Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 1

Musamatekeseke Ndipo Muzidalira Yehova

Musamatekeseke Ndipo Muzidalira Yehova

LEMBA LA CHAKA CHA 2021: “Mudzakhala Amphamvu Mukakhala Osatekeseka ndi Achikhulupiriro.”​—YES. 30:15

NYIMBO NA. 3 Ndinu Mphamvu Zathu, Chiyembekezo Chathu, Komanso Timakudalirani

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Mofanana ndi Mfumu Davide, Kodi anthu ena angafunse funso liti?

TONSEFE timafuna tizikhala mosatekeseka komanso mwamtendere. Palibe amene amafuna kuti azida nkhawa. Komabe nthawi zina tingakumane ndi zinthu zimene zingatidetse nkhawa. Zimenezi zingachititse atumiki ena a Yehova kufunsa funso lofanana ndi limene Mfumu Davide anafunsa Yehova, lakuti: “Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikira liti? Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi chisoni kufikira liti?”​—Sal. 13:2.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Ngakhale kuti sitingapeweretu kuda nkhawa, pali zambiri zimene tingachite kuti tichepetse nkhawazo. Munkhaniyi, tikambirana zinthu zina zimene zimatichititsa kuti tizida nkhawa. Tikambirananso zinthu 6 zimene zingatithandize kuti tisamatekeseke tikamalimbana ndi mavuto amene tikukumana nawo.

KODI NDI ZINTHU ZITI ZIMENE ZINGATICHITITSE KUDA NKHAWA?

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimatichititsa kuti tizida nkhawa, nanga kodi n’zotheka kuzipewa kapena kuzithetsa?

3 Pali zinthu zambiri zimene zingatichititse kuti tizida nkhawa, ndipo zina mwa zimenezi sitingaziletse kuti zisamachitike. Mwachitsanzo, chaka chilichonse sitingaletse kukwera mitengo kwa zinthu monga chakudya, zovala kapena nyumba. Komanso sitingadziwiretu kuti anzathu a ku ntchito kapena kusukulu adzatiyesa kangati kuti tikhale osakhulupirika, kapena kuti tichite makhalidwe oipa. Sitingaletsenso anthu a m’dera limene timakhala kuti asamachite zinthu zophwanya malamulo. Timakumana ndi mavuto amenewa chifukwa tikukhala m’dziko limene anthu ake satsatira mfundo za m’Baibulo. Satana, yemwe ndi mulungu wa nthawi ino, amadziwa kuti “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino” zingachititse anthu ena kusiya kutumikira Mulungu. (Mat. 13:22; 1 Yoh. 5:19) Choncho n’zosadabwitsa kuti m’dzikoli muli mavuto ambiri amene amachititsa kuti anthu azida nkhawa.

4. Kodi n’chiyani chingachitike ngati tikuda nkhawa kwambiri?

4 Nthawi zina anthufe tingamade nkhawa mpaka kufika posiya kuganiza bwino. Mwachitsanzo, tikhoza kumada nkhawa kuti sitizipeza ndalama zokwanira zogulira zinthu zofunika pa moyo wathu, tidwala mpaka kujomba kuntchito, komanso kuti mwina ntchito ikhoza kutithera. Tikhozanso kumaona ngati tidzalephera kukhala okhulupirika tikadzayesedwa kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Posachedwapa Satana adzachititsa anthu amene iyeyo amawatsogolera kuti aukire atumiki a Mulungu. Choncho tikhoza kumada nkhawa n’kumaganiza kuti ‘kodi tidzatani zimenezi zikadzachitika?’ Ndiye mwina mungamadzifunse kuti: ‘Kodi n’kulakwa kukhala ndi nkhawa pa nkhani zimenezi?’

5. Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Lekani kudera nkhawa”?

5 Tikudziwa kuti Yesu anauza otsatira ake kuti: “Lekani kudera nkhawa.” (Mat. 6:25) Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yesu ankayembekezera kuti sitizida nkhawa ndi chilichonse? Ayi. Ndipotu atumiki ena a Yehova okhulupirika m’mbuyomu anadapo nkhawa ndi zinthu zina. Koma si kuti Yehova anasiya kuwakonda. * (1 Maf. 19:4; Sal. 6:3) Apa Yesu ankafuna kutithandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri kuti tipeza bwanji zinthu zimene tikufuna, mpaka kufika polephera kuona kuti utumiki wathu kwa Mulungu ndi wofunika. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tizichepetsa nkhawa?​—Onani bokosi lakuti “ Mmene Mungachitire Zimenezi.”

ZINTHU 6 ZIMENE ZINGATITHANDIZE KUTI TISAMATEKESEKE

Onani ndime 6 *

6. Mogwirizana ndi Afilipi 4:6, 7, kodi n’chiyani chingatithandize kuchepetsa nkhawa?

6 (1) Muzipemphera nthawi zonse. Akhristu amene akumana ndi mavuto amene akuwachititsa kuda nkhawa angalimbikitsidwe ngati atapemphera kwa Yehova. (1 Pet. 5:7) Yehova adzayankha mapemphero athu potipatsa ‘mtendere umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.’ (Werengani Afilipi 4:6, 7.) Iye adzatithandiza kuchepetsa nkhawa zathu potipatsa mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu.​—Agal. 5:22.

7. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamapemphera kwa Mulungu?

7 Mukamapemphera kwa Yehova muzimuuza momasuka zimene zili mu mtima mwanu. Muzitchula zenizeni zimene mukufuna kuti akuchitireni. Muzimuuza mavuto anu ndipo muzimufotokozera mmene mukumvera. Ngati vuto limene mwakumana nalo ndi loti likhoza kuthetsedwa, muzimupempha kuti akupatseni nzeru kuti mudziwe zoyenera kuchita komanso mphamvu zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezo. Koma ngati vutolo ndi loti silingathe, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti musade nkhawa kwambiri. Mukamatchula zenizeni zimene mukufuna popemphera, m’kupita kwa nthawi mudzaona mmene Yehova wayankhira mapemphero anuwo. Koma ngati Yehova sanayankhe nthawi yomweyo, musamagwe ulesi. Si kuti Yehova amangofuna kuti muzimuuza zimene mukufuna m’pemphero koma amafunanso kuti muzipemphera kwa iye mosalekeza.​—Luka 11:8-10.

8. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene tingatchule m’mapemphero athu?

8 Mukamamufotokozera Yehova nkhawa zanu m’pemphero musamaiwalenso kumuthokoza. Muyenera kumaganizira zinthu zabwino zimene Yehova wakuchitirani, ngakhale pamene mukukumana ndi mavuto. Ngati nthawi zina mumalephera kupeza mawu abwino oti mufotokozere mmene mukumvera, muzikumbukira kuti Yehova akhoza kumva pemphero lanu ngakhale litangokhala lonena kuti: ‘Chonde ndithandizeni.’​—2 Mbiri 18:31; Aroma 8:26.

Onani ndime 9 *

9. Kodi tingatani kuti tipeze chitetezo chenicheni?

9 (2) Muzidalira nzeru za Yehova osati nzeru zanu. Cha m’ma 700 B.C.E., Ayuda ankaopa kuti akhoza kuukiridwa ndi Asuri. Chifukwa choti sankafuna kukhala pansi pa ulamuliro wankhanza wa Asuriwo, iwo anayamba kupempha thandizo kwa Aigupto. (Yes. 30:1, 2) Yehova anawachenjeza kuti ngati atapitiriza kudalira Aigupto zinthu sizidzawayendera bwino. (Yes. 30:7, 12, 13) Kudzera mwa mneneri Yesaya, iye anauza Ayudawo zimene angachite kuti apeze chitetezo chenicheni. Iye anawauza kuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”​—Yes. 30:15b.

10. Kodi ndi pa zochitika zina ziti pamene tiyenera kusonyeza kuti timakhulupirira Yehova?

10 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova? Taganizirani zitsanzo izi. Tiyerekeze kuti mwapeza ntchito imene muzilandira ndalama zambiri koma muzifunika kugwira ntchitoyo kwa maola ambiri, ndipo muzilephera kupeza nthawi yochita zinthu zokhudza kulambira. Kapena tiyerekeze kuti munthu wina amene mumagwira naye ntchito wakopeka nanu, koma satumikira Mulungu. Komanso bwanji ngati munthu wa m’banja lanu atakuuzani kuti, ‘Musankhepo pakati pa ine kapena Mulungu.’ Pa zochitika zonsezi, mwina zingakuvuteni kusankha zochita. Komatu Yehova akhoza kukuthandizani kudziwa zoyenera kuchita. (Mat. 6:33; 10:37;1 Akor. 7:39) Ndiye funso ndi lakuti, Kodi mudzadalira malangizo amene Yehova angakupatseni?

Onani ndime 11 *

11. Kodi ndi nkhani za m’Baibulo ziti zimene zingatithandize kuti tisamachite mantha tikamatsutsidwa?

11 (3) Muziphunzira pa zitsanzo za anthu otchulidwa m’Baibulo zoyenera kutengera komanso zoyenera kupewa. M’Baibulo muli nkhani zambiri zimene zimafotokoza chifukwa chake tiyenera kukhala olimba mtima n’kumadalira Yehova. Mukamaphunzira nkhanizi muziganizira zimene zinathandiza atumiki a Mulungu kupitirizabe kukhala olimba mtima pamene ankatsutsidwa. Mwachitsanzo, panthawi imene khoti lalikulu la Ayuda linalamula atumwi kuti asiye kulalikira, iwo sanachite mantha. M’malomwake iwo ananena molimba mtima kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:29) Ngakhale kuti anakwapulidwa, iwo sanatekeseke. Chifukwa chiyani? Iwo ankadziwa kuti Yehova ali kumbali yawo ndipo ankasangalala nawo. Choncho anapitirizabe kulengeza uthenga wabwino. (Mac. 5:40-42) Nayenso Sitefano panthawi imene ankaphedwa, ankaoneka kuti sakuchita mantha moti mpaka nkhope yake inafika pooneka “ngati nkhope ya mngelo.” (Mac. 6:12-15) N’chifukwa chiyani iye sankachita mantha? Chifukwa anali wotsimikiza kuti Yehova akusangalala naye.

12. Mogwirizana ndi 1 Petulo 3:14 ndi 4:14, n’chifukwa chiyani tiyenera kumasangalala pamene tikuzunzidwa?

12 Atumwi anali ndi umboni wokwanira wotsimikizira kuti Yehova anali nawo. Iye anali atawapatsa mphamvu kuti azitha kuchita zodabwitsa. (Mac. 5:12-16; 6:8) Koma umu si mmene zili ndi ife masiku ano. Yehova satipatsa mphamvu zochita zodabwitsa ngati kale. Koma ngakhale zili choncho, kudzera m’Mawu ake mwachikondi amatitsimikizira kuti ngati titavutika chifukwa cha chilungamo iye amasangalala nafe ndipo mzimu wake umakhala nafe. (Werengani 1 Petulo 3:14; 4:14.) Choncho m’malo moganizira zomwe tidzachite tikamadzazunzidwa m’tsogolo, tiziganizira zimene tiyenera kuchita kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova kuti adzatithandiza komanso kutipulumutsa. Mofanana ndi Akhristu oyambirira, tiyenera kukhulupirira lonjezo la Yesu lakuti: “Ndidzakuuzani mawu oti munene ndikukupatsani nzeru, zimene otsutsa anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.” Anatilonjezanso kuti: “Ngati inu mudzapirire, mudzapeza moyo.” (Luka 21:12-19) Komanso tisamaiwale kuti Yehova amakumbukira ngakhale tinthu ting’onoting’ono tokhudza atumiki ake omwe anamwalira ali okhulupirika n’cholinga choti adzawaukitse.

13. Kodi tingapindule bwanji tikamaganizira zitsanzo za anthu amene analephera kudalira Yehova?

13 Tingaphunzirenso kanthu pa zitsanzo za anthu ena amene analephera kudalira Yehova. Kuphunzirapo pa zitsanzo zoipa za anthu amenewa kungatithandize kuti ifenso tisadzachite zimene iwo analakwitsa. Mwachitsanzo kumayambiriro kwa ulamuliro wake, Asa yemwe anali mfumu ya Yuda anadalira Yehova ataukiridwa ndi gulu lalikulu la asilikali, ndipo Yehova anamudalitsa moti anapambana. (2 Mbiri 14:9-12) Koma patapita nthawi, ataukiridwa ndi gulu lochepa la asilikali a Mfumu Basa ya ku Isiraeli, Asa sanadalire Yehova kuti amupulumutse ngati mmene anachitira poyamba. M’malomwake anakapereka ndalama kwa asilikali a Asuri n’cholinga choti amuthandize. (2 Mbiri 16:1-3) Komanso kumapeto kwa moyo wake atadwala kwambiri, iye sanadalire Yehova kuti amuthandize.​—2 Mbiri 16:12.

14. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Asa analakwitsa?

14 Poyamba Asa anadalira Yehova atakumana ndi mavuto. Koma m’kupita kwa nthawi iye sanadalire Mulungu ndipo ankaona kuti akhoza kuthana nawo yekha. Kwa ena, zimene anachita Asa popempha Asuri kuti amuthandize pamene ankalimbana ndi Aisiraeli zingaoneke ngati zothandiza. Koma zimenezi zinangothandiza kwa kanthawi kochepa. Yehova anauza Mfumu Asa kudzera mwa mneneri kuti: “Chifukwa chakuti munadalira mfumu ya Siriya, osadalira Yehova Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya Siriya lathawa m’manja mwanu.” (2 Mbiri 16:7) Tiyenera kukhala osamala kuti tisamadzidalire n’kumaona kuti tikhoza kuthetsa tokha mavuto, m’malo modalira Yehova kuti atithandize kudzera m’mawu ake Baibulo. Ngakhale pamene tikufuna kusankha zochita mofulumira, tizichita zinthu mopanda mantha komanso kudalira Yehova, ndipo iye adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino.

Onani ndime 15 *

15. Kodi tizichita chiyani tikamawerenga Baibulo?

15 (4) Muziloweza mavesi a m’Baibulo. Mukamawerenga Baibulo n’kupeza mavesi amene akusonyeza kuti mungapeze mphamvu chifukwa chodalira Yehova, muziyesa kuloweza mavesi amenewo. Kuti muloweze muziwawerenga motulutsa mawu kapena kuwalemba penapake n’kumawawerenga mobwerezabwereza. Yoswa analamulidwa kuwerenga komanso kuganizira zimene zinali m’buku la Chilamulo n’cholinga choti azichita zinthu mwanzeru. Zimene akanawerenga zikanamuthandiza kuti asamachite mantha koma azichita zinthu molimba mtima potsogolera anthu a Mulungu. (Yos. 1:8, 9) Inunso zimene mungawerenge m’Mawu a Mulungu zingakuthandizeni kukhala ndi mtendere wam’maganizo ngakhale pa nthawi imene mwakumana ndi zinthu zomwe zikanachititsa kuti muzida nkhawa kapena kuchita mantha.​—Sal. 27:1-3; Miy. 3:25, 26.

Onani ndime 16 *

16. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji abale ndi alongo mumpingo pofuna kutithandiza kuti tisamachite mantha koma tizimudalira iyeyo?

16 (5) Muzichita zinthu ndi anthu a Mulungu. Yehova amagwiritsa ntchito abale ndi alongo athu pofuna kutithandiza kuti tisamachite mantha koma tizimudalira iyeyo. Tikakhala pamisonkhano timapindula ndi malangizo a mu nkhani zimene abale amakamba, ndemanga zimene abale ndi alongo amapereka komanso nkhani zolimbikitsa zimene timacheza ndi abale ndi alongo athu. (Aheb. 10:24, 25) Timalimbikitsidwanso kwambiri tikamafotokozera anzathu a mumpingo zinthu zimene zikutidetsa nkhawa. “Mawu abwino” ochokera kwa anzathuwo angatithandize kuti tichepetse nkhawa.​—Miy. 12:25.

Onani ndime 17 *

17. Mogwirizana ndi Aheberi 6:19, kodi chiyembekezo cha Ufumu chingatithandize bwanji kuti tisamachite mantha tikakumana ndi mavuto?

17 (6) Muzikhala ndi chiyembekezo champhamvu. Chiyembekezo chathu cha Ufumu chili “ngati nangula wa miyoyo yathu,” ndipo chimatithandiza kuti tisamatekeseke tikakumana ndi mavuto kapena zinthu zodetsa nkhawa. (Werengani Aheberi 6:19.) Muziganizira zimene Yehova watilonjeza m’tsogolo pa nthawi imene sipadzakhalanso chilichonse chotidetsa nkhawa. (Yes. 65:17) Muzidziyerekezera muli m’dziko latsopano la mtendere momwe simudzakhalanso zinthu zoipa. (Mika 4:4) Mukamauzanso ena zokhudza dziko latsopano mumayamba kukhulupirira kwambiri zimene mukuyembekezera. Muzichita zonse zimene mungathe mukamagwira ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu. Kuchita zimenezi kungathandize “kuti chiyembekezo chanu chikhale chotsimikizika mpaka mapeto.”​—Aheb. 6:11.

18. Kodi n’chiyani chichitike m’tsogolomu, nanga n’chiyani chingatithandize kuti tisamade nkhawa?

18 Pamene mapeto a dziko loipali akuyandikira tizikumana ndi mavuto amene azitipangitsa kuti tizida nkhawa. Lemba la chaka cha 2021 lingatithandize kuti tikakumana ndi mavutowa tisamade nkhawa ndipo tizidalira Yehova osati kudalira mphamvu zathu. Tiyeni tiyesetse kuti chaka chimenechi zochita zathu zizisonyeza kuti tikukhulupirira lonjezo la Yehova lakuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”​Yes. 30:15.

NYIMBO NA. 8 Yehova Ndiye Pothawirapo Pathu

^ ndime 5 Lemba la chaka cha 2021 likufotokoza chifukwa chake tiyenera kudalira Yehova tikakumana ndi mavuto amene amatidetsa nkhawa panopa, komanso amene tingakumane nawo m’tsogolo. Nkhaniyi ifotokoza zimene tingachite kuti tizitsatira malangizo a mulembali.

^ ndime 5 Abale ndi alongo ena okhulupirika amadwala matenda obwera chifukwa cha nkhawa kapena kupanikizika. Nkhawa zamtunduwu ndi vuto lalikulu limene limawononga thanzi la munthu, ndipo ndi zosiyana ndi nkhawa zimene Yesu ananena.

^ ndime 63 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (1) Mlongo akupemphera mochokera pansi pamtima, kumufotokozera Yehova nkhawa zake.

^ ndime 65 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (2) Pa nthawi yopuma kuntchito iye akufufuza m’Mawu a Mulungu kuti apeze nzeru.

^ ndime 67 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (3) Iye akuganizira zitsanzo zoyenera kutengera komanso zoyenera kupewa za anthu a m’Baibulo.

^ ndime 69 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (4) Iye akumata pa firiji lemba lolimbikitsa loti aliloweze.(5) Iye amasangalala akakhala ndi anzake mu utumiki.

^ ndime 71 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (5) Iye amasangalala akakhala ndi anzake mu utumiki.

^ ndime 73 MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: (6) Kuganizira za m’tsogolo kukumuthandiza kuti azikhulupirira kwambiri zimene akuyembekezera.