Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Bwenzi Lenileni

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Bwenzi Lenileni

KODI pa nthawi ina munkamva ngati muli nokhanokha pamene munkakumana ndi mavuto. Tikukhala mu “nthawi yapadera komanso yovuta” zomwe zingachititse kuti tizikhala okhumudwa komanso tizidzimva kuti tili tokhatokha. (2 Tim. 3:1) Komabe tikakhala pamavuto tizikumbukira kuti pali ena omwe angatithandize. Baibulo limanena kuti anzathu enieni amatithandiza “pakagwa mavuto.”—Miy. 17:17.

MMENE ANZATHU ENIENI ANGATITHANDIZIRE

Ngakhale kuti anali pa ukaidi wosachoka panyumba, Paulo anakwanitsa kuchita utumiki wake pothandizidwa ndi anzake okhulupirika

Mtumwi Paulo anathandizidwa m’njira zambiri ndi anzake omwe ankayenda nawo limodzi. (Akol. 4:7-11) Pa nthawi yomwe iye anamangidwa ku Roma, anzake ankamuthandiza kuchita zinthu zomwe sakanatha kuchita. Mwachitsanzo, Epafurodito anapatsa Paulo zinthu zomwe ankafunikira, zimene abale ndi alongo a ku Filipi anatumiza. (Afil. 4:18) Tukiko ankakapereka makalata omwe Paulo ankalembera mipingo yosiyanasiyana. (Akol. 4:7) Paulo ankakwanitsabe kuchita utumiki wake ngakhale kuti anali pa ukaidi wosachoka panyumba kapenanso pamene anali m’ndende. Kodi ifeyo tingatani kuti tikhale bwenzi lenileni?

Masiku ano pali abale ndi alongo omwe amasonyeza zimene mabwenzi enieni ayenera kuchita pothandizana. Elisabet yemwe ndi mpainiya wokhazikika yemwe amakhala ku Spain, anafotokoza mmene mlongo wina anamuthandizira pa nthawi imene anakumana ndi mavuto. Pamene mayi ake a Elisabet anapezeka ndi khansa, mlongoyo ankamutumizira mameseji ambiri omulimbikitsa okhala ndi mavesi a m’Baibulo. Elisabet anati, “Mamesejiwo ankandilimbikitsa ndipo ankandithandiza kuti tsiku lililonse ndisamadzione ngati ndili ndekhandekha.”—Miy. 18:24.

Tingamagwirizanenso ndi Akhristu anzathu tikamawathandiza kupezeka pamisonkhano komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, tingathandize m’bale kapena mlongo wachikulire pokamutenga popita kumisonkhano kapena mu utumiki. Ngati mutachita zimenezo mungasangalale kwambiri ndipo mungalimbikitsane. (Aroma 1:12) Komabe, pali Akhristu ena omwe sangathe kuchoka panyumba. Ndiye kodi tingawasonyeze bwanji kuti ndife bwenzi lenileni?

MUZITHANDIZA AMENE SANGATHE KUCHOKA PANYUMBA

Akhristu ena sangathe kuchoka panyumba chifukwa cha matenda kapena mavuto ena. Chitsanzo ndi David yemwe anapezeka ndi khansa. Kwa miyezi 6, iye ankalandira thandizo la mankhwala. Pa nthawi yonse yomwe ankalandira thandizoli, David ndi mkazi wake Lidia ankalumikizidwa ku misonkhano ali kunyumba.

Kodi anzawo mumpingo ankawathandiza bwanji? Pambuyo pa misonkhano, anthu ena omwe apezeka ku Nyumba ya Ufumu ankayesetsa kuti acheze ndi David ndi Lidia kudzera pa vidiyokomfelensi. Kuwonjezera pamenepo David ndi Lidia akayankha pamisonkhano, abale ndi alongo ankawatumizira mameseji owalimbikitsa. Zimenezi zinachititsa kuti David ndi Lidia asamadzimve kuti ali okhaokha.

Muzigwira ntchito yolalikira ndi ofalitsa omwe sangathe kuchoka panyumba

Tingathenso kukonza zoti tizilalikira ndi abale ndi alongo omwe sangathe kuchoka panyumba. Ngati titasintha zinthu zina zing’onozing’ono pa moyo wathu, tingasonyeze kuti sitinawaiwale anthu ngati amenewa. (Miy. 3:27) Bwanji osakonza zoti mulembe nawo limodzi makalata kapena kulalikira kudzera pa foni? Anthu omwe sangathe kuchoka panyumba akhoza kuchita nawo msonkhano wokonzekera ulaliki kudzera pa vidiyokomfelensi. David ndi Lidia ankayamikira kwambiri dongosolo limeneli. David anafotokoza kuti, “Kungokhala nawo pa nthawi yokonzekera komanso kupemphera limodzi ndi kagulu kathu ka utumiki kunkatilimbikitsa kwambiri.” Kuwonjezera pamenepo, ngati n’zotheka mungakonze zoti nthawi zina muzikaphunzira Baibulo ndi wophunzira wanu kwa wofalitsa yemwe sangathe kuchoka panyumba.

Tikamacheza ndi abale ndi alongo omwe sangathe kuchoka panyumba, timafika podziwa makhalidwe awo abwino ndipo timakhala nawo pa ubwenzi wolimba. Mwachitsanzo, tikamagwira nawo ntchito yolalikira, tingaone mmene akugwiritsira ntchito mwaluso Mawu a Mulungu kuti awafike anthu pamtima, ndipo izi zingachititse kuti tiziwakonda kwambiri. Mukamathandiza Akhristu anzanu kuchita zinthu zokhudza kulambira mungakhale ndi anzanu ambiri.—2 Akor. 6:13.

Paulo anamva bwino mnzake Tito atabwera kudzamulimbikitsa. (2 Akor. 7:5-7) Nkhani ya Pauloyi ikutikumbutsa kuti tingathe kulimbikitsa Akhristu anzathu polankhula nawo mwachikondi, kupeza mpata wocheza nawo komanso kuchita zonse zomwe tingathe kuti tiwathandize.—1 Yoh. 3:18.

MUZITHANDIZA ANZANU AKAMAZUNZIDWA

Abale ndi alongo athu a ku Russia apereka chitsanzo chabwino pa nkhani yothandizana pa nthawi yomwe akuzunzidwa. Taganizirani zimene zinachitikira Sergey ndi mkazi wake Tatyana. Apolisi anabwera kudzafufuza kunyumba kwawo, ndipo kenako anawatengera kupolisi kuti akawafunse mafunso. Tatyana ndi amene anayambirira kutulutsidwa n’kubwerera kunyumba. Sergey anafotokoza kuti, “Tatyana atangofika kunyumba, mlongo wina wolimba mtima anabwera nthawi yomweyo. Anzathu enanso ambiri anabwera kudzatithandiza kusanjanso zinthu m’nyumba mwathu.”

Sergey anawonjezeranso kuti, “Ndimakonda kwambiri lemba la Miyambo 17:17, lomwe limati: ‘Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo mʼbale anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.’ Ndaona kukwaniritsidwa kwa mawu amenewa pa nthawi yomwe ndakhala ndikuzunzidwayi, yomwe sindikanakwanitsa kupirira pandekha. Yehova anandipatsa anzanga olimba mtima omwe ankandithandiza nthawi zonse.” a

Pamene mavuto akuwonjezereka m’dzikoli, tizifunikira anzathu oti atithandize. Ndipo anzathuwo adzatithandiza kwambiri pa nthawi ya Chisautso chachikulu. Choncho tiyeni panopa tiziyesetsa kulimbikitsa komanso kuthandiza anzathu.—1 Pet. 4:7, 8.