Kodi Mukudziwa?
Kodi zolemba pamwala zimene zapezeka zikugwirizana bwanji ndi Baibulo?
KUMALO ena osungirako zinthu zakale ku Jerusalem, kuli mwala umene uli ndi zolemba, zimene zinalembedwa m’zaka za pakati pa 700-600 B.C.E. (Bible Lands Museum). Mwalawu anaupeza kuphanga la manda ena kufupi ndi mzinda wa Hebron ku Israel. Pamwalawu pali mawu akuti: “Hagaf mwana wa Hagav wotembereredwa ndi Yahweh Sabaot.” Kodi mawu amene analembedwa pamwalawa akugwirizana bwanji ndi zimene Baibulo limanena? Mawuwa akusonyeza kuti dzina la Mulungu lakuti Yehova, lomwe limalembedwa kuti YHWH mu Chiheberi linali lodziwika ndipo linkagwiritsidwa ntchito kwambiri m’nthawi yakale. M’makoma a mapangawa mulinso dzina lodziwika la Mulungu komanso mayina ena a anthu okhala ndi mbali ya dzina la Mulungu. Anthu ena ankagwiritsa ntchito mapangawa ngati malo okumanirako kapena obisalirako ndipo ndi amene ankalemba zimenezi.
Ponena za zolemba zimene zinapezekazi, Dr. Rachel Nabulsi wa kuyunivesite ya Georgia ananena kuti: “M’zolembazi dzina lakuti YHWH likupezekamo kambirimbiri. . . . Zimenezi zikusonyeza kuti dzinali linali lofunika kwambiri kwa anthu a ku Isiraeli ndi ku Yuda.” Izi zikusonyezanso kuti Baibulo ndi lolondola, chifukwa dzina la Mulungu lokhala ndi zilembo zimenezi za Chiheberi, limapezekamo nthawi masauzande ambiri. Komanso m’Baibulo muli mayina a anthu okhala ndi mbali ya dzina la Mulungu.
Mawu akuti “Yahweh Sabaot,” omwe analembedwa pamwalawu, amatanthauza kuti “Yehova wamakamu.” Choncho zikuoneka kuti anthu a m’nthawi yakale ankakonda kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso mawu akuti “Yehova wamakamu.” Izi zikutsimikiziranso kuti Baibulo ndi lolondola, chifukwa mawu akuti “Yehova wamakamu” amapezeka m’malo 283 m’Malemba a Chiheberi, makamaka m’mabuku a Yesaya, Yeremiya ndi Zekariya.