NKHANI YOPHUNZIRA 4
Mwambo wa Chikumbutso Umasonyeza Makhalidwe a Mfumu Yakumwamba
“Mkate uwu ukuimira thupi langa. . . . Vinyoyu akuimira ‘magazi anga a pangano.’”—MAT. 26:26-28.
NYIMBO NA. 16 Tamandani Yehova Chifukwa cha Mwana Wake Wodzozedwa
ZIMENE TIPHUNZIRE *
1-2. (a) N’chifukwa chiyani si zodabwitsa kuti Yesu anapereka njira yosavuta yokumbukirira imfa yake? (b) Kodi tikambirana makhalidwe ati a Yesu?
AMBIRIFE tikhoza kufotokoza bwinobwino zimene zimachitika pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Zili choncho chifukwa chakuti mwambowu ndi wosavuta. Komatu mwambo umenewu ndi wofunika kwambiri. Ndiye mwina tingadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani mwambowu uli wosavuta chonchi?’
2 Yesu ali padzikoli ankaphunzitsa mfundo za choonadi zofunika kwambiri m’njira yosavuta kumva. (Mat. 7:28, 29) Choncho n’zosadabwitsa kuti anaperekanso njira yosavuta yochitira mwambo wokumbukira imfa yake. Munkhaniyi tikambirana za mwambo umenewu ndiponso zinthu zina zimene Yesu anachita komanso kulankhula. Tiona kuti Yesu ndi wodzichepetsa, wolimba mtima komanso wachikondi. Tiphunziranso zimene tingachite kuti tizimutsanzira kwambiri.
YESU NDI WODZICHEPETSA
3. Malinga ndi Mateyu 26:26-28, n’chifukwa chiyani tinganene kuti mwambo umene Yesu anayambitsa ndi wosavuta, nanga zinthu ziwiri zimene anagwiritsa ntchito zikuimira chiyani?
3 Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake ali ndi atumwi ake 11 okhulupirika. Iye anangotenga zinthu zimene zinatsala pa Pasika n’kuyambitsa mwambo wosavutawu. (Werengani Mateyu 26:26-28.) Anagwiritsa ntchito mkate wopanda chofufumitsa komanso vinyo amene analipo. Yesu anauza atumwi ake kuti zinthu ziwirizi zikuimira thupi lake lopanda uchimo komanso magazi ake. Iye anali atatsala pang’ono kupereka zinthuzi nsembe. N’kutheka kuti atumwi sanadabwe kuona kuti mwambo watsopanowu unali wosavuta. Kodi n’chifukwa chiyani tikutero?
4. Kodi malangizo amene Yesu anapatsa Marita akutithandiza bwanji kumvetsa chifukwa chake anayambitsa mwambo wosavuta?
4 Taganizirani zimene zinachitika miyezi ingapo Yesu asanayambitse mwambowu. Iye anapita kwa anzake omwe anali Lazaro, Marita ndi Mariya. Anthuwo akucheza, Yesu anayamba kuwaphunzitsa. Marita analipo koma anatanganidwa ndi kukonza chakudya chambiri kuti mlendo wake wapaderayu adye. Yesu ataona zimenezi anamufotokozera mokoma mtima kuti sankayenera kuphika zambiri. (Luka 10:40-42) Ndiyeno Yesu atatsala pang’ono kupereka moyo wake nsembe, anatsatira malangizo amene anapatsa Marita aja. Iye anagwiritsa ntchito zinthu zochepa poyambitsa mwambo wokumbukira imfa yake. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani zokhudza Yesu?
5. Kodi mwambo wosavuta wa Chikumbutso umasonyeza kuti Yesu ndi wotani, nanga zimenezi zikugwirizana bwanji ndi Afilipi 2:5-8?
5 Yesu ankasonyeza kudzichepetsa pa zonse zimene ankalankhula komanso kuchita. Choncho n’zosadabwitsa kuti anasonyezanso kudzichepetsa usiku woti aphedwa mawa lake. (Mat. 11:29) Iye ankadziwa kuti anali atatsala pang’ono kupereka nsembe yofunika kwambiri komanso kuti Yehova adzamuukitsa kuti akakhale ndi udindo waukulu kumwamba. Ngakhale zinali choncho, sankafuna kudzionetsera polamula anthu kuti azichita zambiri pokumbukira imfa yake. M’malomwake, anauza ophunzira ake kuti azichita mwambo wosavuta pokumbukira imfa yake kamodzi pa chaka. (Yoh. 13:15; 1 Akor. 11:23-25) Mwambowu ndi wosavuta koma woyenerera ndipo umasonyeza kuti Yesu si wodzikuza. Timasangalala kwambiri kuti Mfumu yathu yakumwamba ili ndi makhalidwe abwino monga kudzichepetsa.—Werengani Afilipi 2:5-8.
6. Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Yesu tikakumana ndi mavuto?
6 Kodi tingatsanzire bwanji kudzichepetsa kwa Yesu? Tingachite zimenezi tikamaika zofuna za ena patsogolo osati zathu. (Afil. 2:3, 4) Taganiziraninso zimene zinachitika usiku woti Yesu aphedwa mawa lake. Iye ankadziwa kuti afa imfa yopweteka kwambiri koma ankadera nkhawa atumwi ake chifukwa chodziwa kuti adzakhala ndi chisoni kwambiri. Choncho usikuwo anawaphunzitsa komanso kuwalimbikitsa. (Yoh. 14:25-31) Iye ankaganizira kwambiri zofuna za anthu ena osati zofuna zake. Apatu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri.
YESU NDI WOLIMBA MTIMA
7. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima atangoyambitsa mwambo wa Chikumbutso?
7 Yesu atangoyambitsa mwambo wa Chikumbutso anasonyeza kulimba mtima kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti iye anavomera kuchita zimene Atate ake ankafuna. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti adzaimbidwa mlandu wochititsa manyazi wakuti wanyoza Mulungu kenako n’kuphedwa. (Mat. 26:65, 66; Luka 22:41, 42) Yesu anakhalabe wokhulupirika n’cholinga choti alemekeze dzina la Yehova, asonyeze kuti Yehova ndi woyenera kulamulira komanso athandize anthu olapa kuti adzapeze moyo wosatha. Pa nthawi imodzimodziyo, Yesu anathandiza otsatira ake kuti akonzekere zimene adzakumane nazo.
8. (a) Kodi Yesu anauza atumwi ake okhulupirika kuti chiyani? (b) Yesu atamwalira, kodi ophunzira ake ankamutsanzira bwanji pa nkhani yolimba mtima?
8 Yesu anasonyeza kulimba mtima posiya kuganizira mavuto amene akumane nawo n’kumaganizira zimene atumwi ake okhulupirika ankafunikira. Mwambo wosavuta umene anauyambitsa atatulutsa Yudasi unali woti udzakumbutsa otsatira ake odzozedwa zinthu zabwino zimene zikutheka chifukwa cha magazi a Yesu komanso ubwino wokhala m’pangano latsopano. (1 Akor. 10:16, 17) Yesu anafotokozanso zimene iye ndi Atate ake ankafuna kuti otsatira akewo azichita kuti akhale oyenera kupita kumwamba. (Yoh. 15:12-15) Yesu anauzanso atumwi ake mavuto amene iwo adzakumane nawo. Ndiyeno anawalimbikitsa kuti atengere chitsanzo chake powauza kuti, “Limbani mtima.” (Yoh. 16:1-4a, 33) Patapita zaka zambiri, ophunzira a Yesu ankamutsanzirabe pa nkhani yochita zinthu modzipereka komanso molimba mtima. Iwo ankalolera kuvutika n’cholinga choti athandizane pa mavuto osiyanasiyana.—Aheb. 10:33, 34.
9. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yolimba mtima?
9 Ifenso masiku ano timatsanzira Yesu pa nkhani yolimba mtima. Mwachitsanzo, timalimba mtima kuti tithandize abale athu amene akuzunzidwa chifukwa cha zimene amakhulupirira. Nthawi zina, abale athu amamangidwa popanda chifukwa. Zimenezi zikachitika tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwathandize. (Afil. 1:14; Aheb. 13:19) Timasonyezanso kulimba mtima tikamapitiriza kulalikira mopanda mantha. (Mac. 14:3) Mofanana ndi Yesu, timalalikirabe uthenga wa Ufumu ngakhale pamene anthu akutitsutsa kapena kutizunza. Koma nthawi zina tikhoza kuchita mantha. Ndiye kodi tingatani ngati zimenezi zitachitika?
10. Kodi tiyenera kuchita chiyani nyengo ya Chikumbutso ikamayandikira? Perekani chifukwa.
10 Kuti tikhale olimba mtima kwambiri, tiyenera kuganizira zinthu zimene zingatheke chifukwa cha dipo la Khristu. (Yoh. 3:16; Aef. 1:7) Nyengo ya Chikumbutso ikamayandikira timakhala ndi mwayi woganizira zimene Yesu anatichitira n’kumaziyamikira. Choncho, tiyenera kutsatira pulogalamu ya kuwerenga Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso komanso kuganizira kwambiri zimene zinachitika m’masiku otsiriza a moyo wa Yesu padzikoli. Izi zingatithandize kuti tikapita kumwambowu tikamvetse bwino tanthauzo la zizindikiro komanso nsembe yamtengo wapatali imene zimaimira. Tikazindikira zimene Yehova ndi Yesu atichitira n’kumvetsa mmene zimathandizira ifeyo ndi anzathu, chiyembekezo chathu chimakhala champhamvu ndipo zimatilimbikitsa kuti tikhalebe olimba mtima mpaka mapeto.—Aheb. 12:3.
11-12. Kodi pofika pano, takambirana chiyani?
11 Pofika pano, taona kuti mwambo wa Chikumbutso umatithandiza kuyamikira dipo la Yesu komanso kuzindikira makhalidwe ake monga kudzichepetsa komanso kulimba mtima. Timayamikira kwambiri kuti Yesu adakali ndi makhalidwe amenewa pamene akugwira ntchito monga Mkulu wa Ansembe amene amatichonderera kwa Mulungu. (Aheb. 7:24, 25) Kuti tisonyeze kuyamikira, tiyenera kutsatira lamulo la Yesu lakuti tizichita mwambo wokumbukira imfa yake. (Luka 22:19, 20) Tiyenera kuchita zimenezi pa tsiku logwirizana ndi Nisani 14, lomwe ndi tsiku lofunika kwambiri pa chaka.
12 Mwambo wosavuta umene Yesu anauyambitsa umatithandizanso kuzindikira khalidwe lina limene linamuchititsa kulolera kuti atifere. Iye ali padzikoli, ankadziwika kwambiri ndi khalidwe limeneli. Kodi khalidwe lake ndi liti?
YESU NDI WACHIKONDI
13. Kodi lemba la Yohane 15:9 ndi 1 Yohane 4:8-10 limafotokoza bwanji chikondi chimene Yehova ndi Yesu anasonyeza, nanga ndani amapindula ndi chikondi chawo?
13 Zonse zimene Yesu ankachita zimasonyeza mmene Yehova amatikondera. (Werengani Yohane 15:9; 1 Yohane 4:8-10.) Yesu analolera kupereka moyo wake m’malo mwa ife chifukwa ali ndi mtima wachikondi kwambiri. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” timapindula ndi chikondi chimene Yehova ndi Mwana wake anatisonyeza popereka nsembe ya dipo. (Yoh. 10:16; 1 Yoh. 2:2) Zinthu zimene Yesu anagwiritsa ntchito poyambitsa mwambo wa Chikumbutso zimasonyeza kuti iye amakonda kwambiri ophunzira ake. N’chifukwa chiyani tikutero?
14. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda ophunzira ake?
14 Yesu anasonyeza chikondi kwa otsatira ake odzozedwa poyambitsa mwambo wosavuta kuti azichita. Mwambowu unali woti ophunzira odzozedwa aziuchita chaka chilichonse ngakhale pamene akukumana ndi mavuto monga kukhala mundende. (Chiv. 2:10) Ndipo ophunzirawo akhala akukwanitsa kuchita zimenezi chaka chilichonse.
15-16. Kodi zinatheka bwanji kuti anthu ena akwanitse kuchita Chikumbutso ngakhale zinthu zitavuta? Perekani zitsanzo.
15 Akhristu onse akhala akuyesetsa kuti azichita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Iwo amachita Chikumbutso motsatira malangizo a Yesu mmene angathere ngakhale pamene zinthu zavuta kwambiri. Tiyeni tikambirane zitsanzo zina pa nkhaniyi. Pamene M’bale Harold King anali m’chipinda chayekha kundende ya ku China anachita zonse zimene angathe. Iye anagwiritsa ntchito zinthu zimene anali nazo kuti apange mobisa zizindikiro za pa Chikumbutso. Anayesetsanso kuti apeze njira yodziwira tsiku la Chikumbutso. Nthawi ya Chikumbutso itakwana iye anaimba nyimbo, kupemphera komanso kukamba nkhani. Anachita zonsezi ngakhale kuti anali yekhayekha.
16 Chitsanzo china ndi cha alongo amene anali m’ndende pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse. Iwo anaika moyo wawo pa ngozi kuti achite Chikumbutso. Koma popeza mwambowu ndi wosavuta, iwo anakwanitsa kuuchita mobisa. Alongowa anati: “Tinaimirira mozungulira katebulo kamene tinakaphimba ndi nsalu yoyera n’kuikapo zizindikiro. Tinagwiritsa ntchito kandulo chifukwa
magetsi akanatigwiritsa. . . . Pa mwambowu, tinabwerezanso zimene tinalonjeza Atate athu zoti tizigwiritsa ntchito mphamvu zathu zonse kuti dzina lake lopatulika liyeretsedwe.” Alongowatu anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri. Kunena zoona, Yesu anasonyeza chikondi chachikulu pamene anayambitsa mwambo umene tikhoza kuuchita ngakhale zinthu zitavuta.17. Kodi tingachite bwino kudzifunsa mafunso ati?
17 Nyengo ya Chikumbutso ikamayandikira tingachite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ndingatani kuti ndizitsanzira kwambiri Yesu pa nkhani yosonyeza chikondi? Nanga kodi ndimaganizira kwambiri zofuna za Akhristu anzanga kuposa zofuna zanga? Kodi ndimayembekezera zambiri kwa abale ndi alongo anga kuposa zimene angakwanitse?’ Tiyeni nthawi zonse tizitsanzira Yesu posonyeza kuti ‘timamvera chisoni’ anzathu.—1 Pet. 3:8.
TIZIKUMBUKIRA MFUNDO ZIMENE TAPHUNZIRAZI
18-19. (a) Kodi n’chiyani chidzachitike ngakhale tikadzasiya kuchita Chikumbutso? (b) Kodi inuyo muzichita chiyani panopa?
18 Nthawi ina m’tsogolomu tidzasiya kuchita mwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Tikutero chifukwa chakuti Yesu akadzabwera pa chisautso chachikulu, adzasonkhanitsa odzozedwa amene adzakhale adakali padzikoli kuti apite kumwamba. Apa m’pamene tidzasiyire kuchita Chikumbutso.—1 Akor. 11:26; Mat. 24:31.
19 Koma ngakhale titadzasiya kuchita mwambowu, tizidzakumbukirabe mfundo yakuti mwambo wosavutawu unkasonyeza kuti Yesu anali wodzichepetsa, wolimba mtima komanso wachikondi kuposa munthu wina aliyense. Pa nthawi imeneyo, anthu onse amene anachita nawo mwambowu azidzalimbikitsa anzawo powafotokozera zimenezi. Koma kuti tipindule ndi mwambowu panopa, tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa, kulimba mtima komanso chikondi. Tikamatero Yehova adzatidalitsa kwambiri.—2 Pet. 1:10, 11.
NYIMBO NA. 13 Khristu Ndi Chitsanzo Chathu
^ ndime 5 Posachedwapa tichita mwambo wa Chikumbutso pokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Mwambo wosavutawu umasonyeza kuti Yesu ndi wodzichepetsa, wolimba mtima komanso wachikondi. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tizitsanzira makhalidwe a Yesuwa.
^ ndime 55 MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Zikusonyeza atumiki a Mulungu okhulupirika akuchita chikumbutso nthawi ya atumwi, chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kundende ya Nazi komanso m’Nyumba ya Ufumu ya ku South America masiku ano.