Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 2

Mukhoza Kuthandiza Anthu Komanso Kuwalimbikitsa

Mukhoza Kuthandiza Anthu Komanso Kuwalimbikitsa

[Amenewa ndi] antchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo amenewa andithandiza ndi kundilimbikitsa.”​AKOL. 4:11.

NYIMBO NA. 90 Tizilimbikitsana

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi atumiki a Yehova ambiri akukumana ndi mavuto ati?

ATUMIKI a Yehova ambiri padziko lonse akukumana ndi mavuto amene amawadetsa nkhawa. Kodi ndi mmene zililinso mumpingo wanu? Akhristu ena akudwala kwambiri kapena anaferedwa. Pomwe ena ali ndi chisoni chifukwa wachibale wawo kapena mnzawo wapamtima wasiya choonadi. Ndiye pali enanso amene akuvutika chifukwa cha ngozi zachilengedwe. Anthu onsewa amafunika kulimbikitsidwa. Kodi tingawathandize bwanji?

2. N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo ankafunika kulimbikitsidwa nthawi zina?

2 Mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto oopsa motsatizanatsatizana. (2 Akor. 11:23-28) Iye anafunikanso kupirira “munga m’thupi” womwe mwina ukutanthauza vuto linalake lam’thupi mwake. (2 Akor. 12:7) Iye anakhumudwanso pamene mnzake wina dzina lake Dema anamusiya “chifukwa chokonda zinthu za m’nthawi ino.” (2 Tim. 4:10) Paulo anali Mkhristu wodzozedwa, wolimba mtima komanso wodzipereka pothandiza ena, koma nthawi zina ankakhumudwa.​—Aroma 9:1, 2.

3. Kodi ndi ndani amene anathandiza komanso kulimbikitsa Paulo?

3 Chosangalatsa n’chakuti Paulo anathandizidwa komanso kulimbikitsidwa. Choyamba, Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera kuti amulimbikitse. (2 Akor. 4:7; Afil. 4:13) Chachiwiri, anagwiritsa ntchito Akhristu ena kuti alimbikitse Paulo. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti Akhristu ena amene ankatumikira nawo ‘anamuthandiza komanso kumulimbikitsa.’ (Akol. 4:11) Ena mwa anthu amene anawatchula anali Arisitako, Tukiko ndi Maliko. Anthu amenewa analimbikitsa Paulo ndiponso kumuthandiza kuti apirire mavuto ake. Kodi ndi makhalidwe ati amene anathandiza Akhristu atatuwa kuti akhale olimbikitsa? Nanga tingawatsanzire bwanji pothandiza komanso kulimbikitsa anthu ena?

MUZIKHALA OKHULUPIRIKA NGATI ARISITAKO

Tizikhala okhulupirika ngati Arisitako pothandiza abale ndi alongo “pakagwa mavuto” (Onani ndime 4-5) *

4. Kodi Arisitako anasonyeza bwanji kuti anali mnzake wa Paulo wokhulupirika?

4 Arisitako, yemwe anali Mkhristu wochokera ku Tesalonika, anali mnzake wa Paulo wokhulupirika. Baibulo limatchula za Arisitako koyamba pa nthawi imene Paulo anapita ku Efeso pa ulendo wake wachitatu waumishonale. Pamene ankayenda ndi Paulo, Arisitako anagwidwa ndi gulu la anthu. (Mac. 19:29) Atamasulidwa anasonyeza kukhulupirika chifukwa sanachoke koma anakhalabe ndi Paulo. Patapita miyezi ingapo, Arisitako anali adakali ndi Paulo ku Girisi ngakhale kuti anthu ena ankaopseza Paulo. (Mac. 20:2-4) Cha m’ma 58 C.E., Paulo anamangidwa ndipo kenako anatumizidwa ku Roma. Pa ulendo wautaliwu, Arisitako anamuperekeza ndipo anali limodzi pamene ngalawa imene anakwera inasweka. (Mac. 27:1, 2, 41) Atafika ku Roma, zikuoneka kuti Arisitako anakhala limodzi ndi Paulo m’ndende. (Akol. 4:10) M’pake kuti Paulo analimbikitsidwa kwambiri ndi Arisitako yemwe anali mnzake wokhulupirika.

5. Malinga ndi Miyambo 17:17, kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika kwa anzathu?

5 Nafenso tingasonyeze kuti ndife okhulupirika kwa anzathu tikamathandiza abale ndi alongo “pakagwa mavuto.” (Werengani Miyambo 17:17.) Ngakhale mavutowo atatha, m’bale kapena mlongo wathu angafunike kulimbikitsidwa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Frances. * Bambo ake anamwalira ndi khansa kenako miyezi itatu isanathe mayi ake anamwaliranso ndi matenda omwewo. Iye anati: “Ndikuona kuti mavuto aakulu amatisokoneza kwa nthawi yaitali. Ndimayamikira anzanga ena okhulupirika amene amadziwa kuti ndikuvutikabe ngakhale kuti padutsa nthawi yaitali kuchokera pamene makolo anga anamwalira.”

6. Kodi anthu okhulupirika amachita chiyani?

6 Anthu okhulupirika amadzimana zinthu zina kuti azithandiza abale ndi alongo awo. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Peter anamupeza ndi matenda oopsa kwambiri. Mkazi wake, Kathryn, anati: “M’bale ndi mlongo wamumpingo wathu anatiperekeza kuchipatala ndipo tsiku limeneli ndi limene Peter anauzidwa kuti ali ndi matendawa. Nthawi yomweyo, iwo anasankha zoti asatisiye tokha pa nthawi yovutayi ndipo akhala akutithandiza nthawi yonseyi.” Zimatilimbikitsa kwambiri tikadziwa kuti tili ndi anzathu apamtima amene angatithandize kupirira mavuto athu.

MUZIKHALA ODALIRIKA NGATI TUKIKO

Tizikhala odalirika ngati Tukiko kwa abale amene akukumana ndi mavuto (Onani ndime 7-9) *

7-8. Malinga ndi Akolose 4:7-9, kodi Tukiko anasonyeza bwanji kuti anali wodalirika?

7 Munthu wina amene anali mnzake wokhulupirika wa Paulo anali Tukiko wochokera m’chigawo cha Asia. (Mac. 20:4) Cha m’ma 55 C.E., Paulo anakonza zoti abale apereke ndalama zothandizira Akhristu a ku Yudeya ndipo mwina anauza Tukiko kuti athandize pa ntchito yofunikayi. (2 Akor. 8:18-20) Pa nthawi ina pamene Paulo anamangidwa koyamba ku Roma, Tukiko anamuthandiza kwambiri. Iye ankatumiza kumipingo ya ku Asia makalata ndi mauthenga olimbikitsa amene Paulo analemba.​—Akol. 4:7-9.

8 Tukiko anakhalabe mnzake wa Paulo wodalirika. (Tito 3:12) Pa nthawiyo, si Akhristu onse amene anali odalirika ngati iyeyo. Cha m’ma 65 C.E., pa nthawi imene Paulo anamangidwa kachiwiri, iye analemba kuti abale ambiri am’chigawo cha Asia ankapewa kucheza naye mwina chifukwa choopa anthu otsutsa. (2 Tim. 1:15) Koma Paulo ankadalira kwambiri Tukiko ndipo anamupatsa utumiki wina. (2 Tim. 4:12) Paulo ayenera kuti ankayamikira kukhala ndi mnzake wokhulupirikayu.

9. Kodi tingatsanzire bwanji Tukiko?

9 Tingatsanzire Tukiko pokhala odalirika kwa anzathu. Mwachitsanzo, sitimangolonjeza kuti tidzathandiza abale ndi alongo athu pa mavuto koma timayesetsa kuwathandiza. (Mat. 5:37; Luka 16:10) Anthu amene akukumana ndi mavuto amalimbikitsidwa kwambiri akadziwa kuti akhoza kutidalira. Pa nkhani imeneyi, mlongo wina anati: “Zimathandiza kuti usamade nkhawa chifukwa chokayikira ngati anthu adzachitadi zimene analonjeza pa nthawi yake.”

10. Malinga ndi Miyambo 18:24, kodi anthu amene akukumana ndi mavuto angalimbikitsidwe ndi ndani?

10 Anthu amene akumana ndi mavuto amalimbikitsidwa akafotokoza zimene zili mumtima mwawo kwa mnzawo wodalirika. (Werengani Miyambo 18:24.) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Bijay yemwe mwana wake anachotsedwa. Iye anati: “Ndinkafunitsitsa kupeza munthu woti ndimufotokozere mmene ndinkamvera mumtima mwanga.” Nayenso M’bale Carlos atalakwitsa zinthu zina n’kuchotsedwa pa udindo anati: “Ndinkalakalaka kupeza anthu amene angandimvetsere popanda kundiweruza.” Akulu ndi amene anamumvetsera ndipo anamuthandiza kuti apirire vuto lakelo. Iye analimbikitsidwa kudziwa kuti akuluwo anali anzeru ndipo sangauze ena zimene iye ananenazo.

11. Kodi tingatani kuti anthu azitidalira komanso kutifotokozera zamumtima mwawo?

11 Kuti anthu azitidalira komanso kutifotokozera zamumtima mwawo, tiyenera kukhala oleza mtima. Mlongo wina dzina lake Zhanna atasiyidwa ndi mwamuna wake, ankalimbikitsidwa akafotokozera anzake apamtima mmene ankamvera. Iye anati: “Ankandimvetsera moleza mtima ngakhale kuti mwina ndinkangobwereza zinthu zimodzimodzi.” Nanunso mukhoza kukhala odalirika kwa anzanu mukamawamvetsera moleza mtima.

MUZIKONDA KUTUMIKIRA ENA NGATI MALIKO

Zinthu zabwino zimene Maliko anachitira Paulo zinamuthandiza kupirira mavuto ndipo ifenso tingathandize abale athu akamakumana ndi mavuto (Onani ndime 12-14) *

12. Kodi Maliko anali ndani, nanga anasonyeza bwanji kuti ankakonda kutumikira ena?

12 Maliko anali Mkhristu wachiyuda wochokera ku Yerusalemu. Msuweni wake dzina lake Baranaba anali mmishonale wodziwika bwino. (Akol. 4:10) Zikuoneka kuti Maliko ankachokera ku banja lochita bwino koma maganizo ake sanali pa chuma. Pa moyo wake wonse, ankasonyeza mtima wokonda kutumikira ena. Mwachitsanzo, iye ankatumikira limodzi ndi Paulo komanso Petulo. N’kutheka kuti ankawathandiza pa zinthu zina zofunika pa moyo kuti iwo asavutike kukwaniritsa utumiki wawo. (Mac. 13:2-5; 1 Pet. 5:13) Paulo ananena kuti Maliko anali mmodzi mwa ‘anzake pa zinthu zokhudzana ndi ufumu wa Mulungu, ndipo anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’​—Akol. 4:10, 11.

13. Kodi lemba la 2 Timoteyo 4:11 limasonyeza bwanji kuti Paulo ankayamikira zimene Maliko ankamuchitira?

13 Maliko anali mmodzi mwa anthu amene ankagwirizana kwambiri ndi Paulo. Mwachitsanzo, pamene Paulo anamangidwa komaliza ku Roma cha m’ma 65 C.E., analemba kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo. M’kalatayo, Paulo anapempha Timoteyo kuti abwere ku Roma limodzi ndi Maliko. (2 Tim. 4:11) N’zosakayikitsa kuti Paulo ankayamikira zimene Maliko anachita pomuthandiza ndipo ankafuna kuti akhalenso naye pa nthawi yovutayi. N’kutheka kuti Maliko ankathandiza Paulo pomupatsa chakudya kapena zipangizo zogwiritsa ntchito polemba. Zimene anthu ena ankamuchitira Paulo zinamuthandiza kuti apirire mpaka pamene anaphedwa.

14-15. Kodi lemba la Mateyu 7:12 limatiphunzitsa chiyani pa nkhani yothandiza anthu ena?

14 Werengani Mateyu 7:12. Tikakumana ndi mavuto, timayamikira kwambiri ngati anthu ena atithandiza. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Ryan amene bambo ake anafa pa ngozi. Iye anati: “Munthu ukakhala pamavuto, zinthu zina za tsiku ndi tsiku zimakhala zovuta. Ndiye anthu akakuchitira zinthu ngakhale zitakhala zazing’ono, zimakuthandiza kwambiri.”

15 Tikakhala tcheru, tikhoza kupeza njira zimene tingathandizire anzathu. Mwachitsanzo, mlongo wina anathandiza Peter ndi Kathryn, omwe tawatchula kale aja, kuti azipita kuchipatala akafunika kuonana ndi dokotala. Peter ndi Kathryn sankathanso kuyendetsa galimoto choncho mlongoyu anakonza zoti abale ndi alongo osiyanasiyana aziwayendetsa. Zimenezi zinathandiza kwambiri chifukwa Kathryn ananena kuti: “Tinamva ngati atilandira chikatundu cholemera.” Dziwani kuti zimene mungachitire anthu ena pa nthawi yamavuto, ngakhale zitakhala zochepa, zingawathandize kwambiri.

16. Kodi tikuphunzira chiyani kwa Maliko pa nkhani yolimbikitsa ena?

16 Maliko ayenera kuti ankatanganidwa ndithu. Iye anali ndi zochita zambiri monga kulemba buku la Uthenga Wabwino lodziwika ndi dzina lake. Koma ankayesetsa kulimbikitsa Paulo moti Pauloyo anali womasuka kupempha kuti iye amuthandize. Mlongo wina dzina lake Angela anayamikiranso kwambiri pamene anthu ena anamulimbikitsa wachibale wake ataphedwa. Iye anati: “Anthu amene ali ndi mtima wofuna kuthandiza amakhala osavuta kulankhula nawo ndipo samangika kapena kukayikira pothandiza anzawo.” Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi anthu amaona kuti ndili ndi mtima wofuna kuthandiza anthu ena pa mavuto awo?’

MUSASIYE KULIMBIKITSA ENA

17. Kodi lemba la 2 Akorinto 1:3, 4 lingatithandize bwanji kuti tizilimbikitsa anthu ena?

17 Pali abale ndi alongo ambiri amene amafunika kulimbikitsidwa. Powalimbikitsa, tikhoza kugwiritsa ntchito mfundo zimene anthu ena anatilimbikitsa nazo. Chitsanzo ndi mlongo wina dzina lake Nino yemwe agogo ake anamwalira. Iye anati: “Ngati ifeyo titalola, Yehova angatigwiritse ntchito kuti alimbikitse anthu ena.” (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Frances, amene tamutchula kale uja, anati: “Mawu a pa 2 Akorinto 1:4 ndi oona. Timatha kulimbikitsa ena chifukwa choti anthu ena atilimbikitsa ifeyo.”

18. (a) N’chifukwa chiyani anthu ena angaope kulimbikitsa anzawo? (b) Kodi tingalimbikitse bwanji anthu ena? Perekani chitsanzo.

18 Tiyenera kuthandiza anthu ngakhale pamene tikuopa kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, tikhoza kuchita mantha chifukwa chosadziwa zimene tinganene kapena kuchita pothandiza munthu amene wakumana ndi mavuto. M’bale wina dzina lake Paul, yemwe ndi mkulu, akukumbukira zimene anthu ena anachita bambo ake atamwalira. Iye anati: “Ndinkadziwa kuti sizinali zophweka kuti alankhule nane. Iwo ankavutika kupeza mawu abwino. Koma ndinkayamikira kuti ankafunitsitsa kundilimbikitsa komanso kundithandiza.” Chitsanzo china ndi cha m’bale wina dzina lake Tajon yemwe anakhudzidwa ndi chivomezi champhamvu. Iye anati: “Kunena zoona, sindikukumbukira mauthenga amene anthu ananditumizira, koma chimene ndikukumbukira n’chakuti ankandidera nkhawa.” Tikamasonyeza kuti timaganizira anthu ena tikhoza kuwalimbikitsa kwambiri.

19. N’chifukwa chiyani mumafunitsitsa kulimbikitsa komanso kuthandiza anthu ena?

19 Pamene mapeto akuyandikira, zinthu zikhoza kuipiraipira ndipo tingakumane ndi mavuto ambiri. (2 Tim. 3:13) Popeza ndife ochimwa, tidzapitiriza kulakwitsa zinthu zina n’kudzibweretsera mavuto ndipo tidzafunika kulimbikitsidwa. Mtumwi Paulo anakwanitsa kupirira mpaka mapeto a moyo wake ndipo ena amene anamuthandiza anali Akhristu anzake. Tiyeni tiziyesetsa kukhala okhulupirika ngati Arisitako, odalirika ngati Tukiko komanso okonda kutumikira ena ngati Maliko. Tikamachita zimenezi, tidzatha kuthandiza abale ndi alongo athu kuti asasiye kutumikira Yehova mokhulupirika.​—1 Ates. 3:2, 3.

^ ndime 5 Mtumwi Paulo anakumana ndi mavuto ambiri pa moyo wake. Koma panali antchito anzake ena amene ankamuthandiza komanso kumulimbikitsa kwambiri. Munkhaniyi tikambirana makhalidwe atatu amene anathandiza anthuwo kuti akhale olimbikitsa. Tikambirananso zimene tingachite powatsanzira.

^ ndime 5 Mayina ena munkhaniyi asinthidwa.

NYIMBO NA. 111 Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala

^ ndime 56 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Arisitako anali ndi Paulo pamene ngalawa inasweka.

^ ndime 58 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Paulo anapempha Tukiko kuti akapereke makalata ake kumipingo.

^ ndime 60 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Maliko anathandiza Paulo m’njira zambiri.