Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 5

Makhalidwe Amene Amatichititsa Kupezeka Pamisonkhano

Makhalidwe Amene Amatichititsa Kupezeka Pamisonkhano

“Mukulengezabe imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.”1 AKOR. 11:26.

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1-2. (a) Kodi Yehova amaona chiyani anthu mamiliyoni ambiri akasonkhana kuti achite mwambo wa Chikumbutso? (Onani chithunzi patsamba loyamba.) (b) Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

TIKAKHALA pamwambo wa Chikumbutso, sikuti Yehova amangotiona m’chigulugulu. Iye amaona munthu aliyense payekha. Mwachitsanzo, amaona aliyense amene amapezeka pamwambowu chaka chilichonse. Ena mwa anthu amenewa amapezekabe pamwambowu ngakhale kuti akuzunzidwa kwambiri. Palinso ena amene sapezeka pamisonkhano nthawi zonse komabe safuna kuphonya mwambo wa Chikumbutso. Yehova amaonanso anthu amene apezeka koyamba pamwambowu kuti aone zimene zimachitika.

2 N’zosakayikitsa kuti Yehova amasangalala kwambiri kuona anthu ambiri atapezeka pa Chikumbutso. (Luka 22:19) Koma sikuti Yehova amangosangalala ndi kuchuluka kwa anthu amene afika. Iye amasangalala kwambiri akaona zolinga za anthu amene apezekawo. Munkhaniyi tikambirana funso lofunika kwambiri lakuti, N’chifukwa chiyani tiyenera kupezeka pa Chikumbutso komanso pamisonkhano ya mlungu uliwonse yomwe Yehova amakonzera anthu amene amamukonda?

(Onani ndime 1-2) *

KUDZICHEPETSA

3-4. (a) N’chifukwa chiyani timapezeka pamisonkhano? (b) Kodi kupezeka pamisonkhano kumasonyeza kuti tili ndi khalidwe liti? (c) Malinga ndi 1 Akorinto 11:23-26, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuphonya Chikumbutso?

3 Chifukwa chachikulu chimene timapezekera pamisonkhano ya mpingo n’chakuti tilambire Yehova. Timasonkhananso chifukwa chakuti pa nthawi imeneyi timaphunzitsidwa ndi Yehova. Anthu odzikuza safuna kuphunzitsidwa zinthu. (3 Yoh. 9) Koma ifeyo timafuna kuphunzitsidwa ndi Yehova komanso gulu lake.​—Yes. 30:20; Yoh. 6:45.

4 Choncho tikamapezeka pamisonkhano timasonyeza kuti ndife odzichepetsa ndipo timafuna kuphunzitsidwa. Komanso tikamapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu timakhala tikutsatira modzichepetsa lamulo lake lakuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira.” (Werengani 1 Akorinto 11:23-26.) Mwambo umenewu umatithandiza kukhala ndi chiyembekezo champhamvu komanso umatikumbutsa kuti Yehova amatikonda kwambiri. Koma Yehova amadziwa kuti anthufe timafunika kulimbikitsidwa nthawi zonse, osati kamodzi kokha pa chaka. Choncho amatipatsa misonkhano ya mlungu uliwonse ndipo amatilimbikitsa kuti tizipezekapo. Mtima wodzichepetsa umatithandiza kuti tizipezeka pamisonkhano. Ndipo timagwiritsa ntchito nthawi yambiri mlungu uliwonse kuti tizikonzekera misonkhanoyi komanso kupezekapo.

5. N’chifukwa chiyani anthu odzichepetsa amavomera Yehova akawaitana kuti awaphunzitse?

5 Chaka chilichonse, anthu ambiri odzichepetsa amavomera akaitanidwa ndi Yehova kuti awaphunzitse. (Yes. 50:4) Iwo amasangalala kufika pamwambo wa Chikumbutso kenako amayamba kupezekanso pamisonkhano ina. (Zek. 8:20-23) Tonsefe timasangalala kuphunzitsidwa komanso kutsogoleredwa ndi Yehova, yemwe ndi ‘thandizo lathu komanso wopereka chipulumutso.’ (Sal. 40:17) Ndipotu palibe chinthu china chosangalatsa ndiponso chofunika kuposa kuphunzitsidwa ndi Yehova komanso Mwana wake Yesu.​—Mat. 17:5; 18:20; 28:20.

6. Kodi kudzichepetsa kunathandiza bwanji bambo wina kuti apezeke pa Chikumbutso?

6 Chaka chilichonse, timayesetsa kuitanira anthu ambiri kumwambo wa Chikumbutso. Ndipo anthu ambiri apindula kwambiri ataitanidwa kumwambowu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi bambo wina amene anapatsidwa kapepala komuitanira ku Chikumbutso koma ananena kuti sangapiteko. Tsiku la Chikumbutso litafika, m’baleyo anadabwa kuona bambo uja akulowa m’Nyumba ya Ufumu. Bamboyo anasangalala kwambiri ataona kuti analandiridwa bwino ndipo anayamba kupezeka pamisonkhano ina. Chaka chimenecho, iye anangojomba pamisonkhano katatu kokha. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti achite zimenezi? Iye anali wodzichepetsa kwambiri moti anasintha maganizo ake. M’bale amene anamuitanayo anati: “Ndi munthu wodzichepetsa kwambiri.” N’zosachita kufunsa kuti Yehova ndi amene anamukoka kuti azimulambira ndipo panopa anabatizidwa.​—2 Sam. 22:28; Yoh. 6:44.

7. Kodi zimene timaphunzira pamisonkhano komanso kuwerenga m’Baibulo zingatithandize bwanji kukhala odzichepetsa?

7 Zimene timaphunzira kumisonkhano komanso kuwerenga m’Baibulo zingatithandize kukhala odzichepetsa. Kukatsala milungu yochepa kuti tichite Chikumbutso, timakambirana kumisonkhano chitsanzo cha Yesu pa khalidwe la kudzichepetsa limene anasonyeza pololera kupereka moyo wake monga nsembe. Komanso kukatsala masiku ochepa kuti tichite Chikumbutso, timalimbikitsidwa kuti tiziwerenga nkhani za m’Baibulo zokhudza zimene zinamuchitikira atatsala pang’ono kuphedwa ndiponso pambuyo poukitsidwa. Zimene timaphunzira pamisonkhano komanso kuwerenga m’Baibulozi zimatithandiza kuyamikira kwambiri zimene Yesu anatichitira. Zimatithandizanso kuti tizitsanzira kudzichepetsa kwake komanso kuti tizichita zofuna za Yehova ngakhale pa nthawi imene takumana ndi mavuto.​—Luka 22:41, 42.

KULIMBA MTIMA

8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima?

8 Timatsanziranso Yesu pa nkhani yokhala olimba mtima. Taganizirani mmene anasonyezera kulimba mtima kutatsala masiku ochepa kuti aphedwe. Iye ankadziwa kuti posachedwa adani ake amunyoza, kumumenya kenako n’kumupha. (Mat. 20:17-19) Komabe iye analolera kuti zimenezi zimuchitikire. Atatsala pang’ono kugwidwa, anauza ophunzira ake amene anali naye ku Getsemane kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.” (Mat. 26:36, 46) Ndipo gulu la anthu onyamula zida litafika, iye anawayandikira n’kuwauza kuti amene mukumufunayo ndine. Atatero anauza asilikali kuti awasiye ophunzira ake azipita. (Yoh. 18:3-8) Apatu Yesu anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Masiku ano, Akhristu odzozedwa komanso a nkhosa zina amayesetsa kukhala olimba mtima ngati Yesu. Kodi amachita bwanji zimenezi?

Mukamalimba mtima n’kumapezeka pamisonkhano mumalimbikitsa anthu ena (Onani ndime 9) *

9. (a) N’chifukwa chiyani tingafunike kulimba mtima kuti tizisonkhana nthawi zonse? (b) Kodi chitsanzo chathu chingathandize bwanji anthu amene amangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo?

9 Timafunikanso kulimba mtima kuti tizisonkhana nthawi zonse ngakhale pamene zinthu zavuta. Abale ndi alongo ena amasonkhanabe ngakhale atakumana ndi mavuto monga maliro, matenda kapena zinthu zina zokhumudwitsa. Ena amapita kumisonkhano ngakhale kuti amatsutsidwa ndi achibale awo kapena akuluakulu a boma. Kodi mukuganiza kuti chitsanzo chathu chimalimbikitsa bwanji abale amene amangidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo? (Aheb. 13:3) Iwo akamva kuti tikutumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto, amapitiriza kukhulupirira Mulungu, kulimba mtima komanso kukhala okhulupirika. Zoterezi n’zimene zinachitikira mtumwi Paulo. Iye ali kundende, ankasangalala akamva zoti abale akutumikirabe Mulungu mokhulupirika. (Afil. 1:3-5, 12-14) Atatsala pang’ono kumasulidwa kapena atangomasulidwa kumene, analembera kalata Akhristu achiheberi. M’kalatayo analimbikitsa Akhristuwo kuti ‘apitirize kukonda abale’ komanso asaleke kusonkhana.​—Aheb. 10:24, 25; 13:1.

10, 11. (a) Kodi ndi anthu ati amene tiyenera kuwaitanira ku Chikumbutso? (b) Kodi lemba la Aefeso 1:7 limatilimbikitsa bwanji kuchita zimenezi?

10 Timasonyezanso kulimba mtima tikamaitanira ku Chikumbutso achibale athu, anzathu akuntchito komanso anthu oyandikana nawo. Koma kodi n’chifukwa chiyani timawaitana? Kuyamikira zimene Yehova ndi Yesu atichitira n’kumene kumatilimbikitsa kuti tiziitanira anthu ku Chikumbutso. Timafuna kuti nawonso aphunzire mmene angapindulire ndi ‘kukoma mtima kwakukulu’ kwa Mulungu kumene anakusonyeza popereka dipo.​—Werengani Aefeso 1:7; Chiv. 22:17.

11 Tikamalimba mtima n’kumapezeka pamisonkhano, timasonyezanso khalidwe lina labwino limene Mulungu ndi Yesu amalisonyeza m’njira zapadera kwambiri.

CHIKONDI

12. (a) Kodi misonkhano imatithandiza bwanji kuti tizikonda kwambiri Yehova ndi Yesu? (b) Kodi lemba la 2 Akorinto 5:14, 15 limatilimbikitsa kuchita chiyani potsanzira Yesu?

12 Timapitanso kumisonkhano chifukwa chokonda Yehova ndi Yesu. Ndipo zimene timaphunzira kumisonkhanoko zimatithandiza kuti tiziwakonda kwambiri. Tikafika kumisonkhano timakumbutsidwa zimene iwo atichitira. (Aroma 5:8) Komanso mwambo wa Chikumbutso ndi umene umatikumbutsa kwambiri za chikondi chimene atisonyeza. Timazindikira kuti Yehova ndi Yesu amakonda ngakhalenso anthu amene panopa sadziwa za kufunika kwa dipo. Ndiyeno poyamikira chikondichi, timayesetsa kutsanzira Yesu pa moyo wathu. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Timalimbikitsidwanso kutamanda Yehova chifukwa chopereka dipoli. Njira ina imene tingamutamandire ndi kuyankha pamisonkhano ya mpingo.

13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake? Fotokozani.

13 Tingasonyeze kuti timakonda Yehova ndi Yesu pololera kuti tisachite zinthu zina n’cholinga choti tiziwatumikira. Kunena zoona, pamafunika kudzimana zinthu zina kuti tizipezeka pamisonkhano. M’mipingo yambiri, misonkhano ina imachitika mkati mwa mlungu ndipo anthu ambiri amakhala atatopa pambuyo poweruka kuntchito. Misonkhano ina imachitika kumapeto kwa mlungu pa nthawi imene anthu ena amakhala akupuma. Kodi Yehova amadziwa zoti timalolera kupita kumisonkhano ngakhale titatopa? Ee kwambiri. Ndipo tikamayesetsa kuti tipezeke pamisonkhano ngakhale zinthu zitavuta kwambiri m’pamenenso Yehova amayamikira kwambiri.​—Maliko 12:41-44.

14. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali ndi mtima wololera kuvutikira ena?

14 Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yololera kuvutikira ena. Timadziwa kuti iye anafera ophunzira ake. Komatu tsiku lililonse ankaikanso patsogolo zofuna za ophunzira akewo osati zake. Mwachitsanzo, ankayesetsa kuti akumane nawo ngakhale pamene watopa kapena kupanikizika ndi nkhawa. (Luka 22:39-46) Iye ankaganizira kwambiri zimene angachitire anthu osati zimene anthu angamuchitire. (Mat. 20:28) Ngati ifenso timakonda Yehova ndi abale athu, tidzayesetsa kuti tipezeke pa Chikumbutso komanso kuti tizipezeka pamisonkhano yonse ya mpingo.

15. Kodi tiyenera kuyesetsa kuthandiza makamaka anthu ati?

15 Timasangalala kwambiri kukhala m’gulu la Akhristu oona ndipo timafuna kuchita zonse zimene tingathe poitanira anthu ena m’gululi. Koma tiyenera kuyesetsa kuthandiza makamaka “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro” amene panopa afooka. (Agal. 6:10) Tingasonyeze kuti timawakonda powaitanira kumisonkhano makamaka kumwambo wa Chikumbutso. Mofanana ndi Yehova ndi Yesu, timasangalala kwambiri munthu wofooka akabwerera kwa Yehova yemwe ndi Atate wathu wachikondi komanso M’busa wathu.​—Mat. 18:14.

16. (a) Kodi tingatani kuti tizilimbikitsana, nanga kusonkhana kungatithandize bwanji? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti inoyo ndi nthawi yabwino yokumbukira mawu a Yesu a pa Yohane 3:16?

16 Milungu imene ikubwerayi, tiyeni tiyesetse mmene tingathere kuitanira anthu ambiri kumwambo wa Chikumbutso womwe uchitike pa 19 April 2019. (Onani bokosi lakuti, “ Kodi Mudzaitana Anthu?”) Tiyeni tiyesetse kuti chaka chonsechi tizilimbikitsana popezeka pamisonkhano yonse imene Yehova amatikonzera. Pamene mapeto akuyandikira, kusonkhana n’kofunika kwambiri chifukwa kungatithandize kuti tikhalebe odzichepetsa, olimba mtima komanso achikondi. (1 Ates. 5:8-11) Tiyeni tizisonyeza kuyamikira ndi mtima wonse chikondi chimene Yehova ndi Mwana wake atisonyeza.​—Werengani Yohane 3:16.

NYIMBO NA. 126 Khalani Maso, Limbani M’chikhulupiriro, Khalani Amphamvu

^ ndime 5 Mwambo wa Chikumbutso udzachitika Lachisanu pa 19 April 2019, ndipo udzakhala msonkhano wapadera kwambiri pamisonkhano yonse ya chaka chimenechi. Kodi n’chiyani chimatichititsa kupezeka pamsonkhanowu? N’chifukwa chakuti timafuna kusangalatsa Yehova. Munkhaniyi, tikambirana makhalidwe amene amatichititsa kuti tizipezeka pamwambo wa Chikumbutso komanso pamisonkhano ya mlungu uliwonse.

^ ndime 50 CHITHUNZI PATSAMBA LOYAMBA: Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse akuitanidwa ku Chikumbutso

^ ndime 52 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI Tsamba 28-29: M’bale ali kundende ndipo walimbikitsidwa kwambiri ndi kalata imene walemberedwa. Iye akuona kuti sanaiwalidwe ndipo akusangalala kumva kuti banja lake lonse ndi lokhulupirikabe ngakhale kuti zinthu sizili bwino m’dera lawo.