Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 6

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

Timayamikira Yehova Chifukwa Amatikhululukira

Timayamikira Yehova Chifukwa Amatikhululukira

“Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha.”YOH. 3:16.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiphunzira zimene Yehova anachita kuti azitikhululukira. Izi zitithandiza kuti tiziyamikira kwambiri zomwe Yehova anachitazi.

1-2. Kodi anthufe tikufanana bwanji ndi wachinyamata amene watchulidwa mundime 1?

 TIYEREKEZE kuti wachinyamata wina anakulira m’banja lolemera. Ndiyeno tsiku lina makolo ake afa pangozi. Iye akumva chisoni kwambiri ndi zimene zachitikazo. Koma kenako akumvanso nkhani ina yomvetsa chisoni kwambiri. Iye akuuzidwa kuti makolo ake anawononga ndalama zambiri ndipo ali ndi ngongole yaikulu. Ndiye m’malo molandira chuma cha makolo ake, akukhala ndi ngongole yoti abweze. Koma ngongole yake ndi yoti sangathe kuibweza.

2 Ifenso m’njira ina tikufanana ndi wachinyamata ameneyu. Makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava, anali angwiro ndipo ankakhala m’Paradaiso. (Gen. 1:27; 2:7-9) Iwo akanatha kukhala ndi moyo wosangalala mpaka kalekale. Koma kenako zinthu zinasintha. Iwo anathamangitsidwa m’munda wa Edeni ndipo anataya mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. Ndiye kodi Adamu anasiyira chiyani ana ake? Baibulo limati: “Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu] ndipo uchimowo unabweretsa imfa. Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Cholowa chomwe Adamu anatisiyira ndi uchimo, womwe umabweretsa imfa. Uchimo umenewo uli ngati ngongole yaikulu imene palibe munthu amene angathe kubweza.

3. Kodi machimo athu amafanana bwanji ndi “ngongole”?

3 Yesu anayerekezera machimo ndi “ngongole.” (Mat. 6:12; Luka 11:4; mawu a m’munsi) Tikachimwa timakhala ngati tili ndi ngongole kwa Yehova. Timayenera kulipira ngongole ya machimo athu. Ngati sitingalipire ngongoleyo, ingathetsedwe pokhapokha ngati titafa.—Aroma 6:7, 23.

4. (a) Zikanakhala kuti Mulungu sanatithandize, kodi n’chiyani chikanachitikira anthu onse ochimwa? (Sal. 49:7-9) (b) Kodi m’Baibulo mawu akuti tchimo amatanthauza chiyani? (Onani bokosi lakuti, “ Uchimo.”)

4 Kodi n’zotheka kudzapezanso zonse zimene Adamu ndi Hava anataya? Zingatheke koma osati patokha. (Werengani Salimo 49:​7-9.) Popanda kuthandizidwa ndi Yehova sitingakhale ndi chiyembekezo chodzakhalanso ndi moyo kapena kudzaukitsidwa. Ndipotu bwenzi tikungofa popanda chiyembekezo chilichonse ngati zinyama.—Mlal. 3:19; 2 Pet. 2:12.

5. Kodi Atate wathu wachikondi watithandiza bwanji kulipira ngongole ya machimo athu? (Onani chithunzi chapachikuto.)

5 Taganizirani za wachinyamata yemwe tamutchula kumayambiriro uja. Kodi iye angamve bwanji ngati munthu wina wachuma atadzipereka kuti alipire ngongole zake zonse? Mosakayikira, wachinyamatayo angayamikire kwambiri zimene munthuyo angamuchitire. Mofanana ndi zimenezi, Atate wathu wachikondi Yehova, watipatsa mphatso yomwe yalipira ngongole ya uchimo imene tinatengera kwa Adamu. Pofotokoza zimenezi Yesu ananena kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Kuwonjezera pamenepa, mphatsoyi imatithandizanso kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.

Yesu analalikira uthenga wabwino wonena za kukhululuka kwa Yehova komwe kumatheka chifukwa cha dipo. (Yoh. 3:16) Kenako mofunitsitsa, anapereka moyo wake kuti apereke dipolo (Onani ndime 5)


6. Kodi munkhaniyi tikambirana mawu ati a m’Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani?

6 Kodi tingatani kuti tipindule ndi mphatso yamtengo wapataliyi, komanso kuti machimo athu omwe ali ngati ngongole akhululukidwe? Yankho la funso limeneli timalipeza tikaganizira mawu a m’Baibulo monga akuti kugwirizanitsa, kuphimba machimo, dipo, kupulumutsidwa komanso kuonedwa kuti ndi olungama. Munkhaniyi tikambirana matanthauzo a mawu amenewa. Kuganizira zimene Yehova wachita kuti azitikhululukira kutithandiza kuti tizimuyamikira kwambiri.

CHOLINGA: KUGWIRIZANITSA

7. (a) Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene Adamu ndi Hava anataya? (b) Popeza ndife ana a Adamu ndi Hava, kodi timafunikira kwambiri chiyani? (Aroma 5:10, 11)

7 Kuwonjezera pa kutaya mwayi wokhala ndi moyo wosatha, Adamu ndi Hava anatayanso mwayi wokhala pa ubwenzi ndi Atate wawo. Poyamba, Adamu ndi Hava anali m’banja la Mulungu. (Luka 3:38) Koma chifuwa choti sanamvere Yehova, iwo anathamangitsidwa m’banjali, ndipo pa nthawiyi anali asanabereke ana. (Gen. 3:23, 24; 4:1) Popeza kuti ife ndi anawo, tiyenera kugwirizanitsidwanso ndi Yehova. (Werengani Aroma 5:10, 11.) Kunena kwina, tiyenera kukhala pa ubwenzi wabwino ndi iye. Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena, mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kugwirizanitsa,” angatanthauze “kupanga munthu amene anali mdani wako kukhala mnzako.” Koma n’zochititsa chidwi kuti Yehova ndi amene anayamba kuchitapo kanthu kuti zimenezi zitheke. Kodi anachita bwanji?

ZIMENE ANAKONZA: KUPHIMBA MACHIMO

8. (a) Kodi kuphimba machimo n’kutani? (b) Nanga kugwirizanitsa n’kutani?

8 Kuphimba machimo ndi njira imene Yehova anakonza kuti anthu ochimwafe tikhalenso naye pa ubwenzi wabwino. Pochita izi panafunika kusinthanitsa chinthu ndi chinthu china chomwe ndi chofanana nacho. Zimenezi zimathandiza kuti chinthu chimene chatayika kapena kuwonongedwa, chibwezeretsedwe. Malemba a Chigiriki amagwiritsa ntchito mawu akuti kugwirizanitsa omwe ndi ofanana ndi mawu akuti “kuphimba machimo.” (Aroma 3:25) Mawu akuti “kugwirizana” akutanthauza zimene munthu amachita kuti akhalenso pa mtendere ndi Mulungu komanso kukhala naye pa ubwenzi wabwino.

9. Kodi Yehova anauza Aisiraeli kuti azichita chiyani kuti machimo awo azikhululukidwa?

9 Pofuna kuthandiza Aisiraeli kuti akhale naye pa ubwenzi wabwino, Yehova anakhazikitsa njira yoti machimo awo azikhululukidwa. Chaka chilichonse, Aisiraeli ankakhala ndi Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Pa tsikuli, mkulu wa ansembe ankapereka nsembe za nyama m’malo mwa anthu onse. Komabe nsembe za nyamazo sizinkaphimbiratu machimo popeza kuti nyama n’zotsika poyerekezera ndi anthu. Koma Aisiraeli akalapa n’kupereka nsembe zimene Mulungu ankafunazi, iye ankawakhululukira machimo awo. (Aheb. 10:1-4) Kuwonjezera pamenepo, nsembe zomwe ankaperekazo zinkakumbutsa Aisiraeli kuti iwo ndi ochimwa ndipo ankafunika njira yomwe ingaphimbiretu machimo awo.

10. Kodi Yehova anachita chiyani kuti machimo a anthu akhululukidwe?

10 Kodi Yehova anatani kuti aphimbiretu machimo a anthu? Iye anakonza zoti Mwana wake “aperekedwe nsembe kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.” (Aheb. 9:28) Yesu anapereka “moyo wake dipo kuti awombole anthu ambiri.” (Mat. 20:28) Kodi dipo n’chiyani?

MALIPIRO: DIPO

11. (a) Kodi m’Baibulo mawu akuti “dipo” amatanthauza chiyani? (b) N’chiyani chinafunika kuti dipoli liperekedwe?

11 Mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, dipo ndi malipiro amene amaperekedwa pofuna kuphimba machimo komanso kugwirizanitsa anthu ndi Yehova. a Yehova amaona kuti dipo ndi limene limathandiza kubwezeretsa zimene zinatayika. Kumbukirani kuti Adamu ndi Hava anataya moyo wangwiro komanso mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Choncho dipo linayenera kukhala malipiro ofanana ndi zimene zinatayikazo. (1 Tim. 2:6) Linayenera kuperekedwa ndi munthu wamkulu yemwe (1) anali wangwiro, (2) anali ndi mwayi woti akanatha kukhala ndi moyo padziko lapansi mpaka kalekale komanso (3) anali wofunitsitsa kupereka moyo wake ngati nsembe. Apa pokha m’pamene moyo wa munthuyo ukanatha kuphimba machimo komanso kubwezeretsa moyo umene unatayika.

12. N’chifukwa chiyani Yesu anali woyenera kupereka dipo?

12 Tiyeni tikambirane zifukwa zitatu zimene zikuchititsa Yesu kukhala woyenera kupereka dipoli. (1) Iye anali wangwiro ndipo “sanachite tchimo.” (1 Pet. 2:22) (2) Popeza anali wangwiro, akanatha kukhala ndi moyo mpaka kalekale padziko lapansi. (3) Iye analolera kufa n’kupereka moyo wake chifukwa cha ifeyo. (Aheb. 10:9, 10) Popeza Yesu anali wangwiro, ankafanana ndi mmene Adamu analili asanachimwe. (1 Akor. 15:45) Imfa ya Yesu inaphimba tchimo la Adamu, ndipo inabwezeretsa zimene Adamu anataya. (Aroma 5:19) Choncho Yesu anakhala “Adamu womalizira.” Sipakufunikanso munthu wina wangwiro kuti abwere kudzalipira zimene Adamu anataya. Yesu anafa “kamodzi kokha kuti akhale nsembe yothandiza anthu mpaka kalekale.”—Aheb. 7:27; 10:12.

13. Kodi kuphimba machimo kumasiyana bwanji ndi dipo?

13 Kodi kuphimba machimo n’kosiyana bwanji ndi dipo? Kuphimba machimo ndi zimene Mulungu wachita kuti anthu akhale nayenso pa ubwenzi wabwino. Pomwe dipo ndi malipiro amene amaperekedwa kuti machimo a anthu aphimbidwe. Malipiro amenewa akuimiridwa ndi magazi amtengo wapatali a Yesu omwe anakhetsedwa chifukwa cha ife.—Aef. 1:7; Aheb. 9:14.

ZOTSATIRA ZAKE: KUPUMUMUTSIDWA NDIPONSO KUONEDWA KUTI NDI OLUNGAMA

14. Kodi tsopano tikambirana chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

14 Kodi zotsatira za kuphimba machimo ndi zotani? Baibulo limagwiritsa ntchito mawu ambiri pofotokoza zotsatira zake zabwino. Ngakhale kuti matanthauzo a mawuwa ndi ofanana mbali ina, mawu alionse amatsindika mbali ina ya zimene Yehova anachita pofuna kuti akhululukire anthu. Tikamakambirana mawu amenewa, tionanso mmene akutikhudzira ifeyo aliyense payekha.

15-16. (a) Kodi m’Baibulo mawu akuti “kuwombola” amatanthauza chiyani? (b) Kodi timamva bwanji chifukwa chakuti tinawomboledwa?

15 M’Baibulo, mawu akuti kuwombola, amatanthauza kumasula kapena kukhululuka chifukwa chakuti dipo laperekedwa. Mtumwi Petulo anafotokoza zimenezi ponena kuti: “Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani [m’chilankhulo choyambirira, “zinakuwombolani”] ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali a Khristu, omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.”—1 Pet. 1:18, 19.

16 Chifukwa cha nsembe ya dipo tikhoza kumasulidwa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Aroma 5:21) Choncho tiyenera kuyamikira kwambiri Yehova ndi Yesu chifukwa chotimasula pogwiritsa ntchito magazi amtengo wapatali kapena kuti moyo wa Yesu.—1 Akor. 15:22.

17-18. (a) Kodi kuonedwa kuti ndi wolungama kumatanthauza chiyani? (b) Kodi anthu amapindula bwanji chifukwa choonedwa kuti ndi olungama?

17 Kuwonedwa kuti ndi wolungama kumatanthauza kuti milandu yako yathetsedwa, ndipo zimene unalakwitsa zafufutidwa. Yehova akachita zimenezi, amakhala akutsatirabe mfundo zake zachilungamo. Sikuti amationa kuti ndife olungama chifukwa chakuti tachita zinazake. Ndiponso sikuti amakhala akulekerera machimo athu. Koma chifukwa choti timakhulupirira zimene wachita pophimba machimo athu komanso kupereka dipo, Yehova amatikhululukira.—Aroma 3:24; Agal. 2:16.

18 Kodi timapindula bwanji Yehova akamationa kuti ndife olungama? Anthu amene anasankhidwa kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba amaonedwa kale kuti ndi olungama monga ana a Mulungu. (Tito 3:7; 1 Yoh. 3:1) Machimo awo anakhululukidwa. Iwo alibe mbiri iliyonse yoti anapalamula mlandu ndipo ndi oyenera kulowa mu Ufumu. (Aroma 8:1, 2, 30) Amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, amaonedwa kuti ndi olungama monga anzake a Mulungu ndipo machimo awo amakhululukidwa. (Yak. 2:21-23) A khamu lalikulu amene adzapulumuke pa Aramagedo, adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. (Yoh. 11:26) Anthu “olungama” ndi “osalungama” amene anafa, akuyembekezera kudzaukitsidwa. (Mac. 24:15; Yoh. 5:28, 29) Pamapeto pake, atumiki onse okhulupirika a Yehova padzikoli ‘adzakhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:21) Amenewatu ndi madalitso osaneneka omwe timawapeza chifukwa choti machimo athu aphimbidwa ndiponso tagwirizanitsidwa ndi Yehova yemwe ndi Atate wathu.

19. Kodi moyo wathu wasintha bwanji chifukwa cha zimene Yehova ndi Yesu atichitira? (Onaninso bokosi lakuti “ Kukhululuka kwa Yehova.”)

19 Kunena zoona, poyamba tinali ngati wachinyamata amene tamutchula kumayambiriro uja, yemwe anataya chilichonse ndipo anali ndi ngongole yomwe sakanatha kubweza. Koma timayamikira kuti Yehova watithandiza. Moyo wathu wasintha chifukwa cha zimene iye wachita pophimba machimo athu komanso kupereka dipo. Kukhulupirira Yesu Khristu kumathandiza kuti tiwomboledwe kapena kuti timasulidwe ku uchimo ndi imfa. Machimo athunso amakhululukidwa ndipo mbiri yoti tinapalamula imafufutidwa. Koma chofunika kwambiri ndi chakuti panopa tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova.

20. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

20 Tikaganizira zimene Yehova ndi Yesu atichitira, timawayamikira kuchokera pansi pa mtima. (2 Akor. 5:15) Akanapanda kutithandiza, sitikanakhala ndi chiyembekezo chilichonse. Koma kodi zimene Yehova wachita potikhululukira zimakhudza bwanji aliyense payekha? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli.

NYIMBO NA. 10 Tamandani Yehova Mulungu Wathu

a M’zilankhulo zina, mawu akuti “dipo” amamasuliridwa kuti “mtengo wa moyo” kapena “malipiro.”