ngakhale kuti ndi ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.” (Yes. 1:18) Zimakhala zovuta kwambiri kuchotsa zinthu zofiira kapena magazi pachovala. Koma pogwiritsa ntchito fanizoli Yehova akutitsimikizira kuti machimo athu adzayera kwambiri moti sangaonekenso.

“Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri, adzayera kwambiri” (Yes. 1:18)


10. Kodi Yehova amagwiritsanso ntchito fanizo liti pofuna kusonyeza mmene amakhululukira?

10 Monga mmene taonera munkhani yoyamba ija, machimo amayerekezeredwanso ndi “ngongole.” (Mat. 6:12; Luka 11:4) Choncho nthawi iliyonse imene tachimwa, zimakhala ngati tawonjezera ngongole yathu kwa Yehova. Ndipo ngongole yathu imakhala yaikulu kwambiri. Koma akatikhululukira zimakhala ngati wafufuta ngongole imene timafunika kubweza. Iye sayembekezera kuti tilipire ngongole ya machimo amene anatikhululukira. Fanizoli likufotokoza bwino kuti Yehova akatikhululukira timakhala osangalala.

“Mutikhululukire zolakwa zathu” (Mat. 6:12)


11. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamanena kuti machimo athu ‘afafanizidwa’? (Machitidwe 3:19)

11 Yehova akakhululuka machimo athu, sikuti amangowakhwatcha koma amawafafaniza. (Werengani Machitidwe 3:19.) Ngongole ikakhwatchidwa, anthu amangodula mzere papepala limene panalembedwa ngongoleyo koma zimene zinalembedwazo zimatha kumaonekabe. Koma kufafaniza n’kosiyana kwambiri ndi zimenezi. Kuti timvetse zimenezi tiyenera kukumbukira kuti inki yakale inkapangidwa ndi zinthu zosavuta kufufuta. Munthu ankatha kutenga kansalu konyowa n’kufufuta zimene walemba. Choncho ngongole ikafafanizidwa, sinkaonekanso. Munthu sankatha kuonanso zimene zinalembedwa. Zinkangokhala ngati panalibenso ngongole. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova samangokhwatcha machimo athu, koma amawafafaniza.—Sal. 51:9.

“Kuti machimo anu afafanizidwe” (Mac. 3:19)


12. Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la mtambo waukulu?

12 Yehova amagwiritsanso ntchito fanizo lina pofotokoza mmene amafafanizira machimo. Iye ananena kuti: “Ndidzafafaniza zolakwa zako ndipo zidzakhala ngati ndaziphimba ndi mtambo ndipo machimo ako adzakhala ngati ndawaphimba ndi mtambo waukulu.” (Yes. 44:22) Yehova akatikhululukira zimakhala ngati waphimba machimo athu ndi mtambo waukulu moti sangaonekenso.

“Ndidzafafaniza zolakwa zako ndipo zidzakhala ngati ndaziphimba ndi mtambo” (Yes. 44:22)


13. Kodi timamva bwanji Yehova akatikhululukira machimo athu?

13 Kodi tikuphunzira chiyani pa mafanizowa? Yehova akatikhululukira machimo athu sitiyenera kudziimba mlandu kwa moyo wathu wonse. Magazi a Yesu Khristu anachititsa kuti ngongole yathu yonse ifafanizidwe. Zili ngati pamene panalembedwa ngongoleyo sipakuonekanso chilichonse. Umu ndi mmene Yehova amatikhululukira ndi mtima wonse tikalapa machimo athu.

YEHOVA AMALOLA KUTI TIKHALE NAYENSO PA UBWENZI WABWINO

Atate wathu wakumwamba akatikhululukira timakhala nayenso pa ubwenzi wabwino (Onani ndime 14)


14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira Yehova akanena kuti watikhululukira? (Onaninso zithunzi.)

14 Yehova akatikhululukira ndi mtima wonse timakhala nayenso pa ubwenzi wabwino. Zimenezi zimathandiza kuti tisamapitirize kudziimba mlandu chifukwa cha machimo athu. Choncho tisamaganize kuti Yehova akutisungira zifukwa ndipo akufufuza njira yoti atilangire. Iye sangachite zimenezo. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira Yehova akanena kuti watikhululukira? Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Mtumwi Paulo anafotokozanso zofanana ndi zimenezi pamene analemba kuti: “Sindidzakumbukiranso machimo awo.” (Aheb. 8:12) Koma kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani?

“Machimo awo sindidzawakumbukiranso” (Yer. 31:34)


15. Kodi mawu akuti Yehova sakumbukiranso machimo athu amatanthauza chiyani?

15 M’Baibulo mawu akuti “kukumbukira” samangotanthauza kuganizira zinthu zina zimene zinachitika. Koma amatanthauza kuchita zinazake. Mwachitsanzo, chigawenga chimene chinapachikidwa pafupi ndi Yesu chinapempha kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.” (Luka 23:42, 43) Iye sankangopempha Yesu kuti amuganizire pa nthawiyo. Yankho la Yesu linasonyeza kuti iye adzachitapo kanthu poukitsa munthuyu. Choncho Yehova akamatiuza kuti sakumbukiranso machimo athu, zimatanthauza kuti sadzatiimba mlandu chifukwa cha machimowo. Komanso m’tsogolo sadzatilanga chifukwa cha machimo amene anatikhululukira.

16. Kodi Baibulo limafotokoza bwanji ufulu umene timakhala nawo machimo athu akakhululukidwa?

16 Baibulo limagwiritsa ntchito fanizo lina pofuna kutithandiza kumvetsa ufulu umene timakhala nawo Yehova akatikhululukira ndi mtima wonse. Chifukwa chakuti ndife ochimwa ndipo timalakalaka zoipa, tili ngati “akapolo a uchimo.” Koma Yehova akatikhululukira timakhala ngati akapolo amene ‘amasulidwa ku uchimo.’ (Aroma 6:17, 18; Chiv. 1:5) Tikadziwa kuti Yehova watikhululukira timakhala osangalala ngati kapolo amene wamasulidwa.

“Munamasulidwa ku uchimo” (Aroma 6:18)


17. Kodi kukhululuka kumachititsa bwanji kuti tichiritsidwe? (Yesaya 53:5)

17 Werengani Yesaya 53:5. Fanizo lomaliza lomwe tikambirane limatiyerekezera ndi anthu amene akudwala matenda oopsa. Pogwiritsa ntchito nsembe ya Mwana wake mophiphiritsa Yehova amatichiritsa. (1 Pet. 2:24) Dipo limathandiza kuti tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, womwe unasokonekera chifukwa cha matenda oopsa aja. Mofanana ndi munthu amene amasangalala akachiritsidwa matenda aakulu, ifenso timasangalala tikachiritsidwa mwauzimu n’kukhalanso pa ubwenzi ndi Yehova chifukwa chakuti watikhululukira.

“Chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa” (Yes. 53:⁠5)


KODI KUKHULULUKA KWA YEHOVA KUMATITHANDIZA BWANJI?

18. Kodi tikuphunzira chiyani pa mafanizo a m’Baibulo okhudza kukhululuka kwa Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “Mmene Yehova Amatikhululukira.”)

18 Kodi taphunzira chiyani pa mafanizo a m’Baibulo ofotokoza za kukhululuka kwa Yehova? Iye amatikhululukira ndi mtima wonse ndipo nkhaniyo imathera pomwepo. Zimenezi zimatithandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba. Tizikumbukira kuti kukhululuka kwa Yehova ndi mphatso. Iye amatipatsa mphatsoyi chifukwa cha chikondi komanso kukoma mtima kwake kwakukulu. Samatikhululukira chifukwa chakuti ndi ufulu wathu kuti atikhululukire.—Aroma 3:24.

19. (a) N’chifukwa chiyani timayenera kukhala oyamikira? (Aroma 4:8) (b) Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

19 Werengani Aroma 4:8. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chakuti iye ndi Mulungu amene ‘amakhululuka ndi mtima wonse.’ (Sal. 130:4) Koma kuti Yehova atikhululukire timafunika kuchita kanthu kena kofunika kwambiri. Yesu ananena kuti: “Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukiraninso machimo anu.” (Mat. 6:14, 15) Choncho tiyenera kutsanzira Yehova n’kumakhululukira anthu ena. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Nkhani yotsatira itithandiza kuona mmene tingachitire zimenezi.

NYIMBO NA. 46 Tikukuthokozani Yehova

a Mawu a Chiheberi amene anawagwiritsa ntchito palembali ndi mawu okhawo amene amanena za ‘kukhululuka ndi mtima wonse’ ngakhale kuti pali mitundu ina ya kukhululuka. Mabaibulo ambiri sasonyeza kusiyana kumeneku koma Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika limasonyeza kusiyanaku palemba la Salimo 130:4.