ZOTI NDIPHUNZIRE
Kukhala Olimba Mtima Ena Akamatitsutsa
Werengani Yeremiya 38:1-13 kuti muone zimene mungaphunzire kwa mneneri Yeremiya ndi Ebedi-meleki pa nkhani ya kulimba mtima.
Ganizirani nkhani yonse. Kodi Yeremiya anasonyeza bwanji kulimba mtima polengeza uthenga wa Yehova? (Yer. 27:12-14; 28:15-17; 37:6-10) Kodi anthu atamva uthengawo anachita chiyani?—Yer. 37:15, 16.
Fufuzani mozama. Kodi anthu ankafuna kuti Yeremiya achite chiyani? (jr 26-27 ¶20-22) Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza zitsime zakale. (it-1 471) Kodi mukuganiza kuti Yeremiya anamva bwanji pamene anali m’chitsime chamatope? Kodi Ebedi-meleki ayenera kuti ankachita mantha ndi chiyani?—w12 5/1 31 ¶2-3.
Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:
-
‘Kodi nkhaniyi ikundiphunzitsa chiyani ponena za mmene Yehova amatetezera atumiki ake okhulupirika?’ (Sal. 97:10; Yer. 39:15-18)
-
‘Kodi ndi pa nthawi iti pomwe ndingafunike kusonyeza kulimba mtima?’
-
‘Kodi ndingatani kuti ndizilimba mtima n’kuchita zoyenera ndikamatsutsidwa?’ (w11 3/1 30) a
a Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mmene mungamaphunzirire, onani “Mfundo Zothandiza Pophunzira” mu Nsanja ya Olonda yophunzira ya July 2023.